Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 10:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo mfumu Solomoni ananinkha mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse anachipempha iye, osawerenga chimene Solomoni anamninkha mwa ufulu wake. Momwemo iye anabwerera namukanso ku dziko lake, iyeyo ndi anyamata ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo mfumu Solomoni ananinkha mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse anachipempha iye, osawerenga chimene Solomoni anamninkha mwa ufulu wake. Momwemo iye anabwerera namukanso ku dziko lake, iyeyo ndi anyamata ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Mfumu Solomoni adapatsa mfumukazi ya ku Sheba ija zonse zimene inkafuna, ndiponso chilichonse chimene idaapempha, osaŵerengera mphatso zachifumu zimene anali ataipatsa kale. Tsono mfumukaziyo idabwerera ku dziko lakwao pamodzi ndi atumiki ake aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha, osawerengera mphatso zaufumu zimene anali atamupatsa. Choncho inabwerera ku dziko la kwawo pamodzi ndi atumiki ake.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 10:13
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oimbawo; siinafike kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa.


Tsono kulemera kwake kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi kunali matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide.


Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wake waukulu, ndi ngamira zakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.


Ndipo kunali, atatsiriza Solomoni kumanga nyumba ya Yehova, ndi nyumba ya mfumu, ndi chifuniro chonse cha Solomoni anachikhumbacho,


Ndipo mfumu Solomoni anampatsa mfumu yaikazi ya ku Sheba chifuniro chake chonse, chilichonse anachipempha, osawerengera zija adabwera nazo kwa mfumu. Momwemo anabwerera, namuka ku dziko lake, iyeyu ndi anyamata ake.


likupatse cha mtima wako, ndipo likwaniritse upo wako wonse.


Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.


Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.


Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa