1 Mafumu 10:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oimbawo; siinafike kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo mfumu inasema mitengo yambawayo, ikhale mizati ya nyumba ya Yehova, ndi ya nyumba ya mfumu; ndiponso azeze ndi zisakasa za oimbawo; siinafika kapena kuonekanso mpaka lero mitengo yotero yambawa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Mitengo imeneyo mfumuyo idasemera mizati yochirikizira Nyumba ya Chauta ndi ina yochirikizira nyumba yachifumu. Adasemanso azeze ndi apangwe a anthu oimba. Panalibe mitengo yotere imene idabweranso kapena kuwonekanso mu Israele mpaka lero lino. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya alimugi ngati yochirikizira Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndipo anapangiranso azeze ndi apangwe a anthu oyimba. Mitengo yotere sinayitanitsidweponso kapena kuoneka mpaka lero lino). Onani mutuwo |