Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 1:2 - Buku Lopatulika

2 Pamenepo anyamata ake ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Pamenepo anyamata ake ananena naye, Amfunire mbuye wanga mfumu namwali, aimirire pamaso pa mfumu namsunge; nagone m'mfukato mwanu, kuti mbuye mfumu yanga afundidwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Nchifukwa chake nduna zake zidamuuza kuti, “Inu amfumu, tikupezereni namwali woti azikusungani ndi kumakusamalani. Namwaliyo azigona pafupi nanu kuti inu amfumu muzifundidwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Choncho nduna zake zinamuwuza kuti, “Tiloleni tifune namwali woti azikhala nanu ndi kumakusamalirani. Namwaliyo azigona pafupi nanu kuti mbuye wathu mfumu muzimva kufundira.”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 1:2
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.


koma wosaukayo analibe kanthu kena koma kamwana kakakazi ka nkhosa, kamene anakagula ndi kukaweta; ndipo kameneko kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kanadyako chakudya chake cha iye yekha, kanamwera m'chikho cha iye yekha, kanagona pa chifukato chake, ndipo kanali kwa iye ngati mwana wake wamkazi.


Ndipo mfumu Davide anakalamba nachuluka masiku ake; ndipo iwo anamfunda ndi zofunda, koma iye sanafundidwe.


Tsono anafunafuna m'malire monse a Israele namwali wokongola, napeza Abisagi wa ku Sunamu, nabwera naye kwa mfumu.


Ana anga, musazengereza tsopano; popeza Yehova anakusankhani inu muime pamaso pake, kumtumikira Iye, ndi kuti mukhale atumiki ake ndi kufukiza zonunkhira.


Pamenepo anyamata a mfumu omtumikira anati, Amfunire mfumu anamwali okongola;


Ndiponso awiri akagona limodzi afunditsana; koma mmodzi pa yekha kodi adzafunditsidwa bwanji?


Musakhulupirira bwenzi, musatama bwenzi loyanja; usamtsegulire pakhomo pakamwa pako, ngakhale kwa iye wogona m'fukato mwako.


Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino.


Mbale wanu, ndiye mwana wa mai wanu, kapena mwana wanu wamwamuna, kapena mwana wanu wamkazi, kapena mkazi wa kumtima kwanu, kapena bwenzi lanu, ndiye ngati moyo wanuwanu, akakukakamizani m'tseri, ndi kuti, Tipite titumikire milungu ina, imene simunaidziwe, inu, kapena makolo anu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa