Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 1:17 - Buku Lopatulika

17 Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Bateseba adati, “Ai nkwabwino. Koma mbuyanga, paja inu mudaandilonjeza molumbira ine mdzakazi wanu m'dzina la Chauta Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye amene adzaloŵe ufumu m'malo mwanga, nadzakhala pa mpando wanga.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga, inu mwini munalumbira kwa ine mdzakazi wanu mʼdzina la Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwa ine, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.’

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 1:17
7 Mawu Ofanana  

ndipo Sara anaseka m'mtima mwake, nati, Kodi ndidzakhala ndi kukondwa ine nditakalamba, ndiponso mbuyanga ali wokalamba?


Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirire mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?


Taona, uli chilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.


Ndipo Bateseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji?


Ndipo tsopano taonani, Adoniya walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu simudziwa.


zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israele, ndi kuti, Zoonadi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.


monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chilichonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa