Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 1:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo Bateseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Bateseba anawerama nalambira mfumu, ndi mfumu niti, Ufunanji?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Bateseba adagwada nalambira mfumu. Tsono mfumu idamufunsa kuti, “Kodi nkwabwino?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Batiseba anagwada nalambira mfumu. Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi nʼchiyani chimene ukufuna?”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 1:16
10 Mawu Ofanana  

Pamenepo Bateseba analowa kwa mfumu kuchipinda; ndipo mfumuyo inali yokalamba ndithu; ndipo Abisagi wa ku Sunamu anali kutumikira mfumu.


Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu.


Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu.


Pamenepo mkaziyo anati, Ndikupemphani kapempho kamodzi, musandikaniza. Ndipo mfumu inati kwa iye, Tapemphani amai wanga, popeza sindikukanizani.


Nitinso mfumu kwa Estere tsiku lachiwirili pa madyerero a vinyo, Pempho lanu nchiyani, mkazi wamkulu Estere? Lidzapatsidwa kwa inu; mufunanji? Chidzachitika, kufikira limodzi la magawo awiri a ufumu wanga.


Ndipo Iye anati kwa iye, Ufuna chiyani? Iye ananena, Lamulirani kuti ana anga awiri amenewa adzakhale, wina ku dzanja lanu lamanja, ndi wina kulamanzere, mu ufumu wanu.


Ndipo Yesu anaima, nawaitana, nati, Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani?


Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.


Bwino lake Davide yemwe ananyamuka, natuluka m'phangamo, nafuulira Saulo, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakucheuka Saulo, Davide anaweramira nkhope yake pansi, namgwadira.


Ndipo Abigaile pakuona Davide, anafulumira kutsika pabulu, nagwa pamaso pa Davide nkhope yake pansi, namgwadira,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa