Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 1:13 - Buku Lopatulika

13 Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirire mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirira mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Pitani msanga kwa mfumu Davide, mukamfunse kuti, ‘Kodi inu mbuyanga mfumu, suja mudandilonjeza molumbira ine mdzakazi wanu, kuti mwana wanga Solomoni ndiye amene adzaloŵe ufumu m'malo mwanu nadzakhala pa mpando wanu m'malo mwanu? Nanga chifukwa chiyani Adoniya waloŵa ufumu?’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Pitani msanga kwa Mfumu Davide ndipo mukanene kuti, ‘Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbire kwa ine mdzakazi wanu kuti, ‘Ndithu mwana wako Solomoni ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwanga, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu?’ Nanga nʼchifukwa chiyani Adoniya walowa ufumu?’

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 1:13
16 Mawu Ofanana  

Pamenepo Natani ananena ndi Bateseba amake wa Solomoni, nati, Kodi sunamve kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa?


Taona, uli chilankhulire ndi mfumu, inenso ndidzalowa pambuyo pako, ndi kutsimikiza mau ako.


Ndipo iye ananena nayo, Mbuye wanga, munalumbirira mdzakazi wanu pa Yehova Mulungu wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu.


Ndipo Natani anati, Mbuye wanga mfumu, kodi inu munati, Adoniya adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala ndiye pa mpando wanga wachifumu?


zedi monga umo ndinalumbirira iwe pa Yehova Mulungu wa Israele, ndi kuti, Zoonadi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu m'malo mwa ine, zedi nditero lero lomwe.


Pamenepo mumtsate iye, iye nadzadza nadzakhala pa mpando wanga wachifumu, popeza adzakhala iyeyu mfumu m'malo mwanga; ndipo ndamuika iye akhale mtsogoleri wa Israele ndi Yuda.


Ndiponso watero mfumu, Wolemekezeka Yehova Mulungu wa Israele, amene wapereka lero wina wokhala pa mpando wanga wachifumu, maso anga ali chipenyere.


Tsono Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo ufumu wake unakhazikika kwakukulu.


ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.


Momwemo Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Yehova, ndiye mfumu m'malo mwa Davide atate wake, nalemerera, namvera iye Aisraele onse.


Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.


pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wakulamulira pa mpando wa ufumu wake; ndiponso ndi Alevi ansembe, atumiki anga.


Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wachifumu wa ufumu wake, adzilemberere chofanana cha chilamulo ichi m'buku, achitenge pa ichi chili pamaso pa ansembe Alevi;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa