Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 1:12 - Buku Lopatulika

12 Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomoni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ubwere tsono, ndikupangire, kuti usunge moyo wako, ndi moyo wa mwana wako Solomoni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Nchifukwa chake tsono ndikupatseni nzeru kuti mupulumutse moyo wanu pamodzi ndi moyo wa mwana wanu Solomoni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Tsopano ine ndikulangizeni inu mmene mungapulumutsire moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu Solomoni.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 1:12
14 Mawu Ofanana  

Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.


Muka nulowe kwa mfumu Davide, nukati kwa iye, Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbirire mdzakazi wanu, ndi kuti, Zedi Solomoni mwana wako adzakhala mfumu nditamuka ine, nadzakhala pa mpando wanga wachifumu? Ndipo Adoniya akhaliranji mfumu?


Mukapanda kutero, kudzachitika, pamene mbuye wanga mfumu atagona kwa makolo ake, ine ndi mwana wanga Solomoni tidzayesedwa ochimwa.


Pamene Ataliya make wa Ahaziya anaona kuti mwana wake wafa, ananyamuka, naononga mbeu yonse yachifumu.


Atauka tsono Yehoramu mu ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele.


Pamene Ataliya mai wake wa Ahaziya anaona kuti mwana wake adafa, anauka, naononga mbeu yonse yachifumu ya nyumba ya Yuda.


Popanda upo wanzeru anthu amagwa; koma pochuluka aphungu pali chipulumutso.


Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.


Uphungu utsimikiza zolingalira, ponya nkhondo utapanga upo.


Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.


Ndipo Yeremiya anati kwa Zedekiya, Ndikakufotokozerani, kodi simudzandipha ine? Ndipo ndikakupangirani, simudzandimvera ine.


Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.


Paulo anati kwa kenturiyo ndi kwa asilikali, Ngati awa sakhala m'ngalawa inu simukhoza kupulumuka.


Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa