1 Akorinto 7:36 - Buku Lopatulika36 Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201436 Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa36 Koma ngati wina akuganiza kuti akumlakwira namwali wake amene adamtomera, ndipo ngati namwaliyo unamwali wake ukupitirira, tsono munthuyo nkuganiza kuti ayenera kumkwatira, angathe kuchita zimenezo, si kuchimwa ai. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero36 Ngati wina akuganiza kuti akumulakwira namwali yemwe anapalana naye ubwenzi, ndipo ngati chilakolako chake chikunka chikulirakulirabe, ndipo akuona kuti nʼkofunika kumukwatira, ayenera kuchita monga wafunira, kutero si kuchimwa ayi. Onani mutuwo |