Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 16:19 - Buku Lopatulika

19 Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni. Akupatsani moni ndithu inu mwa Ambuye, Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi Mpingo wa m'nyumba yao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Mipingo ya ku Asiya ikupatsani moni. Akupatsani moni ndithu inu mwa Ambuye, Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi Mpingo wa m'nyumba yao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Mipingo ya ku dziko la Asiya ikuti moni. Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi mpingo umene umasonkhana m'nyumba mwao, akuti moni kwa inu nonse, akhristu anzao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mpingo wa mʼchigawo cha ku Asiya ukupereka moni. Akula ndi Prisila akuperekanso moni wachisangalalo, mwa Ambuye, ndiponso mpingo umene umakumana mʼnyumba mwawo ukupereka moni.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 16:19
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anapita padziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau mu Asiya;


Paulo atakhala chikhalire masiku ambiri, anatsazika abale, nachoka pamenepo, napita m'ngalawa ku Siriya, pamodzi naye Prisila ndi Akwila; popeza anameta mutu wake mu Kenkrea; pakuti adawinda.


Ndipo anapeza Myuda wina dzina lake Akwila, fuko lake la ku Ponto, atachoka chatsopano ku Italiya, pamodzi ndi mkazi wake Prisila, chifukwa Klaudio analamulira Ayuda onse achoke mu Roma; ndipo Paulo anadza kwa iwo:


ndipo iye anayamba kulankhula molimba mtima m'sunagoge, koma pamene anamumva iye Prisila ndi Akwila, anamtenga, namfotokozera njira ya Mulungu mosamalitsa.


Ndipo anachita chomwecho zaka ziwiri; kotero kuti onse akukhala mu Asiya anamva mau a Ambuye, Ayuda ndi Agriki.


Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala mu Mesopotamiya, mu Yudeya, ndiponso mu Kapadokiya, mu Ponto, ndi mu Asiya;


Moni kwa Filologo ndi Juliya, Nereo ndi mlongo wake, ndi Olimpasi, ndi oyera mtima onse ali pamodzi nao.


Perekani moni kwa abalewo a mu Laodikea, ndi Nimfa, ndi Mpingowo wa m'nyumba yao.


Pereka moni kwa Prisika ndi Akwila, ndi banja la Onesifore.


ndi kwa Afiya mlongoyo, ndi Arkipo msilikali mnzathu, ndi kwa Mpingo uli m'nyumba yako:


Petro, mtumwi wa Yesu Khristu, kwa osankhidwa akukhala alendo a chibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bitiniya,


ndi kuti, Chimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smirina, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiatira, ndi ku Sardi, ndi ku Filadelfiya, ndi ku Laodikea.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa