Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 16:15 - Buku Lopatulika

15 Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choyamba cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefanasi, kuti ali chipatso choundukula cha Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Abale, mukudziŵa kuti Stefanasi ndi a m'banja mwake ndiwo adayambirira kuloŵa chikhristu m'dziko la Akaiya. Ndipo akhala akudzipereka kutumikira anthu a Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Mukudziwa kuti a mʼbanja la Stefano ndiye anali oyamba kutembenuka mtima ku Akaya, ndipo akhala akudzipereka kutumikira oyera mtima. Choncho ndikukudandaulirani, inu abale,

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 16:15
18 Mawu Ofanana  

Tsono pamene Galio anali chiwanga cha Akaya, Ayuda ndi mtima umodzi anamuukira Paulo, nanka naye kumpando wachiweruziro,


Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.


Koma tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndilikutumikira oyera mtima.


kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;


kuti mumlandire iye mwa Ambuye, monga kuyenera oyera mtima, ndi kuti mumthandize m'zinthu zilizonse adzazifuna kwa inu; pakuti iye yekha anali wosungira ambiri, ndi ine ndemwe.


ndipo mupereke moni kwa Mpingo wa Ambuye wa m'nyumba mwao. Moni kwa Epeneto wokondedwa wanga, ndiye chipatso choyamba cha Asiya cha kwa Khristu.


Koma ndinabatizanso a pa banja la Stefanasi; za ena, sindidziwa ngati ndinabatiza wina yense.


Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso.


Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefanasi, ndi Fortunato, ndi Akaiko; chifukwa iwo anandikwaniritsa chotsalira chanu.


anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima;


Pakutitu za utumiki wa kwa oyera mtima sikufunika kwa ine kulembera inu;


wa mbiri ya ntchito zabwino; ngati walera ana, ngati wachereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a oyera mtima, ngati wathandiza osautsidwa, ngati anatsatadi ntchito zonse zabwino.


Pakuti ndinali nacho chimwemwe chambiri ndi chisangalatso pa chikondi chako, popeza mitima ya oyera mtima yatsitsimuka mwa iwe, mbale.


pakuti Mulungu sali wosalungama kuti adzaiwala ntchito yanu, ndi chikondicho mudachionetsera kudzina lake, umo mudatumikira oyera mtima ndi kuwatumikirabe.


monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;


Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa