Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 16:11 - Buku Lopatulika

11 chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 chifukwa chake munthu asampeputse. Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono wina aliyense asamnyoze, koma mumthandize kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwerera kuli ine kuno. Paja ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Wina aliyense asamunyoze. Muthandizeni kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwereranso kuli ine. Ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 16:11
10 Mawu Ofanana  

Iye wakumvera inu, andimvera Ine; ndipo iye wakukana inu, andikana Ine; ndipo iye wakukana Ine amkana Iye amene anandituma Ine.


Ndipo iwo anaperekezedwa ndi Mpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko cha amitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.


Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza.


Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira ntchito ya Ambuye, monganso ine;


ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yachisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kulikonse ndipitako.


ndipo popyola kwanu kupita ku Masedoniya, ndi kudzanso kwa inu pobwera kufuma ku Masedoniya; ndi kuperekezedwa ndi inu ku Yudeya.


Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.


Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.


Izi lankhula, ndipo uchenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse.


amene anachita umboni za chikondi chako pamaso pa Mpingo; ngati uwaperekeza amenewo pa ulendo wao koyenera Mulungu, udzachita bwino:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa