Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 15:52 - Buku Lopatulika

52 m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa lipenga lotsiriza; pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osavunda, ndipo ife tidzasandulika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Zidzachitika mwadzidzidzi, pa kamphindi ngati kuphethira kwa diso, pamene lipenga lotsiriza lidzalira. Likadzaliratu lipengalo, akufa adzauka ndi matupi amene sangaole, ndipo ife tidzasandulika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Zidzachitika mwadzidzidzi, mʼkamphindi kochepa, monga ngati kuphethira kwa diso, pa lipenga lotsiriza. Pakuti lipenga lidzalira, akufa adzaukitsidwa opanda chovunda, ndipo ife tidzasandulika.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 15:52
24 Mawu Ofanana  

Ha? M'kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zoopsa.


Ndipo kunali tsiku lachitatu, m'mawa, panali mabingu ndi zimphezi, ndi mtambo wakuda bii paphiripo, ndi liu la lipenga lolimbatu; ndi anthu onse okhala kutsasa ananjenjemera.


Ndipo anthu onse anaona mabingu ndi zimphezi, ndi liu la lipenga ndi phiri lilikufuka; ndipo pamene anthu anaziona, ananjenjemera, naima patali.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israele, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamodzi, ndidzakuthani; koma tsopano, vulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe chomwe ndikuchitireni.


Inu nonse akukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika padziko lapansi, potukulidwa chizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.


Ndipo padzakhala tsiku limenelo, lipenga lalikulu lidzaombedwa; ndipo adzafika omwe akadatayika m'dziko la Asiriya, ndi opirikitsidwa a m'dziko la Ejipito; ndipo adzapembedza Yehova m'phiri lopatulika la pa Yerusalemu.


nakaona iye lupanga lilikudzera dziko, nakaomba lipenga ndi kuchenjeza anthu;


Koma mlonda akaona lupanga likudza, osaomba lipenga, osachenjeza anthu, nilidza lupanga, nilichotsa mwa iwo; munthu atengedwadi m'mphulupulu zake, koma mwazi wake ndidzaufunsa padzanja la mlonda.


Ndipo Yehova adzaoneka pamwamba pao, ndi muvi wake udzatuluka ngati mphezi; ndipo Ambuye Mulungu adzaomba lipenga, nadzayenda ndi akamvulumvulu a kumwera.


Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akulu a zikwi a mu Israele, azisonkhana kuli iwe.


Dzipatuleni pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi.


Kwerani kuchoka pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi. Pamenepo adagwa nkhope zao pansi.


Ndipo Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kumphepo zinai, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.


Indetu, indetu, ndinena kwa inu, kuti ikudza nthawi, ndipo ilipo tsopano, imene akufa adzamva mau a Mulungu; ndipo iwo akumva adzakhala ndi moyo.


Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthawi, imene onse ali m'manda adzamva mau ake,


Koma yense m'dongosolo lake la iye yekha, chipatso choyamba Khristu; pomwepo iwo a Khristu, pakubwera kwake.


Chomwechonso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m'chivundi, liukitsidwa m'chisavundi;


Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.


Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.


Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.


Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pamwamba, ndi kunena ndi mau aakulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.


Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri amene amaimirira pamaso pa Mulungu; ndipo anawapatsa malipenga asanu ndi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa