Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 15:47 - Buku Lopatulika

47 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

47 Munthu woyambayo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

47 Adamu woyamba uja anali wochokera ku dothi, anali wapansipano. Koma Khristu, Adamu wachiŵiri uja, anali wochokera Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

47 Munthu woyamba anali wa dziko lapansi, wochokera mʼnthaka koma munthu wachiwiri anali wochokera kumwamba.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 15:47
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m'mphuno mwake; munthuyo nakhala wamoyo.


m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.


Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.


Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.


Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.


pakuti wakubadwirani inu lero, m'mzinda wa Davide, Mpulumutsi, amene ali Khristu Ambuye.


Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse; iye amene ali wa dziko lapansi ali wa dziko lapansi, nalankhula za dziko lapansi: Iye wochokera Kumwamba ali woposa onse.


Pakuti mkate wa Mulungu ndiye wakutsika kuchokera Kumwamba ndi kupatsa moyo kwa dziko lapansi.


Mau amene anatumiza kwa ana a Israele, akulalikira Uthenga Wabwino wa mtendere mwa Yesu Khristu (ndiye Ambuye wa onse)


Koteronso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsirizayo anakhala mzimu wakulenga moyo.


Koma chauzimu sichili choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo chauzimu.


Pakuti tidziwa kuti ngati nyumba ya pansi pano ya msasa wathu ipasuka, tili nacho chimango cha kwa Mulungu, ndiyo nyumba yosamangidwa ndi manja, yosatha, mu Mwamba.


Ndipo povomerezeka, chinsinsi cha kuchitira Mulungu ulemu nchachikulu: Iye amene anaonekera m'thupi, anayesedwa wolungama mumzimu, anapenyeka ndi angelo, analalikidwa mwa amitundu, wokhulupiridwa m'dziko lapansi, wolandiridwa mu ulemerero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa