Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 15:19 - Buku Lopatulika

19 Ngati tiyembekezera Khristu m'moyo uno wokha, tili ife aumphawi oposa a anthu onse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Ngati tiyembekezera Khristu m'moyo uno wokha, tili ife aumphawi oposa a anthu onse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ngati taika chikhulupiriro chathu mwa Khristu chifukwa cha moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa chisoni koposa anthu ena onse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Ngati kukanakhala kuti tili ndi chiyembekezo mwa Khristu mʼmoyo uno wokha, tikanakhala omvetsa chisoni kuposa anthu ena onse.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 15:19
19 Mawu Ofanana  

kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.


Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji?


Khalani mokondwa ndi mkazi umkonda masiku onse a moyo wako wachabe, umene Mulungu wakupatsa pansi pano masiku ako onse achabe; pakuti ilo ndi gawo lako la m'moyo ndi m'ntchito zimene uvutika nazo pansi pano.


Pamenepo adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.


Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;


Ndipo zija zinagwa kumingazi, ndiwo amene adamva, ndipo m'kupita kwao atsamwitsidwa ndi nkhawa, ndi chuma, ndi zokondweretsa za moyo, ndipo sakhwimitsa zipatso zamphumphu.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.


nalimbikitsa mitima ya ophunzira, nadandaulira iwo kuti akhalebe m'chikhulupiriro, ndi kuti tiyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu ndi zisautso zambiri.


ndi kukumbukira kosalekeza ntchito yanu ya chikhulupiriro, ndi chikondi chochitachita, ndi chipiriro cha chiyembekezo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu Atate wathu;


Chifukwa cha ichicho ndinamva zowawa izi; komatu sindichita manyazi; pakuti ndimdziwa Iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira chosungitsa changacho kufikira tsiku lijalo.


Msilikali sakodwa nazo ntchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikali.


Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo.


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


Ndipo ndinamva mau ochokera Kumwamba, ndi kunena, Lemba, Odala akufa akumwalira mwa Ambuye, kuyambira tsopano; inde, anena Mzimu, kuti akapumule ku zolemetsa zao; pakuti ntchito zao zitsatana nao pamodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa