Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 15:17 - Buku Lopatulika

17 ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu chili chopanda pake; muli chikhalire m'machimo anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 ndipo ngati Khristu sanaukitsidwa, chikhulupiriro chanu chili chopanda pake; muli chikhalire m'machimo anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Ndipotu ngati Khristu sadauke, chikhulupiriro chanu nchopanda pake, ndipo mukadali m'machimo anu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe, chikhulupiriro chanu nʼchopanda ntchito; mukanali mu machimo anu.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 15:17
15 Mawu Ofanana  

Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nena kwa nyumba ya Israele, Mumatero inu ndi kuti, Zolakwa zathu ndi zochimwa zathu zitikhalira, ndipo tichita nazo liwondewonde, tidzakhala ndi moyo bwanji?


Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.


amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.


Pakuti ngati, pokhala ife adani ake, tinayanjanitsidwa ndi Mulungu mwa imfa ya Mwana wake, makamaka ndithu, popeza ife tayanjanitsidwa, tidzapulumuka ndi moyo wake.


ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.


Pakuti ngati akufa saukitsidwa, Khristunso sanaukitsidwe;


umenenso mupulumutsidwa nao ngati muugwiritsa monga momwe ndinalalikira kwa inu; ngati simunakhulupirire chabe.


chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.


Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa