Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 14:21 - Buku Lopatulika

21 Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 M'Malembo mudalembedwa kuti, “Ndidzalankhula ndi mtundu uwu kudzera mwa anthu a zilankhulo zachilendo, ndiponso ndi pakamwa pa anthu achilendo. Koma ngakhale nditero, sadzandimvera, akutero Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Zinalembedwa mʼMalamulo kuti, “Ndidzayankhula kwa anthu awa, kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo ndiponso ndi milomo yachilendo. Koma ngakhale nthawi imeneyo sadzandimvera Ine, akutero Ambuye.”

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 14:21
7 Mawu Ofanana  

Taonani, ndidzatengera pa inu mtundu wa anthu akutali, inu nyumba ya Israele, ati Yehova; ndi mtundu wolimba, ndi mtundu wakalekale, mtundu umene chinenero chake simudziwa, ngakhale kumva zonena zao.


Yesu anayankha iwo, Kodi sikulembedwa m'chilamulo chanu, Ndinati Ine, Muli milungu?


Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Akazi akhale chete mu Mipingo. Pakuti sikuloledwa kwa iwo kulankhula. Koma akhale omvera, monganso chilamulo chinena.


Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamve malankhulidwe ao;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa