Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 11:32 - Buku Lopatulika

32 Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Koma Ambuye amatilanga, kuti tiphunzirepo nzeru, kuwopa kuti tingaimbidwe mlandu pamodzi ndi anthu odalira zapansipano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 11:32
22 Mawu Ofanana  

Ndidzakhala atate wake, iye nadzakhala mwana wanga; akachita choipa ndidzamlanga ndi ndodo ya anthu, ndi mikwapulo ya ana a anthu;


Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai.


Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.


Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, choonadi chatha, chadulidwa pakamwa pao.


Sanamvera mau, sanalole kulangizidwa; sanakhulupirire Yehova, sanayandikire kwa Mulungu wake.


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Ndipo mphatso siinadze monga mwa mmodzi wakuchimwa, pakuti mlandu ndithu unachokera kwa munthu mmodzi kufikira kutitsutsa, koma mphatso yaulere ichokera ku zolakwa zambiri kufikira kutiyesa olungama.


Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthawi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitse nzeru ya dziko lapansi?


Pakuti popeza m'nzeru ya Mulungu dziko lapansi, mwa nzeru yake, silinadziwe Mulungu, chidamkonda Mulungu kupulumutsa okhulupirirawo mwa chopusa cha kulalikira.


Chifukwa chake ambiri mwa inu afooka, nadwala, ndipo ambiri agona.


Koma ngati tikadadzizindikira tokha sitikadaweruzidwa.


Chifukwa chake, abale anga, posonkhanira kudya, lindanani.


Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wake, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.


a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.


Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa