Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Akorinto 11:20 - Buku Lopatulika

20 Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Chifukwa chake, pakusonkhana inu pamodzi sikutheka kudya mgonero wa Ambuye;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Pamene musonkhana pamodzi, chimene mumadyatu si Mgonero wa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 11:20
10 Mawu Ofanana  

Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukira mphulupulu yao, nadzalanga zochimwa zao; adzabwerera kunka ku Ejipito.


Ndipo pamene mukadya si ndinu, mukamwa si ndinu kodi?


Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.


Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;


Koma pakulalikira ichi sinditama inu, popeza simusonkhanira chokoma, koma choipa.


Pakuti kuyenera kuti pakhale mipatuko mwa inu, kuti iwo ovomerezedwa aonetsedwe mwa inu.


pakuti pakudyaku yense ayamba watenga mgonero wake wa yekha, ndipo wina ali ndi njala, ndi wina aledzera.


osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.


ochitidwa zoipa kulipira kwa chosalungama; anthu akuyesera chowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zilema, akudyerera m'madyerero achikondi ao, pamene akudya nanu;


Iwo ndiwo okhala mawanga pa maphwando anu a chikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawiri, yozuka mizu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa