Ndikuwona kuti khama lililonse ndilofunika ndikawona zipatso zake! Palibe chomwe chingapambane chisangalalo chokwaniritsa zolinga zako, ngakhale mutadzimana zinthu, kulira, ndi kusowa tulo. Zonse zimaiwalika ukagwira chipatso cha khama lako ndi kudzipereka kwako. Pamenepo ndiye umadziwa kuti unagwiritsa ntchito bwino nthawi yako, kuti sekondi iliyonse inakuthandiza kufika pachimake pa zomwe unakwaniritsa.
Kumaliza maphunziro ndi nthawi yofunika kwambiri pa moyo. Mtima umadzaza ndi malingaliro osiyanasiyana, chisangalalo chosakanikirana ndi misozi zomwe zimasonyeza khama ndi thandizo lomwe unalandira. Pa nthawi ngati imeneyi, umathokoza anthu omwe anakhala nawe kuyambira pachiyambi: banja lako, lomwe linakhulupirira mwa iwe, ndi anzako, omwe anakukhazika mtima kuti usagonje. Ino ndi nthawi yoti uwathokoze ndi kulemekeza miyoyo yawo powalola kukhala nawe pa nthawi yofunika iyi.
Kondwerera, sangalala, ndipo tithokoze Mulungu chifukwa choti wafika pano. Yesetsa kuti nthawi ino ikhale yokumbukika ndi yosangalatsa. Zikomo kwambiri!
Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake;
Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.
Pakuti ife ndife chipango chake, olengedwa mwa Khristu Yesu, kuchita ntchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo.
Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera. Iye amene ayendayenda nalira, ponyamula mbeu yakufesa; adzabweranso ndithu ndi kufuula mokondwera, alikunyamula mitolo yake.
Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.
Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.
Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,
Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.
Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.
Mwananga, usaiwale malamulo anga, mtima wako usunge malangizo anga; motero nkhokwe zako zidzangoti thee, mbiya zako zidzasefuka vinyo. Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye. Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m'dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m'dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira ngwodala. Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha. pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere.
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeza malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikira phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.
Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.
kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;
Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.
Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu.
Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.
Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi.
ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.
Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.
Odala angwiro m'mayendedwe ao, akuyenda m'chilamulo cha Yehova. Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse; ndisasokere kusiyana nao malamulo anu. Ndizindikira koposa okalamba popeza ndinasunga malangizo anu. Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa, kuti ndisamalire mau anu. Sindinapatukana nao maweruzo anu; pakuti Inu munandiphunzitsa. Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga. Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo. Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga. Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima, kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama. Ndazunzika kwambiri: Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu. Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu. Moyo wanga ukhala m'dzanja langa chikhalire; koma sindiiwala chilamulo chanu. Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu. Oipa ananditchera msampha; koma sindinasokera m'malangizo anu. Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga. Ndinalingitsa mtima wanga uchite malemba anu, kosatha, kufikira chimaliziro. Ndidana nao a mitima iwiri; koma ndikonda chilamulo chanu. Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu. Mundichokere ochita zoipa inu; kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga. Mundichirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo; ndipo ndisachite manyazi pa chiyembekezo changa. Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa, ndipo ndidzasamalira malemba anu chisamalire. Mupepula onse akusokera m'malemba anu; popeza chinyengo chao ndi bodza. Muchotsa oipa onse a pa dziko lapansi ngati mphala: Chifukwa chake ndikonda mboni zanu. Inu ndinu wodala Yehova; ndiphunzitseni malemba anu. Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu; ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu. Ndinachita chiweruzo ndi chilungamo; musandisiyira akundisautsa. Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere; odzikuza asandisautse. Maso anga anatha mphamvu pofuna chipulumutso chanu, ndi mau a chilungamo chanu. Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu, ndipo ndiphunzitseni malemba anu. Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni; kuti ndidziwe mboni zanu. Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu; pakuti anaswa chilamulo chanu. Chifukwa chake ndikonda malamulo anu koposa golide, inde golide woyengeka. Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika malangizo anu onse akunena zonse; koma ndidana nazo njira zonse zonyenga. Mboni zanu nzodabwitsa; chifukwa chake moyo wanga uzisunga. Ndinafotokozera ndi milomo yanga maweruzo onse a pakamwa panu. Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa. Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefuwefu; popeza ndinakhumba malamulo anu. Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo, monga mumatero nao akukonda dzina lanu. Khazikitsani mapazi anga m'mau anu; ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse. Mundiombole kunsautso ya munthu: Ndipo ndidzasamalira malangizo anu. Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu; ndipo mundiphunzitse malemba anu. Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu. Inu ndinu wolungama, Yehova, ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika. Mboni zanuzo mudazilamulira zili zolungama ndi zokhulupirika ndithu. Changu changa chinandithera, popeza akundisautsa anaiwala mau anu. Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse. Mau anu ngoyera ndithu; ndi mtumiki wanu awakonda. Wamng'ono ine, ndi wopepulidwa; koma sindiiwala malemba anu. Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi. Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine. Mboni zanu ndizo zolungama kosatha; mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo. Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova; ndidzasunga malemba anu. Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni, ndipo ndidzasamalira mboni zanu. Ndinafuula kusanake: ndinayembekezera mau anu. Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku, kuti ndilingirire mau anu. Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu; mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova. Ndidzalingirira pa malangizo anu, ndi kupenyerera mayendedwe anu. Otsata zachiwembu andiyandikira; akhala kutali ndi chilamulo chanu. Inu muli pafupi, Yehova; ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi. Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu, kuti munazikhazika kosatha, Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse; pakuti sindiiwala chilamulo chanu. Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole; mundipatse moyo monga mwa mau anu. Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu. Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova; mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu. Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri; koma sindinapatukana nazo mboni zanu. Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao; popeza sasamalira mau anu. Penyani kuti ndikonda malangizo anu; mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu. Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu; sindidzaiwala mau anu. Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha. Nduna zinandilondola kopanda chifukwa; koma mtima wanga uchita mantha nao mau anu. Ndikondwera nao mau anu, ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri. Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo; koma ndikonda chilamulo chanu. Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi, chifukwa cha maweruzo anu alungama. Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa. Ndinayembekeza chipulumutso chanu, Yehova, ndipo ndinachita malamulo anu. Moyo wanga unasamalira mboni zanu; ndipo ndizikonda kwambiri. Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu; popeza njira zanga zonse zili pamaso panu. Kufuula kwanga kuyandikire pamaso panu, Yehova; mundizindikiritse monga mwa mau anu. Muchitire chokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo; ndipo ndidzasamalira mau anu. Kupemba kwanga kudze pamaso panu; mundilanditse monga mwa mau anu. Milomo yanga itulutse chilemekezo; popeza mundiphunzitsa malemba anu. Lilime langa liimbire mau anu; pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama. Dzanja lanu likhale lakundithandiza; popeza ndinasankha malangizo anu. Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova; ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa. Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani; ndipo maweruzo anu andithandize. Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu; pakuti sindiiwala malamulo anu. Munditsegulire maso, kuti ndipenye zodabwitsa za m'chilamulo chanu. Ine ndine mlendo pa dziko lapansi; musandibisire malamulo anu. Odala iwo akusunga mboni zake, akumfuna ndi mtima wonse;
Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziwa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziwa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.
Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
Wokolola m'malimwe ndi mwana wanzeru; koma wogona pakutula ndi mwana wochititsa manyazi.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu;
Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
pakuti wakuchita mwa inu kufuna ndi kuchita komwe, chifukwa cha kukoma mtima kwake, ndiye Mulungu.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.
Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.
Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.
Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:
Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,
Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.
Koma chikhulupiriro ndicho chikhazikitso cha zinthu zoyembekezeka, chiyesero cha zinthu zosapenyeka.
Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.
kuti ngati udzavomereza m'kamwa mwako Yesu ndiye Ambuye, ndi kukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka:
Koma wookayo ndi wothirirayo ali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yake ya iye yekha, monga mwa kuchititsa kwake kwa iye yekha.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Ndipo mwa ichi chomwe, pakutengeraponso changu chonse, muonjezerapo ukoma pa chikhulupiriro chanu, ndi paukoma chizindikiritso; ndi pachizindikiritso chodziletsa; ndi pachodziletsa chipiriro; ndi pachipiriro chipembedzo; ndi pachipembedzo chikondi cha pa abale; ndi pachikondi cha pa abale chikondi.
Yehova akhazikitsa mayendedwe a munthu; ndipo akondwera nayo njira yake. Angakhale akagwa, satayikiratu, pakuti Yehova agwira dzanja lake.
Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzafuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati uchotsa pakati pa iwe goli, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,
Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.
Chokhachi, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Khristu: kuti, ndingakhale nditi ndilinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndili kwina, ndikamva za kwa inu, kuti muchilimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino;
chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;
Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;
Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.
Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda Iye.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.
koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.
Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.
Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.
Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.