Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo. Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.
Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Wotsata malamulo ake amakhala ndi nzeru zenizeni. Chauta ndi wotamandika mpaka muyaya.
Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.
Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite.
Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe.
Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.
Komabe pakati pa anthu okhwima m'chikhulupiriro, timalankhula zanzeru. Koma nzeruzo si za masiku anozi, kapena za akulu olamulira dziko lino lapansi, amene mphamvu zao nzodzatha. Nzeru zimene timalankhula, ndi nzeru za Mulungu, zachinsinsi, zobisika kwa anthu. Mulungu asanalenge dziko lapansi, adaakonzeratu zimenezi kuti atipatse ulemerero.
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.
Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.
Amene amakonda nzeru amadzichitira zabwino mwiniwakeyo. Amene ali womvetsa, zinthu zidzamuyendera bwino.
Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.
Nchifukwa chake mundipatse mtumiki wanune nzeru zolamulira anthu anu, kuti ndizidziŵa kusiyanitsa zabwino ndi zoipa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu chotere wa anthu anu?”
Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.
“Koma Mulungu ali ndi nzeru ndi mphamvu zopambana. Ali ndi uphungu wabwino, ndi kumvetsa zinthu zonse.
Ndani adalamulirapo maganizo a Chauta? Ndani adamphunzitsapo kanthu ngati mlangizi wake? Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani, kuti adziŵe zinthu? Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama? Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu? Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu?
Usaiŵale mau a pakamwa pangaŵa, usatayane nawo, Ukhale ndi nzeru, ndiponso khalidwe la kumvetsa zinthu. Usaisiye nzeru, ndipo idzakusunga. Uziikonda, ndipo idzakuteteza.
Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri.
Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.
Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu.
Nzeru zidzaloŵa mumtima mwako, kudziŵa zinthu kudzakusangalatsa. Kuganiziratu zam'tsogolo kudzakusunga, kumvetsa zinthu kudzakuteteza.
Choncho adauza munthu kuti, ‘Kuwopa Ambuye ndiye nzeru zimenezo, kuthaŵa zoipa ndiye luntha limenelo.’ ” Yobe
Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.
Ineyo ndidzakupatsani mau ndi nzeru zimene adani anuwo sadzatha konse kuzikana kapena kuzitsutsa.
Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire?
Si bwino kuti munthu akhale wosadziŵa zinthu, ndipo munthu woyenda mofulumira dziŵi amasokera.
Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.
Paja wondipeza ine, wapeza moyo, ndipo amapeza kuyanja pamaso pa Chauta. Koma wosandipeza ine, akudzipweteka ameneyo. Onse odana ndi ine, ngokonda imfa amenewo.”
Ndimakonda malamulo anu kwambiri, ndimasinkhasinkha za malamulowo tsiku lonse. Malamulo anu amandisandutsa wanzeru kuposa adani anga, popeza kuti malamulowo ndili nawo nthaŵi zonse.
Amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera, kotero kuti cholinga chao sichiphula kanthu. Amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwao, amathetsa msanga zimene akapsala adakonza kuti achite.
Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.
ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.
Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
“Koma nzeru zingapezeke kuti? Luntha lingapezeke kuti? Anthu sadziŵa kufunika kwake kwa nzeruzo, ndipo sizipezeka pa dziko lino lapansi.
Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate. Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao.
Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.
Nzeru zimenezi zimachokera kwa Chauta Wamphamvuzonse. Uphungu wake ndi wodabwitsa, nzeru zake nzopambana.
Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru, koma munthu womvetsa zinthu amatsata zolungama.
Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.
Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe.
Kwa chitsiru kulakwa kumakhala ngati maseŵera, koma kwa munthu womvetsa zinthu kuchita zanzeru ndiye kumapatsa chimwemwe.
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.
Kwa Mulungu, amene ndiye yekha wanzeru, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu mpaka muyaya. Amen.
Ndipo Yesu analikunka nakula m'nzeru ndi mu msinkhu, ndipo Mulungu ndi anthu omwe ankakondwera naye kwambiri.
Tsopano afuna kuti kudzera mwa Mpingo, mafumu ndi aulamuliro onse a Kumwamba adziŵe nzeru za Mulungu zamitundumitundu.
Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.
Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu.
Malamulo anu amandisandutsa wanzeru kuposa adani anga, popeza kuti malamulowo ndili nawo nthaŵi zonse. Ndili ndi nzeru za kumvetsa kupambana aphunzitsi anga onse, pakuti ndimasinkhasinkha za malamulo anu.
Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu, munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu.
Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.
Wonyoza anzake amafunafuna nzeru osaipeza, koma munthu womvetsa amadziŵa bwino zinthu msanga.
Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta. Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja.
Anthu oipa samvetsa kuti chilungamo nchiyani, koma amene amatsata kufuna kwa Chauta amachimvetsa kwathunthu.
Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!
Chifukwa cha ine nzeru, masiku ako adzachuluka, ndipo ndidzaonjezera zaka pa moyo wako.
Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.
Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu.
Mwana wanga, usunge nzeru yeniyeni usunge mkhalidwe wa kulingalira bwino, ziŵiri zimenezi zisakuthaŵe.
Mulungu adapatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka, nzeru zake zinali zopanda malire.
Kodi suja nzeru imaitana? Suja nzeru zomvetsera zinthu zimakweza mau ake? Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri. Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru. Ine nzeru ndimakhalira limodzi ndi kuchenjera. Ndimadziŵa zinthu ndipo ndimaganiza moyenera. Kuwopa Chauta nkudana ndi zoipa. Kunyada, kudzitama, kuchita zoipa ndi kulankhula zonyenga, zonsezo ndimadana nazo. Ndili ndi uphungu ndi maganizo abwino. Ndimamvetsa bwino zinthu, ndilinso ndi mphamvu. Ndimathandiza mafumu polamulira ndine, olamulira ndimaŵathandiza ndine kulamula zolungama. Ndine ndimathandiza akalonga polamula, ndine ndimathandiza akuluakulu poweruza m'dziko. Anthu ondikonda, ine nzeru ndimaŵakonda, anthu ondifunafuna mosamala, amandipeza. Ndili nacho chuma, ndili nawo ulemu, chuma chosatha ndiponso kukhuphuka konkirankira. Zimene mumalandira kwa ine nzokoma kuposa golide, ngakhale golide wosalala. Phindu lochokera mwa ine nloposa siliva wabwino zedi. Nzeru imakhala pa zitunda m'mbali mwa njira, imakaima pa mphambano za miseu.
Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta.
Munthu wosalabadirako za Mulungu amaononga mnzake ndi pakamwa pake; munthu wochita chilungamo amapulumuka chifukwa cha kudziŵa zinthu.
Ukakonzekera kuchita zinthu, uziyamba wafunsa. Usanamenye nkhondo, uyambe wapempha malangizo oyenera.
Zoonadi nzeru za anthu odalira zapansipano, nzopusa pamaso pa Mulungu. Pajatu Malembo akuti, “Mulungu amakola anthu anzeru m'kuchenjera kwao.”
Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.
Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo.
Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye, mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa, mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu, mzimu wopatsa kudziŵa zinthu ndi kuwopa Chauta.
Utchere khutu lako, umve mau a anthu anzeru, uike mtima wako pa zophunzitsa zanga, kuti uzidziŵe.
Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu.
Tsono mundipatse nzeru ndi luntha, kuti ndiŵatsogolere bwino anthu anuŵa. Nanga popanda nzeruzo ndani angathe kulamulira mtundu waukulu wa anthu anu?”
Ngothandiza kuti anthu adziŵe nzeru ndi mwambo, kuti amvetse mau a matanthauzo ozama, Nzeru ikufuula mu mseu, ikulankhula mokweza mau m'misika. Ikufuula pa mphambano za miseu, ikulankhula pa zipata za mzinda, kuti, “Kodi anthu osachangamukanu, mudzakondwerabe kupusaku mpaka liti? Kodi anthu onyodola, adzakhalabe akunyodola mpaka liti? Nanga opusa adzakana kuphunzira zanzeru mpaka liti? Musamale kudzudzula kwangaku, ine ndikuuzani maganizo anga, ndi kukudziŵitsani mau anga. Paja ine ndidaakuitanani, inu nkukana kumvera, ndidaati ndikuthandizeni, koma popanda wosamalako. Uphungu wanga simudaulabadire, kudzudzula kwanga simudakusamale. Ndiye inenso ndidzakusekani, mukadzagwa m'mavuto, ndidzakunyodolani, mukadzazunguzika ndi mantha, pamene mantha adzakukunthani ngati namondwe, pamene tsoka lidzakufikirani ngati kamvulumvulu, pamene mavuto ndi masautso adzakugwerani. Tsono mudzandiitana, koma ine sindidzaitaŵa, mudzandifunafuna mwakhama, koma simudzandipeza. Popeza kuti mudadana ndi nzeru, ndipo simudasankhe kuwopa Chauta, kuti alandire mwambo wochita zinthu mwanzeru, akhale angwiro, achilungamo ndi osakondera. popeza kuti simudasamale malangizo anga, ndipo mudanyoza kudzudzula kwanga konse, basitu tsono mudzadya zipatso zoyenera ntchito zanuzo, mudzakhuta zoipa zimene munkafuna kuŵachita ena. Anthu opusa amaphedwa chifukwa cha kusokera kwao. Zitsiru zimadziwononga zokha nkudzitama kwao. Koma amene amamvera ine adzakhala pabwino, adzakhala mosatekeseka, osaopa choipa chilichonse”. Ngophunzitsa anthu wamba nzeru za kuchenjera, ndi achinyamata kudziŵa zinthu ndi kulingalira bwino.
Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.
Ugule choona, ndipo usachigulitse. Ugulenso nzeru, mwambo ndiponso mtima womvetsa zinthu.
Kuwopa Chauta kumabweretsa moyo, ndipo amene amaopayo amakhala pabwino, ndiye kuti choipa sichidzamgwera.
Udziŵe kuti nzeru ndi yoteronso mumtima mwako. Ukaipeza, zinthu zidzakuyendera bwino m'tsogolo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.
Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere.
Pakamwa panga musapaletse mpang'ono pomwe kulankhula mau anu oona, pakuti ndimakhulupirira malangizo anu. Ndidzatsata malamulo anu kosalekeza mpaka muyaya,
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Adzakupatsani mtendere wokhazikika pa nthaŵi yanu. Adzakuninkhaninso chipulumutso chachikulu, luntha lambiri ndi nzerunso zambiri. Kuwopa Chauta ndiko kumapezetsa chuma chimenechi.
Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru. Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira. Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika.
Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma wochenjera amayang'ana m'mene akuyendera.
Mwana wanga, mvetsetsa mau anga. Tchera khutu ku zimene ndikunena. Zisachoke m'mutu mwakomu, uzisunge bwino mumtima mwako.
Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako. Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako. Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira. Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda. Pamene ukudzuka, zidzakulangiza.
Ndi bwino kuti ndidalangidwa, kuti ndiphunzire malamulo anu. Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.
Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru, nanenso mtima wanga udzasangalala. Mtima wanga udzakondwa ndikadzakumva ukulankhula zolungama.
Ndidzakupatsa chuma chosaoneka poyera ndi katundu wa m'malo obisika. Motero udzadziŵa kuti ndine Chauta, Mulungu wa Israele, amene ndikukuitana pokutchula dzina.
Pajatu munthu wokondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamsandutsa waluntha, wanzeru ndi wosangalala. Koma wochimwa amampatsa ntchito yokunkha ndi younjika zinthu, kenaka zonsezo nkuzipatsa munthu wokondwetsa Mulungu. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.
Maso ako aziyang'ana kutsogolo molunjika, uzipenya kutsogolo osacheukacheuka. Uzisamala m'mene mukupita mapazi ako, ndipo njira zako zonse zidzakhala zosapeneketsa. Usapatukire kumanja kapena kumanzere, usayende pamene pali choipa chilichonse.
Ndikutamanda Chauta amene ali phungu wanga. Mtima wanga umandilangiza ndi usiku womwe.
Nzeru za munthu wochenjera zagona pa kuzindikira bwino njira zake, koma zitsiru zimanyengedwa nkupusa kwao komwe.
Mundidziŵitse mfundo za malamulo anu, ndipo ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zodabwitsa.
Mwana wanga, umvetsere bwino zanzeru ndikukuuzazi, utchere khutu kwa ine womvetsa bwino zinthu, Mwinanso alendo adzadyerera chuma chako, phindu la ntchito zako lidzagwa m'manja mwa munthu wachilendo. Ndipo potsiriza pa moyo wako udzalira chokuwa, thupi lako lonse litatheratu. Pamenepo iwe udzangoti, “Kalanga ine, ndinkadana nkusunga mwambo, mtima wanga unkanyoza chidzudzulo! Sindidamvere mau a aphunzitsi anga, sindidatchere khutu kwa alangizi anga. Pang'onong'ono, bwenzi nditaonongekeratu pakati pa mpingo wonse utasonkhana.” Iwe, uzimwera m'chitsime chakochako, ndiye kuti khala wokhulupirika kwa mkazi wako. Kodi ana ako azingoti mbwee ponseponse ngati madzi ongoyenda m'miseu? Anawo akhale a iwe wekha, osatinso uŵagaŵane ndi alendo. Uzikhutira ndi mkazi wako, uzikondwa ndi mkazi wa unyamata wako. Iye uja ngwokongola ngati mbaŵala, ndi wa maonekedwe osiririka ngati mbalale. Uzikhutitsidwa ndi maŵere ake nthaŵi zonse, uzikokeka ndi chikondi chake pa moyo wako wonse. kuti uziganiza mochenjera, ndipo pakamwa pako pazilankhula zanzeru.
Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro.
Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha.
M'njira ya munthu wosalungama muli minga ndi misampha, koma wodzisamala bwino adzazilewa zonsezo.
Nzeru nzabwino ngati choloŵa chomwe, zimapindulitsa wamoyo aliyense pansi pano. Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.
Inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m'kuŵala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m'kuŵala. Pajatu pamene pali kuŵala, pamapezekanso ubwino wonse, chilungamo chonse ndi choona chonse.
Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu.