Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


124 Mauthenga a za Chopereka

124 Mauthenga a za Chopereka

Tsiku loyamba la sabata lililonse, ndikofunikira kuti ndipatule ndalama zomwe ndapeza, monga mmene mawu a Mulungu amanenera pa 1 Akorinto 16:2. Sizothandiza kuyeyembekezera mpaka ine nditabwera kuti ndiyambe kusonkhanitsa zonse nthawi imodzi.

Monga momwe Paulo analembera Akhristu m'mizinda yosiyanasiyana ya ku Asia, iye anathandiza kukonza zinthu zina m'mipingo, komanso anapereka malangizo okhudza moyo wa tsiku ndi tsiku. Nkhani ya zopereka ndi ndalama sinali yachilendo mu ziphunzitso zake.

Pa Aefeso 5:2, tikuphunzira momwe Khristu anali nsembe yangwiro pamene anadzipereka yekha chifukwa cha ife, ndipo timakumbukira zimenezi nthawi iliyonse yomwe tipereka. Wopereka amakhala ngati Yesu, amene anadzipereka yekha monga nsembe yopanda chifukwa.

Zopereka ndi chizindikiro choyamikira Mulungu, ndipo ndi chinthu chomwe chimachokera pansi pa mtima wa okhulupirira. Ndiponso, pa Chivumbulutso 1:6, tikuuzidwa kuti ntchito ya wansembe ndi kupereka nsembe kwa Mulungu.

Ngakhale ena amakwiya akamva nkhani ya zopereka, ndikofunikira kuzindikira madalitso omwe amabwera chifukwa chopereka. Ambiri amakonda kulandira, koma ndikukulimbikitsani kuti mupereke mokoma mtima, popanda kukakamizidwa, chifukwa Mulungu amakonda wopereka mokondwera ndipo amadalitsa ntchito ya manja ake.




Deuteronomo 15:10

Dzampatseni mwaufulu mosaŵinya, ndipo Chauta adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:6-7

Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:14

“Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndi ayani kuti tingathe kupereka mwaufulu motere? Paja zinthu zonse zimachokera kwa Inu ndipo zimene tikupereka kwa Inu nzanu zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:25

Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:38

Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:8

Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:10-12

Mulungu amene amapatsa mbeu kwa wobzala, ndiponso chakudya choti adye, adzakupatsani mbeu zoti mubzale, ndipo adzazichulukitsa. Adzachulukitsanso zipatso zake za chifundo chanu. Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko. Zoonadi ntchito imeneyi yomwe mukuchitira anthu a Mulungu, siingoŵathandiza pa zosoŵa zao, komanso chotsatira chake china nchakuti anthu ochuluka adzathokoza Mulungu kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:24

Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:1-2

Kunena za zopereka zothandizira akhristu a ku Yerusalemu, inunso muchite monga momwe ndidalongosolera m'mipingo ya ku Galatiya. Ngati Timoteo afika kwanuko, samalani kuti pasakhale kanthu komdetsa nkhaŵa pakati panu, pakuti iyenso akugwira ntchito ya Ambuye, monga ine. Tsono wina aliyense asamnyoze, koma mumthandize kupitiriza ulendo wake mwamtendere kubwerera kuli ine kuno. Paja ndikumuyembekeza pamodzi ndi abale ena. Kunena za mbale wathu, Apolo, ndamuumiriza kolimba kuti pamodzi ndi abale ena abwere kwanuko kudzakuwonani, koma iye sadafune kupita tsopano. Akadzapeza mpata wabwino, adzabwera. Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu. Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi. Abale, mukudziŵa kuti Stefanasi ndi a m'banja mwake ndiwo adayambirira kuloŵa chikhristu m'dziko la Akaiya. Ndipo akhala akudzipereka kutumikira anthu a Mulungu. Tsono ndikukupemphani kuti inunso muziŵamvera anthu otere, ndiponso aliyense wogwira ntchito ndi kutumikira modzipereka pamodzi nawo. Ndakondwa kuti Stefanasi, Fortunato ndi Akaiko afika, pakuti ngakhale inu simuli nane, iwo achita ngati kuloŵa m'malo wanu. Adandisangulutsa ine monga adasangulutsanso inu. Anthu otere muziŵalemekeza. Mipingo ya ku dziko la Asiya ikuti moni. Akwila ndi Prisika, pamodzi ndi mpingo umene umasonkhana m'nyumba mwao, akuti moni kwa inu nonse, akhristu anzao. Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 27:30

“Chigawo chilichonse chachikhumi cham'dziko, kaya ndi cha mbeu zam'nthaka, kaya ndi cha zipatso zam'mitengo, nchake cha Chauta. Chimenecho nchopatulikira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:10

Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:11-12

Tsono ngati mwakhala osakhulupirika pa chuma chonyengachi, ndani nanga adzakusungizeni chuma chenicheni? Ndipo ngati mwakhala osakhulupirika ndi za wina, ndani adzakupatseni zimene zili zanuzanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:2

Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 12:17-18

Ku midzi yonse kumene mukakhale, musadzadye chachikhumi cha tirigu wanu, kapena cha vinyo wanu kapena cha mafuta anu aolivi. Kumenekonso musakadye kalikonse kamene mwakapereka kwa Chauta, monga ana a ng'ombe ndi a zoŵeta zina oyamba kubadwa, kapena mphatso zimene mwalonjeza kuti mudzapereka kwa Chauta, kapena zopereka zanu zaufulu, kapena zopereka zina zilizonse. Inuyo ndi ana anu, pamodzi ndi antchito anu, ndi Alevi amene akhala m'midzi mwanu, muzikadya zopereka zonsezi pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzakhala atasankha. Kumenekonso muzidzasangalala pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, chifukwa cha ntchito zanu zonse zoyenda bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 14:22-23

Chachikhumi muziika padera, ndiye kuti limodzi mwa magawo khumi a zokolola zanu za chaka ndi chaka. Tsono pitani mukakhale pa malo amodzi amene Chauta, Mulungu wanu, adzasankhula kuti anthu azidzampembedzerapo. Ndipo magawo achachikhumi ameneŵa mudyere pa malo amenewo, pamaso pa Mulungu wanu. Magawo ameneŵa ndi a tirigu, vinyo ndi mafuta aolivi, ndiponso ana oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a nkhosa. Muzichita zimenezi masiku onse, kuti motero muphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 16:17

Ndipo pobwera pamaso pa Chauta, asamadzakhale chimanjamanja, koma munthu aliyense azidzabwera ndi mphatso monga momwe angathere, molingana ndi madalitso amene Chauta, Mulungu wanu, adampatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 31:5

Tsono lamulo limenelo atangolilengeza, pomwepo Aisraele adayamba kupereka kwambiri zipatso zoyamba kucha za tirigu, vinyo, mafuta, uchi ndi zonse zam'minda. Adabweranso ndi zachikhumi zambirimbiri za zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 10:37

Ndipo ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, tidzaperekanso kwa ansembewo mtanda wathu wa buledi wa ufa woyamba, ndiponso mphatso zathu zina, monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa Alevi chimodzi mwa zigawo khumi za zinthu za m'minda mwathu, pakuti Alevi ndiwo amene amasonkhanitsa zigawo zonse zachikhumi m'midzi yathu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:1-3

Chauta akuthandize pa tsiku lamavuto. Mulungu wa Yakobe akuteteze. Akutumizire chithandizo kuchokera ku malo ake oyera, akuchirikize kuchokera ku Ziyoni. Alandire zopereka zako zonse, akondwere ndi nsembe zako zopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-21

“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:7

Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:10-12

Aliyense abwere ndi chachikhumi chathunthu ku Nyumba yanga, kuti m'menemo mukhale chakudya chambiri. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Mundiyese tsono, ndipo muwone ngati sinditsekula zipata zakumwamba ndi kukugwetserani madalitso ochuluka. Ndidzaletsa tizilombo kuti tisadye mbeu zanu, mipesa yanu sidzaleka kubala. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Motero anthu a mitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:8

Ine ndikuti, Kodi munthu angathe kubera Mulungu? Komabe inu mumandibera. Inu mumati, ‘Kodi timakuberani bwanji?’ Ine ndikuti, Mumandibera pa zachikhumi zanu ndi zopereka zina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 28:18-22

Yakobeyo adadzuka m'maŵa kwambiri, natenga mwala uja adaatsamirawu, nauimiritsa kuti ukhale mwala wachikumbutso. Tsono adauthira mafuta mwalawo. Ndipo malowo adaŵatchula Betele. Poyamba mudziwo unkatchedwa Luzi. Konzeka, upite ku Mesopotamiya, kwao kwa Betuele, bambo wa mai wakoyu. Kumeneko ukakwatire mmodzi mwa ana aakazi a Labani, mlongo wa mai wako. Pomwepo Yakobe adalumbira kwa Mulungu, adati, “Mukakhala nane ndi kunditchinjiriza pa ulendo wangawu, ndipo mukandipatsa chakudya ndi zovala, ndi kundibwezera bwino kwathu kwa atate anga, mudzakhala Mulungu wanga. Mwala wachikumbutso ndauimiritsawu udzakhala nyumba yanu, ndipo ine ndidzakupatsani gawo lachikhumi la zonse zimene mudzandipatse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:10

Aliyense abwere ndi chachikhumi chathunthu ku Nyumba yanga, kuti m'menemo mukhale chakudya chambiri. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse. Mundiyese tsono, ndipo muwone ngati sinditsekula zipata zakumwamba ndi kukugwetserani madalitso ochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:21

Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:6

Nkhanitu ndi iyi: wobzala pang'ono, adzakololanso pang'ono, wobzala zochuluka, adzakololanso zochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:5

‘Muzipereka zopereka kwa Chauta. Tsono aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka, azibwera ndi zopereka izi: golide, siliva, mkuŵa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 54:6

Ndidzapereka nsembe kwa Inu mwaufulu. Ndidzatamanda dzina lanu, Inu Chauta, popeza kuti ndinu abwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:16

Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:1-4

Yesu atakweza maso, adaona anthu olemera akuponya zopereka zao m'bokosi la ndalama m'Nyumba ya Mulungu. Yesu adaŵauzanso kuti, “Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi zazikulu. Kudzakhala njala ndi mliri ku malo osiyanasiyana. Kudzakhalanso zoopsa ndi zizindikiro zodabwitsa mu mlengalenga. “Koma zisanachitike zonsezi, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzapita nanu ku milandu ku nyumba zamapemphero, nadzakuponyani m'ndende. Adzakuperekani kwa mafumu ndi kwa akulu ena a Boma chifukwa chotsatira Ine. Umenewu udzakhala mpata wanu wondichitira umboni. Tsono mudziŵiretu kuti musadzachite kukonzekera mau oti mudzaŵayankhe pamlandupo. Ineyo ndidzakupatsani mau ndi nzeru zimene adani anuwo sadzatha konse kuzikana kapena kuzitsutsa. Makolo anu omwe, abale anu, anansi anu, ndi abwenzi anu, amenewo adzakuperekani kwa adani anu, ndipo ena mwa inu mudzaphedwa. Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma silidzatayikapo tsitsi lanu ndi limodzi lomwe. Mukadzalimbikira, ndiye mudzapate moyo wanu.” Adaonanso mai wina wamasiye akuponyamo tindalama tiŵiri. “Pamene mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, dziŵani kuti chiwonongeko chake chafika. Pamenepo amene ali m'Yudeya athaŵire ku mapiri, amene ali mumzinda atulukemo, ndipo amene ali ku minda asadzaloŵenso mumzindamo. Chifukwa masiku amenewo adzakhala masiku akulipsira, kuti zonse zija zimene zidaalembedwa m'Malembo zipherezere. Ali ndi tsoka azimai amene adzakhale ndi pathupi, ndiponso azimai oyamwitsa ana masiku amenewo. Pakuti padzagwa masautso aakulu pa dziko lino, ndipo Mulungu adzaŵakwiyira Aisraeleŵa. Adzaphedwa pa nkhondo yoopsa, nkutengedwa ngati akapolo a anthu a mitundu ina. Kenaka Yerusalemu akunja adzampondereza mpaka pa mapeto ake a nthaŵi ya akunjawo.” Dan. 9.26; Mika 3.12; Zak. 11.6. “Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuŵa, pa mwezi ndi pa nyenyezi. Pansi pano anthu a mitundu yonse adzada nkhaŵa nkutha nzeru, pomva kukokoma kwa nyanja ndi mafunde ake. Ena adzakomoka ndi mantha poyembekezera zimene zikudza pa dziko lonse lapansi, pakuti mphamvu zonse zakuthambo zidzagwedezeka. Pamenepo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo, ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire nkukweza mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.” Pambuyo pake Yesu adaŵaphera fanizo adati, “Yang'anani mkuyu ndi mitengo ina yonse. Pamenepo Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa ena onseŵa. Mukamaona kuti masamba akuphuka, mumadziŵa kuti chilimwe chayandikira kale. Momwemonso, mukadzaona zija ndanenazi zikuchitika, mudzadziŵe kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi. Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse. Thambo ndi dziko lapansi zidzatha, koma mau anga sadzatha mphamvu konse.” “Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa. Pajatu lidzaŵagwera ngati msampha anthu onse okhala pa dziko lonse lapansi. Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.” Masiku onse Yesu ankaphunzitsa m'Nyumba ya Mulungu, koma usiku ankatuluka kukakhala ku phiri lotchedwa Phiri la Olivi. Tsono anthu onse ankalaŵirira m'mamaŵa kubwera kwa Iye ku Nyumba ya Mulungu kudzamva mau ake. Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:2

Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:18

Ndalandiradi zonse, ndipo ndili nazo zochuluka. Ndili ndi zonse zofunika tsopano, popeza kuti ndalandira kwa Epafrodito zimene mudanditumizira. Zili ngati chopereka cha fungo lokoma, ngati nsembe imene Mulungu ailandira ndi kukondwera nayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:6

Munthu amene akuphunzira mau a Mulungu, agaŵireko mphunzitsi wake zabwino zonse zimene iye ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:5

Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:8

Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:12

Malinga munthu akakhala ndi changu cha kupereka, Mulungu amalandira mokondwa zimene munthuyo ali nazo, ndipo samkakamiza kuti apereke zimene alibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:18

Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:12-13

Ndidzambwezera chiyani Chauta pa zabwino zonse zimene adandichitira? Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:21

Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:26

Tsiku lathunthu anthu oipa amasirira zinthu, koma omvera Mulungu amapatsa ndipo alibe kaliwumira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:18

Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:14-15

“Koma perekani nsembe zanu zothokozera kwa Mulungu, ndipo muchite zimene mudalumbira kwa Wopambanazonse. Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto. Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:17

Mulungu wanga, ndikudziŵa kuti Inu mumapenyetsetsa mtima, ndipo mumakondwera ndi anthu achilungamo. Ndapereka mwaufulu zinthu zonse ndi mtima wolungama, ndipo tsopano ndaŵaona anthu anu amene ali panoŵa nawonso akupereka mwaufulu ndi mokondwa kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:7

Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:9

Mukudziŵa kukoma mtima kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ngakhale anali wolemera, adakhala mmphaŵi chifukwa cha inu, kuti ndi umphaŵi wakewo inu mukhale olemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 26:1-2

Mukadzaloŵa ndi kukhazikika m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo, Motero tsopano, ndikubwera kwa Chauta ndi gawo la zokolola zoyamba za m'dziko limene wandipatsa.” Apo mutatula pansi dengulo pamaso pa Mulungu, mumpembedze pomwepo. Kondwani popeza kuti Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani zabwino, inu ndi a m'banja mwanu. Mukondwe inu ndi Alevi, ndiponso alendo amene mumakhala nawo. Chaka chachitatu chilichonse muzipereka chopereka chachikhumi cha zokolola zanu kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, kuti kumizinda kumene amakhala iwoŵa, adzakhale ndi chakudya chokwanira. Mutachita zimenezi, munene kwa Chauta kuti, “Palibe nchimodzi chomwe chopereka chachikhumi chimene chatsalako m'nyumba mwanga. Zonse ndapereka kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, monga mudandilamulira. Sindidanyoze kapena kuiŵalapo malamulo anu ndi limodzi lomwe. Pa za chachikhumi sindidadyepo nchimodzi chomwe pamene ndinkalira maliro. Pamene ndinali woipitsidwa pa zachipembedzo, sindidagwirepo nchimodzi chomwe. Ndipo sindidaperekepo nchimodzi chomwe kuperekera anthu akufa. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndakumverani. Zonse zimene mudalamula za chopereka chachikhumi ndachita. Yang'anani pansi kuchokera kumwambako ku malo anu oyera, ndipo mudalitse anthu anu Aisraele. Mudalitsenso dziko ili lamwanaalirenji limene mwatipatsali, monga momwe mudalonjezera makolo athu.” Chauta, Mulungu wanu, akukulamulani lero lino kuti mumvere malangizo ndi malamulo ake. Tsono muŵamveredi ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Lero mwamdziŵa Chauta kuti ndi Mulungu wanu. Mwalonjeza kumvera Iyeyo, kusunga malangizo ndi malamulo ake, ndi kuchita zonse zimene akulamulani. Lero Chauta wakulandirani ngati anthu ake, monga momwe adakulonjezerani, malinga nkusunga malamulo ake onse. Motero pa matamando, pa mbiri ndi pa ulemerero adzakukwezani kupambana mitundu ina yonse ya anthu imene adailenga, ndipo mudzakhala anthu ake oyera mtima, monga momwe adalonjezera. aliyense mwa inu pa zokolola zonse zoyamba zimene adazipeza m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, atengeko zina ndi kuziika m'dengu, ndipo apite nazo ku malo amene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azidzapembedzerako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 36:5

nadzauza Mose kuti, “Anthu akubwera ndi zipangizo za ntchitoyi zochuluka, kuposa m'mene zidzafunikire pogwira ntchito imene Chauta adalamula kuti ichitike.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 4:5

Perekani nsembe zanu ndi mtima wolungama, ikani mitima yanu pa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:33-34

Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:3-4

Koma iwe ukamapereka zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziŵe zimene dzanja lako lamanja likuchita. Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu? “Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’ Paja zimenezi amazifunafuna ndi anthu akunja. Atate anu akumwamba amadziŵa kuti mukuzisoŵa zonsezi. Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso. Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira. Ukatero, zachifundo zakozo zidzakhala zodziŵa iwe wekha. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:10

Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:23

Koma wopereka mtima wake kwa Ine mothokoza, ndiye amene amandilemekeza. Woyenda m'njira zolungama, ndidzamuwonetsa chipulumutso changa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 14:20

Atamandike Mulungu Wopambanazonse, amene adakupatsa mphamvu zogonjetsera adani ako onse.” Pamenepo Abramu adapereka kwa Melkizedeki chigawo chachikhumi cha zinthu zonse zimene adaalanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:35

Pa zonse ndakuwonetsani kuti pakugwira ntchito kolimba motere, tiyenera kuthandiza ofooka. Kumbukirani mau aja a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupatsa kumadalitsa munthu koposa kulandira.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:9

Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:27

Chauta ndi Mulungu, ndipo watipatsa kuŵala. Yambani mdipiti wachikondwerero mutatenga nthambi, mpaka kukafika ku guwa lansembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:5

Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:26

Pakuti mipingo ya ku Masedoniya, ndi ya ku Akaiya idakoma mtima mpaka kupereka zothandiza osauka pakati pa anthu a Mulungu a ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:40

Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:21

Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:27

Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:35

M'maŵa mwake adatulutsa ndalama ziŵiri zasiliva, nazipereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Adamuuza kuti, ‘Msamalireni bwino, ndipo mukamwazanso ndalama zina, ndidzakubwezerani pobwera.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:10

Adangopempha chokhachi kuti tisaleke kukumbukira anthu ao aumphaŵi. Ndipotu chimenechi ndicho ndakhala ndikuchita moikapo mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:5

Nchifukwa chake ndidaganiza kuti ndiyenera kupempha abale ameneŵa kuti abwere kwa inu ndisanafike ineyo, ndipo kuti akonzeretu mphatso imene mudalonjeza kale. Pamenepo mphatsoyo idzakhala yokonzekeratu, ndipo idzakhaladi mphatso yeniyeni, osati kanthu kamene mwapereka mokakamizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:5

Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:12

Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika, salephera kumva kulira kwao ndipo amalanga anthu oŵazunzawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:1

Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:15

Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:17

Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 41:1

Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:27

Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:8

Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:44-45

Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:8

Chiphuphu chili ngati mankhwala amwai kwa wochiperekayo, kulikonse kumene amapita, amalemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:8

Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:29

Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:19

Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:108

Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:10

mukamadyetsa anthu anjala, ndi kuthandiza anthu ozunzika, ndiye kuti mdima wokuzingani udzasanduka kuŵala ngati kwa usana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:7

Zonse mudalandira pakulu, monga kukhulupirira, kulankhula, kudziŵa zinthu, kuchita changu pa zonse, ndiponso kutikonda. Motero tifuna kuti muperekenso pakulu zachifundozi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:13

Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:17

Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:8

Nsembe ya anthu oipa mtima imamuipira Chauta, koma pemphero la anthu olungama limamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:3

Komanso kuwonjezera pa zonse zimene ndidaperekera Nyumba yoyerayo, ndili nachonso chuma changa cha golide ndi siliva. Ndipo chifukwa cha kudzipereka kwanga pa Nyumba ya Chauta wanga, ndikuchiperekanso chumacho kwa Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:3

Yohana, mkazi wa Kuza, kapitao wa Herode; Suzana, ndiponso azimai ena ambiri amene ndi ndalama zao ankathandiza Yesu ndi ophunzira ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:29

Chifukwa cha Nyumba yanu ya ku Yerusalemu, mafumu amabwera ndi mphatso kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:16-17

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto. Kuli bwino kudyera masamba pali chikondi, kupambana kudyera nyama ya ng'ombe yonenepa pali chidani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:11

Adzakulemeretsani pa zonse, kuti mukhale oolowa manja ndithu, kotero kuti ambiri adzathokoza Mulungu chifukwa cha mphatso yanu imene tiŵatengereko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 21:2

Mwaipatsa zimene mtima wake umakhumba, simudaimane zimene pakamwa pake padapempha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:8

Koma munthu wa mtima wabwino amalingalira zabwino, ndipo amalimbikira kuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:32

Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:23

“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:9

Amapereka chithandizo mwaufulu, amaoloŵa manja kwa anthu osauka. Chilungamo chake chidzakhala chamuyaya, adzakhala wamphamvu ndipo anthu adzampatsa ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:24-25

Wina amatha kupatsako anzake zinthu mwaufulu, komabe amanka nalemereralemerera. Wina nkukhala wakaligwiritsa, nakhalabe wosauka. Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:15

Inu Afilipi, mukudziŵa inu nomwe kuti pamene ndidachoka ku Masedoniya, masiku oyamba aja akulalika Uthenga Wabwino, panalibe mpingo wina wogwirizana nane pa zoyenera kulipira kapena kulandira, koma inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17

Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:10

Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:6

Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:31

Wopondereza mmphaŵi, amachita chipongwe Mlengi wake, koma wochitira chifundo osauka, amalemekeza Mlengi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:21

Ndipo munthu aliyense, monga momwe mtima wake unkafunira, adabwera kwa Chauta ndi zopereka zopangira chihema chamsonkhano cha Chauta. Adabwera nazo zonse zogwiritsira ntchito potumikira, ndi zonse zopangira zovala zopatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:1

Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 16:16-17

Anthu aamuna onse a mtundu wanu azidzabwera kudzapembedza Chauta, Mulungu wanu, ku malo achipembedzo, katatu pa chaka. Azidzafika pa nthaŵi ya Paska, pa nthaŵi ya chikondwerero cha kholola ndiponso pa nthaŵi ya chikondwerero cha misasa. Ndipo pobwera pamaso pa Chauta, asamadzakhale chimanjamanja, koma munthu aliyense azidzabwera ndi mphatso monga momwe angathere, molingana ndi madalitso amene Chauta, Mulungu wanu, adampatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 4:4

Abele nayenso adatenga ana oyamba kubadwa a nkhosa zake, naŵapereka ngati nsembe, pamodzi ndi mafuta ake omwe. Tsono Chauta adakondwera ndi Abele, nalandira nsembe yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:23-24

“Nchifukwa chake ngati wabwera ndi chopereka chako ku guwa, nthaŵi yomweyo nkukumbukira kuti mnzako wina ali nawe nkanthu, siya chopereka chakocho kuguwa komweko, ndipo pita, kayambe wayanjana naye mnzakoyo. Pambuyo pake ndiye ubwere kudzapereka chopereka chako chija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 12:41-44

Tsiku lina Yesu adaakhala pansi kuyang'anana ndi bokosi loponyamo ndalama zopereka ku Nyumba ya Mulungu. Ankayang'anitsitsa m'mene anthu ankaponyera ndalama zao. Anthu ambiri achuma ankaponyamo ndalama zambiri. Koma padafika mai wina wamasiye, wosauka. Iyeyu adangoponyamo tindalama tiŵiri. Tsono Yesu adaitana ophunzira ake naŵauza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti mai wamasiye wosaukayu waponyamo koposa anthu ena onseŵa, amene akuponya ndalama m'bokosimu. Chifukwa ena onseŵa angoponyamo zimene atapa pa zochuluka zimene ali nazo. Koma maiyu, mwa umphaŵi wake, waponyamo zonse zimene anali nazo, ngakhale zimene akadagulira chakudya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:29

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Bwerani ndi zopereka, ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake. Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:8

Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Bwerani ndi zopereka, ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:2-3

Akutumizire chithandizo kuchokera ku malo ake oyera, akuchirikize kuchokera ku Ziyoni. Alandire zopereka zako zonse, akondwere ndi nsembe zako zopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 35:29

Motero Aisraele onse, amuna ndi akazi omwe, amene adafuna ndi mtima wao wonse kupereka zao ku ntchito zimene Chauta adalamula kudzera mwa Mose, adabwera ndi zopereka zao kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:5

“Mukamapereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, Mulungu wanu, muchite mwa njira yoti mulandiridwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:9

Tsono anthu adakondwa chifukwa chakuti akulu aowo ankapereka mwaufulu ndiponso ndi mtima wao wonse. Nayenso mfumu Davide adakondwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:2

“Uza Aisraele apereke zopereka zao kwa Ine. Tsono iwe ulandire zoperekazo kwa munthu aliyense wa mtima wofuna kupereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu, ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kwakukulu. M'dzina la Yesu, ndabwera kudzakuthokozani ndi mtima wachimwemwe chifukwa cha kukhulupirika kwanu ndi kupereka kwanu. Ndimapereka mtima wanga kukulemekezani ndi kukutamandani ndi chuma changa, ndi ntchito ya manja anga, pakuti chilichonse chimene ndalandira kuchokera kwa inu, ndikubwezerani. Atate okondedwa, ikani mumtima mwathu mbewu yofuna kubzala mu ufumu wanu, kuti tikulitse mawu anu pano padziko lapansi kudzera mu chopereka chathu m'nyumba mwanu. Tikukupatsani zabwino koposa chifukwa mudatipatsa zabwino koposa chifukwa cha chikondi chanu pa ife, landirani chopereka chathu ndipo chikweze ngati fungo labwino pamaso panu. Mawu anu amati: "Wobzala pang'ono, adzakolola pang'ono; wobzala mochuluka adzakolola mochuluka." Ambuye, momwemonso, tilole kuti tikhale njira yodalitsira ndi kubzala m'miyoyo ya ena, tipatseni mtima wopatsa ndi wosunga, chifukwa kupatsa n'kwabwino kuposa kulandira, yeretsani zolinga zathu, kuti miyoyo yathu ikhale nsembe yokondweretsa inu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa