Ndikudziwa kuti zizolowezi zoipa zimakhala ndi zotsatirapo zoipa pa moyo wathu, osati kungowononga thupi lathu lokha, komanso mzimu wathu. Zimamanga munthu ngati chingwe champhamvu. Mwina ukuganiza kuti n’zovuta kusiya chizolowezi chimene chikukuvuta, koma ndikufuna ndikuuze za yankho labwino kwambiri: magazi a Yesu.
Ukapita kwa Iye ndi kulira kwa Iye, ndiye wabwino komanso wolungama kuti akuthandize ndi kukulimbitsa m’zofooka zako zonse. Sikuti udzitheke pa mphamvu zako, chifukwa sizingatheke ndi mphamvu zako wekha. Ndi mphamvu ya Khristu yosintha moyo ikugwira ntchito mwa iwe.
Ndikukulimbikitsa kuti usataye mtima. Ukadapumabe, pali chiyembekezo. Yesu angasinthe moyo wako ndi kukupanga munthu watsopano ngati ungomupempha ndi kumufunafuna Iye, pakuti zonse n’zotheka mwa Khristu wokulimbitsa.
Mawu a Mulungu m’buku la Yesaya 5:11 amati: “Tsoka kwa iwo akuuka mamawa kuti atsate moŵa; amene akhala usiku kufikira vinyo awatentha!”
Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse.
Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]
Usakhale pakati pa anthu amene amaledzera, kapena pakati pa anthu odya nyama mwadyera. Paja chidakwa ndi munthu wadyera adzasanduka amphaŵi, ndipo munthu waulesi adzasanduka mvalansanza.
Ndani ali ndi tsoka? Ndani ali ndi chisoni? Ndani ali pa mkangano? Ndani akudandaula? Ndani ali ndi zilonda zosadziŵika magwero ake? Ndani ali wofiira maso? Usasirire zakudya zake zokoma, poti zimenezi ndi zakudya zonyenga. Ndi amene amakhalitsa pamene pali vinyo, amene amamwa nawo vinyo wosanganiza ndi zina. Usatengeke mtima ndi kufiira kwa vinyo, pamene akututuma m'chikho namakoma poloŵa ku m'mero. Potsiriza pake amaluma ngati njoka, ndipo amanjenjedula ngati mphiri.
Yesu adaŵayankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo.
Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pa kuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo. Tidziŵa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse. Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.
Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Anthu okhuta vinyo amanyodola anzao, omwa zaukali amautsa phokoso. Aliyense wosokera nazo zimenezi ndi wopanda nzeru.
Zochita za khalidwe lokonda zoipa zimaonekera poyera. Ndi izi: Dama, kuchita zonyansa, kusadziletsa, Ndiye mvetsani, ine Paulo ndikukuuzani kuti mukalola kukuumbalani, Khristu simupindula nayenso konse ai. kupembedza mafano, ufiti, chidani, kukangana, kaduka, kupsa mtima, kudzikonda, kusagwirizana, kuchita mipatuko, dumbo, kuledzera, kudakwa pa maphwando achipembedzo, ndi zina zotere. Ndikukuchenjezani tsopano, monga ndidaachitanso kale, kuti anthu amene amachita zotere, sadzalandirako Ufumu wa Mulungu.
Munthu wosadzimanga mtima ali ngati mzinda umene adani authyola nkuusiya wopanda malinga.
Chitsiru chimene chimabwerezabwereza za uchitsiru wake chili ngati galu wodya masanzi ake omwe.
Iwe Lemuwele, mafumu sayenera kumamwa vinyo, olamulira asamalakalaka zakumwa zaukali, kuwopa kuti angaiŵale malamulo a dziko, ndi kukhotetsa zinthu zoyenerera anthu osauka.
Potsata nzeruzo ndidaayesa kudzisangalatsa ndi vinyo, koma umenewo unali uchitsiru. Ndinkati mwina kapena njira yotere nkukhala yopambana, imene anthu amatsata pofuna kusangalala pa masiku oŵerengeka a moyo wao.
Tsoka kwa amene amadzuka m'mamaŵa nathamangira chakumwa choledzeretsa, amene amamwa mpaka usiku kufikira ataledzera kotheratu.
Tsoka kwa zidakwa zimene zimaika mtima pa vinyo! Tsoka kwa anthu amene saopa konse kusakaniza zakumwa zaukali!
Nawonso aŵa ali punzipunzi chifukwa cha vinyo, akudzandira ndi zakumwa zaukali. Ansembe ndi aneneri ali punzipunzi ndi zakumwa zaukali. Onsewo ndi osokonezeka chifukwa cha vinyo, ali dzandidzandi chifukwa cha zakumwa zaukali. Amamvetsa molakwa zimene amaziwona m'masomphenya, amalephera kuweruza milandu imene amadzaŵatulira. Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha, palibenso malo opanda uve.
Munthuyo akuchita ngati kudya phulusa, maganizo ake opusa amsokeretsa kotero kuti sangapulumutsenso moyo wake. Sangathenso kudzifunsa kuti, “Kodi chinthu chili m'manja mwangachi si chabodza?”
Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo.
“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Koma kutanganidwa ndi zapansipano, kukondetsa chuma ndi kukhumba zinthu zina zambiri kumaloŵapo nkufooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso.
Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”
“Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.”
Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake.
Mukudziŵa paja kuti mukadzipereka kuti mukhale akapolo a munthu nkumamumvera, ndiye kuti ndinu akapolo a munthu womumverayo. Tsono ngati ndinu akapolo a uchimo, mudzafa. Koma ngati ndinu akapolo a Mulungu, mudzakhala olungama pamaso pake.
Ndikukupherani fanizo la ukapololi kuti mungalephere kumvetsa bwino zimenezi. Kale munkadzipereka kuti mukhale akapolo a zonyansa ndi zosalongosoka zonkirankira. Chonchonso tsopano mudzipereke kuti musanduke atumiki a Mulungu ochita zachilungamo, kuti mukhale oyera mtima.
Ndikudziŵa kuti mwa ine simukhala kanthu kabwino. Ndikamati, “ine”, ndikunena khalidwe langa lokonda zoipa. Ngakhale ndimafuna kuchita zabwino, komabe sindizichita. Sindichita zabwino zimene ndifuna, koma ndimachita zoipa zimene sindifuna. Mwachitsanzo, malamulo amati mkazi wokwatiwa ngwomangidwa kwa mwamuna wake, nthaŵi yonse pamene mwamuna wakeyo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi uja amamasuka ku malamulo okhudza za mwamuna wake aja. Ngati ndichita zimene sindizifuna, sindinenso amene ndimazichita, koma uchimo umene umakhala mwa ine.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa.
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene.
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
Monga inu simudziŵa kuti pa mpikisano wa liŵiro onse amathamanga, koma mmodzi yekha ndiye amalandira mphotho? Tsono kuthamanga kwanu kukhale kwakuti nkukalandira mphothoyo. Aliyense wothamanga pa mpikisano wa liŵiro amadziletsa pa zonse. Iwowo amachita zimenezi kuti akalandire mphotho ya nkhata yamaluŵa yotha kufota. Koma mphotho imene ife tidzalandira, ndi yosafota. Nchifukwa chake ndimathamanga monga munthu wodziŵa kumene walinga. Ndiponso ndikamachita mpikisano womenyana, sindichita ngati munthu amene angomenya mophonya. Ndimazunza thupi langa ndi kuligonjetsa, kuti likhale ngati kapolo wondimvera. Ndimachita zimenezi kuwopa kuti ine ndemwe, amene ndidaitana ena ku mpikisano, ndingapezeke wosayenera kuchita nao mpikisanowo.
Zinthu zonse nzololedwa, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwa, koma si zonse zimathandiza.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti, “Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo. Ndidzakhala Mulungu wao, iwo adzakhala anthu angaanga.” Nchifukwa chake Ambuye akuti, “Tulukani pakati pao, ndi kudzipatula. Musakhudze kanthu kosayera, ndipo ndidzakulandirani. Ndidzakhala Atate anu, inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi, akutero Ambuye Mphambe.”
Tsono, inu okondedwa, popeza kuti tili ndi malonjezo ameneŵa, tiyeni tidzichotsere zinthu zonse zodetsa thupi lathu kapena mtima wathu. Ndipo pakuwopa Mulungu tiziyesetsa ndithu kukhala oyera mtima.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka. Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.
Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha.
Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.
Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.
Nchifukwa chake tsono tisagone tulo monga momwe amachitira anthu ena, ife tikhale maso, tikhale osaledzera. Anthu ogona tulo, amagona usiku, anthu oledzera amaledzera usiku. Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.
ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse. Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.
Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo. Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola. Pamenepo chilakolakocho chimachita ngati chatenga pathupi nkubala uchimo. Tsono uchimowo utakula msinkhu, umabala imfa.
Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso. Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.
Nchifukwa chake mtima wanu ukhale wokonzeka. Khalani tchelu. Khazikitsani chiyembekezo chanu kotheratu pa kukoma mtima kwa Mulungu pamene Yesu Khristu adzaoneke. Muzikhala ngati ana omvera, osatsatanso zimene munkalakalaka pamene munali osadziŵa. Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse.
Okondedwa anga, popeza kuti ndinu alendo pansi pano, ndikukupemphani kuti musagonjere zilakolako zathupi zimene zimachita nkhondo ndi mzimu wanu.
Tsono popeza kuti Khristu adamva zoŵaŵa m'thupi mwake, valani dzilimbe ndi maganizo omwewo, chifukwa munthu amene wamva zoŵaŵa m'thupi mwake, ndiye kuti walekana nawo machimo. Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen. Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo. Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu. Anthu akakuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, chifukwa ndiye kuti Mzimu wa ulemerero, Mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu. Pakati panu pasakhale ndi mmodzi yemwe wogwa m'mavuto chifukwa choti wapha munthu, kapena waba, kapena wachita choipa, kapena waloŵerera za eniake. Koma ngati mumva zoŵaŵa chifukwa chakuti ndinu akhristu, musachite manyazi, koma mulemekeze Mulungu chifukwa cha dzinalo. Nthaŵi ndiye yafika yoti Mulungu ayambe kuweruza anthu ake. Tsono ngati chiweruzocho chiyambira pa ife, nanga podzafika pa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, ndiye kuti chidzakhala chotani? Paja mau a Mulungu akuti, “Ngati wolungama yemwe adzapulumuka movutikira, nanga munthu wochimwa, wonyozera za Mulungu, adzatani?” Nchifukwa chake anthu amene amamva zoŵaŵa monga Mulungu afunira, adzipereke m'manja mwa Mlengi wao wokhulupirika, ndi kumachitabe ntchito zabwino. Choncho, pa nthaŵi yatsala yoti mukhale pansi pano, simudzatsatanso zilakolako za anthu, koma mudzatsata kufuna kwa Mulungu. Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye. Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi.
Amaŵalonjeza ufulu, chonsecho eniakewo ndi akapolo a chivunde. Pajatu munthu amasanduka kapolo wa chimene chamugonjetsa.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Munthu amene amachimwa, ndi wa Satana, pakuti Satana ndi wochimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu adaoneka ndi cholinga chakuti aononge zochita za Satana.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.
Tikudziŵa kuti aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamsunga, ndipo Woipa uja sangamkhudze.
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku. Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera.
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Chauta adaŵatulutsa anthuwo mu mdima ndi m'chisoni muja, ndipo adadula maunyolo ao.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
“Kusala koona kumene ndimafuna ndi uku: masulani maunyolo ozunzira anzanu, masulani nsinga za goli la kuweruza mokondera. Opsinjidwa muŵapatse ufulu, muthetse ukapolo uliwonse.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu. Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Ngati diso lako la ku dzanja lamanja likuchimwitsa, likolowole nkulitaya. Ndi bwino koposa kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kusiyana nkuti thupi lako lonse aliponye ku Gehena. “Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.”
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha. Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse.
Mulungu adapereka Malamulo kuti anthu azindikire kuchuluka kwa machimo ao. Koma pamene uchimo udachuluka, kukoma mtima kwa Mulungu kudachuluka koposa.
Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene Mzimu wa Mulungu amaŵatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye. Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno. Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa.
Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe. Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga, ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo. Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Pamenepo wokhala pampando wachifumu uja adati, “Tsopano ndisandutsa zonse kuti zikhale zatsopano.” Adanenanso kuti, “Lemba zimenezi, pakuti mau ameneŵa ndi oona ndi oyenera kuŵakhulupirira.”