Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


104 Mauthenga a Mulungu Pankhani ya Kutchova Njuga

104 Mauthenga a Mulungu Pankhani ya Kutchova Njuga

Baibulo limatiphunzitsa kuti tiyenera kugwiritsa ntchito bwino chuma chathu posamalira mabanja athu, osati kuyika pachiwopsezo poganiza kuti tidzapeza chochulukirapo. Ngakhale Malemba sakamba mwachindunji za kutchova juga, amatipatsa malangizo oti timvetse maganizo a Mulungu pa nkhaniyi.

Mu Luka 12:15, timatichenjezedwa kuti: "Samalani ndipo musakhale adyera; moyo wa munthu sudalira kuchuluka kwa chuma chake." Uku kukundikumbusa kuti ndiyenera kusamala ndi zomwe ndili nazo.

Komanso, Baibulo limatilimbikitsa kukhala oyang'anira abwino pa chilichonse chimene tapatsidwa (Luka 12:42): "Ndani kwenikweni amene ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene ambuye wake adzamuyika kuti aziyang'anira antchito ake apakhomo, kuti azigawira chakudya chawo pa nthawi yake?" Izi zikutanthauza kuti ndiyenera kugwiritsa ntchito bwino chuma changa molingana ndi luso langa, ndikuyamikira zonse zomwe Mulungu wandipatsa, kuti ndisapote chifukwa cha zosankha zopanda nzeru.




1 Timoteyo 6:10

Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:22

Munthu wakaliwumira amafunitsitsa kulemera mofulumira, koma sadziŵa kuti umphaŵi udzamgwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:4

Usadzitopetse nkufuna chuma, udziŵe kuchita zinthu mwanzeru ndi kudziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:10

Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:11

Chuma chochipeza mofulumira chidzanka chitha pang'onopang'ono, koma chochipeza pang'onopang'ono chidzanka chichulukirachulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:11

Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:12

Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:17

“Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:13

“Musachenjeretse mnzanu kapena kumubera zinthu zake. Musasunge malipiro a munthu wantchito usiku wonse mpaka m'maŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:21

“Usasirire mkazi wa mnzako. Usasilire nyumba yake, munda wake, wantchito wake wamwamuna, wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzakoyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:2

Chuma chochipeza monyenga sichipindulitsa, koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:4

Manja aulesi amagwetsa munthu mu umphaŵi, koma manja achangu amalemeretsa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:4

Pa tsiku la mkwiyo wa Mulungu chuma sichithandiza konse, koma chilungamo ndiye chimapulumutsa ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:28

Wokhulupirira chuma chake adzafota, koma anthu a Mulungu adzaphukira ngati tsamba laliŵisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:27

Munthu wofunafuna phindu monyenga amavutitsa banja lake, koma munthu wodana ndi ziphuphu adzapeza bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:21

Choloŵa chopata mofulumira poyamba, sichidzakhala dalitso pambuyo pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:17

Amene amakondetsa zosangalatsa, adzasanduka munthu wosauka. Amene amakondetsa vinyo ndi mafuta, sadzalemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:20

Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma munthu wopusa amachiwononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:7

Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womkongozayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:16

Amene amapondereza osauka kuti aonjezere pa chuma chake, kapena amene amangopatsa zinthu olemera okha, adzasanduka wosauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:4-5

Usadzitopetse nkufuna chuma, udziŵe kuchita zinthu mwanzeru ndi kudziletsa. Ukangopeza chuma, uwona chapita kale, pakuti chimachita ngati chamera mapiko mwadzidzidzi, nkuyamba kuuluka kunka kumwamba ngati chiwombankhanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:6

Munthu wosauka amene amayenda mwaungwiro amaposa kwambiri munthu wolemera amene ali wonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:19-20

Wolima m'munda mwake adzakhala ndi chakudya chambiri, koma wonka nafuna zopanda pake adzasauka kwambiri. Eni dziko akachita zaupandu, oŵalamulira amachuluka. Koma anthu akakhala omvetsa ndi odziŵa zinthu, dzikolo limakhazikika nthaŵi yaitali. Munthu wokhulupirika adzakhala ndi madalitso ambiri, koma wofunitsitsa kulemera msanga sadzalephera kupeza chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:13-15

Pansi pano pali choipa china chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndachiwona: Chuma chopweteka mwiniwake yemwe. Ndiye chuma chimenecho chikamwazika moipa, munthuyo nkukhala ndi ana, amachita kusoŵa choŵapatsa ana akewo. Monga momwe munthu adabadwira m'mimba mwa mai wake opanda kanthu, chonchonso adzapita maliseche. Pa zonse zimene adakhetsera thukuta, palibe nchimodzi chomwe chimene adzatenge m'manja mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:2

Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene saadya? Chifukwa chiyani malipiro anu mukuwonongera zinthu zimene sizingakuchotseni njala? Mvetsetsani zimene ndikunena Ine, ndipo muzidya zimene zili zabwino, muzidzisangalatsa ndi zakudya zonona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 65:11-12

Koma inu amene mumakana Chauta, amene mumaiŵala phiri langa lopatulika, amene mumapembedza Gadi ndi Meni, milungu yobweretsa mwai ndi tsoka, nonsenu ndidzakufetsani ku nkhondo. Nonsenu mudzaphedwadi, chifukwa simudayankhe m'mene ndidakuitanani, ndipo simudamve m'mene ndidalankhula, koma mudachita zoipa pamaso panga. Mudasankha kuchita zoipa m'malo mwa zabwino.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:11

Munthu wopeza chuma pobera anthu ena, ali ngati nkhwali yokonkhomola mazira amene sidaikire. Masiku asanachuluke, chumacho chimamthera, potsiriza amasanduka ngati chitsilu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 7:19

Adzataya siliva wao m'miseu, ndipo golide wao adzamuwona ngati wonyansa. Siliva wao ndi golide wao sadzatha kuŵapulumutsa pa tsiku limene Chauta adzaonetse ukali wake. Chuma chaochi sichingaŵathandize kuthetsa njala, kapena kukhala okhuta, pakuti ndicho chidaŵagwetsa m'machimo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 2:1-2

Tsoka kwa anthu amene amakonzekera chiwembu, amene usiku wonse amalingalira ntchito zoipa. Akadzuka m'maŵa amakazichitadi, pakuti mphamvu zake ali nazo. Nyamukani, chokani, ano simalo opumulirapo. Zonyansa zanu zaŵaipitsa, zadzetsapo chiwonongeko choopsa. Munthu wina atamapita uku ndi uku akulalika zabodza kuti, ‘Ndithudi mudzakhala ndi vinyo ndi zakumwa zamphamvu zambiri,’ mlaliki wotere ndi amene anthu aŵa angamkonde. “Koma inu banja lonse la Yakobe, ndidzakusonkhanitsani. Onse otsala a ku Israele ndidzaŵasonkhanitsa pamodzi ngati nkhosa m'khola, ngati gulu la zoŵeta pa busa lake. Malowo adzakhala thithithi ndi chinamtindi cha anthu.” Woŵapulumutsa adzaŵatsogolera, ndipo onse adzathyola pa chipata nathaŵa. Idzayambira ndi mfumu yao kudutsa, Chauta adzakhala patsogolo pao. Akasirira minda, amailanda. Akakhumbira nyumba, amazilanda. Amavutitsa munthu ndi banja lake, naŵatengera zonse zimene ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 6:10-12

Kodi Ine ndingathe kuiŵala chuma chimene chili m'nyumba za anthu oipa, chimene adachipata monyenga, ndiponso muyeso wopereŵera umene uli wotembereredwa? Kodi ndingathe kulekerera munthu amene ali ndi sikelo zobera anzake ndiponso miyeso yonyenga? Anthu olemera amachita zankhondo. Anthu onse ndi abodza, amangokhalira kunama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Habakuku 2:9

Tsoka kwa amene amalemera ndi phindu lobera anzake, kuti akweze malo ake ndi kupewa zovuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-21

“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:26

Nanga ndiye kuti munthu angapindulenji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake? Munthu angalipire chiyani choti aombolere moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:21-24

Yesu adamuuza kuti, “Ngati ufuna kukhala wabwino kotheratu, pita, kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Koma pamene munthu uja adamva mau ameneŵa, adangochokapo ali wovutika mu mtima, chifukwa anali wolemera kwambiri. Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti nkwapatali kwambiri kuti munthu wolemera adzaloŵe mu Ufumu wakumwamba. Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:25

“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatsuka kunja kwa chikho ndi kwa mbale koma m'kati mwake m'modzaza ndi nzeru zakuba, ndi zaumbombo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:14-30

“Za Ufumu wakumwamba tingazifanizirenso motere: Munthu wina ankapita pa ulendo. Asananyamuke adaitana antchito ake, naŵasiyira chuma chake. Wina adampatsa ndalama zisanu, wina ziŵiri, wina imodzi. Aliyense adampatsa molingana ndi nzeru zake, iye nkuchokapo. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adapita nakachita nazo malonda nkupindula ndalama zinanso zisanu. Chimodzimodzinso amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adapindula ndalama zinanso ziŵiri. Koma amene adaalandira ndalama imodzi uja, adapita nakaikumbira pansi ndalama ya mbuye wake ija. “Patapita nthaŵi yaitali, mbuye wao uja adabwerako naŵaitana antchito ake aja kuti amufotokozere za zimene adaachita ndi ndalama zija. Asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ochenjera. Wantchito amene adaalandira ndalama zisanu uja adabwera ndi zisanu zinanso nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama zisanu. Onani, ndidapindula zisanu zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ Nayenso wantchito amene adaalandira ndalama ziŵiri uja, adabwera nati, ‘Ambuye, mudaandisiyira ndalama ziŵiri. Onani, ndidapindula ziŵiri zinanso: izi.’ Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’ “Nayenso amene adaalandira ndalama imodzi uja adabwera nati, ‘Ambuye, ine ndinkadziŵa kuti inu ndinu munthu wankhwidzi. Mumakolola kumene simudabzale, ndipo mumasonkhanitsa dzinthu kumene simudafese mbeu. Ndiye ndinkachita mantha, choncho ndidaakaikumbira pansi ndalama yanu ija. Nayi tsono ndalama yanuyo.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa ndi waulesi. Kani unkadziŵa kuti ineyo ndimakolola kumene sindidabzale, ndipo ndimasonkhanitsa dzinthu kumene sindidafese mbeu? Tsonotu udaayenera kukaiika ku banki ndalama yangayo, ine pobwera ndikadadzailandira pamodzi ndi chiwongoladzanja chake. Mlandeni ndalamayi, muipereke kwa amene ali ndi ndalama khumiyo. Pajatu aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina, choncho adzakhala ndi zochuluka koposa. Koma amene alibe kanthu, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe. Asanu opusa aja adangotenga nyale zao, osatenga mafuta ena apadera. Tsono mtumiki wopandapakeyu kamponyeni kunja ku mdima. Kumeneko azikalira ndi kukukuta mano.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 8:36

Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse za pansi pano, iyeyo nkutaya moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:14

Mbeu zogwera pa zitsamba zaminga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, koma pambuyo pake nkhaŵa, kukondetsa chuma, ndiponso khumbo la zokondweretsa za moyo uno zimaŵalepheretsa, ndipo zipatso zao sizikhwima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:15

Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:21

Potsiriza Yesu adati, “Zimatero ndi munthu amene amadziwunjikira chuma, koma sali wachuma konse pamaso pa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:33-34

Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupatse amphaŵi. Mudzipezere matumba a ndalama amene safwifwa, ndi kudziwunjikira chuma chokhalitsa Kumwamba; kumeneko mbala sizingafikeko, ndipo njenjete sizingachiwononge. Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:13

“Palibe wantchito amene angathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkunyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:14

Afarisi atamva zonsezi, adamseka Yesu, chifukwa iwo anali okonda ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:19-31

“Panali munthu wina wachuma, amene ankavala zovala zamtengowapatali, ndipo ankasangalala ndi kudyerera masiku onse. Tsono mbuye wakeyo adamuitana, namufunsa kuti, ‘Nchiyani chimene ndikumva za iwe? Undifotokozere za ukapitao wako, pakuti sungakhalenso kapitao ai.’ Panalinso munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadzagona pa khomo la munthu wachuma uja. Iyeyu anali ndi zilonda m'thupi lonse. Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma si pokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake. “Munthu wosauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m'manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m'manda. Pamene ankazunzika ku Malo a anthu akufa, wachuma uja adayang'ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro ali pambali pakepa. Pamenepo adanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m'madzi kuti adzaziziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m'moto muno.’ Koma Abrahamu adati, ‘Mwana wanga, kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zoŵaŵa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri. Ndiponso pakati pa ife ndi inu pali chiphompho, kotero kuti ofuna kuchoka kuno kuwolokera kwanuko, sangathe ai. Chimodzimodzinso kuchoka kwanuko kuwolokera kuno.’ “Apo wachuma uja adati, ‘Ndipotu ndikukupemphani atate, kuti mumtume Lazaroyo apite ku nyumba ya bambo wanga. Kumeneko ndili ndi abale anga asanu. Akaŵachenjeze, kuwopa kuti iwonso angabwere ku malo ano amazunzo.’ Koma Abrahamu adati, ‘Iwo ali ndi mabuku a Mose ndi a aneneri. Amvere zam'menemo.’ Apo kapitaoyo adayamba kuganiza mumtima mwake kuti, ‘Ndichite chiyani, popeza kuti mbuye wanga akundilanda ukapitao? Kulima, ai, ndilibe mphamvu. Kupemphapempha, ainso, kukundichititsa manyazi. Iye adati, ‘Iyai, atate Abrahamu, koma wina atauka kwa akufa nkupita kwa iwo, apo adzatembenuka mtima.’ Koma Abrahamu adamuuza kuti, ‘Ngatitu iwo samvera Mose ndi aneneri, sangathekenso ngakhale wina auke kwa akufa.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:22-25

Pamene Yesu adamva zimenezi, adamuuza kuti, “Ukusoŵabe chinthu chimodzi: kagulitse zonse zimene uli nazo. Ndalama zake ukapatse anthu osauka, ndipo chuma udzachipeza Kumwamba. Kenaka ubwere, uzidzanditsata.” Koma pamene munthu uja adamva zimenezi, adavutika mu mtima, pakuti adaali wolemera kwambiri. Yesu adamuyang'ana, nanena kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu. Nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 2:15-16

Apo Yesu adapanga mkwapulo wazingwe nayamba kuŵatulutsira onse kunja, pamodzi ndi nkhosa ndi ng'ombe zao zomwe. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama aja, naŵamwazira ndalama zao. Ndipo adalamula ogulitsa nkhunda aja kuti, “Izi zitulutseni muno. Nyumba ya Atate anga musaisandutse nyumba yochitiramo malonda.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:1-3

Munthu winanso, dzina lake Ananiya, pamodzi ndi mkazi wake Safira, adagulitsa munda wao. Pomwepo adagwa pansi ku mapazi a Petro, naafa. Pamene achinyamata aja adaloŵa, adampeza atafa kale. Adamnyamula nakamuika pafupi ndi mwamuna wake. Ndipo mpingo wonse ndi anthu onse amene adamva zimenezi, adagwidwa ndi mantha aakulu. Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Khonde la Solomoni. Mwa anthu enawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaalimba mtima kuti azisonkhana nawo, komabe anthu onse ankaŵatama. Ndipo anthu okhulupirira Ambuye ankachulukirachulukira, mwakuti linali ndithu gulu lalikulu la amuna ndi akazi omwe. Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m'miseu yamumzinda, nkumaŵagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiŵafike. Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yoŵaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa. Pamenepo mkulu wa ansembe onse pamodzi ndi anzake aja, ndiye kuti a m'chipani cha Asaduki, onsewo adadukidwa nazo. Tsono adagamula zochitapo kanthu. Adagwira atumwi aja, naŵatsekera m'ndende ya Boma. Koma usiku mngelo wa Ambuye adatsekula zitseko za ndendeyo naŵatulutsa. Adaŵauza kuti, Mopangana ndi mkazi wake, adapatulapo ndalama zina za mundawo, nakapereka zotsala kwa atumwi. “Pitani m'Nyumba ya Mulungu muzikauza anthu mau onse okhudza za moyo watsopanowu.” Atumwi aja adamveradi zimenezi, adakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu m'mamaŵa, nayamba kuphunzitsa. Pamene mkulu wa ansembe onse adafika pamodzi ndi anzake aja, adaitanitsa msonkhano wa Bungwe Lalikulu, ndiye kuti Bwalo lonse la akuluakulu a Aisraele. Tsono adatuma anthu kuti apite ku ndende akaŵatenge atumwi aja. Koma pamene anthuwo adafika kundendeko, sadaŵapezemo. Adabwerako nadzaŵafotokozera. Adati, “Takapeza ndende ili chitsekere ndithu, ndipo alonda ali chilili pa makomo, koma titatsekula zitseko, sitidapezemo munthu.” Pamene mkulu wa asilikali a ku Nyumba ya Mulungu ndi akulu a ansembe adamva mau ameneŵa, adatha nawo nzeru, osadziŵa kwachitika zotani. Koma munthu wina adadzaŵauza kuti, “Anthu amene mudaŵatsekera m'ndende aja, ali m'Nyumba ya Mulungu ndipo akuphunzitsa anthu.” Pamenepo mkulu wa asilikali uja pamodzi ndi asilikaliwo adapita nkukaŵatenga atumwiwo. Sadaŵatenge mwankhondo ai, chifukwa ankaopa kuti anthu angaŵaponye miyala. Atafika nawo, adaŵakhazika pamaso pa Bungwe Lalikulu lija, ndipo mkulu wa ansembe onse adayamba kuŵafunsa mafunso. Adati, “Paja tidakuletsani mwamphamvu kuti musaphunzitse konse m'dzina la Yesu, koma inu mwafalitsa zophunzitsa zanuzo m'Yerusalemu monse, ndipo mukufuna kusenzetsa ife imfa ya munthu ameneyu.” Koma Petro ndi atumwi enawo adati, “Tiyenera kumvera Mulungu koposa kumvera anthu. Koma Petro adamufunsa kuti, “Iwe Ananiya, chifukwa chiyani walola mtima wako kugwidwa ndi Satana mpaka kumanamiza Mzimu Woyera pakupatula ndalama zina za munda wako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:18-20

Simoni uja ataona kuti Mzimu Woyera waperekedwa kwa iwo atumwi aja ataŵasanjika manja, adafuna kuŵapatsa ndalama atumwiwo. Adati, “Bwanji mutandipatsako inenso mphamvu imeneyi, kuti aliyense amene ndikamsanjike manja, akalandire Mzimu Woyera.” Anthu ena okonda Mulungu adakaika maliro a Stefano namlira kwambiri. Petro adamuyankha kuti, “Ndalama zakozo ukatayike nazo pamodzi. Iwe ukuganiza kuti ungathe kupata mphatso ya Mulungu pakupereka ndalama kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:11

Koma ndidaakulemberani kuti musamayanjane ndi munthu amene amati ndi mkhristu, pamene chikhalirecho ndi munthu wadama, kapena waumbombo, wopembedza mafano, waugogodi, chidakwa, kapena wachifwamba. Munthu wotere musamadye naye nkomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:24

Munthu asamangodzifunira yekha zabwino, koma makamaka azifunira anzake zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:31

Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:2

Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:7

Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:28

Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:3-5

Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu. Amatero chifukwa Mpingowo ndi thupi lake, ndipo ife ndife ziwalo zake. Paja mau a Mulungu akuti, “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti aŵiriwo asanduke thupi limodzi.” Mau ameneŵa akutiwululira chinsinsi chozama, ndipo ndikuti chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo. Komabe akunenanso za inu, kuti mwamuna aliyense azikonda mkazi wake monga momwe amadzikondera iye mwini, ndiponso kuti mkazi aliyense azilemekeza mwamuna wake. Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopandapake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu. Mudziŵe ichi, kuti munthu aliyense wadama, kapena wochita zonyansa, kapena wa masiriro oipa (pakuti wa masiriro oipa ali ngati wopembedza fano) sadzaloŵa nao mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5

Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:11-12

Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja, kuti akunja azikulemekezani, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:22

ndipo mupewe choipa cha mtundu uliwonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:3

Asakhale chidakwa, asakhale wandeu, koma wofatsa, wosakangana ndi anthu, ndi wosakonda ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:17-19

Anthu amene ali olemera pa zinthu zapansipano, uŵalamule kuti asanyade kapena kudalira chuma chimene sichidziŵika ngati chidzakhalitsa. Koma azidalira Mulungu amene amatipatsa zonse moolowa manja kuti tisangalale nazo. Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao. Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:7

Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:34

Munkasaukira limodzi ndi amene adaaponyedwa m'ndende, ndipo mudalola mokondwa kuti alande chuma chanu, mutadziŵa kuti muli ndi chuma choposa ndi chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:5-6

Mverani, abale anga okondedwa, kodi suja Mulungu adasankha ooneka amphaŵi m'maso mwa anthu, kuti akhale olemera pa chikhulupiriro, ndi kuti alandire madalitso amene Iye adalonjeza anthu omukonda? Koma inuyo mwakhala mukumnyoza mmphaŵiyo. Kodi si anthu olemera amene amakupsinjani? Si anthu olemera kodi amene amakukokerani ku mabwalo amilandu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:13-15

Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,” m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira. Kwenikweni muyenera kumanena kuti, “Ambuye akalola, tikakhala ndi moyo, tidzachita chakutichakuti.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:1-3

Mverani tsono, inu anthu achumanu. Lirani ndi kufuula chifukwa cha zovuta zimene zikudzakugwerani. Abale, kumbukirani chitsanzo cha aneneri amene adalankhula m'dzina la Ambuye. Iwo adamva zoŵaŵa, komabe adapirira. Anthu amene timaŵatchula odala, ndi amene anali olimbika. Mudamva za kulimbika kwa Yobe, ndipo mudaona m'mene Ambuye adamchitira potsiriza, pakuti Ambuye ngachifundo ndi okoma mtima. Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula. Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu. Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo. Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe. Eliya anali munthu monga ife tomwe. Iye uja adaapemphera kolimba kuti mvula isagwe, ndipo mvula siidagwedi pa zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi. Atapempheranso, mvula idagwa, nthaka nkuyambanso kumeretsa mbeu zake. Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza, Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa. Golide wanu ndi siliva zachita dzimbiri, ndipo dzimbirilo lidzakhala mboni yokutsutsani. Lidzaononga thupi lanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano amene ali otsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2

Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:3

Chifukwa chokondetsa chuma, iwo adzayesa kupeza phindu pakukuuzani mau onyenga. Komatu chilango chao nchokonzeratu kale, ndipo chiwonongeko chao chikuŵadikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:15-17

Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17

Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:21

Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:17-18

Paja inu mumati, ‘Ndife olemera, ndife achuma, sitisoŵa kanthu;’ osadziŵa kuti ndinu ovutika, ochititsa chifundo, amphaŵi, akhungu ndi amaliseche. Choncho ndikukulangizani kuti mugule kwa Ine golide woyeretsedwa ndi moto, kuti mukhale olemera. Mugulenso kwa Ine zovala zoyera, kuti muvale ndi kubisa maliseche anu ochititsa manyaziwo. Ndiponso mugule kwa Ine mankhwala a maso kuti mupenye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:4

Chuma chimachulukitsa abwenzi atsopano, koma wosauka abwenzi ake amamthaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:7

Wina amadziyesa wolemera, m'menemo alibe nkanthu komwe. Wina amadziyesa wosauka, m'menemo ali nchuma chochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:12-26

Adati, “Munthu wina, wa fuko lomveka, adapita ku dziko lakutali kukalandira ufumu kuti pambuyo pake abwerenso kwao. Adaitana khumi mwa antchito ake naŵapatsa ndalama zasiliva khumi, aliyense yakeyake. Adaŵauza kuti, ‘Bachita nazoni malonda mpaka nditabwera.’ Koma anthu ake ankadana naye, choncho m'mbuyo muno adatuma nthumwi kuti zipite ku dziko lomwelo nkukanena kuti, ‘Ife sitikufuna konse kuti munthu ameneyu akhale mfumu yathu.’ “Komabe iye adalandira ufumu uja. Tsono atabwerera kwao, adaitanitsa antchito aja adaaŵapatsa ndalamaŵa kuti adziŵe zimene adapindula. Woyamba adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi khumi.’ Mbuye wake adamuuza kuti, ‘Udachita bwino, ndiwe mtumiki wabwino. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zochepa kwambiri, udzalamulira midzi khumi.’ Wachiŵiri adadza nati, ‘Ambuye, ndalama yanu ija idapindula ndalama makumi asanu.’ Iyenso mbuye wake adamuuza kuti, ‘Iwe udzalamulira midzi isanu.’ Kudafika munthu wina, dzina lake Zakeyo. Iyeyo anali mkulu wa okhometsa msonkho, ndipo anali wolemera. Koma wina adadza nati, ‘Ambuye, nayi ndalama yanu ija. Ndidaaimanga pa kansalu. Ndinkakuwopani, popeza kuti ndinu munthu wankhwidzi. Mumalonjerera zimene simudaikize, ndiponso mumakolola zimene simudabzale.’ Apo mbuye wake uja adamuuza kuti, ‘Ndiwe wantchito woipa, ndikutsutsa ndi mau ako omwe. Kani unkadziŵa kuti ndine munthu wankhwidzi, amene ndimalonjerera zimene sindidaikize, ndipo ndimakolola zimene sindidabzale. Nanga bwanji osaiika ku banki ndalama yangayo, kuti ine pobwera ndiilandire pamodzi ndi chiwongoladzanja chake?’ Atatero adauza anthu amene anali pomwepo kuti, ‘Mlandeni ndalamayi muipereke kwa amene ali ndi ndalama makumi khumiyo.’ “Iwo adamuyankha kuti, ‘Pepani, ambuye, ameneyu ali kale ndi ndalama makumi khumi.’ Koma iye adati, ‘Ndikunenetsa kuti aliyense amene ali ndi kanthu, adzamuwonjezera zina. Koma amene alibe, ngakhale kamene ali nakoko adzamlandabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:22

Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu. Koma kutanganidwa ndi za pansi pano ndi kukondetsa chuma kumafooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:3-5

Paja kale mudakhala mukutaya nthaŵi yochuluka pakuchita zinthu zimene akunja amazikonda. Munkatsata zonyansa, zilakolako zoipa, kuledzera, dyera, maphokoso apamoŵa, ndi kupembedza mafano konyansa. Anthu akunja amadabwa tsopano poona kuti mwaleka kuthamangira nao zoipitsitsa zimene iwo amachita mosadziletsa konse. Nchifukwa chake amalalata. Koma iwo adzayenera kufotokoza okha mlandu wao kwa Mulungu amene ali wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:13

Tsono tiyeni tileke kumaweruzana. Makamaka mutsimikize kuti musachite kanthu kalikonse kophunthwitsa mbale wanu, kapena komchimwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:9

Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:3

“Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:6

Koma mai wamasiye amene amangodzisangalatsa ndi zapansipano, ameneyo wafa kale ngakhale akali moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 6:7-9

Munthu amagwira ntchito zolemetsa kuti apeze chakudya, komabe satha kukhutira kotheratu. Nanga munthu wanzeru ali ndi chiyani chimene amapambana nacho chitsiru? Kodi mmphaŵi amene amangodziŵa kukhala bwino pamaso pa anzake, ndiye kuti wapindulapo chiyani? Kuli bwino kumangopenya zinthu ndi maso kupambana kumazilakalaka chamumtima. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:25

Iye adasankha kuzunzikira nawo limodzi ana a Mulungu, koposa kukondwerera zosangalatsa za uchimo kanthaŵi pang'ono.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:19

Ameneŵa ndiwo mathero a anthu opata chuma mwankhondo. Chumacho chimapha eniake ochikundika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:25-26

Munthu amene amakonda moyo wake, adzautaya, koma amene saikapo mtima pa moyo wake pansi pano, adzausungira ku moyo wosatha. Ngati munthu anditumikira Ine, anditsatire, motero kumene kuli Ine, komwekonso kudzakhala mtumiki wanga. Munthu akanditumikira Ine, Atate anga adzamlemekeza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11

Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:40

Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:14

Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:16

Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:15

Ndipo Iye adaŵauza kuti, “Inu mumadziwonetsa olungama pamaso pa anthu, koma Mulungu amaidziŵa mitima yanu. Pajatu zimene anthu amaziyesa zamtengowapatali, m'maso mwa Mulungu zimaoneka zonyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:25

Nanga ndiye kuti munthu wapindulanji atapata zonse zapansipano, iyeyo nkutaya moyo wake kapena kuuwononga?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Chauta Wamuyaya, Ambuye Wapamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, woyenera ulemerero ndi kulambira konse. Atate Woyera, ndikubwera kwa Inu, podziwa kuti Inu nokha muli ndi Mphamvu yosintha, kumasula, ndi kukonzanso moyo wanga. Ndikupemphani kuti muphwanye unyolo uliwonse ndi chomangira chilichonse chomwe chimandikokera ku chizolowezi cha kutchova juga, kuti Mzimu Wanu Woyera undipatse mphamvu zolamulira maganizo anga, malingaliro anga, ndi kuwagonjetsa ku chifuniro Chanu kuti nditsatire mawu Anu. Mundilole kukhala kutali ndi anthu omwe amandilimbikitsa kuchita izi, kuti chizolowezi ichi chisalandire moyo wanga kapena wa banja langa. Atate Woyera, tsikani pa ine, mubweretse kusintha kwa maganizo anga ndi kudalira kotheratu kukhalapo Kwanu. Chofunika kwambiri ndikusangalatsani Inu kuti tsiku lililonse ndibale zipatso zabwino za kulapa, chifukwadi mawu Anu amati: “Palibe munthu angathe kutumikira ambuye awiri; pakuti adzadana ndi mmodzi, nakonda winayo; kapena adzakhulupirika kwa mmodzi, nanyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi chuma.” Kuyambira tsopano ndidzilengeza kuti ndine womasuka ndipo ndikusiya chizolowezi ichi. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa