Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


147 Mau a Mulungu Pa Nzeru ndi Miyambi

147 Mau a Mulungu Pa Nzeru ndi Miyambi


Miyambo 1:7

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7

Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:10

Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:6

Paja Chauta ndiye amapatsa nzeru, Iye ndiye kasupe wa kudziŵa zinthu ndi wa kumvetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:2

Kunyada kukaloŵa, pamafikanso manyazi, koma pali kudzichepetsa, palinso nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:16

Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:20

Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:15

Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:33

Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:10

Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:29

Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:8

Amene amakonda nzeru amadzichitira zabwino mwiniwakeyo. Amene ali womvetsa, zinthu zidzamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:1

Kuyankha kofatsa kumazimitsa mkwiyo, koma mau ozaza amakolezera ukali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:19

Mau akachuluka, zolakwa sizisoŵa, koma amene amasunga pakamwa ndi wanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:27

Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu, munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:11

Wopusa amaonetsa mkwiyo wake, koma munthu wanzeru amadzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:3

Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:13-14

Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:11

Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:22

Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu, koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:3-4

Nyumba imamangidwa ndi anthu anzeru, ndipo imakhazikika ndi anthu a mtima wodziŵa zinthu. Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba. Wodziŵa zinthu angathe kudzaza zipinda zake ndi chuma chokondweretsa ndi cha mtengo wapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:12

Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:23

Kwa chitsiru kulakwa kumakhala ngati maseŵera, koma kwa munthu womvetsa zinthu kuchita zanzeru ndiye kumapatsa chimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:15

Munthu wochenjera amafuna kuphunzirabe zambiri, amafunitsitsa kudziŵa bwino zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:11

Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:23

Mtima wako uziwulonda bwino, pakuti m'menemo ndimo muli magwero a moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:8

Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:16

Munthu wanzeru ngwochenjera, ndipo amalewa choipa, koma chitsiru chimadudukira zinthu mosasamalako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:14

Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:15

Pali golide ndi miyala yambirimbiri yamtengowapatali, koma mau olankhula zanzeru ali ndi mtengo woposa zonsezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:30

Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:17

Utchere khutu lako, umve mau a anthu anzeru, uike mtima wako pa zophunzitsa zanga, kuti uzidziŵe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:5

Munthu wanzeru ndi wamphamvu kupambana munthu wa nyonga zambiri, munthu wophunzira amaposa munthu wamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:7

Usamadziwona ngati wanzeru. Uziwopa Chauta, ndipo uleke zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:1-2

Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:9

Wanzeru ukamlangiza, adzakhala wanzeru koposa. Munthu wochita chilungamo ukamuphunzitsa, adzadziŵa zambiri koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:1

Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:30

Kukhala moyo wangwiro kumapezetsa moyo, koma kusatsata malamulo kumaononga moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:20

Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:1

Mkazi wanzeru amamanga banja lake, koma wopusa amalipasula ndi zochita zake zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:8

Nzeru za munthu wochenjera zagona pa kuzindikira bwino njira zake, koma zitsiru zimanyengedwa nkupusa kwao komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:12

Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu, koma kopherezera kwake nku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:14

Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:31

Amene makutu ake amalandira bwino kudzudzula koyenera, adzakhala m'gulu la anthu anzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:20

Munthu wovomera malangizo, zinthu zidzamuyendera bwino, ndi wodala amene amadalira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:24

Munthu wanzeru amaika mtima pa nzeru, koma chitsiru chimangoti maso mwalamwala pa dziko lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:4

Mau a munthu angathe kukhala kasupe wa nzeru, ozama ngati nyanja yamchere yaikulu, omweka ngati a mu mtsinje wothamanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:6-7

Mau a chitsiru amautsa mkangano, ndipo pakamwa pake pamaitana mkwapulo. Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake. Mau ake ali ngati msampha wodzikolera mwiniwakeyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:2

Si bwino kuti munthu akhale wosadziŵa zinthu, ndipo munthu woyenda mofulumira dziŵi amasokera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:1

Anthu okhuta vinyo amanyodola anzao, omwa zaukali amautsa phokoso. Aliyense wosokera nazo zimenezi ndi wopanda nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ndi yofunika kupambana chuma chambiri, kupeza kuyanja nkopambana siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:23

Ugule choona, ndipo usachigulitse. Ugulenso nzeru, mwambo ndiponso mtima womvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:6

Pafunika malangizo abwino kuti ukamenye nkhondo. Aphungu akachuluka, kupambana kuli pomwepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:12

Kwa munthu womvetsera bwino, kudzudzula kuli ngati mphete yagolide, kapena chokongoletsera china chagolide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:12

Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi, pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:26

Samvazaanzake nchitsiru, koma wotsata nzeru za ena adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:16

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:5-6

Usaiŵale mau a pakamwa pangaŵa, usatayane nawo, Ukhale ndi nzeru, ndiponso khalidwe la kumvetsa zinthu. Usaisiye nzeru, ndipo idzakusunga. Uziikonda, ndipo idzakuteteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:21-22

Mwana wanga, usunge nzeru yeniyeni usunge mkhalidwe wa kulingalira bwino, ziŵiri zimenezi zisakuthaŵe. Zimenezi zidzakupatsa moyo, moyo wake wokongola ngati mkanda wam'khosi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:14

Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:10

Munthu wanzeru amamva kamodzi, munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:32

Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo, amene amadzigwira mtima amapambana msilikali wogonjetsa mzinda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:1

Woipa mtima amangodzithaŵira popanda wina wompirikitsa, koma wochita zabwino amalimba mtima ngati mkango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:18

Ukakonzekera kuchita zinthu, uziyamba wafunsa. Usanamenye nkhondo, uyambe wapempha malangizo oyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:10

Ukataya mtima pamene upeza zovuta, ndiye kuti mphamvu zako ndi zochepa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:4

Mkazi wabwino ali ngati chisoti chaulemu kwa mwamuna wake, koma mkazi wochititsa manyazi ali ngati chilonda chamafinya kwa mwamuna wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:12

Chinthu chochiyembekeza chikalephereka, chimafooketsa mtima, koma chinthu chochilakalaka chikachitikadi, chili ngati mtengo wopatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:9

Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:2

Chitsiru sichisamalako za kumvetsa zinthu. Koma chimangolankhula za maganizo ake okha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:21

Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:6

Anthu ambiri amalankhula za kukhulupirika kwao, koma ndani angathe kumpeza munthu wokhulupirika kwenikweni?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:28

Munthu wosadzimanga mtima ali ngati mzinda umene adani authyola nkuusiya wopanda malinga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:20

Moto umazima pakasoŵa nkhuni, chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:20

Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 2:26

Pajatu munthu wokondweretsa Mulungu, Mulunguyo amamsandutsa waluntha, wanzeru ndi wosangalala. Koma wochimwa amampatsa ntchito yokunkha ndi younjika zinthu, kenaka zonsezo nkuzipatsa munthu wokondwetsa Mulungu. Zimenezinso nzopanda phindu, ndipo kuyesa kuzimvetsa nkungodzivuta chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:5

Kuli bwino kuti munthu azimva kudzudzula kwa anthu anzeru, kupambana kumvera nyimbo zotamanda za zitsiru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:9

Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:13

Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:1

Usamanyadira zamaŵa, pakuti sudziŵa zimene zidzachitika pa tsikulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:16

Kukwiya kwa munthu wopusa kumadziŵika msanga, koma munthu wanzeru salabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:25

Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:4

Mau ofatsa amakhala ngati mtengo wopatsa moyo, koma mau oipa amapweteka mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:17

Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:12

Chidani chimautsa mikangano, koma chikondi chimaphimba zolakwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:13

Amene amanka nachita ukazitape, amaulula zinsinsi. Koma wa mtima wokhulupirika, amasunga pakamwa pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:20

Mumtima mwa anthu opangana zoipa mumakhala kunama, koma anthu olinga zabwino amakhala ndi chimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:21

Amene amanyoza mnzake ngwochimwa, koma ngwodala amene amachitira chifundo amphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:24

Mau okometsera ali ngati chisa cha uchi, amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:24

Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:24-25

Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga, ndipo usamayenda naye munthu waukali, kuwopa kuti ungadzaphunzireko mayendedwe ake, ndi kukodwa mu msampha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:15-16

Mwana wanga, mtima wako ukakhala wanzeru, nanenso mtima wanga udzasangalala. Mtima wanga udzakondwa ndikadzakumva ukulankhula zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:11

Mau amodzi olankhula moyenera ali ngati zokongoletsera zagolide m'choikamo chasiliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:27

Amene amakumba dzenje adzagwamo yekha, amene amakunkhuniza mwala, udzampsinja iye yemweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:17

Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 10:10

Nkhwangwa ikakhala yobuntha, nkupandanso kuinola, imalira mphamvu zambiri potema. Koma nzeru zimathandiza munthu kuti athedi kudula kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:13

Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:23

Kuwopa Chauta kumabweretsa moyo, ndipo amene amaopayo amakhala pabwino, ndiye kuti choipa sichidzamgwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:17

Wosamala malangizo amayenda pa njira ya moyo, koma wokana chidzudzulo amasokera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:25

Pamakhala njira ina yooneka yowongoka kwa munthu, koma kumapeto kwake imakhala njira ya ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:23

Amene amagwira pakamwa ndi kusamala zokamba zake, sapeza mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:12

Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:13

Mtima wosangalala umaonetsa nkhope yachimwemwe, koma mtima wachisoni umaphwanya moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:35

Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:1

Muyeso wonyenga umanyansa Chauta, koma muyeso wachilungamo umamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa, mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa, mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:27

Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Chauta, nyaleyo imafufuza ziwalo zake zonse zam'kati.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:25

Kuwopa anthu kuli ngati msampha, koma wodalira Chauta amakhala pabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:3

Amene amagwira pakamwa pake amasunga moyo wake, koma amene amangolakatika amaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:24

Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda, koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:12

Mtima wako ukhale pa malangizo, ndipo makutu ako azimvetsera mau anzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:23

Pa ntchito iliyonse pali phindu lake, koma kumangolakatika kumabweretsa umphaŵi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:18

Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wa mtima wodzikuza adzagwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:7

Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womkongozayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:10

Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:20

Munthu wokhulupirika adzakhala ndi madalitso ambiri, koma wofunitsitsa kulemera msanga sadzalephera kupeza chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:4

Mphotho ya munthu wodzichepetsa ndi woopa Chauta, ndi chuma, ulemu ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:11

Wolima munda wake mwakhama amapeza chakudya chambiri, koma wotsata zopanda pake ngwopanda nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:4

Munthu waulesi amakhumbira zinthu koma sapeza kanthu, m'menemo munthu wakhama amalemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:15

Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse, koma wochenjera amayang'ana m'mene akuyendera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:29

Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso? Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:2

Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:18

Amene amasamalira mkuyu adzadya zipatso zake, chonchonso amene amasamalira mbuyake adzalandira ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:25

Munthu wa mtima waufulu adzalemera, wothandiza anzake nayenso adzalandira thandizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:5

Anthu oipa samvetsa kuti chilungamo nchiyani, koma amene amatsata kufuna kwa Chauta amachimvetsa kwathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:22

Madalitso a Chauta ndiwo amalemeretsa, ntchito za munthu siziwonjezerapo kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:13

Amene amatseka m'khutu wosauka akamalira, adzalira iyenso, koma kulira kwakeko sikudzamveka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:27

Kuwopa Chauta ndiye kasupe wa moyo, kumapewetsa misampha ya imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:9

Amene ali ndi diso lachifundo adzadalitsidwa, poti amagaŵana chakudya chake ndi anthu osauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:27-28

Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho. Usamuuze mnzakoyo kuti, “Pita, ukachite kubweranso, ndidzakupatsa maŵa,” pamene uli nazo tsopano lino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:29

Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:18-19

Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu. Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:3

Maso a Chauta ali ponseponse, amayang'ana oipa ndi abwino omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:17

Amene amakondetsa zosangalatsa, adzasanduka munthu wosauka. Amene amakondetsa vinyo ndi mafuta, sadzalemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:17-18

Mtima wako usamachita nsanje ndi anthu ochimwa, koma upitirire kumaopa Chauta tsiku ndi tsiku. Ndithu, zakutsogolo zilipo, ndipo chikhulupiriro chako sichidzakhala chachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:23

Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri, ndipo usamalire ziŵeto zako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:11

Ndi Chauta amene amafuna kuti miyeso ndi masikelo zikhale zachilungamo. Miyala yonse yoyesera yam'thumba adaipanga ndi Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:19-20

Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri. Pamene adatumphutsa madzi kuchoka kunsi kwa dziko, ndipo mitambo idagwetsa mvula, adaonetsa nzeru zodziŵa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:5

Mboni yonama sidzalephera kulangidwa, wolankhula mabodza sadzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:3-4

Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako. Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse. Usachite naye nsanje munthu wachiwawa, usatsanzireko khalidwe lake lililonse. Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo. Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa. Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza, koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima. Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi. Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa