Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


108 Mau a m'Baibulo Pa Utsogoleri

108 Mau a m'Baibulo Pa Utsogoleri

Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, Yesu ndiye chitsanzo chathu tonse. Iye anali ndi mphamvu, nzeru, ndi masomphenya ochulukirapo kuposa wina aliyense. Koma chodabwitsa n’chakuti utumiki wake unali wodzichepetsa, wodzipereka, wachikondi, komanso wopatsa chiyembekezo kwa ena.

Ziweruzo zake zinali zolimbikitsa komanso zotsutsa maganizo athu, koma nthawi yomweyo zinkatonthoza ndi kutitsutsa kuti tisinthe makhalidwe athu. M’mabuku a Uthenga Wabwino muli nkhani zambiri zosonyeza utsogoleri wa Yesu kwa anthu ndi ophunzira ake.

Inu mtsogoleri amene mukuwerenga mawu awa, ndikufuna ndikuuzeni kuti chitsanzo chabwino kwambiri chimene mungatsatire ndi Yesu. Lolani Iye akuphunzitseni njira zake, atsogolere mapazi anu, ndipo mudzasiya chizindikiro chabwino m'miyoyo ya anthu amene akuzungulirani.

Njira ya Yesu ndiyo yabwino koposa. Choncho, tisiyeni tidzichepetse, titsatire mapazi a Mphunzitsi wa aphunzitsi, munthu wanzeru woposa onse amene anakhalapo padziko lapansi. Iye ndi wokonzeka kukutsogolerani kuti mupite patsogolo pa chilichonse chimene mungachite.

Mwa Iye, timapeza utsogoleri wabwino, dongosolo, nzeru, mgwirizano, mphamvu, ndi masomphenya. Mulungu akudalitseni.




Yohane 15:16

Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:26

Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:24

Munthu asamangodzifunira yekha zabwino, koma makamaka azifunira anzake zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 18:21

Komanso sankhulani amuna anzeru, ndipo muŵaike kuti akhale atsogoleri a anthu, motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe. Ayenera kukhala anthu oopa Mulungu, okhulupirika, ndiponso osakopeka ndi ziphuphu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:6

Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:72

Davide adaŵasamala ndi mtima wolungama, naŵatsogolera ndi dzanja lake mwaluso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:1

Muzitiwona ngati antchito a Khristu, ngati akapitao osamala zinsinsi za Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:11

Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:14

Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:17

Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:14

Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:5-7

Motero nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu: Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse. Koma adadzitsitsa kotheratu pakudzitengera umphaŵi wa kapolo, ndi kukhala munthu wonga anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:15

Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:45

Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:9

Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:18-19

Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko, ndipo munthu wa mtima wodzikuza adzagwa. Kuli bwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu osauka, kupambana kumagaŵana chuma ndi anthu onyada.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:28

Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu, chilungamo ndiye chimalimbitsa ufumu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:1

Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wa madzi m'manja mwa Chauta. Amauwongolera ku zimene Iyeyo akufuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:29

Kodi ukumuwona munthu wochita ntchito zake mwaluso? Iye adzatumikira mafumu, sadzatumikira anthu wamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:2

Mu dziko mukakhala chilungamo, anthu amakondwa, koma chilungamo chikasoŵa, anthu amadandaula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:11

Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:25-28

Koma Yesu adaŵaitana ophunzira akewo naŵauza kuti, “Mukudziŵa kuti olamulira amadyera anthu ao masuku pa mutu. Akuluakulu aonso amaonetsadi mphamvu zao pa anthu ao. Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu. Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:11-12

Pakati panupa wamkulu akhale mtumiki wanu. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:43-45

Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, azikhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, azikhala kapolo wa onse. Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:26-27

Koma pakati pa inu zisamatero ai. Kwenikweni wamkulu mwa inu azikhala ngati wamng'ono mwa onse, ndipo mtsogoleri azikhala ngati wotumikira. Kodi wamkulu ndani? Ndi amene alikudya, kapena amene akumtumikira? Si amene alikudyayo nanga? Koma Ine ndili pakati panu ngati wotumukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:12-15

Yesu atatsuka mapazi a ophunzira ake, adavalanso mwinjiro wake nakakhalanso podyera paja. Kenaka adaŵafunsa kuti, “Kodi mwazimvetsa zimene ndakuchitiranizi? Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene. Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi. Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:8

Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1

Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:27-28

Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo. Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:24

Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:11-12

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:12-13

Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani. Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:1-7

Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu akuti, “Ngati munthu afuna ntchito ya kuyang'anira Mpingo, akukhumba ntchito yaulemu.” Iwonso ayambe ayesedwa, ndipo pambuyo pake, ngati alibe chokayikitsa, ndiye asenze udindo wa atumiki. Momwemonso akazi akhale ochita zachiukulu, osasinjirira, odzigwira, ndi okhulupirika pa zonse. Atumiki a mpingo akhale a mkazi mmodzi yekha. Akhale olera ana ao bwino, oyendetsanso bwino mabanja ao. Paja anthu ogwira bwino ntchito ya utumiki, amadzitengera mbiri yabwino, ndipo amalimba mtima kwenikweni pakuika chikhulupiriro chao mwa Khristu Yesu. Pamene ndikukulembera zimenezi, ndikuyembekeza kudzafika kwanuko posachedwa. Koma zina zikandichedwetsa, zimene ndanenazi zidzakudziŵitsa za m'mene anthu ayenera kukhalira m'banja la Mulungu, limene lili Mpingo wa Mulungu wamoyo, ndi mzati wochirikiza choona. Ndithudi, chinsinsi cha chipembedzo chathu nchachikulu: “Iye uja adaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu Woyera adamchitira umboni kuti ndi wolungama, angelo adamuwona, adalalikidwa pakati pa anthu a mitundu yonse, anthu a pa dziko lonse lapansi adamkhulupirira, Iyeyo adatengedwa kunka kumwamba mu ulemerero.” Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa. Asakhale chidakwa, asakhale wandeu, koma wofatsa, wosakangana ndi anthu, ndi wosakonda ndalama. Akhale wodziŵa kuyendetsa bwino banja lake, ndi kulera bwino ana ake, kuti akhale omvera ndi aulemu kwenikweni. Ngati munthu sadziŵa kuyendetsa bwino banja lake, nanga angasunge bwanji Mpingo wa Mulungu? Asakhale munthu wolandiridwa mu mpingo chatsopano, kuwopa kuti angadzitukumule nkulangidwa monga momwe Satana adalangidwira. Kuwonjezera pamenepo, akhale munthu woti ndi akunja omwe amamlemekeza, mwinamwina nkudzayamba kunyozedwa nagwa mu msampha wa Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:17

Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:5-9

Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira. Mkulu wa mpingo akhale munthu wosapalamula konse, ndipo akhale wa mkazi mmodzi yekha. Ana ake akhalenso okhulupirira Khristu, opanda mbiri yoti ngosakaza kapena yoti ngosaweruzika. Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama. Akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziŵa kudzilamula, wolungama, woyera mtima, ndiponso wodzigwira. Asunge mogwiritsa mau okhulupirika, amene ali ogwirizana ndi zimene tidaphunzitsidwa. Pakutero adzatha kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona, ndiponso kugonjetsa otsutsana nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:17

Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:1

Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:1-4

Tsopano ndili nawo mau akulu a mpingo amene ali pakati panu, ine mkulu mnzao. Ndinenso mboni ya zoŵaŵa za Khristu, ndipo ndikuyembekeza kudzalandira nao ulemerero umene uti udzaoneke. Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha. Iye ndiye mwini mphamvu mpaka muyaya. Amen. Kalatayi ndalembetsa Silivano mwachidule. Ndimamuwona kuti ndi mbale wokhulupirika. Ndafuna kukulimbitsani mtima, ndi kuchita umboni wakuti kukoma mtima kwenikweni kwa Mulungu nkumeneku. Chifukwa cha kukoma mtimako, limbikani. Anzanu a mu mpingo wa ku Babiloni akuti moni. Marko, mwana wanga, nayenso akuti moni. Mupatsane moni mwachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli ake a Khristu. Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo. Ndipo pamene Mbusa wamkulu adzaonekera, mudzalandira mphotho yosafota yaulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:8

Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 143:10

Phunzitseni, kuti ndizichita zofuna Inu, pakuti ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:5

Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:22

Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:1

Munthu wodzipatula mwa anzake amangotsata zomkomera iyeyo, amangofuna kutsutsana ndi zimene onse akudziŵa kuti ndi zoona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:6

Pafunika malangizo abwino kuti ukamenye nkhondo. Aphungu akachuluka, kupambana kuli pomwepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:3

Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:3

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14-16

“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:24-27

“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba. Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:16

“Mumvetse bwino! Ndikukutumani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Ndiye inu khalani ochenjera ngati njoka, ndi ofatsa ngati nkhunda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:19-20

“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18-20

Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano. Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:14

Tsono adasankhapo khumi ndi aŵiri, naŵatcha dzina loti, “Atumwi.” Adaŵauza kuti, “Ndasankha inu kuti muzikhala nane, ndidzakutumani kukalalika,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:12-13

Masiku amenewo Yesu adapita ku phiri kukapemphera, ndipo adachezera usiku wonse akupemphera kwa Mulungu. Kutacha adaitana ophunzira ake, nasankhapo khumi ndi aŵiri. Adaŵatcha “atumwi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:14-15

Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziŵa, ndipo izozo Ineyo zimandidziŵa, monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 6:3-4

Nchifukwa chake abale, pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi aŵiri, a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndiponso ndi nzeru. Tidzapatsa iwowo ntchitoyi. Koma ife tidzadzipereka ku ntchito ya kupemphera ndi kulalika mau a Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:2-3

Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” “Pambuyo pake adaŵapatsa oweruza kufikira nthaŵi ya mneneri Samuele. Kenaka anthu adapempha kuti aŵapatse mfumu, ndipo Mulungu adaŵapatsa Saulo, mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, iye nkuŵalamulira pa zaka makumi anai. Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ Mwa zidzukulu za Davideyo Mulungu adasankha Yesu kuti akhale Mpulumutsi wa Aisraele, monga momwe adaalonjezera kale. Iyeyo asanayambe ntchito, Yohane ankalalikira Aisraele onse kuti atembenuke mtima ndi kubatizidwa. Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’ “Ine abale, zidzukulu za Abrahamu, ndi ena nonse oopa Mulungu, uthenga wa chipulumutsowu Mulungu watumizira ife. Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu. Ngakhale sadapeze konse chifukwa chomuphera, komabe adapempha Pilato kuti Yesuyo aphedwe. Ndipo atachita zonse zimene zidalembedwa za Iye, adamtsitsapo pa mtanda paja namuika m'manda. Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:28

Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:11-12

Ndikulakalakadi kukuwonani, kuti ndikugaŵireni mphatso zina zauzimu, kuti motero ndikulimbikitseni. Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:14

Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:1-2

Muzitiwona ngati antchito a Khristu, ngati akapitao osamala zinsinsi za Mulungu. Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu. Ife ndife ofooka, koma inu ndinu amphamvu. Inu mumalandira ulemu, koma ife timanyozedwa. Mpaka tsopano lino timamva njala ndi ludzu, ndipo ndife ausiŵa. Anthu akutimenya, ndipo tilibe pokhala penipeni. Tikugwira ntchito kolimba ndi manja athu kuti tidzisunge. Anthu akamatichita chipongwe, timapempha kuti Mulungu aŵadalitse. Anthu akamatizunza, timangopirira. Anthu akamatilalatira, timangoŵayankha moleza. Tasanduka onyozeka, ngati zinyatsi za dziko lapansi, ndipo mpaka tsopano anthu onse akutiyesa zinyalala. Ndikukulemberani zonsezi, osati kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni, chifukwa ndinu ana anga okondedwa. Ngakhale mutakhala nawo aphunzitsi ambirimbiri m'moyo wanu wachikhristu, simukhala ndi atate ambiri ai. Pajatu m'moyo wanu wachikhristu ine ndidachita ngati kukubalani pakukulalikirani Uthenga Wabwino. Ndikukupemphani tsono kuti muzinditsanzira. Nchifukwa chake ndakutumizirani Timoteo, mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iyeyu adzakukumbutsani za mayendedwe anga achikhristu, amene sasiyana ndi zimene ndimaphunzitsa ponseponse m'mipingo yonse. Ena mwayamba kudzitukumula, monga ngati sindidzabwerako kwanu. Koma Ambuye akalola, ndidzabwera kwanuko posachedwa. Pamenepo ndidzadziŵa zimene odzitukumulawo angathe kuchita, osati zimene amangonena chabe. Chofunika chachikulu pa akapitao otere nchakuti akhale okhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 11:1

Muzinditsanzira ine monga momwe inenso ndimatsanzira Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:20

Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13

Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:1-2

Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira. Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye. Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse. Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi. Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera. Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.” Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru. Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa. Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite. Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:28

Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:11-12

Paja mukudziŵa kuti, tinkasamala aliyense mwa inu monga momwe amachitira bambo ndi ana ake. Tinkakulimbitsani mtima, kukuthuzitsani mtima ndi kukupemphani kuti mayendedwe anu akhale okomera Mulungu, amene amakuitanani kuti mukaloŵe mu Ufumu wake waulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:6

Abale, tsopano tikukulamulani m'dzina la Ambuye Yesu Khristu kuti muziŵapewa abale onse a makhalidwe aulesi, osafuna kutsata mwambo umene tidaŵapatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:18

Iwe Timoteo, mwana wanga, ndikukupatsa malangizo ameneŵa molingana ndi zimene aneneri adaanenapo kale za iwe. Mau amenewo akuthandize kumenya nkhondo yabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:11-12

Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa. Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:7-8

Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu. Mau ako akhale oona, kuti anthu asadzathe kuŵatsutsa. Motero wotsutsana nawe adzachita manyazi, atasoŵa kalikonse koipa kuti atinenere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:12

Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:21

Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:16

Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:4-5

Mibadwo ndi mibadwo idzatamanda ntchito zanu, idzalalika ntchito zanu zamphamvu. Ndidzasinkhasinkha za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu, ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7

Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:26

Munthu wochita zabwino amatsogolera anzake pa njira yokhoza, koma njira ya munthu woipa imaŵasokeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:20

Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:21

Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:36-37

Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:48

Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:46-47

Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:6-9

Ineyo ndidabzala mbeu, Apolo nkuzithirira, koma amene adazimeretsa ndi Mulungu. Motero wobzala kapenanso wothirira sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amameretsa, ndiye ali kanthu. Tsono wobzala sasiyana ndi wothirira, ndipo aliyense adzalandira mphotho yake molingana ndi ntchito imene adaigwira. Komabe ife ndife okhaokha ogwira ntchito ya Mulungu, inuyo ndinu munda wa Mulungu, ndinunso nyumba ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 3:6

Ndiye amene adatipatsa mphamvu kuti tikhale otumikira chipangano chatsopano, osati mwa malamulo olembedwa, koma mwa Mzimu Woyera. Paja malamulo olembedwa amadzetsa imfa, koma Mzimu Woyera amapatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:16

umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:12

Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:14

Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:1

Uziŵakumbutsa anthu onse kuti azigonjera akulu oweruza ndi olamulira. Aziŵamvera ndipo azikhala okonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:7

Muzikumbukira atsogoleri anu amene ankakulalikirani mau a Mulungu. Muzilingalira za moyo wao ndi m'mene adafera, ndipo muzitsanzira chikhulupiriro chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:19

Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:9

Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama, amaŵaphunzitsa njira zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:68

Inu ndinu abwino, ndipo mumachita zabwino, phunzitseni malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa. Atate, zikomo chifukwa muli, ndipo mudzakhala mtsogoleri wabwino koposa, ndithudi m'nthawi ino mukutifuna kuti tikhale anthu otsogolera monga momwe mawu anu amanenera. Monga Nehemiya, yemwe anali munthu wofunitsitsa kuchita chifuniro chanu, kusiya zofuna zake ndi chitonthozo chake kuti agwire ntchito yokonzanso mpanda wa Yerusalemu. Ambuye, mundiphunzitse kukhala mtsogoleri amene cholinga chake chikhale ubwino wa ena, osafuna changa, koma cha mnzanga, ndikuwonetsa chidwi, ndikubala zipatso zabwino pa chilichonse chimene ndichita. Pakuti mtsogoleri wauzimu weniweni sabadwa, koma inuyo mumamupanga! Ndikupempha kuti pakhale atsogoleri aamuna ndi akazi omwe ali ndi mtima womwewo womwe munali nawo, wakutumikira osati kutumikiridwa, kukhala oyang'anira abwino ndi ogwira nawo ntchito mu ufumu wanu, okonzeka nthawi zonse kuchita ntchito iliyonse yabwino, kutaya mtima wonyada ndi wodzikuza. Wadzazani ndi kudzichepetsa, kuti azilemekeza ena kuposa iwo eni, chifukwa amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu adzakhala mtumiki wanu. Zikomo, Ambuye, chifukwa kutumikira ena ndi gawo la cholinga chanu m'miyoyo yathu. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa