Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


124 Mau a m'Baibulo a Tsiku la Abusa

124 Mau a m'Baibulo a Tsiku la Abusa

Abale ndi alongo, ndikufuna ndikuuzeni za abusa athu. Ntchito yawo yotsogolera anthu a Mulungu ndi yaikulu kwambiri. Amafunika kukhala chitsanzo chabwino kuti ife tionetse Mulungu mwa iwo.

Kutsogolera mpingo ndi mwayi waukulu wochokera kwa Mulungu. Ngakhale nthawi zina sitizindikira khama lawo, Mulungu akuona zonse ndipo ali ndi mphoto yaikulu kwa iwo kumwamba.

Tisaiwale kuti abusa athu nawonso ndi ana a Mulungu. Ndi anthu, amalakwitsa, ndipo ali ndi maganizo ngati ife. Mawu olimbikitsa ndi oyamikira amawasangalatsa kwambiri.

Tiyeni tipempherere abusa athu, kuti Mulungu awasamalire ndi kuwatsogolera nthawi zonse. Tiwalemekeze ndi kuwathandiza m’njira iliyonse yomwe tingathe, kuti adziwe kuti tikuwayamikira.




1 Atesalonika 5:12-13

Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani. Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 52:7

Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m'mapiri, akubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 21:17

Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziŵa zonse. Mukudziŵa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:28

Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
3 Yohane 1:2

Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 6:24-26

Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:21

Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 3:15

“Kumeneko ndidzakupatsani abusa a kukhosi kwanga. Adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:7

Muzikumbukira atsogoleri anu amene ankakulalikirani mau a Mulungu. Muzilingalira za moyo wao ndi m'mene adafera, ndipo muzitsanzira chikhulupiriro chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:17

Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:11

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:8

Poyamba ndikuthokoza Mulungu wanga mwa Yesu Khristu chifukwa cha inu nonse, pakuti pa dziko lonse lapansi anthu akusimba za chikhulupiriro chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1

Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:2-3

Timathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kumakutchulani m'mapemphero athu. Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:2

Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:14

Tsono Yesu adati, “Inde oitanidwa ngambiri, komatu osankhidwa ngoŵerengeka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:14

Tsono adasankhapo khumi ndi aŵiri, naŵatcha dzina loti, “Atumwi.” Adaŵauza kuti, “Ndasankha inu kuti muzikhala nane, ndidzakutumani kukalalika,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:34

Pamene Yesu adatuluka m'chombomo, adaona chikhamu chachikulu cha anthu. Adaŵamvera chifundo anthuwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa, choncho adayamba kuŵaphunzitsa zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 21:16

Yesu adamufunsanso kachiŵiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Ŵeta nkhosa zanga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2

Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:1

“Kunena zoona, munthu woloŵa m'khola la nkhosa osadzera pa khomo, koma kuchita kukwerera pena, ameneyo ndi wakuba ndi wolanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:15

monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:23

Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri, ndipo usamalire ziŵeto zako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:7

Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:15

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2-4

Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo. Ndipo pamene Mbusa wamkulu adzaonekera, mudzalandira mphotho yosafota yaulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:70-72

Mulungu adasankhula Davide mtumiki wake, ndipo adakamtenga ku makola a nkhosa. Adamtenga kumene ankaŵeta nkhosa zimene zinali ndi ana, kuti adzakhale mbusa wa Yakobe, fuko lake, wa Israele, choloŵa chake. Davide adaŵasamala ndi mtima wolungama, naŵatsogolera ndi dzanja lake mwaluso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:11

Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:22

Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:13

Paja anthu ogwira bwino ntchito ya utumiki, amadzitengera mbiri yabwino, ndipo amalimba mtima kwenikweni pakuika chikhulupiriro chao mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 34:2-4

“Iwe mwana wa munthu, ulengeze mau oimba mlandu abusa a Israele. Ulengeze, uŵauze kuti ‘Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: Tsoka kwa inu abusa a ku Israele, amene mumangodzisamala inu nokha. Kodi suja abusa amayenera kusamala nkhosa? “Tsono Ine Ambuye Chauta ndikukuuzani kuti, Ineyo mwiniwake ndidzaweruza ndekha pakati pa inu nkhosa zonenepanu ndi zinzanu zoondazo. Zofooka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nkuzimwazira kutali. Koma ndidzazipulumutsa nkhosa zangazo, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso. Ndidzaziikira mbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala, ndipo adzakhala mbusa wake. Pamenepo Ine Chauta ndidzakhala Mulungu wake, ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yake. Ndatero Ineyo Chauta.” “Ndidzapangana nazo chipangano chamtendere. Zilombo zonse zolusa ndidzazichotsa m'dziko, kuti nkhosa zanga zizidzakhala mwamtendere, ngakhale m'chipululu kapena m'thengo. Ndidzakhazika anthu anga kufupi ndi phiri langa, ndipo ndidzaŵagwetsera mvula pa nthaŵi yake, mvula yake ya madalitso. Mitengo ya m'minda idzabereka zipatso, ndipo minda idzakhala ndi zokolola zake, tsono anthu adzakhala mwamtendere m'dziko lao. Adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, pamene ndidzathyole magoli ao ndi kuŵapulumutsa kwa amene adaŵagwira ukapolo. Anthu a mitundu ina sadzaŵafunkhanso, ndipo zilombo zakuthengo sizidzaŵadya. Adzakhala mwamtendere popanda wina woŵaopsa. Ndidzachulukitsa zolima zao, mwakuti sadzafanso ndi njala m'dzikomo, ndipo choncho anthu a mitundu ina sadzaŵanyozanso. Chambiko mumadya, zaubweya mumavala, ndipo nyama zonenepa mumapha, koma nkhosa osasamala konse. Motero adzadziŵa kuti Ine Chauta Mulungu wao ndili nawo, ndipo kuti iwowo, Aisraelewo, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. ‘Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimadyetsa, ndipo Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.’ ” Nkhosa zofooka simudazilimbikitse, zodwala simudazichiritse, zopweteka simudazimange mabala ake, zosokera simudazibweze, ndipo zotayika simudazifunefune. Koma munkaziŵeta mozunza ndi mwankhalwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 34:11-12

“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi, Tsopano nkhosa zangazo ndidzazifunafuna ndekha mwiniwakene, ndipo ndidzazisamala. Monga mbusa amanka nafunafuna nkhosa zake, pamene zina zabalalikira kutali, Inenso ndidzatero, kunka ndikufunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa konse kumene zidamwazikira pa nthaŵi yamdima ndi yankhungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 34:16

Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:36

Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:6

Koma makamaka mupite kwa Aisraele amene ali ngati nkhosa zotayika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:12-14

“Tsono mukuganiza bwanji? Munthu atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nkutayika, kodi sangasiye 99 zina zija m'phiri nkukafunafuna imodzi yotayikayo? Ndithu ndikunenetsa kuti ataipeza, chimwemwe chake chokondwerera imeneyo chimapambana chokondwerera zina zija zimene sizidatayike. Chonchonso Atate anu amene ali Kumwamba safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:26-28

Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu. Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:35-40

Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’ Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa? Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani? Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife nkudzakuchezetsani?’ Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao. Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:15

Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:42

Yesu adati, “Tsono kapitao wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 15:4-7

“Ndani mwa inu ali ndi nkhosa 100, imodzi itatayikapo, sangasiye nkhosa zina zonse 99 zija ku busa, nkukafunafuna yotayikayo mpaka ataipeza? Ndipo ataipeza, amaisenza pamapewa pake mokondwa. Pofika kwao, amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndaipeza nkhosa yanga idaatayika ija.’ ” Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:11

“Ine ndine mbusa wabwino. Mbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:14-15

Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziŵa, ndipo izozo Ineyo zimandidziŵa, monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 21:15-17

Iwo atafisula, Yesu adafunsa Simoni Petro kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi koposa m'mene amandikondera aŵa?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala anaankhosa anga.” Yesu adamufunsanso kachiŵiri kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi?” Iye adati, “Inde Ambuye, mukudziŵa kuti ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Ŵeta nkhosa zanga.” Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziŵa zonse. Mukudziŵa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:6-8

Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu. Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu. Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:1-2

Muzitiwona ngati antchito a Khristu, ngati akapitao osamala zinsinsi za Mulungu. Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu. Ife ndife ofooka, koma inu ndinu amphamvu. Inu mumalandira ulemu, koma ife timanyozedwa. Mpaka tsopano lino timamva njala ndi ludzu, ndipo ndife ausiŵa. Anthu akutimenya, ndipo tilibe pokhala penipeni. Tikugwira ntchito kolimba ndi manja athu kuti tidzisunge. Anthu akamatichita chipongwe, timapempha kuti Mulungu aŵadalitse. Anthu akamatizunza, timangopirira. Anthu akamatilalatira, timangoŵayankha moleza. Tasanduka onyozeka, ngati zinyatsi za dziko lapansi, ndipo mpaka tsopano anthu onse akutiyesa zinyalala. Ndikukulemberani zonsezi, osati kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni, chifukwa ndinu ana anga okondedwa. Ngakhale mutakhala nawo aphunzitsi ambirimbiri m'moyo wanu wachikhristu, simukhala ndi atate ambiri ai. Pajatu m'moyo wanu wachikhristu ine ndidachita ngati kukubalani pakukulalikirani Uthenga Wabwino. Ndikukupemphani tsono kuti muzinditsanzira. Nchifukwa chake ndakutumizirani Timoteo, mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iyeyu adzakukumbutsani za mayendedwe anga achikhristu, amene sasiyana ndi zimene ndimaphunzitsa ponseponse m'mipingo yonse. Ena mwayamba kudzitukumula, monga ngati sindidzabwerako kwanu. Koma Ambuye akalola, ndidzabwera kwanuko posachedwa. Pamenepo ndidzadziŵa zimene odzitukumulawo angathe kuchita, osati zimene amangonena chabe. Chofunika chachikulu pa akapitao otere nchakuti akhale okhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:28

Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:24

Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:11-12

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:3-5

Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:28

Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:1-7

Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu akuti, “Ngati munthu afuna ntchito ya kuyang'anira Mpingo, akukhumba ntchito yaulemu.” Iwonso ayambe ayesedwa, ndipo pambuyo pake, ngati alibe chokayikitsa, ndiye asenze udindo wa atumiki. Momwemonso akazi akhale ochita zachiukulu, osasinjirira, odzigwira, ndi okhulupirika pa zonse. Atumiki a mpingo akhale a mkazi mmodzi yekha. Akhale olera ana ao bwino, oyendetsanso bwino mabanja ao. Paja anthu ogwira bwino ntchito ya utumiki, amadzitengera mbiri yabwino, ndipo amalimba mtima kwenikweni pakuika chikhulupiriro chao mwa Khristu Yesu. Pamene ndikukulembera zimenezi, ndikuyembekeza kudzafika kwanuko posachedwa. Koma zina zikandichedwetsa, zimene ndanenazi zidzakudziŵitsa za m'mene anthu ayenera kukhalira m'banja la Mulungu, limene lili Mpingo wa Mulungu wamoyo, ndi mzati wochirikiza choona. Ndithudi, chinsinsi cha chipembedzo chathu nchachikulu: “Iye uja adaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu Woyera adamchitira umboni kuti ndi wolungama, angelo adamuwona, adalalikidwa pakati pa anthu a mitundu yonse, anthu a pa dziko lonse lapansi adamkhulupirira, Iyeyo adatengedwa kunka kumwamba mu ulemerero.” Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa. Asakhale chidakwa, asakhale wandeu, koma wofatsa, wosakangana ndi anthu, ndi wosakonda ndalama. Akhale wodziŵa kuyendetsa bwino banja lake, ndi kulera bwino ana ake, kuti akhale omvera ndi aulemu kwenikweni. Ngati munthu sadziŵa kuyendetsa bwino banja lake, nanga angasunge bwanji Mpingo wa Mulungu? Asakhale munthu wolandiridwa mu mpingo chatsopano, kuwopa kuti angadzitukumule nkulangidwa monga momwe Satana adalangidwira. Kuwonjezera pamenepo, akhale munthu woti ndi akunja omwe amamlemekeza, mwinamwina nkudzayamba kunyozedwa nagwa mu msampha wa Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:2

uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:5-9

Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira. Mkulu wa mpingo akhale munthu wosapalamula konse, ndipo akhale wa mkazi mmodzi yekha. Ana ake akhalenso okhulupirira Khristu, opanda mbiri yoti ngosakaza kapena yoti ngosaweruzika. Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama. Akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziŵa kudzilamula, wolungama, woyera mtima, ndiponso wodzigwira. Asunge mogwiritsa mau okhulupirika, amene ali ogwirizana ndi zimene tidaphunzitsidwa. Pakutero adzatha kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona, ndiponso kugonjetsa otsutsana nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:17

Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:25

Munali ngati nkhosa zosokera, koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang'anirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:1-4

Tsopano ndili nawo mau akulu a mpingo amene ali pakati panu, ine mkulu mnzao. Ndinenso mboni ya zoŵaŵa za Khristu, ndipo ndikuyembekeza kudzalandira nao ulemerero umene uti udzaoneke. Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha. Iye ndiye mwini mphamvu mpaka muyaya. Amen. Kalatayi ndalembetsa Silivano mwachidule. Ndimamuwona kuti ndi mbale wokhulupirika. Ndafuna kukulimbitsani mtima, ndi kuchita umboni wakuti kukoma mtima kwenikweni kwa Mulungu nkumeneku. Chifukwa cha kukoma mtimako, limbikani. Anzanu a mu mpingo wa ku Babiloni akuti moni. Marko, mwana wanga, nayenso akuti moni. Mupatsane moni mwachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli ake a Khristu. Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo. Ndipo pamene Mbusa wamkulu adzaonekera, mudzalandira mphotho yosafota yaulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:4-5

Mibadwo ndi mibadwo idzatamanda ntchito zanu, idzalalika ntchito zanu zamphamvu. Ndidzasinkhasinkha za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu, ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Akuchiritsa a mtima wachisoni, ndipo akumanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:5

Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:14

Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:15

Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:1

Munthu wodzipatula mwa anzake amangotsata zomkomera iyeyo, amangofuna kutsutsana ndi zimene onse akudziŵa kuti ndi zoona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:18

Ukakonzekera kuchita zinthu, uziyamba wafunsa. Usanamenye nkhondo, uyambe wapempha malangizo oyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:23-27

Uzidziŵe bwino nkhosa zako m'mene ziliri, ndipo usamalire ziŵeto zako. Paja chuma sichikhala mpaka muyaya. Kodi ufumu umakafika mpaka ku mibadwo yonse? Udzu ukatha, msipu nkuphuka, ndipo atatuta udzu wakumapiri, anaankhosa adzakupatsa chovala, ndi ubweya wao, ndipo pogulitsa mbuzi udzapeza chogulira munda. Udzakhala ndi mkaka wambiri wa mbuzi kuti uzidya, iweyo ndi banja lako, ndiponso ndi adzakazi ako omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1-2

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14-16

“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:15-20

“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai. Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu. Choncho mudzaŵadziŵira zochita zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:37-38

Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:18

“Nayu mtumiki wanga amene ndamsankha. Ndimamkonda, ndipo mtima wanga umasangalala naye kwambiri. Ndidzaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzalalika za chilungamo kwa anthu a mitundu ina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:40

Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:3-4

Iyeyo mlonda amamtsekulira. Nkhosa zimamva mau ake, ndipo amaziitana maina nkhosa zakezo, nazitulutsa. Ine ndi Atate ndife amodzi.” Anthuwo adatolanso miyala kuti amlase. Yesu adaŵafunsa kuti, “Ndakuwonetsani ntchito zabwino zambiri zimene Atate adandichititsa. Nanga mwa zimenezi ntchito imene mukuti mundiponyere miyala ndi iti?” Anthu aja adamuyankha kuti, “Sitikufuna kukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ai, koma chifukwa ukunyoza Mulungu. Iwe, amene uli munthu chabe, ukudziyesa Mulungu.” Yesu adati, “Kodi m'Malamulo mwanu suja mudalembedwa kuti ‘Mulungu adati, Ndinu milungu?’ Paja mau a m'Malembo ngoona mpaka muyaya, ndipo Mwiniwakeyo adaŵatcha milungu anthu aja Iye ankalankhula nawoŵa. Inetu Atate adandipatula nandituma pansi pano. Tsono inuyo munganene bwanji kuti ndikunyoza Mulungu, chifukwa ndati ndine Mwana wa Mulungu? Ngati sindichita ntchito zimene Atate anga adandipatsa, musandikhulupirire. Koma ngati ndimazichitadi, khulupirirani ntchitozo, ngakhale simukhulupirira Ine. Apo mudzadziŵa mosapeneka konse kuti Atate amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa Atate.” Pamenepo anthu aja adafunanso kumgwira, koma Iye adazemba. Akazitulutsa nkhosa zake zonse, amazitsogolera, izo nkumamtsatira, chifukwa zimadziŵa mau ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:42

Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 6:3

Nchifukwa chake abale, pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi aŵiri, a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndiponso ndi nzeru. Tidzapatsa iwowo ntchitoyi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:11-12

Ndikulakalakadi kukuwonani, kuti ndikugaŵireni mphatso zina zauzimu, kuti motero ndikulimbikitseni. Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:5-9

Kodi Apolo nchiyani? Paulonso nchiyani? Ndi atumiki chabe a Mulungu, amene adakufikitsani ku chikhulupiriro. Aliyense adangogwira ntchito imene Mulungu adampatsa. Ineyo ndidabzala mbeu, Apolo nkuzithirira, koma amene adazimeretsa ndi Mulungu. Motero wobzala kapenanso wothirira sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amameretsa, ndiye ali kanthu. Tsono wobzala sasiyana ndi wothirira, ndipo aliyense adzalandira mphotho yake molingana ndi ntchito imene adaigwira. Komabe ife ndife okhaokha ogwira ntchito ya Mulungu, inuyo ndinu munda wa Mulungu, ndinunso nyumba ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:20

Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:10

Kodi ponena zimenezi ndiye kuti ndikufuna kuti anthu andivomereze? Iyai, koma kuti andivomereze ndi Mulungu. Kodi ndikuyesa kukondweretsa anthu? Ndikadayesabe kukondweretsa anthu, si bwenzi ndilinso mtumiki wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:15-16

Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:11-12

Paja mukudziŵa kuti, tinkasamala aliyense mwa inu monga momwe amachitira bambo ndi ana ake. Tinkakulimbitsani mtima, kukuthuzitsani mtima ndi kukupemphani kuti mayendedwe anu akhale okomera Mulungu, amene amakuitanani kuti mukaloŵe mu Ufumu wake waulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:1

Potsiriza, abale, mutipempherere kuti mau a Ambuye afalikire msanga, ndipo anthu aŵalandire mauwo mwaulemu, monga momwe mudachitira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:18

Iwe Timoteo, mwana wanga, ndikukupatsa malangizo ameneŵa molingana ndi zimene aneneri adaanenapo kale za iwe. Mau amenewo akuthandize kumenya nkhondo yabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:7

Nchifukwa chake ine adandiika kuti ndikhale mlaliki wake ndiponso mtumwi, wophunzitsa anthu a mitundu ina mau a chikhulupiriro choona. Sindikunamatu ai, ndikunena zoona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:7-8

Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu. Mau ako akhale oona, kuti anthu asadzathe kuŵatsutsa. Motero wotsutsana nawe adzachita manyazi, atasoŵa kalikonse koipa kuti atinenere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:19

Ife timakonda Mulungu chifukwa ndiye adayamba kutikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:4-5

Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:10

Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:17-18

Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga, ndipo ndikulalikabe ntchito zanu zodabwitsa. Choncho Inu Mulungu, musandisiye ndekha ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbu, mpaka nditalalika mphamvu zanu kwa mibadwo yonse yakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7-9

Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu. Uziilemekeza nzeruyo, ndipo idzakukweza. Uifungate ndipo idzakupatsa ulemerero. Idzaika pamutu pako nsangamutu yokongola yamaluŵa. Idzakuveka chisoti chaufumu chaulemu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:20-21

Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona. Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:8

Muzikachiritsa odwala, muzikaukitsa akufa, muzikachotsa khate, muzikatulutsa mizimu yoipa. Mwalandira mwaulere, kaperekeni mwaulere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:19-20

“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:1

Pambuyo pake Ambuye adasankha anthu 72, naŵatuma aŵiriaŵiri kuti atsogole kupita ku mudzi uliwonse ndi ku malo aliwonse kumene Iye ankati apiteko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:12

Lamulo langa ndi lakuti muzikondana monga momwe Ine ndakukonderani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:3

Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:12-13

Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:8

Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13-14

Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi. Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:10

Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 4:5-6

Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe. Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 3:12

Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:1-2

Pitirizani kukondana monga abale. Ife tili ndi guwa, ndipo ansembe otumikira m'chihema chachipembedzo cha Ayuda saloledwa kudyako zoperekedwa pamenepo. Mkulu wa ansembe wachiyuda amaloŵa ndi magazi a nyama ku Malo Opatulika kuti magaziwo akhale nsembe yopepesera machimo. Koma nyama yeniyeniyo amaiwotchera kunja kwa misasa. Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake. Tiyeni tsono tipite kwa Iye kunja kwa misasa kuti tikanyozekere naye limodzi. Paja ife tilibe mzinda wokhazikika pansi pano, tikufunafuna wina umene ulikudza. Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera. Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu. Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe. Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo. Ndikukupemphani makamaka kuti mupemphere kuti Mulungu andibwezere kwa inu msanga. Musanyozere kumalandira bwino alendo m'nyumba mwanu. Pali ena amene kale adaalandira bwino alendo, ndipo mosazindikira adaalandira angelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:1

Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:12

Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:50

Chimene chimandisangalatsa m'masautso anga nchakuti malonjezo anu amandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 133:1

Ati kukoma ndi kukondweretsa ati, anthu akakhala amodzi mwaubale!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:16

Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse! Ndikubwera kwa Inu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, Inu nokha ndinu Woyenera kutamandidwa ndi kulambiridwa kwakukulu. Ndikukupemphani chifukwa cha m'busa wanga, kuti mafuta a Mzimu Woyera akhale pa moyo wake ndipo tsiku lililonse mulimbitse utumiki umene mwamupatsa. Mudzaze ndi nzeru kuti akhale woyang'anira bwino ndi kuphunzitsa mpingo wanu molingana ndi mawu anu. Dalitsani moyo wake ndi wa banja lake. Muthandizeni kukhalabe mu mgwirizano wa mtendere kuti nthawi zonse azitsatira khalidwe labwino, akusonyeza umboni ndi chikondi cha Khristu. Mawu anu amati: "Koma mkulu ayenera kukhala wosalakidwa, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodziletsa, wanzeru, waulemu, wokonda alendo, wolangiza bwino." Muthandizeni tsiku lililonse kukhala ndi moyo wopemphera ndi kuyanjana nanu kotero kuti chofunika kwambiri pa moyo wake chikhale kukhalapo kwa Mzimu Woyera wanu. Ndikukupemphani kuti muunikire nkhope yanu pa iye, kuti chisomo chanu ndi chiyanjo chanu zikhalebe pa moyo wake. Muzikonzanso mphamvu zake kuti athe kukumana ndi zovuta ndi mavuto kaya muutumiki, zachuma kapena za m'banja. Mulimbitse kuti apulumuke mu mayesero ndi ziyeso m'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa