Ine ndili munthu wochimwa, ndakhala mu mdima ndi kuipa, koma Mulungu wandiyitana ine dzina langa kuti ndipulumuke ndi chisomo chake.
Ndagulidwa ndi magazi amtengo wapatali a Yesu amene anafera pa mtanda. Sindikuyendayenda ndekha chifukwa Yesu ndiye m'busa wanga.
Aliyense amene wabadwanso mwa uthenga wabwino ndi wa Yesu, M'busa Wamkulu amene anatifera tonse. Sindikusochera njira chifukwa ndikutsogozedwa ndi M'busa wabwino koposa, Yesu Khristu, amene amandikonda ndi chikondi chosatha.
Ngakhale Mulungu amatipatsa abusa kuti atiyang'anire mwauzimu, ndife anthu a Mulungu ndi nkhosa zake. Ana a Mulungu ali ngati nkhosa, osati ngati mbuzi, njoka kapena mkango, koma Mulungu angasinthe mbuzi kukhala nkhosa.
“Nkhosa zanga zimva mawu anga, ndipo ine ndizizindikira, ndipo zinditsata.” (Yohane 10:27)
Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.
Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.
Pambuyo pake Yesu adaŵauza kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya usiku uno. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa za msambiwo zidzangoti balala.’
“Anthu anga anali ngati nkhosa zotayika. Abusa ao adaŵasokeza ndi kuŵayalukitsa ku mapiri. Ankangoyendayenda ku zitunda ndi ku mapiri, mpaka kuiŵala kwao.
Inu mukamuuze kuti, ‘Ife bwana, ndife oŵeta zoŵeta kuyambira ubwana wathu, monga momwe ankachitira makolo athu.’ Mukatero, ndiye kuti mudzatha kukakhala m'dziko la Goseni.” Yosefe adaanena zimenezi chifukwa choti Aejipito ankanyansidwa ndi abusa.
Mulengeze kwa khamu lonse la Aisraele kuti pa tsiku lakhumi la mwezi uno, munthu aliyense adzasankhulire banja lake mwanawankhosa mmodzi. Banja lililonse lidzatenge mwanawankhosa mmodzi.
Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.
Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa, naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta. Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao.
Yakobe akulankhulabe ndi iwowo, Rakele adafika ndi nkhosa za atate ake. Iyeyo ndiye ankaŵeta nkhosazo.
Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake, ndife nkhosa zodyera m'manja mwake. Lero mukadamverako mau ake!
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi, Tsopano nkhosa zangazo ndidzazifunafuna ndekha mwiniwakene, ndipo ndidzazisamala. Monga mbusa amanka nafunafuna nkhosa zake, pamene zina zabalalikira kutali, Inenso ndidzatero, kunka ndikufunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa konse kumene zidamwazikira pa nthaŵi yamdima ndi yankhungu.
Zotayika ndidzazifunafuna, zosokera ndidzazibweza, zopweteka ndidzazimanga mabala ake. Zofooka ndidzazilimbikitsa, koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaŵeta nkhosa zanga mwachilungamo.”
Yesu adati, “Inetu Mulungu adandituma kwa amene ali ngati nkhosa zotayika pa mtundu wa Aisraele.”
“Tsono mukuganiza bwanji? Munthu atakhala ndi nkhosa 100, imodzi nkutayika, kodi sangasiye 99 zina zija m'phiri nkukafunafuna imodzi yotayikayo? Ndithu ndikunenetsa kuti ataipeza, chimwemwe chake chokondwerera imeneyo chimapambana chokondwerera zina zija zimene sizidatayike. Chonchonso Atate anu amene ali Kumwamba safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike.
“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera ndi ulemerero wake, pamodzi ndi angelo onse, adzachita kukhalira pa mpando wake wachifumu. Adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse pamaso pake, ndipo adzaŵalekanitsa monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Nkhosa adzazikhazika ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi ku dzanja lake lamanzere.
Anthu onse okhometsa msonkho ndi Ayuda enanso onyozera Malamulo ankabwera kwa Yesu kudzamva mau ake. Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.” Yesu adatinso, “Munthu wina adaali ndi ana aamuna aŵiri. Wamng'ono adapempha bambo wake kuti, ‘Atate, bwanji mugaŵiretu tsopano chuma chanu, ine mundipatsiretu chigawo changa.’ Bamboyo adaŵagaŵiradi ana ake aja chuma chake. Patangopita masiku oŵerengeka wamng'ono uja adagulitsa chigawo chake chonse, nachoka kwaoko ndi ndalama zake kupita ku dziko lakutali. Kumeneko adamwaza chuma chakecho ndi mayendedwe oipa. Chitamthera chuma chake chonse, mudaloŵa njala yaikulu m'dziko limeneli, mwakuti iye yemwe adayamba kusauka. Pamenepo adapita kukakhala nao kwa nzika ina ya m'dzikomo. Nzikayo idamtuma ku busa kukaŵeta nkhumba zake. Mnyamata uja ankalakalaka kudya makoko amene nkhumba zinkadya, koma panalibe munthu wompatsako ngakhale makokowo. “Atakhalakhala adadzidzimuka mumtima mwake, ndipo adati, ‘Achulukirenji antchito a bambo wanga amene ali ndi chakudya chokwanira mpaka kutsalako, pamene ine kuno ndikufa ndi njala. Basi ndinyamuka, ndipita kwa bambo wanga, ndipo ndikanena kuti: Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kutchedwanso mwana wanu. Mundilole ndisanduke mmodzi mwa antchito anu.’ Tsono Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo adayamba kuŵinya nkumanena kuti, “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa, nkumadya nawo pamodzi.” “Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona. Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’ Koma bambo wake adauza antchito ake kuti, ‘Thamangani mukatenge mkanjo wabwino kwambiri, mumuveke. Mumuvekenso mphete ku chala, ndi nsapato ku mapazi. Ndipo katengeni mwanawang'ombe wonenepa uja, muphe kuti tidye, tikondwere. Chifukwa mwana wangayu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ Ndiye pompo chikondwerero chidayamba. “Koma mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Pochokera kumundako, atafika pafupi ndi nyumba, adamva anthu akuimba ndi kuvina. Adaitana wantchito mmodzi namufunsa kuti, ‘Kodi kwagwanji?’ Iye adati, ‘Mng'ono wanu uja wabwera, ndiye bambo apha mwanawang'ombe wonenepa uja chifukwa amlandira ali wamoyo.’ Atamva zimenezo mwana wamkuluyo adapsa mtima, nakana kuloŵa. Apo bambo wake adatuluka, nkumupempha mopemba kuti aloŵe. Koma iye adayankha bambo akewo kuti, ‘Ine zaka zonsezi ndakhala ndikukugwirirani ntchito ndipo sindidalakwirepo lamulo lanu. Komabe inu simudandipatsepo ndi katonde komwe kuti ndikondwere pamodzi ndi anzanga. Tsono Yesu adaŵaphera fanizo ili, adati, Koma mwana wanuyu, chuma chanu chonse adaonongera akazi achiwerewere, ndipo pamene wabwera, mwamuphera mwanawang'ombe wonenepa uja!’ “Bambo wakeyo adamuyankha kuti, ‘Mwana wanga, iwe uli ndi ine nthaŵi zonse, ndipo zanga zonse nzako. Kunayenera kuti tikondwere ndi kusangalala, chifukwa mng'ono wakoyu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ ” “Ndani mwa inu ali ndi nkhosa 100, imodzi itatayikapo, sangasiye nkhosa zina zonse 99 zija ku busa, nkukafunafuna yotayikayo mpaka ataipeza? Ndipo ataipeza, amaisenza pamapewa pake mokondwa. Pofika kwao, amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndaipeza nkhosa yanga idaatayika ija.’ ” Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”
Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.”
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Monga anthu onse amamwalira chifukwa ndi ana a Adamu, momwemonso anthu onse adzauka chifukwa cholumikizana ndi Khristu.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana. Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.
Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.
Aŵa ndi mau otsimikizika, oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa.
Mulungu wopatsa mtendere, adaukitsa kwa akufa Ambuye athu Yesu, amene ndiye Mbusa wamkulu wa nkhosa, chifukwa cha imfa yake yotsimikizira Chipangano chamuyaya. Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza, Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.
Munali ngati nkhosa zosokera, koma tsopano mwabwerera kwa Mbusa amene ndi wokuyang'anirani.
Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo. Ndipo pamene Mbusa wamkulu adzaonekera, mudzalandira mphotho yosafota yaulemerero.
Ndaima pakhomo pano, ndipo ndikugogoda. Wina akamva mau anga, nkutsekula chitseko, ndiloŵa, ndipo Ine ndi iye tidyera limodzi.
Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
Yesu adaŵayankha kuti, “Ndani mwa inu atakhala ndi nkhosa imodzi, nkhosayo nkugwa m'dzenje pa tsiku la Sabata, angapande kuigwira nkuitulutsa? Nanji munthu, amene amaposa nkhosa kutalitali! Ndiye kutitu Malamulo amalola kuchita zabwino pa tsiku la Sabata.”
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Chonchonso Atate anu amene ali Kumwamba safuna kuti ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa atayike.
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Paja anthu amati, ‘Ikapita miyezi inai, ndiye kuti yafika nyengo yokolola.’ Koma ndithu, taonani m'mindamu, kodi simukuwona kuti mbeu zacha kale kudikira kholola?
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.
Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”
Paja Khristu adamwalira nakhalanso ndi moyo, kuti akhale Mbuye wa anthu akufa ndiponso wa anthu amoyo.
Kwa amene ali ndi chikhulupiriro chofooka, ndidakhala ngati wa chikhulupiriro chofooka, kuti ndiŵakope ofookawo. Kwa anthu onse ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ngati nkotheka ndikope ena mwa iwo.
Koma ngakhale Uthenga Wabwino umene timalalika uli wophimbika, ngwophimbika kwa okhawo amene akutayika. Iwoŵa sakhulupirira, popeza kuti Satana, amene ali mulungu wa dziko lino lapansi, adachititsa khungu maganizo ao, kuwopa kuti angaone kuŵala kwa Uthenga Wabwino. Kuŵalako kumaonetsa ulemerero wa Khristu, ndipo mwa Iyeyu Mulungu mwini amaoneka.
Ndikudabwa kuti mukupatuka msangamsanga motere, kusiya Mulungu amene adakuitanani mwa kukoma mtima kwa Khristu, ndipo kuti mukutsata uthenga wabwino wina.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu zonse. Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.
Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona. Mulungu adakuitanirani zimenezi kudzera mwa Uthenga Wabwino umene tidakulalikirani. Adakuitanani kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu.
Komatu tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthaŵi pang'ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zoŵaŵa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse.
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife motere: Iye nkukhala ndi Mwana mmodzi yekha, koma adamtuma pansi pano, kuti mwa Iye tikhale ndi moyo.
Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona chinamtindi cha anthu osaŵerengeka. Anthuwo anali ochokera m'mitundu yonse ya anthu, ndi m'mafuko onse, ndipo anali a zilankhulo zonse. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Mwanawankhosa uja; anali atavala mikanjo yoyera, nthambi zakanjedza zili m'manja.
Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
“Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuŵamva ifeyo, ndipo adalandira zoŵaŵa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa. Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
“Ndidaakusiya pa kamphindi kochepa, koma ndidzakutenganso ndi chikondi chachikulu. Ndidaakufulatira pa mphindi yaing'ono ndili wokwiya zedi, koma ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya,” akuterotu Chauta, Momboli wako.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Iye sadzatsiriza bango lothyoka, nyale yofuka sadzaizimitsa, mpaka atapambanitsa chilungamo.
Afarisi pamodzi ndi aphunzitsi ao a Malamulo adayamba kuŵinya, nafunsa ophunzira ake kuti, “Bwanji mukudya ndi kumwa pamodzi ndi okhometsa msonkho, ndi anthu ochimwa?” Yesu adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala. Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa, kuti atembenuke mtima.”
“Ndani mwa inu ali ndi nkhosa 100, imodzi itatayikapo, sangasiye nkhosa zina zonse 99 zija ku busa, nkukafunafuna yotayikayo mpaka ataipeza? Ndipo ataipeza, amaisenza pamapewa pake mokondwa. Pofika kwao, amasonkhanitsa abwenzi ake ndi anzake oyandikana nawo, naŵauza kuti, ‘Mukondwere nane pamodzi, chifukwa ndaipeza nkhosa yanga idaatayika ija.’ ”
monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.
Apo Filipo adayamba kumlalikira Uthenga Wabwino wa Yesu kuyambira pa Malembo ameneŵa.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Wochita zonsezi ndi Mulungu, amene mwa Khristu adatiyanjanitsa ndi Iye mwini, ndipo adatipatsa ntchito yolalikira anthu chiyanjanitsocho.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu.
Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano. Inu ana, muzimvera anakubala anu pa zonse, pakuti kutero kumakondwetsa Ambuye. Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, kuti angataye mtima. Inu antchito, muziŵamvera pa zonse ambuye anu apansipano. Musamangochitatu zimenezi pamene muli pamaso pao kuti akuyamikireni, koma muziŵamvera ndi mtima wonse, chifukwa choopa Ambuye. Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu. Koma munthu amene amachita zosalungama, zidzamubwerera, chifukwa Mulungu amaweruza mosakondera. Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye.
nchifukwa chake ndilikumva masautsoŵa. Koma sindichita manyazi, pakuti ndimamdziŵa Iye amene ndakhala ndikumkhulupirira, ndipo sindikayika kuti Iyeyo angathe kusunga bwino, mpaka tsiku la chiweruzo, zimene adandisungiza ine.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
Inu Chauta, kumbukirani chifundo chanu ndi chikondi chanu chosasinthika, chifukwa mudaziwonetsa kuyambira kalekale. Musakumbukire machimo a unyamata wanga ndi mphulupulu zanga. Koma mundikomere mtima, Inu Chauta, chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.
Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo. Nthaŵi imeneyo mudzandiitana ndi kumanditama mopemba, ndipo ine ndidzakumverani. Mudzandifunafuna, ndipo mudzandipeza. Mukadzandifunafuna ndi mtima wanu wonse,
‘Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimadyetsa, ndipo Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.’ ”
“Inu nkhosa zanga, ngakhale muli oŵerengeka, musaope, pakuti kudakomera Atate anu kuti akupatseni Ufumu wake.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani? Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama. Koma munthu wokonda mnzake, amakhala m'kuŵala, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. Munthu wodana ndi mnzake, ali mu mdima, ndipo akuyenda mu mdima. Sadziŵa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa m'maso. Inu ana, ndikukulemberani popeza kuti Mulungu wakukhululukirani machimo anu chifukwa cha dzina la Khristu. Inu atate, ndikukulemberani, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Inu achinyamata, ndikukulemberani, chifukwa mwampambana Woipa uja. Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja. Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya. Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi. Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu. Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali. Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa. Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani? Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga. Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya. Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse.