Kale lomwe, kuvina sikunali kololedwa m’malo olambirira monga masikono, m’makachisi, m’masunagoge, komanso sikunali mbali ya kulambira kwa mpingo woyamba. Koma masiku ano, ndimaona kuti kuvina ndi njira yotamandira Mulungu, kufotokoza ndi thupi langa zimene nthawi zina sindingathe kufotokoza ndi mawu.
Kuvina ndi njira yolemekezera Wapamwamba, kusonyeza chisangalalo changa, ndi kukondwerera zipambano zimene amandipatsa tsiku ndi tsiku. Ndikukumbukira kuti koyamba kuvina kutchulidwa m’Baibulo kunali pamene Aisiraeli anaoloka Nyanja Yofiira.
M’buku la Ekisodo 15:20-21, timawerenga mmene Miriamu, mlongo wake wa Aroni, anatengera chimbale ndipo akazi anzake anamutsatira ndi zimbale ndi mavina, akuimbira Yehova chifukwa cha ukulu wake ndi chifukwa chogonjetsa ankhondo a Aigupto panyanja. Chochititsa chidwi n’chakuti chikondwererochi chinachitikira panja, kusonyeza kuti Mulungu amafuna kuti tikondwerere ndi chisangalalo, kulumpha, ndi chimwemwe pazonse zimene atichitira, tikukhala m’ufulu wathunthu.
Miriyamu, mneneri wamkazi, mlongo wa Aroni, adatenga kang'oma, ndipo akazi onse adamtsata pambuyo akuimba ting'oma, ndi kumavina.
Pamene Bokosi lachipangano lija lidadza ku mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo, adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake.
Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo.
Tsono Davide pamodzi ndi Aisraele onse ankakondwerera kwambiri kulemekeza Chauta poimba ndi mphamvu zao zonse nyimbo ndi azeze, apangwe, tizing'wenyeng'wenye, maseche ndi ziwaya zamalipenga.
Pamene anthu ankabwerera kwao, Davide atapha Mfilisti uja, akazi adatuluka m'mizinda yonse ya Aisraele akuimba ndi kuvina, kuti achingamire mfumu Saulo. Ankaimba ndi kumavina mokondwa, kwinaku ng'oma ndi zitoliro zikugundika.
Anamwali adzavina mokondwa, achinyamata ndi okalamba omwe adzasangalala. Kulira kwao kuja ndidzakusandutsa chimwemwe. Ndidzaŵasangalatsa, ndidzaŵakondwetsa, nkuchotsa chisoni chao.
Pambuyo pake Yefita adabwerera kwao ku Mizipa. Ndipo adangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamchingamira, akuimba ng'oma ndi kumavina. Iye anali mwana wake mmodzi yekhayo. Analibenso mwana wina, wamwamuna kapena wamkazi.
Ndidzakusamaliraninso inu anthu a ku Israele, motero mudzapezanso bwino. Mudzakondwanso poimba ting'oma tolira, ndipo mudzapita nawo limodzi anthu ovina mwachimwemwe.
Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”
Ombani m'manja inu anthu a mitundu yonse. Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe.
Pamene Bokosi lachipangano linkaloŵa mu mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Saulo adasuzumira pa windo, naona mfumu Davide akulumphalumpha ndi kuvina molemekeza Chauta. Pamenepo mkaziyo adayamba kunyoza Davide mumtima mwake.
Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Bwerani ndi zopereka, ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake. Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera.
Davide pamodzi ndi akuluakulu osamalira za utumiki adapatulanso anthu ena otumikira mwa ana a Asafu, a Hemani ndi a Yedutuni amene ankalosa poimba ndi apangwe ndi azeze ndiponso ziwaya zamalipenga. Mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchitoyo ndiponso mndandanda wa ntchito zao nawu:
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.
Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani.
Kankhani zipata za mzinda, tsekulani zitseko zakalekalezo, kuti Mfumu yaulemerero iloŵe. Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta wanyonga ndi wamphamvu, Chauta ndiye ngwazi pa nkhondo.
Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera.
Inu Mulungu, mdipiti wa anthu anu oyenda mwaulemu ukuwoneka, mdipiti wolemekeza Mulungu wanga, Mfumu yanga, wokaloŵa m'malo opatulika. Oimba nyimbo zapakamwa atatsogola, oimba ndi zipangizo ali pambuyo, anamwali oimba ting'oma ali pakati.
Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse. Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.
Ndidzaimbira Chauta moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Chauta, nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu. Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe kuti likhale chipangano chokhazikika mu Israele mpaka muyaya. Adati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani kuti likhale choloŵa chako chokhalira iweyo.” Pamene anali anthu oŵerengeka, anthu osatchuka, ongokhala nawo m'dzikomo, omangoyendayenda kuchokera ku mtundu wina wa anthu kupita ku mtundu wina, kuchokera ku ufumu wina kupita ku ufumu wina, sadalole ndi mmodzi yemwe kuti aŵapsinje, adalanga mafumu ena chifukwa cha anthu akewo. Adati, “Musakhudze odzozedwa anga, musaŵachite choipa aneneri anga.” Pamene Chauta adadzetsa njala m'dziko la Kanani ndi kuwononga chakudya chonse, Iye anali atatuma munthu patsogolo pa anthu ake, Yosefe uja amene adagulitsidwa ngati kapolo. Mapazi ake adapwetekedwa ndi matangadza, khosi lake lidavekedwa unyolo, mpaka zimene Yosefe adanena zija zidachitikadi. Mau a Chauta adatsimikiza kuti iye sadalakwe. Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda, lalikani za ntchito zake zodabwitsa.
Apereke nsembe zothokozera, ndi kulalika ntchito za Chauta, poimba nyimbo zachimwemwe.
Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu, mtima wanga wakonzekadi! Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda. Lumpha, iwe mtima wanga. Ndani adzandifikitse ku mzinda wamalinga? Ndani adzanditsogolere ku Edomu? Si wina ai koma ndinu Mulungu amene mwatitaya, ndinu Mulungu amene mwaleka kuperekeza ankhondo athu. Tithandizeni kulimbana ndi adani athuwo, pakuti chithandizo cha munthu nchopandapake. Mulungu akakhala nafe, tidzamenya nkhondo molimba mtima, pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu. Inu zeze ndi pangwe, tiyeni lirani. Ndidzadzutsa dzuŵa ndi nyimbo zanga. Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a m'maiko onse,
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse. Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima. Aisraele asangalale ndi Mlengi wao. Anthu a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yao.
Tamandani Chauta! Tamandani Mulungu m'malo ake opatulika. Mtamandeni ku thambo lake lamphamvu. Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu, mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana. Mtamandeni pomuimbira lipenga, mtamandeni ndi gitara ndi zeze. Mtamandeni poimba ng'oma ndi povina, mtamandeni ndi zipangizo zansambo ndi mngoli. Mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira, mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira kwambiri. Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Chauta. Tamandani Chauta!
Tsiku limenelo mudzati: “Thokozani Chauta, tamandani dzina lake. Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, mulalike kuti dzina lake ndi lopambana. “Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu. Zimenezi zidziŵike pa dziko lonse lapansi.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala mwezi, ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Chauta.
“ ‘Tidaakuimbirani ng'oma yaukwati, bwanji inu osavina? Tidaabuma maliro, bwanji inu osalira?’
Pamenepo Maria adati, “Mtima wanga ukutamanda Ambuye, ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga,
“Ndinu odala anthu akamadana nanu, akamakusalani ndi kukuchitani chipongwe, ndipo akamaipitsa dzina lanu chifukwa cha Ine Mwana wa Munthu.
Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza. Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.”
Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Nanga pamenepa nkutani? Ndidzapemphera ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Ndidzaimba ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga.
Tithokoze Mulungu amene mwa Khristu amatitsogolera nthaŵi zonse m'kupambana kwake. Kudzera mwa ife Mulungu akupatsa anthu onse nzeru zodziŵira Khristu, ndipo nzeruzo zikuwanda ponseponse ngati fungo labwino.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.
Mtima wanga umaŵawa ndikamakumbukira m'mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu, poŵatsogolera ku Nyumba ya Mulungu. Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala, akuimba nyimbo zothokoza ndipo akuchita chikondwerero.
Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.
Koma anthu anu Mulungu, akondwere, asangalale pamaso panu, inde, asekere ndi chimwemwe.
Pakamwa panga padzafuula ndi chimwemwe, pamene ndikukuimbirani nyimbo zotamanda. Nawonso mtima wanga umene mwauwombola, udzaimba moyamika.
Pomaliza Ambuye adachita ngati kudzuka kutulo, ngati munthu wamphamvu wofuula chifukwa choledzera.
Nkwabwino kuthokoza Chauta, kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse. Koma ine mwandilimbitsa ngati njati. Mwandidzoza ndi mafuta atsopano. Maso anga aona kuwonongeka kwa adani anga, makutu anga amva za kugwa kwa adani ondiwukira. Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni. Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu. Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira, imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota. Nkwabwino m'maŵa kulalika za chikondi chanu chosasinthika, ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu, poimba nyimbo zokoma ndi gitara, zeze ndi pangwe.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Mverani nyimbo m'mahema mwa anthu a Mulungu, nyimbo zokondwerera kupambana, zakuti, “Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu, dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”
Atamande Mulungu kwambiri mokweza mau, malupanga akuthwa konsekonse ali m'manja, kuti alipsire mafuko achikunja, kuti alange mitundu ina ya anthu. Amange mafumu ao ndi maunyolo, amange atsogoleri ao ndi zitsulo, kuti aŵalange monga momwe Mulungu adalamulira. Umenewu ndiwo ulemerero wa anthu okhulupirira Chauta. Tamandani Chauta!
Pali nthaŵi yomva chisoni ndi nthaŵi yosangalala, nthaŵi yolira maliro ndi nthaŵi yovina.
Koma inu anthu a Mulungu, mudzakondwa ndi kuimba monga m'mene mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika. Mudzasangalala ngati anthu opita naimba toliro ku phiri la Chauta, thanthwe la Israele.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Kodi nditenge chiyani kuti ndifike pamaso pa Chauta, kuti ndikapembedze Mulungu Wakumwamba? Kodi nditenge anaang'ombe a chaka chimodzi kuti ndipereke nsembe zopsereza? Kodi Chauta adzakondwera ndi nkhosa zamphongo zikwi zingapo kapena mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndidzapereke mwana wanga wachisamba chifukwa cha zolakwa zanga? Kodi mwana wanga adzakhale nsembe yolipira tchimo langa? Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsera mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.
Mwadzidzidzi Yesu adakumana nawo nati, “Monitu azimai!” Iwo adadza pafupi, nkugwira mapazi ake, nampembedza.
Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adadzaza Yesu ndi chimwemwe, mwakuti Yesuyo adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu.
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Mpaka tsopano simunapemphe kanthu potchula dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, kuti chimwemwe chanu chikhale chathunthu.”
Adalumpha, naimirira, nayamba kuyenda, ndipo adaloŵa nao m'Nyumba ya Mulungu akuyenda ndi kulumpha ndi kutamanda Mulungu.
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Inetu zimene ndidalandira kwa Ambuye ndi zimene nanenso ndidazipereka kwa inu, zakuti usiku umene adaperekedwa uja, Ambuye Yesu adaatenga mkate. Ndipo atathokoza Mulungu, adaunyemanyema nati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.” Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.” Pakuti nthaŵi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye, mpaka adzabwerenso.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi. Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.
Inu mwakhala mukutsata chitsanzo chathu ndi cha Ambuye. Ngakhale mudapeza masautso ambiri, mudalandira mau athu mwa chimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha. Paja Mulungu wathu ndi moto wopsereza.
Chimene tidachiwona ndi kuchimva, tikukulalikirani, kuti inunso mukhale a mtima umodzi ndi ife. Kuyanjana kwathu tikuyanjana ndi Atate, ndiponso ndi Mwana wao, Yesu Khristu.
Anthu aja ankaimba nyimbo yatsopano pamaso pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Zamoyo zinai zija, ndi Akuluakulu aja. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kuiphunzira nyimboyo, kupatula anthu zikwi 144 aja amene anali ataomboledwa mu ukapolo wa dziko lapansi.
Pambuyo pake ndidamva ngati mau amphamvu a chinamtindi cha anthu Kumwamba. Mauwo ankati, “Aleluya! Chipulumutso, ulemerero ndi mphamvu ndi zake za Mulungu wathu, Apo ndidadzigwetsa ku mapazi ake kuti ndimpembedze. Koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ndiponso ngati abale ako amene amachitira Yesu umboni. Iwe pembedza Mulungu.” Pajatu kuchitira Yesu umboni ndiye thima la uneneri. Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama. Maso ake anali psuu ngati malaŵi a moto, ndipo pamutu pake panali zisoti zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lolidziŵa iye yekha, osati wina aliyense. Chovala chake chinali choviika m'magazi, ndipo ankatchedwa, “Mau a Mulungu.” Magulu a ankhondo a Kumwamba ankamutsatira atakwera akavalo oyera, ndipo iwowo atavala zabafuta, zoyera ndi zangwiro. M'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa lotulukira kunja, loti adzalangire mitundu ya anthu. Adzaŵalamulira ndi ndodo yachitsulo, ndipo m'chopondera mphesa adzaponda mphesa za vinyo wa mkwiyo waukali wa Mulungu Mphambe. Pa mkanjo wake, ndi pantchafu pake padaalembedwa dzina loti, “Mfumu ya mafumu onse, ndi Mbuye wa ambuye onse.” Kenaka ndidaona mngelo mmodzi ataimirira pa dzuŵa. Adafuula mokweza mau, nauza mbalame zonse zouluka mu mlengalenga kuti, “Dzasonkhaneni ku mgonero waukulu wa Mulungu. Bwerani, mudzadye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi wa okwerapo, mnofu wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, ang'onoang'ono ndi akuluakulu.” Pambuyo pake ndidaona chilombo chija pamodzi ndi mafumu a pa dziko lapansi, ndi magulu ao ankhondo. Adaasonkhana kuti amenyane nkhondo ndi wokwera pa kavalo uja, pamodzi ndi gulu lake la ankhondo. pakuti chiweruzo chake chilichonse nchoona ndi cholungama. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene ankaipitsa dziko lapansi ndi chigololo chake, wamlanga chifukwa cha kupha atumiki ake.” Chilombocho chidagwidwa pamodzi ndi mneneri wonama uja amene anali atachita zozizwitsa pamaso pake. Zozizwitsazo, iye anali atanyenga nazo anthu amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, ndiponso anthu amene anali atapembedza fano lake lija. Chilombo chija ndi mneneri wonama uja, onse aŵiri adaŵaponya m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala yoyaka ya sulufure. Ena onse adaphedwa ndi lupanga lija lotuluka m'kamwa mwa wokwera pa kavalo uja. Ndipo mbalame zonse zidadya ndi kukhuta mnofu wa anthuwo. Kachiŵiri mau aja adanenanso kuti, “Aleluya! Utsi wa mzindawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”
Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu, thambo limasonyeza ntchito za manja ake. Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide, ngakhale golide wambiri wamtengowapatali, nzotsekemera kupambana uchi, ngakhale uchi wozuna kwambiri. Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu. Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake? Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika. Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu. Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga. Usana umasimbira zimenezo usana unzake, usiku umadziŵitsa zimenezo usiku unzake.
Monga momwe mbaŵala imakhumbira mtsinje wamadzi, ndimo m'mene mtima wanga umakhumbira Inu Mulungu wanga.
Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a m'maiko onse,
Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.
Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.