Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, kutamanda Mulungu kumatanthauza kuvomereza zabwino zonse zimene Mulungu watichitira. Timamuyamika chifukwa cha mphamvu zake zopambana zonse ndipo nthawi zonse timakweza dzina lake.
Ngati tili mu utumiki wotamanda Mulungu, tiyenera kukhala pa ubwenzi ndi Mzimu Woyera nthawi zonse. Chifukwa kudzera mu ubwenzi ndi Iye, timadziwa bwino Mulungu m'miyoyo yathu. Timam'tamanda chifukwa cha zimene tazidziwa tokha, osati zimene tamva kwa ena. Umu ndi momwe timatamanditsira Mulungu Wamuyaya ndikutsogolera anthu kuti amulemekeze ndi kumukweza.
Mwayi wotamanda Mulungu si wa aliyense. Choncho, ndikofunikira kusunga mitima yathu yoyera ndi kupita pamaso pa Mulungu opanda chilema. Tisachite chilichonse chomwe chingatichititse manyazi. Tiyenera kuyamikira mwayi wotumikira Mulungu ndi kumupatsa ulemerero nthawi zonse. Tiyenera kulola kuti nyimbo zatsopano zotamanda Yesu zizituluka m'kamwa mwathu.
Komanso, tiyenera kukumbukira kuti monga atumiki, tiyenera kutetezerana ndikudikirirana kuti mdani asatiipitse. Tiyenera kuyang'ana pa zinthu zoyera, zabwino, ndi zolungama. Monga thupi limodzi, cholinga chathu chikhale choti dzina la Mulungu litamandike pakati pa anthu amoyo.
Ine ndine Chauta, dzina langa nlimenelo. Ulemerero wanga sindidzapatsa wina aliyense. Mayamiko oyenera Ine, sindidzalola kuti mafano alandireko.
Ndiyenera kuchita zimene ndidalumbira kwa Inu Mulungu. Ndidzapereka kwa Inu nsembe zothokozera.
Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita pamaso pa onse okumverani.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse. Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu.
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa. Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani. Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse. Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika, salephera kumva kulira kwao ndipo amalanga anthu oŵazunzawo. Mundikomere mtima, Inu Chauta. Onani m'mene akundisautsira anthu ondida. Inu mumandipulumutsa ku imfa, kuti ndithe kuyamika ntchito zanu zonse, pakati pa anthu anu a mu Ziyoni. Zoonadi ndidzakondwa chifukwa mwandipulumutsa. Akunja agwera m'mbuna yokumba iwo omwe. Phazi lao lakodwa mu ukonde wobisika wotcha iwo omwe. Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe. Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu. Koma anthu aumphaŵi Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse, anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala mpang'ono pomwe. Dzambatukani, Inu Chauta, munthu asakunyozeni. Azengeni mlandu anthu akunja. Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Ine ndidzathokoza Chauta chifukwa cha kulungama kwake, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Chauta, Wopambanazonse uja.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa.
Pa nthaŵiyo nyenyezi zakuvuma zinkaimba pamodzi, ndipo angelo onse a Mulungu ankafuula mokondwa?
Ndidzatamanda dzina la Mulungu pomuimbira nyimbo, ndidzalalika ukulu wake pomuthokoza.
Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a maiko onse,
Pamodzi ndi iyeyo tikutuma mbale wathu uja, amene mipingo yonse ikumuyamika chifukwa cha ntchito yake yolalika Uthenga Wabwino.
Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani.
Mataniyo, mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, amene anali mtsogoleri pa mapemphero achiyamiko m'Nyumba ya Mulungu, ndiponso Bakibukiya, amene anali wachiŵiri pakati pa abale ake. Panalinso Abida, mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.
Tsono Alevi aŵa, Yesuwa, Kadimiyele, Bani, Hasabeniya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya adalengeza kuti, “Imirirani, mumtamande Chauta, Mulungu wanu, nthaŵi zonse. Litamandike dzina lake laulemerero limene anthu sangathe kulilemekeza ndi kulitamanda mokwanira.”
Adamanganso guwa la Chauta, namaperekerapo nsembe zachiyanjano ndiponso nsembe zothokozera. Tsono adalamula anthu a ku Yuda kuti azitumikira Chauta Mulungu wa Israele.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta, inu anthu ake oyera mtima, mumthokoze chifukwa cha dzina lake loyera.
Iwowo ankaimba potsata malangizo a bambo wao m'Nyumba ya Mulungu. Ankaimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira ku Nyumba ya Mulungu. Asafu, Yedutuni ndi Hemani inkaŵalamulira ndi mfumu imene.
Ankatumikira akuimba nyimbo pakhomo pa malo opatulika a m'chihema chamsonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu. Ndipo ankagwira ntchito yao yotumikirayo potsata malamulo amene adaaŵapatsa.
Pamene anthu adati apereke kwa Mulungu khoma lozinga mzinda wa Yerusalemu, adaitana Alevi kuchokera konse kumene ankakhala, kuti abwere ku Yerusalemu kudzachita mwambo wopereka khomalo mokondwera, mothokoza ndiponso poimba pamodzi ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi mapangwe.
Alevi anali aŵa: Yesuwa, Binuyi, Kadimiyele, Serebiya ndi Yuda. Panalinso Mataniya, amene ankayang'anira za maimbidwe a nyimbo zachiyamiko, pamodzi ndi anzakewo.
Pa nthaŵi ya Davide ndi Asafu, panali mtsogoleri wa anthu oimba nyimbo, ndiponso panali nyimbo zotamanda ndi zothokoza Mulungu.
anthu 4,000 adzakhale alonda apakhomo, ndipo anthu 4,000 enawo azidzatamanda Chauta ndi zipangizo zoimbira zimene ndazipereka kuti zikhale zotamandira Chauta.”
Iwo aja atayamba kuimba ndi kutamanda, Chauta adaŵatchera msampha Aamoni, Amowabu ndiponso anthu a ku phiri la Seiri, amene adaadzalimbana ndi anthu a ku Yuda, kotero kuti adaŵagonjetsa onse.
Pamenepo Hezekiya adati, “Tsopano inu mwadzipereka kuti mugwire ntchito ya Chauta. Idzani pafupi, mubwere nazo nsembe ndi zopereka zothokozera ku Nyumba ya Chauta.” Msonkhanowo udabwera nazo nsembe ndi zopereka zothokozera. Anthu onse amene anali ndi mtima waufulu adabwera ndi nsembe zopsereza.
Atayang'ana, adaona mfumu itaima pa nsanja yake pa khomo, atsogoleri ndi anthu oimba malipenga ali pafupi ndi mfumuyo. Anthu onse am'deralo ankakondwa, namaimba malipenga. Anthu oimba nyimbo ali ndi zipangizo zao zoimbira, ndiwo amene ankatsogolera chikondwererocho. Pamenepo Ataliyayo adang'amba zovala zake ndipo mofuula adati, “Akundiwukira! Akundiwukira!”
Ndidzayamika Chauta nthaŵi zonse, pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza. Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino. Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta. Ndani mwa inu amakhumba moyo ndi kulakalaka kuti akhale masiku ambiri, kuti asangalale ndi zinthu zabwino? Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa, pakamwa pako pasakambe zonyenga. Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola. Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu. Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa, anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano. Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima. Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse. Moyo wanga umanyadira Chauta. Anthu ozunzika amve ndipo akondwere. Chauta amasunga thupi la munthuyo, palibe fupa limene limasweka. Choipa chitsata mwini, anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa. Chauta amaombola moyo wa atumiki ake. Palibe wothaŵira kwa Iye amene adzalangidwe. Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta, tiyeni limodzi tiyamike dzina lake.
Ombani m'manja inu anthu a mitundu yonse. Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe. Paja Chauta Wopambanazonse, ndi woopsa, ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.
Ansembe adaimirira m'malo mwao, pamene Alevi ankatamanda Chauta poimba nyimbo zothokoza Chauta ndi zipangizo zimene Davide adapanga, pakuti chikondi cha Mulungu chimakhala mpaka muyaya. Anthu onseŵa ankatero nthaŵi zonse Davide akamapereka matamando kudzera mwa iwo. Poyang'anana ndi iwowo panali ansembe oliza malipenga. Ndipo Aisraele onse adaakhala chilili.
Chauta ndi wamkulu, ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera,
Koma wopereka mtima wake kwa Ine mothokoza, ndiye amene amandilemekeza. Woyenda m'njira zolungama, ndidzamuwonetsa chipulumutso changa.”
Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo. Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera.
Inu Mulungu, anthu azikutamandani ku Ziyoni, achitedi zimene adalumbira kwa Inu. Inu mumathirira kwambiri makwaŵa am'mizere, mumasalaza nthumbira zake, mumafeŵetsa nthaka ndi mvula, ndipo mumadalitsa mbeu. Pakutha pa chaka mumapereka zokolola zambiri mwa ubwino wanu, kulikonse kumene Inu mupita, kumapezeka dzinthu dzambiri. Ngakhale ku mabusa akuchipululu kumamera msipu wambiri, ndipo mapiri amadzazidwa ndi chimwemwe. Madambo adzaza ndi zoŵeta, zidikha zadzaza ndi dzinthu, zonsezo zikufuula ndi kuimbira limodzi mwachimwemwe. Inu amene mumamvera pemphero, anthu onse adzabwera kwa Inu,
Muimbireni Mulungu, imbani nyimbo zotamanda dzina lake. Kwezani nyimbo yotamanda Iye amene amayenda pa mitambo. Dzina lake ndi Chauta, musangalale pamaso pake.
Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.
Tikukuthokozani Inu Mulungu, ndithu tikukuthokozani. Tikutchula dzina lanu mopemphera ndipo tikulalika ntchito zanu zodabwitsa.
Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pa busa lanu, tidzakuthokozani mpaka muyaya, tidzakutamandani m'mibadwo yonse.
Ngodala anthu amene amakhala m'Nyumba mwanu, namaimba nyimbo zotamanda Inu nthaŵi zonse.
Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa. Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.” Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo. Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano! Imbirani Chauta, anthu a m'dziko lonse lapansi! Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu. Dziko lonse lidakhazikitsidwa molimba, silidzagwedezeka konse. Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.” Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere, nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo. Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam'menemo. Mitengo yam'nkhalango idzaimba mokondwa pamaso pa Chauta, pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, adzalamulira anthu a mitundu yonse moona. Imbirani Chauta, tamandani dzina lake! Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Inu ndi anthu a Chauta, kondwerani mwa iye, ndipo mumthokoze potchula dzina lake loyera.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, popeza kuti wachita zodabwitsa. Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa. Chauta waonetsa kuti Iye wapambana pa nkhondo, waulula pamaso pa anthu a mitundu yonse kuti Iye ndi wolungama. Wakumbukira chikondi chake chosasinthika ndi kukhulupirika kwake pa fuko la Israele. Anthu a ku mathero a dziko lonse lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse. Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa. Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake. Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake! Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife. Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi. Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo. Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake. Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake. Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.
Ndidzaimbira Chauta moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Chauta, nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu. Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe kuti likhale chipangano chokhazikika mu Israele mpaka muyaya. Adati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani kuti likhale choloŵa chako chokhalira iweyo.” Pamene anali anthu oŵerengeka, anthu osatchuka, ongokhala nawo m'dzikomo, omangoyendayenda kuchokera ku mtundu wina wa anthu kupita ku mtundu wina, kuchokera ku ufumu wina kupita ku ufumu wina, sadalole ndi mmodzi yemwe kuti aŵapsinje, adalanga mafumu ena chifukwa cha anthu akewo. Adati, “Musakhudze odzozedwa anga, musaŵachite choipa aneneri anga.” Pamene Chauta adadzetsa njala m'dziko la Kanani ndi kuwononga chakudya chonse, Iye anali atatuma munthu patsogolo pa anthu ake, Yosefe uja amene adagulitsidwa ngati kapolo. Mapazi ake adapwetekedwa ndi matangadza, khosi lake lidavekedwa unyolo, mpaka zimene Yosefe adanena zija zidachitikadi. Mau a Chauta adatsimikiza kuti iye sadalakwe. Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda, lalikani za ntchito zake zodabwitsa. Motero mfumu idalamula kuti akammasule, wolamulira mitundu ya anthuyo adammasuladi. Adamsandutsa mbuye wa nyumba yake, ndi wolamulira chuma chake chonse, kuti azilangiza nduna zake monga momwe ankafunira, ndi kuŵaphunzitsa nzeru akuluakulu. Tsono Israele adafika ku Ejipito. Yakobeyo adakhala nawo m'dziko la Hamu. Chauta adalola kuti anthu ake achuluke, naŵasandutsa amphamvu kupambana adani ao. Adaumitsa mitima ya adaniwo kuti adane ndi anthu ake ndi kuŵapanganirana zaupandu. Kenaka adatuma Mose mtumiki wake pamodzi ndi Aroni amene adamsankha. Iwo adachita zizindikiro m'dzina lake pakati pa anthuwo, adachita ntchito zozizwitsa m'dziko la Hamu. Chauta adatumiza mdima, nasandutsa dzikolo kuti likhale lamdima. Komabe anthuwo adakaniratu mau a Chauta. Iye adasandutsa madzi ao kukhala magazi, ndipo nsomba zao zidafa. Munyadire dzina lake loyera. Ikondwe mitima ya anthu amene amapembedza Chauta.
Tamandani Chauta. Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Athokoze Chauta chifukwa cha chikondi chake chosasinthika, chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa kwa anthu onse. Chauta amapha ludzu la munthu womva ludzu, amamudyetsa zinthu zabwino munthu womva njala.
Tamandani Chauta. Ndidzathokoza Chauta ndi mtima wanga wonse pa msonkhano wa anthu olungama mtima.
Tamandani Chauta! Mtamandeni, inu atumiki ake, tamandani dzina la Chauta. Yamikani Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya. Dzina la Chauta litamandike kuyambira ku matulukiro a dzuŵa mpaka ku maloŵero ake.
Akufa satamanda Chauta otsikira ku dziko lachete satamanda Chauta. Koma ife tidzatamanda Chauta kuyambira tsopano mpaka muyaya. Tamandani Chauta!
Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, ndipo chikondi chake nchamuyaya. Adani a mitundu yonse adandizinga, koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Adandizinga, inde adandizinga pa mbali zonse, koma ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Adandizinga ngati njuchi, koma adatha msanga ngati moto wapaminga. Ndidaŵaononga ndi mphamvu za dzina la Chauta. Adandikankha kwambiri, kotero kuti ndinali pafupi kugwa, koma Chauta adandithandiza. Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga. Ndiye mpulumutsi wanga. Mverani nyimbo m'mahema mwa anthu a Mulungu, nyimbo zokondwerera kupambana, zakuti, “Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu, dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.” Sindidzafa, ndidzakhala moyo, ndipo ndidzalalika ntchito za Chauta. Chauta wandilanga koopsa, koma sadandisiye kuti ndife. Tsekulireni zipata za Nyumba ya Mulungu, kuti ndifike ku malo ake achilungamo, ndikathokoze Chauta. Aisraele anene kuti, “Chikondi chake nchamuyaya.”
Tamandani Chauta. Tamandani dzina la Chauta, Perekani matamando, inu atumiki a Chauta, Ndiye amene adaononga mitundu yambiri ya anthu, ndi kupha mafumu amphamvu aja, Sihoni, mfumu ya Aamori, ndi Ogi, mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi maufumu onse a ku Kanani. Adapereka dziko lao kuti likhale choloŵa, choloŵa cha Aisraele, anthu ake. Dzina lanu, Inu Chauta, nlamuyaya, kutchuka kwanu ndi kwa pa mibadwo yonse. Pakuti Chauta adzaweruza anthu ake kuti alibe mlandu, adzachitira chifundo atumiki ake. Mafano a mitundu ina ya anthu ndi asiliva ndi agolide chabe, ndi opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula, maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva, ndipo alibe mpweya m'kamwa mwao. Anthu amene amapanga mafanowo afanefane nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira. Inu a m'banja la Israele, tamandani Chauta! Inu a m'banja la Aroni, tamandani Chauta! inu amene mumatumikira m'Nyumba ya Chauta, m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu! Inu a banja la Levi, tamandani Chauta! Inu amene mumaopa Chauta, tamandani Chauta! Atamandike ku Ziyoni Chauta, amene amakhala ku Yerusalemu! Tamandani Chauta! Tamandani Chauta, pakuti ngwabwino. Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, pakuti nlokoma kwambiri.
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse. Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu. Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse.
Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu. Anthu amenewo adzakhala pamaso panu.
Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga, ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse mpaka muyaya. Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta, anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani. Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu, adzasimba za mphamvu zanu, kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu. Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ulamuliro wanu ndi wa pa mibadwo yonse. Chauta ndi wokhulupirika pa mau ake onse, ndi wokoma mtima pa zochita zake zonse. Chauta amachirikiza onse ogwa m'mavuto, amakweza onse otsitsidwa. Maso onse amayang'anira kwa Inu, ndipo mumaŵapatsa chakudya pa nthaŵi yake. Mumafumbatula dzanja lanu, ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake. Chauta ndi wolungama m'zochita zake zonse, ndi wachifundo pa zonse zimene achita. Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa. Ndidzakuthokozani tsiku ndi tsiku, ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya. Onse amene amakonda Chauta, amaŵasunga, koma Chauta adzaononga oipa onse. Pakamwa panga padzayamika Chauta, zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka muyaya. Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
Tamandani Chauta! Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse. Tamandani Chauta! Ndidzatamanda Chauta pa moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Tamandani Chauta! Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu, nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera.
Tamandani Chauta! Tamandani Chauta inu okhala kumwamba, mtamandeni inu okhala mu mlengalenga! Inu nyama zakutchire ndi zoŵeta zonse, inu zinthu zokwaŵa ndi mbalame zouluka! Inu mafumu a pa dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akuluakulu ndi olamulira dziko lapansi! Inu anyamata pamodzi ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe! Onsewo atamande dzina la Chauta, pakuti dzina lake lokha nlolemekezeka, ulemerero wake ndi woposa, pansi pano nkumwamba komwe. Chauta wakweza anthu ake poŵapatsa mphamvu. Walemekeza anthu ake onse oyera mtima, Aisraele amene Iye amaŵakonda. Tamandani Chauta! Mtamandeni inu angelo ake onse, mtamandeni inu magulu a ankhondo ake onse! Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi, mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala! Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo! Zonsezo zitamande dzina la Chauta! Paja Iye adaalamula, izo nkulengedwa.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima. Aisraele asangalale ndi Mlengi wao. Anthu a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yao. Atamande dzina lake povina, amuimbire nyimbo yokoma ndi ng'oma ndi pangwe.
Tamandani Chauta! Tamandani Mulungu m'malo ake opatulika. Mtamandeni ku thambo lake lamphamvu. Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu, mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana. Mtamandeni pomuimbira lipenga, mtamandeni ndi gitara ndi zeze. Mtamandeni poimba ng'oma ndi povina, mtamandeni ndi zipangizo zansambo ndi mngoli. Mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira, mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira kwambiri. Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Chauta. Tamandani Chauta!
Tsiku limenelo aliyense mwa inu adzati: “Ndikukuthokozani Inu Chauta, pakuti ngakhale mudaandipsera mtima, mkwiyo wanu udaleka, ndipo mwandilimbitsa mtima. “Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
nafunsa Yesu kuti, “Kodi mukumva zimene akunenazi?” Yesu adaŵayankha kuti, “Inde. Kani simudaŵerenge konse mau a Mulungu aja akuti, ‘Mudaphunzitsa ana ndi makanda omwe kukutamandani kotheratu?’ ”
Pamenepo Maria adati, “Mtima wanga ukutamanda Ambuye, ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga,
Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona. Adati, “Ndi yodala Mfumu imene ilikudza m'dzina la Ambuye. Mtendere Kumwamba, ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.” Apo Afarisi ena amene adaali m'khamumo adauza Yesu kuti, “Aphunzitsi, auzeni ophunzira anuŵa aleke zimenezi.” Tsono adathamangira kutsogolo, nakakwera mu mkuyu kuti amuwone, chifukwa Yesu ankayenera kudzera pamenepo. Iye adati, “Ndikutitu iwoŵa akangokhala chete, ifuula ndi miyalayi.”
Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera.
Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.”
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu. Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera. Musanyozere kumachita zachifundo ndi kumathandizana, chifukwa nsembe zotere zimakondweretsa Mulungu.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
“Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu, ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu, pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse. Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.”
Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero kumwamba kudamveka mau okweza. Mauwo adati, “Tsopano mphamvu zolamulira dziko lapansi zili m'manja mwa Ambuye athu ndi mwa Wodzozedwa wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”
Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati, “Ambuye, Mulungu Mphambe, ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa. Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona. Ambuye, ndani angapande kukuwopani ndi kutamanda dzina lanu? Paja ndinu nokha oyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani, popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”
Pambuyo pake ndidamva ngati mau amphamvu a chinamtindi cha anthu Kumwamba. Mauwo ankati, “Aleluya! Chipulumutso, ulemerero ndi mphamvu ndi zake za Mulungu wathu, Apo ndidadzigwetsa ku mapazi ake kuti ndimpembedze. Koma iye adandiwuza kuti, “Zimenezo iyai. Ndine mtumiki chabe, ngati iwe wemwe, ndiponso ngati abale ako amene amachitira Yesu umboni. Iwe pembedza Mulungu.” Pajatu kuchitira Yesu umboni ndiye thima la uneneri. Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama. Maso ake anali psuu ngati malaŵi a moto, ndipo pamutu pake panali zisoti zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lolidziŵa iye yekha, osati wina aliyense. Chovala chake chinali choviika m'magazi, ndipo ankatchedwa, “Mau a Mulungu.” Magulu a ankhondo a Kumwamba ankamutsatira atakwera akavalo oyera, ndipo iwowo atavala zabafuta, zoyera ndi zangwiro. M'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa lotulukira kunja, loti adzalangire mitundu ya anthu. Adzaŵalamulira ndi ndodo yachitsulo, ndipo m'chopondera mphesa adzaponda mphesa za vinyo wa mkwiyo waukali wa Mulungu Mphambe. Pa mkanjo wake, ndi pantchafu pake padaalembedwa dzina loti, “Mfumu ya mafumu onse, ndi Mbuye wa ambuye onse.” Kenaka ndidaona mngelo mmodzi ataimirira pa dzuŵa. Adafuula mokweza mau, nauza mbalame zonse zouluka mu mlengalenga kuti, “Dzasonkhaneni ku mgonero waukulu wa Mulungu. Bwerani, mudzadye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi wa okwerapo, mnofu wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, ang'onoang'ono ndi akuluakulu.” Pambuyo pake ndidaona chilombo chija pamodzi ndi mafumu a pa dziko lapansi, ndi magulu ao ankhondo. Adaasonkhana kuti amenyane nkhondo ndi wokwera pa kavalo uja, pamodzi ndi gulu lake la ankhondo. pakuti chiweruzo chake chilichonse nchoona ndi cholungama. Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja amene ankaipitsa dziko lapansi ndi chigololo chake, wamlanga chifukwa cha kupha atumiki ake.” Chilombocho chidagwidwa pamodzi ndi mneneri wonama uja amene anali atachita zozizwitsa pamaso pake. Zozizwitsazo, iye anali atanyenga nazo anthu amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, ndiponso anthu amene anali atapembedza fano lake lija. Chilombo chija ndi mneneri wonama uja, onse aŵiri adaŵaponya m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala yoyaka ya sulufure. Ena onse adaphedwa ndi lupanga lija lotuluka m'kamwa mwa wokwera pa kavalo uja. Ndipo mbalame zonse zidadya ndi kukhuta mnofu wa anthuwo. Kachiŵiri mau aja adanenanso kuti, “Aleluya! Utsi wa mzindawo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Tsono ndidzakuthokozani pa msonkhano waukulu, ndidzakutamandani pa chinamtindi cha anthu anu.
Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Ndiyenera kuchita zimene ndidalumbira kwa Inu Mulungu. Ndidzapereka kwa Inu nsembe zothokozera. Pakuti mwalanditsa moyo wanga ku imfa. Inde mwandichirikiza mapazi kuti ndisagwe, kuti motero ndiziyenda pamaso pa Mulungu m'kuŵala kwa amoyo.
Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi. Inu Mulungu, mwatiyesa, mwatiyeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Inu mudatiloŵetsa mu ukonde wa adani, mudatisenzetsa katundu wolemera pamsana pathu. Inu mudalola kuti adani atikwere pa mutu, tidaloŵa m'moto ndiponso m'madzi, komabe Inu mwatifikitsa ku malo opulumukirako. Ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzachitadi zimene ndidazilumbira kwa Inu, zimene ndidalankhula ndi pakamwa panga, ndiponso zimene ndidalonjeza pamene ndinali pa mavuto. Ndidzapereka kwa Inu nsembe zopsereza za nyama zonenepa, utsi wa nsembe za nkhosa zamphongo udzafika kwa Inu. Ndidzaperekanso ngati nsembe ng'ombe zamphongo ndi mbuzi. Bwerani mudzamve, inu nonse amene opembedza Mulungu, ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira. Ndidafuula kwa Iye, ndipo ndidamtamanda ndi pakamwa panga. Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera. Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa. Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu.
Inu mwakhala wondichirikiza kuyambira pa nthaŵi imene ndidabadwa. Inu ndinu amene mudanditulutsa m'mimba mwa mai wanga. Ndimatamanda Inu nthaŵi zonse. Ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri, koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu. Pakamwa panga pakutamanda Inu, pakulalika ulemerero wanu tsiku lonse.
Apereke nsembe zothokozera, ndi kulalika ntchito za Chauta, poimba nyimbo zachimwemwe.
Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta, anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani. Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu, adzasimba za mphamvu zanu, kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu.
Ndidzatamanda Chauta pa moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni. Paja amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako. Amadalitsa anthu amene ali mwa iwe.
“Chauta wandipulumutsa, ndipo tidzamtamanda poimba ndi azeze m'Nyumba mwa Chauta pa moyo wathu wonse.”
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”
Atate anga amalemekezedwa pamene mubereka zipatso zambiri, ndipo pakutero mumaonetsa kuti ndinu ophunzira anga enieni.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire? Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, “Ndani amadziŵa maganizo a Chauta, ndani angamupatse malangizo? Ndani adaayamba waperekapo kanthu kwa Mulungu, kuti Mulunguyo amubwezereko kanthu?” Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Ndipo timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuŵala.
ponena mau akuti, “Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzakutamandani pa msonkhano wa anthu anu.”
Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.
Pakamwa panga padzakutamandani, chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu. Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama.
Mafumu onse a m'dziko adzakutamandani, Inu Chauta, chifukwa amva mau a pakamwa panu. Adzaimba nyimbo zotamanda njira za Chauta, pakuti ulemerero wa Chauta ndi waukulu.
Pakamwa panga padzayamika Chauta, zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka muyaya.
“Atamandike Ambuye, Mulungu wa Aisraele, chifukwa adadzayendera anthu ao, ndi kudzaŵaombola. Adautsa wina, wa fuko la mtumiki wake Davide, kuti akhale Mpulumutsi wathu wamphamvu.
Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona.