Mwina mukumva nkhani za atsogoleri amphamvu ndi odzozedwa m'Baibulo, koma chochititsa chidwi kwambiri ndi mtima wawo wowongoka komanso wodzichepetsa. Mulungu sakuona kuchuluka kwa ntchito zomwe timachita m'dzina lake, koma mtima wathu womwe timachitira zimenezo. Masiku ano, Mulungu akufuna atsogoleri okhulupirika, osunga mawu ake, ndi owopa kumupsetsa mtima chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife.
Ngakhale Mulungu ankadziwa kuti tidzalakwitsa, Iye anatipatsa madalitso chifukwa cha ntchito zathu ndi kumvera kwathu. Anatisankha chifukwa cha mitima yathu yoyera. Mu mipingo yathu ndi m'nyumba mwathu, muli atsogoleri achikhristu ambiri oyenera kulimbikitsidwa ndi kupempherera.
Apa pansi pali mavesi a m'Baibulo oti muwalemekeze chifukwa cha utumiki wawo wabwino. [mwina apa ndi pomati muyike mavesiwo]
Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m'mapiri, akubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu.”
Chauta akudalitseni, ndipo akusungeni. Chauta akuyang'aneni mwachikondi ndipo akukomereni mtima. Chauta akuyang'aneni mwachifundo, ndipo akupatseni mtendere.”
“Inu Chauta, mwini mpweya wopatsa moyo anthu onse, musankhe munthu kuti aziyang'anira mpingowu. Munthuyo aziŵatsogolera pa nkhondo ndi kuŵalamula, kuti mpingo wanu usamakhale ngati nkhosa zopanda mbusa.”
Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu.
Palibe munthu amadzitengera yekha ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma amachita kuitanidwa ndi Mulungu, monga momwe adaaitanidwira Aroni.
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
Sankhani anthu ena anzeru, omvetsa ndi odziŵa zinthu bwino, pakati pa mafuko anu, ndipo ine ndidzaŵaika kuti akhale atsogoleri pakati panu.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.
Nchifukwa chake abale, pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi aŵiri, a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndiponso ndi nzeru. Tidzapatsa iwowo ntchitoyi.
Komanso sankhulani amuna anzeru, ndipo muŵaike kuti akhale atsogoleri a anthu, motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe. Ayenera kukhala anthu oopa Mulungu, okhulupirika, ndiponso osakopeka ndi ziphuphu.
Mu dziko mukakhala chilungamo, anthu amakondwa, koma chilungamo chikasoŵa, anthu amadandaula.
Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.
Munthuyo ataloŵa mu ufumu wakewo, adzalembe m'buku lakelake malamulo a Mulunguŵa ochokera mu buku la malamulo limene lili m'manja mwa ansembe Achilevi. Buku limeneli adzalisunge ndipo azidzaŵerengamo pa moyo wake wonse, kuti adzaphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wake, pakutsata mokhulupirika zonse zolembedwa m'bukumo. Mwina padzapezeka kuti mu mzinda wina umene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani, muli munthu wina wamwamuna kapena wamkazi amene wachimwira Chauta, Mulungu wanu, Zimenezi zidzamthandiza kudziŵa kuti iyeyo saposa Aisraele anzake, ndiponso kuti sayenera kukhala wonyozera malamulo a Chauta mpang'ono pomwe. Motero iyeyo, pamodzi ndi zidzukulu zake zomwe, adzalamulira nthaŵi yaitali mu Israele.
Zimene amachita munthu wopusa mwiniwakeyo amaziyesa zolungama, koma munthu wanzeru amamvetsera malangizo a ena.
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu, chilungamo ndiye chimalimbitsa ufumu wake.
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike. Munthu sati akayatsa nyale, nkuivundikira ndi mbiya. Koma amaiika pa malo oonekera, ndipo imaunikira anthu onse amene ali m'nyumbamo. Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, akhale kapolo wanu. Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Pakati panupa wamkulu akhale mtumiki wanu. Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”
Koma pakati pa inu zisamatero ai. Aliyense wofuna kukhala mkulu pakati panu, azikhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense wofuna kukhala mtsogoleri pakati panu, azikhala kapolo wa onse. Chitani monga m'mene adachitira Mwana wa Munthu: adabwera osati kuti ena adzamtumikire ai, koma kuti Iyeyo adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake kuti aombole anthu ochuluka.”
Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake.
Yesu adati, “Tsono kapitao wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake? Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi.
Yesu atatsuka mapazi a ophunzira ake, adavalanso mwinjiro wake nakakhalanso podyera paja. Kenaka adaŵafunsa kuti, “Kodi mwazimvetsa zimene ndakuchitiranizi? Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene. Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi. Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu.
Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.
Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana.
Muzitiwona ngati antchito a Khristu, ngati akapitao osamala zinsinsi za Mulungu. Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu. Ife ndife ofooka, koma inu ndinu amphamvu. Inu mumalandira ulemu, koma ife timanyozedwa. Mpaka tsopano lino timamva njala ndi ludzu, ndipo ndife ausiŵa. Anthu akutimenya, ndipo tilibe pokhala penipeni. Tikugwira ntchito kolimba ndi manja athu kuti tidzisunge. Anthu akamatichita chipongwe, timapempha kuti Mulungu aŵadalitse. Anthu akamatizunza, timangopirira. Anthu akamatilalatira, timangoŵayankha moleza. Tasanduka onyozeka, ngati zinyatsi za dziko lapansi, ndipo mpaka tsopano anthu onse akutiyesa zinyalala. Ndikukulemberani zonsezi, osati kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni, chifukwa ndinu ana anga okondedwa. Ngakhale mutakhala nawo aphunzitsi ambirimbiri m'moyo wanu wachikhristu, simukhala ndi atate ambiri ai. Pajatu m'moyo wanu wachikhristu ine ndidachita ngati kukubalani pakukulalikirani Uthenga Wabwino. Ndikukupemphani tsono kuti muzinditsanzira. Nchifukwa chake ndakutumizirani Timoteo, mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iyeyu adzakukumbutsani za mayendedwe anga achikhristu, amene sasiyana ndi zimene ndimaphunzitsa ponseponse m'mipingo yonse. Ena mwayamba kudzitukumula, monga ngati sindidzabwerako kwanu. Koma Ambuye akalola, ndidzabwera kwanuko posachedwa. Pamenepo ndidzadziŵa zimene odzitukumulawo angathe kuchita, osati zimene amangonena chabe. Chofunika chachikulu pa akapitao otere nchakuti akhale okhulupirika.
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.
Kodi ponena zimenezi ndiye kuti ndikufuna kuti anthu andivomereze? Iyai, koma kuti andivomereze ndi Mulungu. Kodi ndikuyesa kukondweretsa anthu? Ndikadayesabe kukondweretsa anthu, si bwenzi ndilinso mtumiki wa Khristu.
Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.
Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino, osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Abale, tikukupemphani kuti muziŵalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene Ambuye adaŵaika kuti azikutsogolerani ndi kumakulangizani. Mwa chikondi muziŵachitira ulemu kwambiri chifukwa cha ntchito yao. Muzikhalitsana ndi mtendere pakati panu.
Aŵa ndi mau otsimikizika ndithu akuti, “Ngati munthu afuna ntchito ya kuyang'anira Mpingo, akukhumba ntchito yaulemu.” Iwonso ayambe ayesedwa, ndipo pambuyo pake, ngati alibe chokayikitsa, ndiye asenze udindo wa atumiki. Momwemonso akazi akhale ochita zachiukulu, osasinjirira, odzigwira, ndi okhulupirika pa zonse. Atumiki a mpingo akhale a mkazi mmodzi yekha. Akhale olera ana ao bwino, oyendetsanso bwino mabanja ao. Paja anthu ogwira bwino ntchito ya utumiki, amadzitengera mbiri yabwino, ndipo amalimba mtima kwenikweni pakuika chikhulupiriro chao mwa Khristu Yesu. Pamene ndikukulembera zimenezi, ndikuyembekeza kudzafika kwanuko posachedwa. Koma zina zikandichedwetsa, zimene ndanenazi zidzakudziŵitsa za m'mene anthu ayenera kukhalira m'banja la Mulungu, limene lili Mpingo wa Mulungu wamoyo, ndi mzati wochirikiza choona. Ndithudi, chinsinsi cha chipembedzo chathu nchachikulu: “Iye uja adaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu Woyera adamchitira umboni kuti ndi wolungama, angelo adamuwona, adalalikidwa pakati pa anthu a mitundu yonse, anthu a pa dziko lonse lapansi adamkhulupirira, Iyeyo adatengedwa kunka kumwamba mu ulemerero.” Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa. Asakhale chidakwa, asakhale wandeu, koma wofatsa, wosakangana ndi anthu, ndi wosakonda ndalama. Akhale wodziŵa kuyendetsa bwino banja lake, ndi kulera bwino ana ake, kuti akhale omvera ndi aulemu kwenikweni. Ngati munthu sadziŵa kuyendetsa bwino banja lake, nanga angasunge bwanji Mpingo wa Mulungu? Asakhale munthu wolandiridwa mu mpingo chatsopano, kuwopa kuti angadzitukumule nkulangidwa monga momwe Satana adalangidwira. Kuwonjezera pamenepo, akhale munthu woti ndi akunja omwe amamlemekeza, mwinamwina nkudzayamba kunyozedwa nagwa mu msampha wa Satana.
Akulu a mpingo otsogolera mpingo bwino, akhale oyenera kuŵalemekeza moŵirikiza, makamaka amene amagwira ntchito yolalika mau a Mulungu ndiponso yophunzitsa.
Mau amene udamva kwa ine pamaso pa mboni zambiri, uŵasungitse anthu okhulupirika amene adzathe kuŵaphunzitsanso kwa ena.
Muzikumbukira atsogoleri anu amene ankakulalikirani mau a Mulungu. Muzilingalira za moyo wao ndi m'mene adafera, ndipo muzitsanzira chikhulupiriro chao.
Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.
Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse.
Tsopano ndili nawo mau akulu a mpingo amene ali pakati panu, ine mkulu mnzao. Ndinenso mboni ya zoŵaŵa za Khristu, ndipo ndikuyembekeza kudzalandira nao ulemerero umene uti udzaoneke. Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha. Iye ndiye mwini mphamvu mpaka muyaya. Amen. Kalatayi ndalembetsa Silivano mwachidule. Ndimamuwona kuti ndi mbale wokhulupirika. Ndafuna kukulimbitsani mtima, ndi kuchita umboni wakuti kukoma mtima kwenikweni kwa Mulungu nkumeneku. Chifukwa cha kukoma mtimako, limbikani. Anzanu a mu mpingo wa ku Babiloni akuti moni. Marko, mwana wanga, nayenso akuti moni. Mupatsane moni mwachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli ake a Khristu. Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo. Ndipo pamene Mbusa wamkulu adzaonekera, mudzalandira mphotho yosafota yaulemerero.
Phunzitseni, kuti ndizichita zofuna Inu, pakuti ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Munthu wodzipatula mwa anzake amangotsata zomkomera iyeyo, amangofuna kutsutsana ndi zimene onse akudziŵa kuti ndi zoona.
Pafunika malangizo abwino kuti ukamenye nkhondo. Aphungu akachuluka, kupambana kuli pomwepo.
Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa.
Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.
“Nayu mtumiki wanga amene ndamsankha. Ndimamkonda, ndipo mtima wanga umasangalala naye kwambiri. Ndidzaika Mzimu wanga mwa iyeyo, ndipo adzalalika za chilungamo kwa anthu a mitundu ina.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Nchifukwa chake abale, pakati panupa sankhanipo amuna asanu ndi aŵiri, a mbiri yabwino, odzazidwa ndi Mzimu Woyera ndiponso ndi nzeru. Tidzapatsa iwowo ntchitoyi. Koma ife tidzadzipereka ku ntchito ya kupemphera ndi kulalika mau a Mulungu.”
Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao.
Ndikulakalakadi kukuwonani, kuti ndikugaŵireni mphatso zina zauzimu, kuti motero ndikulimbikitseni. Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa.
Popeza kuti mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandiitana kuti ndikhale mtumwi, ndikukuuzani inu nonse kuti musadziyese anzeru koposa m'mene muliri. Makamaka maganizo anu akhale odzichepetsa, molingana ndi kukula kwa chikhulupiriro chimene Mulungu wapatsa aliyense mwa inu.
Kodi Apolo nchiyani? Paulonso nchiyani? Ndi atumiki chabe a Mulungu, amene adakufikitsani ku chikhulupiriro. Aliyense adangogwira ntchito imene Mulungu adampatsa. Ineyo ndidabzala mbeu, Apolo nkuzithirira, koma amene adazimeretsa ndi Mulungu. Motero wobzala kapenanso wothirira sali kanthu, koma Mulungu yekha amene amameretsa, ndiye ali kanthu. Tsono wobzala sasiyana ndi wothirira, ndipo aliyense adzalandira mphotho yake molingana ndi ntchito imene adaigwira. Komabe ife ndife okhaokha ogwira ntchito ya Mulungu, inuyo ndinu munda wa Mulungu, ndinunso nyumba ya Mulungu.
Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo. Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.
Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.
Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu. Ndi cholinga chimenechi ndikugwiradi ntchito kwambiri ndi mphamvu ya Khristu imene ikugwira ntchito kolimba mwa ine.
Koma tidakhala ofatsa pakati panu ngati mai wosamalira ana ake. Tinkakukondani, ndipo chifukwa cha kukulakalakani kwambiri, tidatsimikiza zogaŵana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso ngakhale moyo wathu womwe.
Iwe Timoteo, mwana wanga, ndikukupatsa malangizo ameneŵa molingana ndi zimene aneneri adaanenapo kale za iwe. Mau amenewo akuthandize kumenya nkhondo yabwino,
Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima. Mpaka pamene ndidzabwere, uchite khama kuŵerengera anthu mau a Mulungu, kuŵalalikira ndi kuŵaphunzitsa. Usanyozere mphatso yaulere ija ili mwa iweyi, imene udailandira kudzera m'mau otchulidwa m'dzina la Mulungu, pamene gulu la akulu a Mpingo lidaakusanjika manja. Ntchito zimenezi uzizichita mosamala ndi modzipereka, kuti anthu onse aone kuti moyo wako wautumiki ukukulirakulira. Udziyang'anire bwino wekha, ndi kusamala zimene umaphunzitsa. Ulimbikire kutero, chifukwa pakuchita zimenezi udzadzipulumutsa iwe wemwe, ndiponso anthu amene amamva mau ako.
Ndidakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene zinali zisanalongosokebe, ndi kuti uike akulu a mpingo mu mzinda uliwonse, monga momwe ndidakulamulira. Mkulu wa mpingo akhale munthu wosapalamula konse, ndipo akhale wa mkazi mmodzi yekha. Ana ake akhalenso okhulupirira Khristu, opanda mbiri yoti ngosakaza kapena yoti ngosaweruzika. Woyang'anira mpingo azikhala wosapalamula konse, chifukwa ali ngati kapitao m'banja la Mulungu. Asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena chidakwa, kapena wandeu, kapenanso wokonda kudya phindu la ndalama. Akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziŵa kudzilamula, wolungama, woyera mtima, ndiponso wodzigwira. Asunge mogwiritsa mau okhulupirika, amene ali ogwirizana ndi zimene tidaphunzitsidwa. Pakutero adzatha kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona, ndiponso kugonjetsa otsutsana nacho.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira.
Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye. Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja.
Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Phunzitseni njira zanu, Inu Chauta, kuti ndiziyenda m'zoona zanu. Mundipatse mtima wosagaŵikana, kuti ndiziwopa dzina lanu.
Kodi amene amakonzekera zoipa sachimwa? Koma amene amakonzekera zabwino anthu amaŵaonetsa chifundo ndi kukhulupirika.
Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona. Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”
Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Yesu adauza anthu 72 aja kuti, “Wokumverani inu, akumvera Ine amene. Wokukanani inu akukana Ine amene. Ndipo wondikana Ine, akukananso Atate amene adandituma.”
Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu. Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu. Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.
Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
Motero polalika sitidzilalika tokha, koma timalalika Yesu Khristu, kuti ndiye Ambuye. Ife ndife atumiki anu chabe chifukwa cha Yesuyo.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Mayendedwe anu pakati pa anthu akunja azikhala anzeru, ndipo muzichita changu, osataya nthaŵi pachabe.
Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu.
Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa. Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.