Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


119 Mau a Mulungu Okhudza Aphunzitsi

119 Mau a Mulungu Okhudza Aphunzitsi

Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, aphunzitsi ndi ofunika kwambiri pa moyo wathu wauzimu. Amatipatsa njira yotsatira m'tsogolo, akutiphunzitsa makhalidwe abwino amene amatipangitsa kukhala osiyana ndi ena. Mulungu ndiye amawasankha kuti atithandize kupeza Khristu ndikutitsogolera m'chipembedzo komanso m'moyo wathu watsiku ndi tsiku.

Ngati muli ndi aphunzitsi otere, tiyeni tiwalemekeze mwa kuwapempherera nthawi zonse ndikuphunzira kwa iwo modzichepetsa. Tiyenera kuzindikira nthawi yomwe amatipatsa ndikuthokoza chifukwa cha zimene tikuphunzira kwa iwo. Kumbukirani, Mulungu ndiye wawasankha.

Zikomo kwambiri chifukwa cha nthawi yanu. Mulungu akudalitseni.




1 Akorinto 12:29

Kodi onse ndi atumwi? Kodi onse ndi aneneri? Kodi onse ndi aphunzitsi? Kodi onse ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:6

Munthu amene akuphunzira mau a Mulungu, agaŵireko mphunzitsi wake zabwino zonse zimene iye ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:24

Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:11

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:12

Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:20

mlangizi wa anthu opusa, ndiponso mphunzitsi wa anthu osadziŵa. Umatsimikiza kuti m'Malamulowo umapezamo nzeru zonse ndi zoona zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:3

Angathe kupezeka munthu wophunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosavomereza mau oona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso chogwirizana ndi moyo wolemekeza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:8

“Koma inuyo anthu asati azikutchulani aphunzitsi, pakuti muli ndi Mphunzitsi mmodzi yekha, ndipo nonsenu muli pa chibale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:13

Sindidamvere mau a aphunzitsi anga, sindidatchere khutu kwa alangizi anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:11

Mulungu adandiika kuti ndikhale mlaliki, mtumwi ndi mphunzitsi wa Uthenga Wabwino umenewu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:28

Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:16

Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:10

Anthu asatinso azikutchulani atsogoleri, popeza kuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi yekha, ndiye Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:7

Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:20

Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 18:20

Muyenera kuŵaphunzitsa mau ndi malamulo a Mulungu, ndi kuŵafotokozera m'mene azikhalira ndi m'mene azichitira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:6-7

Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:7

Iwo amafuna kukhala aphunzitsi a Malamulo a Mulungu, chonsecho samvetsa zimene iwo omwe akunena kapena zimene akufuna kutsimikiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:99

Ndili ndi nzeru za kumvetsa kupambana aphunzitsi anga onse, pakuti ndimasinkhasinkha za malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:14

Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:24

Paja wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo wantchito saposa mbuye wake ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:40

Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense pamene watsiriza maphunziro ake, adzafanafana ndi mphunzitsi wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:13

Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:4-5

Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:19

Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:8

Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:33-34

Chauta, phunzitseni njira zosungira malamulo anu, ndipo ndidzazitsata mpaka kumathero. Patseni nzeru kuti ndizisunga malamulo anu, ndiziŵatsata ndi mtima wanga wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:6-7

Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu. Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:11

Uzilamula ndi kuphunzitsa zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:1

Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:5

Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:7

Chachikulu pa nzeru ndi ichi: Kaya nchiyani chimene ungapate, peza nzeruyo, usalephere kupata khalidwe la kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:9

Wanzeru ukamlangiza, adzakhala wanzeru koposa. Munthu wochita chilungamo ukamuphunzitsa, adzadziŵa zambiri koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:14

Anzeru amakundika nzeru, koma kubwebwetuka kwa chitsiru kumadzetsa chiwonongeko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu, koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:22

Popanda uphungu zolinga zako zimalakwika, koma aphungu akachuluka, zolinga zako zimathekadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:15

Munthu wochenjera amafuna kuphunzirabe zambiri, amafunitsitsa kudziŵa bwino zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:20-21

Ngakhale Ambuye adzakuloŵetseni m'zovuta, adzakhala komweko kumakuphunzitsani, sadzabisala, mudzaŵaona. Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:24-27

“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba. Koma aliyense wongomva mau angaŵa, osaŵagwiritsa ntchito, ali ngati munthu wopusa amene adaamanga nyumba yake pa mchenga. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo, ndipo idagwa. Kugwa kwake kunali koopsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:24-25

Paja wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo wantchito saposa mbuye wake ai. Kumkwanira wophunzira kuti alingane ndi mphunzitsi wake, ndiponso wantchito kuti alingane ndi mbuye wake. Tsono ngati mwini banja anthu adamutcha Belezebulu, nanji a m'banja mwake, kodi sadzaŵatcha maina oipa koposa apa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 4:1-2

Yesu adayambanso kuphunzitsa pambali pa Nyanja ya Galileya. Anthu ochuluka adasonkhana kumeneko, kotero kuti Iye adaayenera kuloŵa m'chombo, nakhala pansi m'menemo panyanjapo. Anthu onse adaakhala pansi pa mtunda m'mphepete mwa nyanjayo, Pamene Yesu anali payekha, ophunzira khumi ndi aŵiri aja pamodzi ndi enanso amene ankakhala naye adadzamufunsa za mafanizowo. Iye adaŵayankha kuti, “Inuyo Mulungu adakuululirani zobisika zokhudza Ufumu wake. Koma enaŵa amene ali kunja, zonse amazimvera m'mafanizo chabe, kuti choncho, monga mau a Mulungu aja amanena, “ ‘Kuyang'ana ayang'ane ndithu, koma asapenye kanthu, ndipo kumva amve ndithu, koma asamvetse kanthu, kuti angatembenuke mtima, ndipo Mulungu angaŵakhululukire.’ ” Pambuyo pake Yesu adaŵafunsa kuti, “Monga simukulimvetsadi fanizo limeneli? Nanga mudzamvetsa bwanji fanizo lina lililonse? Wofesa mbeu uja ndi amene amafesa mau a Mulungu. Mbeu zogwera m'njira zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma nthaŵi yomweyo Satana amabwera, nkuchotsa mau aja amene adafesedwa m'mitima mwao. Mbeu zofesedwa pa nthaka yamiyala zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu, nthaŵi yomweyo nkuŵalandira ndi chimwemwe. Tsono popeza kuti mauwo sadazike mizu yozama, anthuwo amangolimbika kanthaŵi pang'ono chabe. Mwakuti pakangofika mavuto kapena masautso chifukwa cha mau aja, nthaŵi yomweyo anthuwo amabwerera m'mbuyo. Mbeu zofesedwa pa zitsamba za minga zija zikutanthauza anthu amene amaŵamva mau a Mulungu. Koma kutanganidwa ndi zapansipano, kukondetsa chuma ndi kukhumba zinthu zina zambiri kumaloŵapo nkufooketsa mau aja, motero sabereka konse zipatso. ndipo Yesu adayamba kuŵaphunzitsa zambiri m'mafanizo. Poŵaphunzitsa adati,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:21

Nthaŵi yomweyo Mzimu Woyera adadzaza Yesu ndi chimwemwe, mwakuti Yesuyo adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira. Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:13-15

Paja inu mumanditchula kuti, ‘Aphunzitsi’ ndiponso, ‘Ambuye.’ Apo mumalondola, pakuti ndine amene. Tsono ngati Ine Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu ndakusambitsani mapazi anu, ndiye kuti inunso muyenera kumasambitsana mapazi. Ndakupatsani chitsanzo, kuti inunso muzichita monga momwe Ine ndakuchitirani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:22

Motero Mose adaphunzira nzeru zonse za anthu a ku Ejipito, ndipo mau ake ndi ntchito zake zinali zamphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 18:26

Tsono adayamba kulankhula molimba mtima m'nyumba yamapemphero ya Ayuda. Koma pamene Prisila ndi Akwila anamumva, adamtenga namufotokezera Njira ya Mulungu molongosoka koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:21-23

Tsono iwe wophunzitsa ena, bwanji sukudziphunzitsa wekha? Iwe wolalika kuti, “Osamaba,” bwanji iwenso umaba? Nanga iwe wonena kuti, “Osamachita chigololo,” bwanji iwenso umachita chigololo? Iwe amene umanyansidwa ndi mafano, bwanji umaba za m'nyumba zopembedzeramo mafanowo? Iwe wonyadira Malamulo a Mulungu, bwanji umachititsa Mulungu manyazi pakuphwanya Malamulowo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:6-8

Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu. Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu. Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:1-2

Muzitiwona ngati antchito a Khristu, ngati akapitao osamala zinsinsi za Mulungu. Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu. Ife ndife ofooka, koma inu ndinu amphamvu. Inu mumalandira ulemu, koma ife timanyozedwa. Mpaka tsopano lino timamva njala ndi ludzu, ndipo ndife ausiŵa. Anthu akutimenya, ndipo tilibe pokhala penipeni. Tikugwira ntchito kolimba ndi manja athu kuti tidzisunge. Anthu akamatichita chipongwe, timapempha kuti Mulungu aŵadalitse. Anthu akamatizunza, timangopirira. Anthu akamatilalatira, timangoŵayankha moleza. Tasanduka onyozeka, ngati zinyatsi za dziko lapansi, ndipo mpaka tsopano anthu onse akutiyesa zinyalala. Ndikukulemberani zonsezi, osati kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni, chifukwa ndinu ana anga okondedwa. Ngakhale mutakhala nawo aphunzitsi ambirimbiri m'moyo wanu wachikhristu, simukhala ndi atate ambiri ai. Pajatu m'moyo wanu wachikhristu ine ndidachita ngati kukubalani pakukulalikirani Uthenga Wabwino. Ndikukupemphani tsono kuti muzinditsanzira. Nchifukwa chake ndakutumizirani Timoteo, mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iyeyu adzakukumbutsani za mayendedwe anga achikhristu, amene sasiyana ndi zimene ndimaphunzitsa ponseponse m'mipingo yonse. Ena mwayamba kudzitukumula, monga ngati sindidzabwerako kwanu. Koma Ambuye akalola, ndidzabwera kwanuko posachedwa. Pamenepo ndidzadziŵa zimene odzitukumulawo angathe kuchita, osati zimene amangonena chabe. Chofunika chachikulu pa akapitao otere nchakuti akhale okhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 3:5-6

Pakuti mwa ife tokha mulibe kanthu kamene kangatiganizitse kuti tingathe kuchita ntchitoyi patokha. Amene amatipatsa mphamvu ndi Mulungu kuti tithe kuichita. Ndiye amene adatipatsa mphamvu kuti tikhale otumikira chipangano chatsopano, osati mwa malamulo olembedwa, koma mwa Mzimu Woyera. Paja malamulo olembedwa amadzetsa imfa, koma Mzimu Woyera amapatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:11-12

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:4

Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:9

Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:28

Khristuyo ndiye amene timamlalika. Timachenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense ndi nzeru zonse zimene tili nazo. Pakuti tikufuna kusandutsa munthu aliyense kuti akhale wangwiro mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16

Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:7-8

Koma tidakhala ofatsa pakati panu ngati mai wosamalira ana ake. Tinkakukondani, ndipo chifukwa cha kukulakalakani kwambiri, tidatsimikiza zogaŵana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso ngakhale moyo wathu womwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:7

Nchifukwa chake ine adandiika kuti ndikhale mlaliki wake ndiponso mtumwi, wophunzitsa anthu a mitundu ina mau a chikhulupiriro choona. Sindikunamatu ai, ndikunena zoona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:2

Woyang'anira Mpingo azikhala munthu wopanda chokayikitsa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, akhale wodzigwira, wa maganizo anzeru, waulemu, wosamala bwino alendo, ndi wotha kuphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:11-12

Uzilamula ndi kuphunzitsa zimenezi. Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:13-14

Uŵagwiritse mau oona amene udamva kwa ine, kuti akhale chitsanzo choti uzitsata. Uzichita zimenezi mwa chikhulupiriro ndi mwa chikondi, zimene zili mwa Khristu Yesu. Usunge bwino zokoma zimene adakusungitsa pakutsata Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:2

Mau amene udamva kwa ine pamaso pa mboni zambiri, uŵasungitse anthu okhulupirika amene adzathe kuŵaphunzitsanso kwa ena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:9

Asunge mogwiritsa mau okhulupirika, amene ali ogwirizana ndi zimene tidaphunzitsidwa. Pakutero adzatha kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona, ndiponso kugonjetsa otsutsana nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:7

Pa zonse iwe wemwe ukhale chitsanzo cha ntchito zabwino. Zophunzitsa zako zikhale zoona, ndipo uziphunzitse mwaulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 5:12-14

Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba. Ngati wina aliyense angomwa mkaka, ndiye kuti akali mwana wakhanda, sangathe kutsata chiphunzitso chofotokoza za chilungamo. Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2-3

Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:7

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:13-18

Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:1

Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:10-11

Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri. Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:16

Kupata nzeru kumapambana kupata golide. Kumvetsa zinthu nkwabwino, kumapambana kukhala ndi siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:17

Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:37-40

Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe. Idatumanso antchito ena nkunena kuti, ‘Kaŵauzeni oitanidwa aja kuti chakudya chakonzeka. Ndapha ng'ombe ndi nyama zina zonenepa. Zonse zakonzeka, bwerani ku phwando laukwati.’ Malamulo onse a Mose ndiponso zonse zimene aneneri adaphunzitsa zagona pa malamulo aŵiriŵa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:3-4

Tsono popeza kuti inenso ndalondola mosamala kwambiri m'mene zonsezo zidachitikira kuyambira pa chiyambi, ndaganiza kuti nkwabwino kuti ndikulembereni zimenezo mwatsatanetsatane. Mngeloyo adamuuza kuti, “Musaope, Maria, Mulungu wakukomerani mtima. Mudzatenga pathupi, ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mudzamutcha dzina lake Yesu. “Adzakhala wamkulu, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu Wopambanazonse. Ambuye Mulungu adzamlonga ufumu wa kholo lake Davide, ndipo adzakhala Mfumu ya Aisraele mpaka muyaya. Ufumu wake sudzatha konse.” Koma Maria adafunsa mngeloyo kuti, “Zimenezi zidzachitika bwanji, popeza kuti sindidziŵa mwamuna?” Mngeloyo adayankha kuti, “Mzimu Woyera adzakutsikirani, ndipo mphamvu za Mulungu Wopambanazonse zidzakuphimbani. Nchifukwa chake Mwana wodzabadwayo adzakhala Woyera, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu. “Onani, mbale wanu uja Elizabeti, nayenso akuyembekezera mwana wamwamuna mu ukalamba wake. Anthu amati ngwosabala, komabe uno ndi mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. Pajatu palibe kanthu kosatheka ndi Mulungu.” Apo Maria adati, “Ndine mtumiki wa Ambuye; zindichitikire monga mwaneneramo.” Ndipo mngeloyo adamsiya. Patapita masiku oŵerengeka, Maria adanyamuka napita mofulumira ku dera lamapiri, ku mudzi wina wa ku Yudeya. Ndatero kuti mudziŵe ndithu kuti zimene adakuphunzitsanizo nzoonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:31-32

Yesu adauza anthu amene adamkhulupirirawo kuti, “Ngati mumvera mau anga nthaŵi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziŵa zoona zenizeni, ndipo zoonazo zidzakusandutsani aufulu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:42

Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:2

Iwoŵa anali okwiya chifukwa chakuti atumwi aŵiriwo ankaphunzitsa anthu ndi kulalika kuti, “Popeza kuti Yesu adauka kwa akufa, ndiye kuti akufa adzaukanso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:30-31

Filipo adathamangira nduna ija, ndipo adaimva ikuŵerenga buku la mneneri Yesaya. Tsono adaifunsa kuti, “Bwana, kodi mukumvetsa zimene mukuŵerengazi?” Iye adati, “Ha, ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Motero adaitana Filipo kuti adzakwere ndi kukhala naye pagaletapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:14-15

Kodi anthu angatame Mulungu bwanji mopemba ngati sadamkhulupirire? Ndipo angamkhulupirire bwanji ngati sadamve za Iye? Ndipo angamve za Iye bwanji ngati palibe wina wolalika? Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:4-5

Ndipo pamene ndinkalankhula kapena kulalika, sindinkalankhula moonetsa nzeru, kuyesa kukopa anthu, koma mau anga anali otsimikizika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:31

Iyai, koma inu muike mtima wanu pa mphatso zopambana. Tsonotu ndikuwonetseni njira yopambana kwenikweni:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:20

Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:17-18

ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20-21

Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza. Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:3-5

Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai. Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 3:2

Choncho tidatuma Timoteo, mbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yolalika Uthenga Wabwino wa Khristu. Tidamtuma kuti adzakulimbitseni mtima ndi kukukhazikitsani m'chikhulupiriro chanu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:6

Abale, tsopano tikukulamulani m'dzina la Ambuye Yesu Khristu kuti muziŵapewa abale onse a makhalidwe aulesi, osafuna kutsata mwambo umene tidaŵapatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:11

Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:2

uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:15

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:27

Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:12

Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:12

Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:32

Munthu wonyoza malangizo amangodzinyoza yekha, koma wovomera kudzudzula amapindula nzeru yomvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:17-19

Utchere khutu lako, umve mau a anthu anzeru, uike mtima wako pa zophunzitsa zanga, kuti uzidziŵe. Chidzakhala chokondwetsa ukazisunga, ndi kukhala wokonzeka kumazilankhula pa nthaŵi yake. Ndakudziŵitsa zimenezi lero kuti makamaka iweyo uzikhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:12

Mwana wanga, uchenjere ndi kalikonse kobzola pamenepa. Kulemba mabuku sikutha, ndipo kuphunzira kwambiri kumatopetsa thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 50:4

Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:20

Pajatu odzalankhula si ndinu ai, koma Mzimu wa Atate anu ndiye amene adzalankhula kudzera mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:46-49

“Bwanji mumangoti, ‘Ambuye, Ambuye,’ koma chonsecho simuchita zimene ndimanena? Munthu aliyense wodza kwa ine, namva mau anga nkumaŵagwiritsa ntchito, ndikuuzani amene amafanafana naye. Amafanafana ndi munthu womanga nyumba, amene adaakumba mozama, naika maziko pa thanthwe. Tsono chigumula chitafika, madzi ake adagunda nyumbayo, koma sadaigwedeze, chifukwa adaaimanga bwino. Koma munthu wongomva mau anga, osaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu amene adaamanga nyumba pamwamba pa nthaka, osakumba maziko. Pamene madzi a chigumula adagunda nyumbayo, pompo idagwa, ndipo kuwonongeka kwake kunali kotheratu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 13:34-35

Ndikukupatsani lamulo latsopano, lakuti muzikondana. Monga momwe Ine ndidakukonderani, inunso muzikondana. Mukamakondana, anthu onse adzadziŵa kuti ndinudi ophunzira anga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:42

Tsono tsiku ndi tsiku ankaphunzitsabe ndi kulalika m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba za anthu, Uthenga Wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:11-12

Ndikulakalakadi kukuwonani, kuti ndikugaŵireni mphatso zina zauzimu, kuti motero ndikulimbikitseni. Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:10

Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:24

Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1-2

Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa. Nchifukwa chake tsono, nthaŵi zonse tikapeza mpata, tizichitira anthu onse zabwino, makamaka abale athu achikhristu. Onani malemba akuluakulu amene ndikulemba ndi dzanja langalanga tsopano. Onse amene afuna kuti akome pamaso pa anthu, akukukakamizani kuti muumbalidwe. Ali ndi cholinga chimodzi chokha, chakuti asazunzidwe chifukwa cha mtanda wa Khristu. Pakuti ngakhale iwo omwe amene amaumbalidwa satsata Malamulo, komabe amafuna kuti inu muumbalidwe, kuti athe kunyadira kuumbalidwa kwanuko. Koma ine sindinganyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu basi. Popeza kuti Iye adafa pa mtanda, tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa. Kuumbalidwa si kanthu, kusaumbalidwa si kanthunso, chachikulu nchakuti Mulungu apatse munthu moyo watsopano. Mulungu aŵapatse mtendere, ndipo aŵachitire chifundo anthu a Mulungu onse amene amatsata njira imeneyi. Kuyambira tsopano asandivutenso munthu wina aliyense, pakuti zipsera zimene ine ndili nazo pa thupi langa, zikutsimikiza kuti ndine wakewake wa Yesu. Abale, Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni inu nonse. Amen. Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:1-3

Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako. Iye amene adaatsika, ndi yemweyo amene adakwera, nabzola Kumwamba konse, kuti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu. Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi. Tsono m'dzina la Ambuye ndikukuuzani, ndipo ndikunenetsa, kuti musayendenso monga amachitira akunja potsata maganizo ao achabe. Nzeru zao zidachita chidima, sangalandire nao konse moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene udadza mwa iwo kaamba ka kuuma mtima kwao. Mitima yao idaludzulala ndipo adangodzipereka ku zonyansa, kuti azichita zoipa zilizonse mosadziletsa. Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai, ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu. Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni. Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu. Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni. Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa. M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo. ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:1-2

Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:11-12

Paja mukudziŵa kuti, tinkasamala aliyense mwa inu monga momwe amachitira bambo ndi ana ake. Tinkakulimbitsani mtima, kukuthuzitsani mtima ndi kukupemphani kuti mayendedwe anu akhale okomera Mulungu, amene amakuitanani kuti mukaloŵe mu Ufumu wake waulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:15

Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 3:13

Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Chauta Wamuyaya, Ambuye Wapamwamba! M'dzina la Yesu ndikubwerera kwa Inu, chifukwa Inu nokha ndinu woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa. Atate, limbitsani ndi kukulitsa utumiki wa aphunzitsi onse a chikhulupiriro, wadzani ndi chisomo chanu kuti aphunzitse monga momwe Inu mumachitira ndi nzeru, kuleza mtima, ndi mphamvu. Dalitsani miyoyo yawo, awathandizeni kuchita ntchito yawo yophunzitsa, ndipo ziphunzitso zonse zikhale zozikika pa Mawu anu. Ndikupempha kuti m'mitima yawo musakhale kokha chikhumbo chophunzitsa, komanso chikhumbo chofuna kuphunzira nthawi zonse, kuti Mzimu wanu Woyera awatsogolere ku choonadi chonse ndi kukulitsa chidziwitso chawo kotero kuti miyoyo ya ophunzira awo ikhudzidwe ndi kumangidwa kudzera m'ziphunzitso zawo. Inu mwanena m'Mawu anu kuti: "Wophunzira sapambana mphunzitsi wake; koma yense wophunzitsidwa bwino adzakhala ngati mphunzitsi wake." Zikomo Atate, chifukwa cha miyoyo ya aphunzitsi onse, omwe mudawaika kuti atiphunzitse ndi kukulitsa chidziwitso chathu cha Baibulo. Ndikupempha kuti muteteze miyoyo yawo ndi ya mabanja awo, kuti asakhale odziwa zambiri zokha, komanso ochita Mawu anu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa