Munthu amene mumayenda naye amakukhudzani, kaya bwino kaya moyipa. Ndipo lemba la Miyambo 13:20 limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru, koma mnzawo wa zitsiru adzaphwanyidwa.”
Mabwenzi oipa amakubweretserani mavuto ambiri, nthawi zonse mumakhala ngati mukupereka zambiri kuposa zomwe mukupeza, ndipo mumakhala osasangalala. Zimakhala ngati mukuzungulira mu bwalo la mavuto basi.
M’Malemba Opatulika muli nkhani zambiri zokhudza mabwenzi oipa. Mwachitsanzo, Aisiraeli atayandikira Dziko Lolonjezedwa, Yehova anawachenjeza kuti asayanjane ndi anthu a m’dzikomo komanso kuti asamapembedze milungu yachilendo.
M’moyo wanu mumapeza machenjezo nthawi zonse okhudza zinthu zomwe simuyenera kuchita, zomwe sizingakupindulitseni. Ndikofunika kuti mumvere machenjezo amenewa, chifukwa mudzapulumutsa moyo wanu ku mavuto aakulu amene amabwera chifukwa cha kusamvera.
Pali anthu ena amene angadzitche kuti ndi mabwenzi anu, koma ngati akukutulutsani m’malamulo a Mulungu, akhoza kukutsogolerani ku imfa mosavuta. Yesu sakufunirani zimenezo. Choncho, mupemphe Mulungu kuti akuwongolereni ndiponso kuti chifuniro chake chichitike m’moyo wanu.
Mupemphere Mulungu kuti akupezeni mabwenzi abwino. Ndikukutsimikizirani kuti adzayankha pemphero lanu, ndipo adzakuthandizani kusiya mabwenzi oipa amene akukutsogolerani ku zoipa ndi chiwerewere.
Inu anthu osakhulupirikanu, kodi simudziŵa kuti kuchita chibwenzi ndi zapansipano nkudana ndi Mulungu? Choncho munthu wofuna kukhala bwenzi la zapansipano, ameneyo amadzisandutsa mdani wa Mulungu.
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu,
Wina aliyense akadza kwa inu osaphunzitsa zimenezi, musamlandire m'nyumba mwanu. Musampatse ndi moni womwe, pakuti wopatsa munthu wotere moni, akuvomereza zochita zake zoipa.
Usachite naye chibwenzi munthu wopsa mtima msanga, ndipo usamayenda naye munthu waukali, kuwopa kuti ungadzaphunzireko mayendedwe ake, ndi kukodwa mu msampha.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye.
Woyenda ndi anthu anzeru nayenso amakhala ndi nzeru, koma woyenda ndi zitsiru adzaonongeka.
Koma ndidaakulemberani kuti musamayanjane ndi munthu amene amati ndi mkhristu, pamene chikhalirecho ndi munthu wadama, kapena waumbombo, wopembedza mafano, waugogodi, chidakwa, kapena wachifwamba. Munthu wotere musamadye naye nkomwe.
Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.
Munthu woipa mtima amafalitsa mkangano, kazitape amadanitsa anthu okhala pa chibwenzibwenzi.
Ukungolira usiku wonse, misozi ikungoti mbwembwembwe pamasaya pake. Mwa onse amene ankaukonda, palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala woti aziwusangalatsa. Abwenzi ake onse auchita zaupandu, onse asanduka adani ake.
Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.
Abale, tsopano tikukulamulani m'dzina la Ambuye Yesu Khristu kuti muziŵapewa abale onse a makhalidwe aulesi, osafuna kutsata mwambo umene tidaŵapatsa.
Amene amakukonda, ngakhale akupweteke, chikondi chake chimakhalapobe, mdani wako ngakhale akumpsompsone, nkunyenga chabe kumeneko.
Munthu woyambitsa mipatuko, utamdzudzula kaŵiri konse, usakhale nayenso nkanthu. Paja ukudziŵa kuti munthu wotere ngwosokonezeka ndipo ngwochimwa. Mwini wake yemwe amadziimba mlandu yekha.
Wolima m'munda mwake adzakhala ndi chakudya chambiri, koma wonka nafuna zopanda pake adzasauka kwambiri.
Koma mneneri Yehu, mwana wa Hanani, adatuluka kuti akumane naye, ndipo adafunsa mfumu Yehosafati kuti, “Kodi ndi bwino kuŵathandiza anthu oipa amene amadana ndi Chauta? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Chauta ulikudza kwa inu.
Sindikhala pamodzi ndi anthu onyenga, sindiyenda ndi anthu achiphamaso. Ndimadana ndi anthu ochita zoipa, sindikhala pamodzi ndi anthu oipa.
Ngati wina aliyense akana kumvera mau amene talemba m'kalatayi, mumuwonetsetse ameneyo, ndipo musayanjane naye, kuti choncho achite manyazi. Koma musamuwone ngati mdani. Makamaka mumchenjeze ngati mbale.
Nzeru nzabwino kupambana zida zankhondo, koma wochimwa mmodzi amatha kuwononga zabwino zambiri.
Munthu wochita zabwino amatsogolera anzake pa njira yokhoza, koma njira ya munthu woipa imaŵasokeretsa.
Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku. Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.
Musamagwirizana ndi anthu akunja, monga ngati kuti iwo ndi inu mumafanana. Nanga kulungama kungagwirizane bwanji ndi kusalungama? Kapena kuŵala kungayanjane bwanji ndi mdima?
Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali. Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa. Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani? Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga.
Munkathamanga bwino lomwe. Tsono adakuletsani ndani kuti musamverenso choona? Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Mulungu amene amakuitanani. Chofufumitsira chapang'ono chabe chimafufumitsa buledi yense.
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya.
Ndikukupemphani abale, chenjera nawoni anthu amene amapatutsa anzao naŵachimwitsa. Iwo amaphunzitsa zosiyana ndi zimene inu mudaphunzira. Muziŵalewa, pakuti anthu otere satumikira Khristu Ambuye athu, koma amangotumikira zilakolako zao basi. Ndi mau okoma ndi oshashalika amanyenga anthu a mitima yoona.
Koma iwe, munthu wa Mulungu, uzipewe zonsezi. Uzikhala ndi mtima wofunafuna chilungamo, wolemekeza Mulungu, wokhulupirika, wachikondi, wolimbika ndi wofatsa. Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Mwana wanga, anthu oipa akafuna kukukopa, usamaŵamvera. Adzati, “Tiye kuno, tikabisale kuti tiphe anthu, tiye tikalalire anthu osalakwa. Tiyeni tiŵameze amoyo ngati manda, tiŵameze athunthu ngati anthu otsikira ku manda. Motero tidzapata zinthu zambiri zamtengowapatali, nyumba zathu tidzazidzaza ndi zofunkha. Tiye uloŵe m'gulu lathu, chuma chathu tidzagaŵana tonse.” Mwana wanga, usamayenda nawo anthu amenewo, usatsagane nawo pa njira yaoyo.
Munthu woyenda mwaungwiro, amayenda mosatekeseka. Koma woyenda njira zoipa, adzadziŵika.
Anthu akunja amadabwa tsopano poona kuti mwaleka kuthamangira nao zoipitsitsa zimene iwo amachita mosadziletsa konse. Nchifukwa chake amalalata.
“Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa.
Kukhulupirira munthu wosakhulupirika pa nthaŵi yamavuto kuli ngati kudya ndi dzino loŵaŵa, kapena kuyenda ndi mwendo wothyoka.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Uthaŵe zilakolako zoipa zachinyamata. Pamodzi ndi anthu onse otama Ambuye mopemba ndi mtima woyera, uzifunafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere.
Ndidzakhala kutali ndi anthu a mtima woipa, sindidzalola choipa chilichonse kuloŵa mwa ine.
Mitima yao idadzaza ndi zosalungama zamitundumitundu, monga kuipa, umbombo ndi dumbo. Amangolingalira za kaduka, za kupha anthu, za ndeu, za kunyenga, ndi za njiru. Amachita ugogodi, Umasimba za Mwana wake, Yesu Ambuye athu. Poyang'anira umunthu wake, kholo lake ndi Davide, amasinjirira, ndipo amadana ndi Mulungu. Ndi achipongwe, odzikuza, ndi onyada. Amafunafuna njira zatsopano zochitira zoipa, samvera makolo ao. Ndi opusa, osakhulupirika, okhakhala moyo, ndi opanda chifundo. Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi.