Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


60 Mau a M'Baibulo Okhudza Chikhululukiro

60 Mau a M'Baibulo Okhudza Chikhululukiro

Ndikakuuzani, mukadzichepetsa pamaso pa Mulungu ndi mtima wonse, ndikulapa machimo anu, Iye ndi wokhulupirika ndi wolungama, ndipo adzakukhululukirani machimo anu onse ndi kukutsukani ku zoipa zonse. Chifukwa cha nsembe ya Yesu Khristu pa mtanda, ndife omasuka kulandira chikhululukiro.

Mulungu amafunanso kuti ife tikhululukire ena monga momwe Iye anatikhululukira, kuti tisonyeze chikondi chake kwa anthu omwe atizungulira, ndi kuwasonyeza Yesu nthawi zonse. Tikamakhululukira ena, timadzimasula tokha, machimo athu amachiritsidwa, ndipo timapeza ufulu ku zinthu zomwe zimativuta.

Tiyeni tizikhala oyamikira nthawi zonse ndi kupewa machimo, ndi kuyandikira Mulungu ndi mtima wolapa, pakuti Iye adzatikhululukira. [Mateyu 6:14-15]




Mateyu 6:14-15

“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:32

Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:14

“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:7

Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:14

ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:37

“Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:1

Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake afafanizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:3

Ndiye amene amakhululukira machimo ako onse, ndi kuchiritsa matenda ako onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:12

Mutikhululukire ife machimo athu, monga ifenso takhululukira otilakwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 11:25

Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye nkanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu.” [

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:13

Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:38

Tsono abale, dziŵani kuti chifukwa cha Yesuyo tikukulalikirani zakuti machimo amakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:31

Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakhululukira anthu tchimo lililonse, ngakhale mau achipongwe omunyoza Iyeyo. Koma munthu wochita chipongwe Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:10

“Aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira, koma wonyoza Mzimu Woyera ndi mau achipongwe, Mulungu sadzamkhululukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:2

Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:13-14

Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 8:12

Mwachifundo ndidzaŵakhululukira zochimwa zao, sindidzakumbukiranso machimo ao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:5

Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:15

Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:30

Mulungu adaaŵalekerera anthu pa nthaŵi imene iwo anali osadziŵa, koma tsopano akuŵalamula anthu onse ponseponse kuti atembenuke mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:19

Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:11

Malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, Inu Chauta, mundikhululukire machimo anga pakuti mlandu wanga ndi waukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:21-22

Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:12

Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:18

Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 4:7-8

“Ngodala anthu amene Mulungu adaŵakhululukira machimo ao, amene Iye adaŵafafanizira machimo ao. Ngwodala munthu amene Ambuye saŵerengeranso machimo ake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:8

Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:9

Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:7

Ngodala anthu ochitira anzao chifundo, pakuti iwonso Mulungu adzaŵachitira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 2:10-11

Mukakhululukira munthu, inenso ndimkhululukira. Ngati ine ndakhululukira, patakhala kanthu koti ndakhululukira, ndiye kuti ndakhululukira chifukwa cha inu pamaso pa Khristu. Cholinga chake nkuti Satana asatichenjerere, paja tikudziŵa njira zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:19-20

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa. Koma makamaka, monga mau a Mulungu akunenera, “Ngati mdani wako wamva njala, iwe umpatse chakudya. Ngati wamva ludzu, iwe umpatse madzi akumwa. Ukatero udzamchititsa manyazi kwambiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:1-2

Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu. Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera. Pamenepo ochimwa ndidzaŵaphunzitsa njira zanu, ndipo iwo adzabwerera kwa Inu. Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu. Ambuye, tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu. Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani. Ndikadapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo. Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza. Muŵachitire zabwino anthu a ku Ziyoni, chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Mumangenso kachiŵiri makoma a Yerusalemu. Pamenepo mudzakondwera ndi nsembe zoyenera, nsembe zootcha ndi zopsereza kwathunthu. Choncho adzapereka ng'ombe zamphongo pa guwa lanu lansembe. Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga, mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:3-4

Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke. “Tsiku limenelo, amene ali pa denga, asadzatsike kukatenga katundu wake m'nyumba. Chimodzimodzinso amene ali ku munda, asadzabwerere ku nyumba. Kumbukirani za mkazi wa Loti. Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga. Kunena zoona, usiku umenewo, padzakhala anthu aŵiri pa bedi limodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja pamodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya, Anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.” Apo ophunzira ake adamufunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti, Ambuye?” Yesu adati, “Kumene kwafera chinthu, nkumeneko kumasonkhana miphamba.” Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 130:4

Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:9

Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:28

Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:19

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:9

Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 130:3-4

Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye? Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:25

“Ine, Ineyo ndithu, ndine amene ndimafafaniza machimo anu, kuti ulemerero wanga uwoneke. Sindidzasungabe mlandu wa machimo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 15:18-20

Basi ndinyamuka, ndipita kwa bambo wanga, ndipo ndikanena kuti: Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kutchedwanso mwana wanu. Mundilole ndisanduke mmodzi mwa antchito anu.’ Tsono Afarisi ndi aphunzitsi a Malamulo adayamba kuŵinya nkumanena kuti, “Munthu uyu amalandira anthu ochimwa, nkumadya nawo pamodzi.” “Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 23:34

Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:13

Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:17

Pambuyo pake akutinso, “Sindidzaŵakumbukiranso konse machimo ao ndi zolakwa zao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 15:20-24

“Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona. Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’ Koma bambo wake adauza antchito ake kuti, ‘Thamangani mukatenge mkanjo wabwino kwambiri, mumuveke. Mumuvekenso mphete ku chala, ndi nsapato ku mapazi. Ndipo katengeni mwanawang'ombe wonenepa uja, muphe kuti tidye, tikondwere. Chifukwa mwana wangayu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ Ndiye pompo chikondwerero chidayamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:19-21

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa. Koma makamaka, monga mau a Mulungu akunenera, “Ngati mdani wako wamva njala, iwe umpatse chakudya. Ngati wamva ludzu, iwe umpatse madzi akumwa. Ukatero udzamchititsa manyazi kwambiri.” Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:1-2

Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake afafanizidwa. Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika. Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe. Ngwodala amene Chauta samuŵerengera mlandu wake, amene mumtima mwake mulibe zonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:7

Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:36

Monga Atate anu akumwamba ali achifundo, inunso mukhale achifundo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 20:23

Anthu amene mudzaŵakhululukira machimo ao, adzakhululukidwadi, koma amene simudzaŵakhululukira, sadzakhululukidwa ai.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:11

Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:13-14

Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu zonse. Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:1-2

“Musamaweruza anthu ena kuti ndi olakwa, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni. Kapena atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha? Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa. “Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka. “Chenjera nawoni aneneri onyenga. Amadza kwa inu ali ndi maonekedwe ofatsa ngati nkhosa, koma m'kati mwao ndi mimbulu yolusa. Mudzaŵadziŵira zochita zao. Kodi mitengo yaminga nkubala mphesa? Kodi mitula nkubala nkhuyu? Chonchonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo woipa umabala zipatso zoipa. Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, kapena mtengo woipa kubala zipatso zabwino ai. Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula nkuuponya pa moto. M'mene inu mumaweruzira ena, ndi m'menenso Mulungu adzakuweruzirani inuyo. Ndipo muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:10

Mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:23-24

popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:2

Kumeneko anthu ena adabwera kwa Iye ndi munthu wa ziwalo zakufa ali chigonere pa machira. Poona chikhulupiriro chao, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Limba mtima, mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:20

Poona chikhulupiriro chaocho, Yesu adati, “Mbale wanga, machimo ako akhululukidwa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:5

Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga opulumutsa, lero ndikukuimbirani ndi kufuna nkhope yanu! M'dzina la Yesu, ndikupemphani kuti mundisunge, musalole kuti ndipatukane ndi choonadi cha uthenga wanu wabwino ndi kunditeteza kuti ndisachimwireni. Ambuye, mwandipatsa mwayi wodziwa mawu anu, chikhululukiro chanu, chisomo chanu ndi Mzimu wanu Woyera. Ndipo nditha kuona ndi kukhala mboni ya zodabwitsa zanu, zozizwitsa, machiritso ndi zizindikiro. Mawu anu amati: "Aliyense wonyoza Mzimu Woyera sadzakhululukidwa konse, koma ali ndi mlandu wa uchimo wosatha." Atate, ndisungeni ku kusadziwa ndi kuuma mtima, kuti ndisagwere mu uchimo woopsa uwu wonyoza ndi kutukwana Mzimu wanu Woyera, chifukwa ndiwo uchimo wokha umene simukhululukira ndipo mumaweruza kwamuyaya. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa