Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo,
ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu. Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera. Pamenepo ochimwa ndidzaŵaphunzitsa njira zanu, ndipo iwo adzabwerera kwa Inu. Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu. Ambuye, tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu. Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani. Ndikadapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo. Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza. Muŵachitire zabwino anthu a ku Ziyoni, chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Mumangenso kachiŵiri makoma a Yerusalemu. Pamenepo mudzakondwera ndi nsembe zoyenera, nsembe zootcha ndi zopsereza kwathunthu. Choncho adzapereka ng'ombe zamphongo pa guwa lanu lansembe. Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga, mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.
Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”
Kodi kapena ukupeputsa chifundo chachikulu cha Mulungu, kuleza mtima kwake, ndi kupirira kwake? Kodi sukudziŵa kuti Mulungu akukuchitira chifundo chifukwa afuna kuti utembenuke mtima?
Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Wobisa machimo ake sadzaona mwai, koma woulula ndi kuleka machimo, adzalandira chifundo.
Yesu adapitiriza mau kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti momwemonso Kumwamba kudzakhala chimwemwe chifukwa cha munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima, kuposa anthu olungama 99 amene alibe chifukwa chotembenukira mtima.”
Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje.
Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu, sindidabise kuipa kwanga. Ndidati, “Ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,” pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga.
Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kulalika kuti, “Tembenukani mtima, chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.”
“Munthu wochimwa akaleka machimo ake amene ankachita, namamvera malamulo anga onse, ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndithudi ameneyo adzakhala ndi moyo, sadzafa. Zoipa zake zonse zidzakhululukidwa. Adzakhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zolungama. Ine Ambuye Chauta ndikuti, Kodi imfa ya munthu woipa Ine ndimakondwera nayo? Iyai, koma ndikadakonda kuti woipa aleke njira zake zoipa ndi kukhala ndi moyo.
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Koma Chauta akunena kuti, “Ngakhale tsopano bwererani kwa Ine ndi mtima wanu wonse, mukusala zakudya, mukukhetsa misozi ndi kulira mwachisoni. Ng'ambani mitima yanu, osati zovala zanu chabe.” Bwererani kwa Chauta, Mulungu wanu, poti Iye ngwokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chosasinthika. Nthaŵi zonse ndi wokonzeka kukhululuka.
Kamvetsetseni tanthauzo la mau a Mulungu aja akuti, ‘Ndimafuna chifundo, osati nsembe ai.’ Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa.”
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Ungovomera kulakwa kwako. Vomera kuti udaukira Chauta Mulungu wako, kuti udapembedza nao milungu yachilendo patsinde pa mitengo yogudira, ndiponso kuti sudamvere mau anga,’ ” akuterotu Chauta.
Yesu popitiriza mau adati, “Ndikunenetsa kuti ndi m'menenso angelo a Mulungu amakondwerera munthu mmodzi wochimwa amene watembenuka mtima.”
Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.
Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu.
Mulungu adaaŵalekerera anthu pa nthaŵi imene iwo anali osadziŵa, koma tsopano akuŵalamula anthu onse ponseponse kuti atembenuke mtima.
kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Ndachotsa zolakwa zako ngati mtambo ndiponso machimo ako ngati nkhungu. Bwerera kwa Ine poti ndakuwombola.”
Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye? Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani.
Tsopano poti tatembenuka mtima, tikumva chisoni. Tsopano poti taphunzira, tikudzigunda pa mtima. Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa, chifukwa cha machimo athu apaubwana.’
Malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, Inu Chauta, mundikhululukire machimo anga pakuti mlandu wanga ndi waukulu.
Inu ana anga, ndikukulemberani zimenezi kuti musamachimwa. Komabe wina akachimwa, tili nayo Nkhoswe yotinenera kwa Atate, ndiye Yesu Khristu amene ali wolungama. Koma munthu wokonda mnzake, amakhala m'kuŵala, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa. Munthu wodana ndi mnzake, ali mu mdima, ndipo akuyenda mu mdima. Sadziŵa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa m'maso. Inu ana, ndikukulemberani popeza kuti Mulungu wakukhululukirani machimo anu chifukwa cha dzina la Khristu. Inu atate, ndikukulemberani, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Inu achinyamata, ndikukulemberani, chifukwa mwampambana Woipa uja. Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja. Musamalikonde dziko lapansi kapena zinthu zapansipano. Munthu akamakonda dziko lapansi, chikondi chokonda Atate sichikhalamo mwa iye. Paja zonse zapansipano, zilakolako zathupi, zinthu zimene maso amakhumbira, ndiponso kunyadira za moyo uno, zonsezi sizichokera kwa Atate, koma ku mkhalidwe woipa wa dziko lapansi. Ndipotu dziko lapansi likupita, pamodzi ndi zake zonse zimene anthu amazilakalaka. Koma munthu wochita zimene Mulungu afuna, amakhalapo mpaka muyaya. Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi. Anthuwo adachita kuchoka pakati pathu, komabe sanali a gulu lathu kwenikweni. Pakuti akadakhala a gulu lathu, bwenzi akali nafebe. Koma adatichokera, kuti aonekere poyera kuti panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene anali wa gulu lathu. Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.
Zitsiru sizilabadako za kulapa machimo ao, kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
Chauta adayankha kuti, “Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso, ndipo udzanditumikiranso. Ukamalankhula zenizeni, osati zachabe, udzakhala wondilankhulira. Anthu ameneŵa ayenera kudzabweranso kwa iwe, koma iwe usabwerere kwa iwowo.
Basi ndinyamuka, ndipita kwa bambo wanga, ndipo ndikanena kuti: Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kutchedwanso mwana wanu. Mundilole ndisanduke mmodzi mwa antchito anu.’
“Ine, Ineyo ndithu, ndine amene ndimafafaniza machimo anu, kuti ulemerero wanga uwoneke. Sindidzasungabe mlandu wa machimo anu.
Pamene otsutsana naye aja adamva zimenezi, adaleka mitsutsoyo. Adatamanda Mulungu adati, “Kodi kani! Ndiye kuti Mulungu wapatsadi ndi akunja omwe mwai woti atembenuke mtima ndi kulandira moyo!”
Maiyo adati, “Inde Ambuye, palibe.” Tsono Yesu adamuuza kuti, “Inenso sindikukuzengani mlandu. Pitani koma kuyambira tsopano musakachimwenso.”]
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.
Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza.
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo.
ndipo adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba.
Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, nayamba kulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.”
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.” Apo Yesu adamuuza kuti, “Chipulumutso chafika m'banja lino lero, popeza kuti ameneyunso ndi mwana wa Abrahamu.
Koma ndidalalika poyamba kwa anthu a ku Damasiko ndi a ku Yerusalemu, ndipo bwino lake ku dziko lonse la Yudeya, ndiponso kwa anthu a mitundu ina. Ndidalalika kuti atembenuke mtima, kutembenukira kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zotsimikiza kuti atembenukadi mtima.
Tsono, ali akapolo kuchilendoko, akazindikira kuchimwa kwao natembenuka mtima ndi kupemphera kwa Inu modzichepetsa m'dziko la anthu amene adaŵagwira ukapolowo, nkumanena kuti, ‘Tachimwa, tachita zosayenera, tapalamula ndithu’. Anthuwo akabwerera kwa Inu ndi nzeru zao zonse ndi mtima wao wonse, m'dziko la adani ao kumene adaŵatengera ukapolo, ndipo akapemphera kwa Inu choyang'ana ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Aisraele inu, aliyense mwa inu ndidzamuweruza molingana ndi ntchito zake. Lapani, tembenukani mtima, kuti machimo anu asakuwonongeni. Tayani zoipa zanu zonse zakale zimene mudachimwira Ine. Mukhale ndi mtima watsopano ndi nzeru zatsopano. Nanga muferenji, inu anthu a ku Israele?
Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika. Mudzatichitiranso chifundo. Mudzapondereza pansi zolakwa zathu, mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja.
Musakumbukire machimo a unyamata wanga ndi mphulupulu zanga. Koma mundikomere mtima, Inu Chauta, chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.
Aŵa ndi mau otsimikizika, oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa.
Koma wokhometsa msonkho uja adaima kutali, osafuna nkuyang'ana kumwamba komwe. Ankangodzigunda pa chifuwa ndi chisoni nkumanena kuti, ‘Mulungu, mundichitire chifundo ine wochimwane.’ ”
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Ayuda ndi Agriki omwe ndidaŵapempha kolimba kuti atembenukire kwa Mulungu molapa, ndi kumakhulupirira Ambuye athu Yesu.
Zolakwa zanga ndikuzidziŵa, kuchimwa kwanga ndikukuzindikira nthaŵi zonse. Ndachimwira Inu, Inu nokha, ndachita choipa pamaso panu. Motero mwakhoza ponditchula wolakwa, simudalakwe pogamula mlandu wanga.
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Enanu munali otere kale, koma mudayeretsedwa, mudasanduka anthu a Mulungu, ndipo mudapezeka olungama pamaso pake. Zimenezi zidachitika m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndiponso mwa Mzimu wa Mulungu wathu.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithudi, pali Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa. Ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo. Inu Aisraele, muferanji? Tembenukani, lekani zoipa zimene mukuchita.
Musandizenge mlandu ine mtumiki wanu, popeza kuti palibe munthu wamoyo amene ali wolungama pamaso panu.
Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”
Mulungu mwini, amene amatipatsa mtendere, akusandutseni angwiro pa zonse. Akusungeni athunthu m'nzeru, mumtima ndi m'thupi, kuti mudzakhale opanda chilema pobwera Ambuye athu Yesu Khristu.
popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.
Tsono tisangoima pa maphunziro oyamba enieni a Khristu. Tisachite kubwerezanso kuphunzitsa zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu,
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake? Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika. Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu.
Tsono, inu okondedwa, popeza kuti tili ndi malonjezo ameneŵa, tiyeni tidzichotsere zinthu zonse zodetsa thupi lathu kapena mtima wathu. Ndipo pakuwopa Mulungu tiziyesetsa ndithu kukhala oyera mtima.
Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera. Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa. Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu. Mulungu atamandike chifukwa sadakane pemphero langa, sadachotse chikondi chake chosasinthika kwa Ine.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Chifukwa cha kudzipereka ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake. Chifukwa choopa Chauta munthu amalewa zoipa.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
nthaŵi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziŵa zonse. Inu okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, titha kuima mopanda mantha pamaso pa Mulungu.
Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu.
Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’
Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo. Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona. Pamenepo nzeru zao zidzabweramo, ndipo adzapulumuka mu msampha wa Satana, amene adaaŵagwira kuti azichita zofuna zake.
Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse.
“Nchifukwa chake ngati wabwera ndi chopereka chako ku guwa, nthaŵi yomweyo nkukumbukira kuti mnzako wina ali nawe nkanthu, siya chopereka chakocho kuguwa komweko, ndipo pita, kayambe wayanjana naye mnzakoyo. Pambuyo pake ndiye ubwere kudzapereka chopereka chako chija.
Chikondi chenicheni ndi ichi, chakuti sindife tidakonda Mulungu ai, koma Mulungu ndiye adatikonda ifeyo, natuma Mwana wake kuti akhale nsembe yopepesera machimo athu.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni.
Zinthu zonsezi ndidazilenga ndine, tsono zonsezi nzanga,” akutero Chauta. “Anthu amene ndimakondwera nawo ndi aŵa: odzichepetsa ndi olapa, ondiwopa ndi omvera mau anga.
Pambuyo pake Yesu adapeza wochira uja m'Nyumba ya Mulungu, namuuza kuti, “Ona, wachira tsopano. Usakachimwenso, kuti chingakugwere choopsa china kuposa pamenepa.”
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera. Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.
Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Tsono iye adatuluka mu mzinda wake kukakomana ndi Asa, ndipo adamuuza kuti, “Ndimvereni inu Asa, Ayuda nonsenu ndi inu Abenjamini. Chauta ali nanu nthaŵi yonse imene inu muli ndi Iye. Mukamfunafuna mudzampeza. Koma mukamsiya, nayenso adzakusiyani.
Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni. Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.
“Ine ndimakubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenuka mtima. Koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Ndikukupemphani ndi mtima wanga wonse, mundikomere mtima molingana ndi malonjezo anu aja.
Ndipo adati, “Inu, mukandikumbikire mukakafika mu Ufumu wanu.” Yesu adamuyankha kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino ukhala nane ku Malo a Chisangalalo, Kumwamba.”
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Aneneri onse adamchitira umboni, ndi kunena kuti chifukwa cha dzina lake, Mulungu adzakhululukira machimo a munthu aliyense wokhulupirira Iyeyu.”
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwanso kwatsopano, sangauwone Ufumu wa Mulungu.”
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzakhala woyera. Mundisambitse, ndipo ndidzayera kupambana chisanu chambee.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.
Nchifukwa chake tembenuka mtima, uleke choipa chakochi. Pempha Ambuye kuti mwina mwake nkukukhululukira maganizo a mumtima mwakoŵa.
Mulungutu waonetsa kukoma mtima kwake kofuna kupulumutsa anthu onse. Kukoma mtima kwakeko kumatiphunzitsa kusiya moyo wosalemekeza Mulungu, ndiponso zilakolako za dziko lapansi. Kumatiphunzitsa kuti moyo wathu pansi pano ukhale wodziletsa, wolungama ndi wolemekeza Mulungu.
Mwakuti kunena zoona, chikondi chachikulu chimene iyeyu waonetsa, chikutsimikiza kuti Mulungu wamkhululukiradi machimo ake amene ali ochuluka. Koma munthu amene wakhululukidwa zochepa, amangokonda pang'ono.”
Inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m'kuŵala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m'kuŵala.
Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko. Pa kupembedzapo muwonjezerepo chifundo chachibale, ndipo pa chifundo chachibalecho muwonjezepo chikondi. Ngati zonsezi zikhala mwa inu, nkumachuluka, simudzakhala olephera ndi opanda phindu pa nzeru zodziŵira Ambuye athu Yesu Khristu. Paja munthu wopanda zimenezi ndiye kuti ngwakhungu, sangathe kuwona patali, ndipo waiŵala kuti adamtsuka machimo ake akale.
Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.
Ndi waukulu ubwino wanu umene mwaŵasungira anthu okumverani, umene mwaŵachitira anthu othaŵira kwa Inu, aliyense waona zimenezi.
Pajatu Inu mudati, “Muzifunafuna nkhope yanga.” Inu Chauta, ndidzafunafuna nkhope yanu.
Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke. “Tsiku limenelo, amene ali pa denga, asadzatsike kukatenga katundu wake m'nyumba. Chimodzimodzinso amene ali ku munda, asadzabwerere ku nyumba. Kumbukirani za mkazi wa Loti. Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga. Kunena zoona, usiku umenewo, padzakhala anthu aŵiri pa bedi limodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja pamodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya, Anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.” Apo ophunzira ake adamufunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti, Ambuye?” Yesu adati, “Kumene kwafera chinthu, nkumeneko kumasonkhana miphamba.” Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.”
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Paja Yohane Mbatizi adaabwera nadzakuwonetsani njira ya chilungamo, inu osamkhulupirira, m'menemo okhometsa msonkho ndi akazi adama adamkhulupirira. Inuyo ngakhale mudaziwona zimenezo, simudasinthe maganizo pambuyo pake kuti muzimkhulupirira.”
Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi. Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao akhululukidwe.
Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Komabe Inu Chauta, ndinu Atate athu. Ife tili ngati mtapo, Inu muli ngati woumba. Mudatipanga tonse ndi manja anu.
Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Chauta, nyaleyo imafufuza ziwalo zake zonse zam'kati.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka. Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.