Mu Bukhu la Marko, timapeza lemba ili: “Pakuti ngati simukhululukira ena, Atate anu akumwamba nawonso sadzakhululukira machimo anu.” (Marko 11:26) Kukhululukira ndiye sitepe yoyamba pochiza mabala ndikutulutsidwa ku mkwiyo womwe umatilepheretsa kupita patsogolo m'miyoyo yathu.
Mulungu amafuna mtendere ndi mgwirizano m'nyumba za mabanja onse padziko lapansi, kuti azikondana mopanda dyera, mopanda malire, komanso mopanda kudzudzulana. N’zoona kuti m’moyo nthawi zonse pamakhala nthawi imene mabanja amakangana ndi kukangana, zomwe zimachitika kawirikawiri, koma chomwe sitingalole ndi chakuti mkwiyo ulamulire mtima wanu kufikira pokusiyanitsani ndi omwe mumawakonda chifukwa cha mkangano waung'ono chabe. Zimenezi sizimachokera kwa Mulungu, ndipo Iye sakondwera ndi anthu osayanjanitsidwa.
Mulungu ndi Mulungu wa mabanja, ndipo chifuniro chake ndi chakuti dongosolo lake labwino lilame pakati panu nonse. Choncho, yanjanani nthawi zonse kuti musapatse Mdyerekezi malo mumtima mwanu.
Tipemphere kwa Mulungu kuti atithandize kukhala anthu okhululukira ndi kuchiritsa mitima yathu. Tiyeni lero titengere sitepe yoyamba yoyanjirana ndi kukhala ogwirizana. Musakhale odzikuza kapena onyada, chifukwa Mulungu akutiona kuchokera kutali, koma ali pafupi ndi anthu odzichepetsa.
Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye nkanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu.” [ “Koma ngati inu simukhululukira anzanu, Atate anunso amene ali Kumwamba sadzakhululukira machimo anu.”]
Pamenepo Petro adadzafunsa Yesu kuti, “Ambuye, kodi mbale wanga atamandichimwira, ndidzamkhululukire kangati? Kodi ndidzachite kufikitsa kasanunkaŵiri?” Yesu adamuyankha kuti, “Kodi ndikuti kasanunkaŵiri kokha ngati, iyai, koma mpaka kasanunkaŵiri kuchulukitsa ndi makumi asanu ndi aŵiri.
“Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani. Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”
Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino.
“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo.
“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.
Chikondi chizikhala chopanda chiphamaso. Muzidana ndi zoipa, nkumaika mtima pa kuchita zabwino.
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso.
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.
Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo,
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
Tsono abale, dziŵani kuti chifukwa cha Yesuyo tikukulalikirani zakuti machimo amakhululukidwa. Ndipo kudzera mwa Iye yemweyo aliyense wokhulupirira amapeza chipulumutso chathunthu chimene simukadatha kuchipata potsata malamulo a Mose.
Ndipo pamene mukuti mupemphere, muziyamba mwakhululukira mnzanu ngati muli naye nkanthu. Mukatero, Atate anunso amene ali Kumwamba adzakukhululukirani machimo anu.” [
Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika.
“Musamaweruza anthu ena kuti ngolakwa, ndipo Mulungu sadzakuweruzani. Musamaimba ena mlandu, ndipo Mulungu sadzakuimbani mlandu. Muzikhululukira ena, ndipo Mulungu adzakukhululukirani.
Mwakuti kunena zoona, chikondi chachikulu chimene iyeyu waonetsa, chikutsimikiza kuti Mulungu wamkhululukiradi machimo ake amene ali ochuluka. Koma munthu amene wakhululukidwa zochepa, amangokonda pang'ono.”
Tsono abale, dziŵani kuti chifukwa cha Yesuyo tikukulalikirani zakuti machimo amakhululukidwa.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
Chachikulu nchakuti muzikondana mosafookera, popeza kuti chikondi chimaphimba machimo ochuluka.
Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke. “Tsiku limenelo, amene ali pa denga, asadzatsike kukatenga katundu wake m'nyumba. Chimodzimodzinso amene ali ku munda, asadzabwerere ku nyumba. Kumbukirani za mkazi wa Loti. Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga. Kunena zoona, usiku umenewo, padzakhala anthu aŵiri pa bedi limodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja pamodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya, Anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.” Apo ophunzira ake adamufunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti, Ambuye?” Yesu adati, “Kumene kwafera chinthu, nkumeneko kumasonkhana miphamba.” Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.”
Wokhululukira cholakwa amafunafuna chikondi, koma wosunga nkhani kukhosi amapha chibwenzi.
Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.
Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.
“Nchifukwa chake ngati wabwera ndi chopereka chako ku guwa, nthaŵi yomweyo nkukumbukira kuti mnzako wina ali nawe nkanthu, siya chopereka chakocho kuguwa komweko, ndipo pita, kayambe wayanjana naye mnzakoyo. Pambuyo pake ndiye ubwere kudzapereka chopereka chako chija.
Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
Ngati wina aliyense adachita kanthu kolasa mtima, si ineyo amene adalasa mtima, koma pang'ono ponse adalasako nonsenu, kunenatu mosakulitsa nkhani. Munthu woteroyo, pafupi nonse mwamtsutsa, choncho chilangocho nchokwanira. Tsono makamaka nkwabwino mumkhululukire ndi kumlimbitsa mtima, kuwopa kuti angamve chisoni chachikulu chomtayitsa mtima kotheratu. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mumtsimikizirenso kuti mumamkonda ndithu.
Nchifukwa chake tsono ndikugwadira Atate, amene banja lililonse Kumwamba ndi pansi pano limatchulidwa ndi dzina lao.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.
Nzeru zimapatsa munthu mtima wosakwiya msanga, ulemerero wake wagona pa kusalabadako za chipongwe.
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi, Koma umu si m'mene inu mudaphunzirira za Khristu ai, ngatitu mudamva za Iyeyo, ngatinso mudaphunzitsidwa za Iye, motsata choona chimene chili mwa Yesu. Mudaphunzira kuti muleke mayendedwe anu akale, muvule moyo wanu wakale uja umene unkadziwononga ndi zilakolako zake zonyenga. Mtima wanu, umene uli gwero la maganizo anu, usanduke watsopano. Ndipo muvale moyo watsopano, umene Mulungu adaulenga, wofanafana naye. Apo mudzakhala olungama ndi oyera mtima kwenikweni. Tsono lekani kunama. Aliyense azilankhula zoona zokhazokha ndi mkhristu mnzake, pakuti tonse pamodzi mogwirizana ndife ziwalo za thupi la Khristu. Inde mwina nkupsa mtima, koma musachimwe, ndipo musalole kuti dzuŵa likuloŵereni muli chikwiyire. Musampatse mpata Satana woti akugwetseni. Amene ankaba, asabenso, koma makamaka azigwira ntchito kolimba ndi kumachita zolungama ndi manja ake, kuti akhale nkanthu kopatsa osoŵa. M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo. ndipo muziyesetsa kusunga umodzi mwa Mzimu Woyera pa kulunzana mu mtendere.
Inu Chauta, mukadaŵerengera machimo, ndani akadakhala chilili opanda mlandu, Ambuye? Koma inu mumakhululukira, nchifukwa chake timakulemekezani.
Mukakhululukira munthu, inenso ndimkhululukira. Ngati ine ndakhululukira, patakhala kanthu koti ndakhululukira, ndiye kuti ndakhululukira chifukwa cha inu pamaso pa Khristu. Cholinga chake nkuti Satana asatichenjerere, paja tikudziŵa njira zake.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi. Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.” Koma ngati muyamba kulumana ndi kukadzulana, muchenjere kuti mungaonongane kotheratu.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse.
Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone. Lamulo limene Iye adatipatsa ndi lakuti, wokonda Mulungu azikondanso mbale wake.
Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu. Kwenikweni adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati ndi opembedza Mulungu. Akazi pophunzitsidwa, azikhala chete ndi a mtima wodzichepetsa. Sindilola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa amuna. Mkazi kwake nkukhala chete. Paja Adamu ndiye adaayambira kulengedwa, pambuyo pake Heva. Ndiponso si Adamu amene adaanyengedwa, koma mkaziyo ndiye adaanyengedwa, naphwanya lamulo la Mulungu. Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima. Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza.
Aŵa ndi mau otsimikizika, oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Mutikhululukire ife machimo athu, pakuti ifenso timakhululukira aliyense wotilakwira. Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa.’ ”
Mundichitire chifundo, Inu Mulungu, malinga ndi chikondi chanu chosasinthika. Mufafanize machimo anga, malinga ndi chifundo chanu chachikulu. Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika. Musandipirikitse pamaso panu, musachotse Mzimu wanu woyera mwa ine. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera. Pamenepo ochimwa ndidzaŵaphunzitsa njira zanu, ndipo iwo adzabwerera kwa Inu. Mundikhululukire mlandu wanga wokhetsa magazi, Inu Mulungu, Mulungu Mpulumutsi wanga, ndipo ndidzakweza mau poimba za chipulumutso chanu. Ambuye, tsekulani milomo yanga, ndipo pakamwa panga padzalankhula zotamanda Inu. Si nsembe wamba imene Inu imakusangalatsani. Ndikadapereka nsembe yopsereza, sibwenzi Inu mutakondwera nayo. Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza. Muŵachitire zabwino anthu a ku Ziyoni, chifukwa cha kukoma mtima kwanu. Mumangenso kachiŵiri makoma a Yerusalemu. Pamenepo mudzakondwera ndi nsembe zoyenera, nsembe zootcha ndi zopsereza kwathunthu. Choncho adzapereka ng'ombe zamphongo pa guwa lanu lansembe. Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga, mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.
Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto. Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona. Pamenepo nzeru zao zidzabweramo, ndipo adzapulumuka mu msampha wa Satana, amene adaaŵagwira kuti azichita zofuna zake.
Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.
Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi. Ndilibenso wina wonga amene ali ndi mtima wosamala za inu kwenikweni. Paja ena onse amangofuna zokomera iwo okha, osati zokomera Yesu Khristu. Koma mukudziŵa kuti mkhalidwe wa Timoteo ndi wotsimikizika kale kuti ngwabwino. Mukudziŵanso kuti adagwira mogwirizana nane ntchito yofalitsa Uthenga Wabwino, monga mwana ndi bambo wake. Ndikuyembekeza tsono kumtumiza kwa inu msanga, nditadziŵa za m'mene ziyendere zanga. Koma ndikhulupirira kuti, Ambuye akalola, inenso ndidzafika kwanuko msanga. Ndaganiza kuti nkofunikadi kuti ndikutumizireni mbale wathu uja, Epafrodito. Mudaamtuma kuti adzandithandize pa zosoŵa zanga, ndipo wagwiradi ntchito ndi kumenya nkhondo yachikhristu pamodzi ndi ine. Tsonotu akukulakalakani nonsenu, ndipo ndi wokhumudwa podziŵa kuti inu mudamva zoti iye ankadwala. Nzoonadi adaadwala zedi mpaka pafupi kufa. Mwai kuti Mulungu adamchitira chifundo. Ndipotu sadangochitira chifundo iye yekhayu, komanso ineyo, kuti chisoni changa chisakhale chosanjikizana. Nchifukwa chake ndikufunitsitsa ndithu kumtumiza kwa inu, kuti podzamuwonanso mudzasangalale, kutinso nkhaŵa yanga ichepeko. Mlandireni mwachikhristu ndi chimwemwe chachikulu. Anthu otere muziŵachitira ulemu. Musamachita kanthu ndi mtima wodzikonda, kapena wodzitukumula chabe. Koma khalani odzichepetsa, ndipo aliyense aziwona anzake kuti ngomuposa iyeyo. Chifukwa cha kugwira ntchito ya Khristu, iyeyu adaali pafupifupi kufa. Adaadzipereka osaopa ngakhale kutaya moyo wake kuti azindithandiza pa zimene inu simudathe kukwaniritsa pondithandiza. Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu.