Ndili ndi chimwemwe chodabwitsa chifukwa cha Yesu amene anatiyandikira kwa Mulungu pomwalira pa mtanda. Tsopano nditha kupempherera Akhristu anzanga, komanso anthu amene asokera, kuti Mulungu akwaniritse zofuna zawo monga mmene Iye akufunira.
Mulungu amafuna kuti tonsefe, okhulupirira, tizipemphera mwachangu, kupemphererana. Ndi mwayi waukulu kwambiri umene tili nawo woti tilankhule momasuka pamaso pa Mulungu Wamphamvuyonse ndi mapemphero athu!
Mawu a Mulungu amati: “Ndani adzaimba mlandu osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye wolungamitsa. Ndani adzatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene anafa, ndithu, amenenso anaukitsidwa kwa akufa, amene ali kudzanja lamanja la Mulungu, amenenso amatipempherera.” (Aroma 8:34)
Mulungu akuitana ife tonse Akhristu kuti tizipemphererana.
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.
Ndidafunafuna munthu pakati pao woti amange linga, woti pamaso panga aime pamene padagumuka, kuti ateteze dziko ndi kundipepesa kuti ndisaliwononge. Koma munthu woteroyo sindidampeze.
Muzikometsa ku mizinda kumene ndidakupirikitsirani ku ukapoloko, kuti zonse zizikuyenderani bwino. Muzipempherera mizindayo kwa Chauta, chifukwa choti mizindayo ikakhala pa mtendere, inunso mudzakhala pabwino.
Komanso kunena za ine, sindifuna kuchimwira Chauta, pakuleka kukupemphererani. Ndidzakuphunzitsani zimene zili zabwino ndi zolungama kuti muzizichita.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka. Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
Timathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kumakutchulani m'mapemphero athu.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.
Potsiriza, abale, mutipempherere kuti mau a Ambuye afalikire msanga, ndipo anthu aŵalandire mauwo mwaulemu, monga momwe mudachitira inu.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu. Kwenikweni adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati ndi opembedza Mulungu. Akazi pophunzitsidwa, azikhala chete ndi a mtima wodzichepetsa. Sindilola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa amuna. Mkazi kwake nkukhala chete. Paja Adamu ndiye adaayambira kulengedwa, pambuyo pake Heva. Ndiponso si Adamu amene adaanyengedwa, koma mkaziyo ndiye adaanyengedwa, naphwanya lamulo la Mulungu. Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima. Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza. Zimenezi nzabwino ndi zokondweretsa pamaso pa Mulungu, Mpulumutsi wathu.
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu. Kwenikweni adzikongoletse ndi ntchito zabwino, monga ayenera kuchitira akazi amene amati ndi opembedza Mulungu. Akazi pophunzitsidwa, azikhala chete ndi a mtima wodzichepetsa. Sindilola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kukhala ndi ulamuliro pa amuna. Mkazi kwake nkukhala chete. Paja Adamu ndiye adaayambira kulengedwa, pambuyo pake Heva. Ndiponso si Adamu amene adaanyengedwa, koma mkaziyo ndiye adaanyengedwa, naphwanya lamulo la Mulungu. Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima. Muziŵapempherera mafumu ndi onse amene ali ndi ulamuliro, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, tizitamanda Mulungu pa zonse ndi kumadzilemekeza.
Ndipo anthu adabwera kwa Mose, namuuza kuti, “Pepani tidachimwa poti tidakangana ndi Chauta ndi inu nomwe. Mupemphere kwa Chauta kuti atichotsere njokazi.” Choncho Mose adaŵapempherera anthuwo.
Inu nomwe muthandizane nafe pakutipempherera. Pamenepo anthu ambiri adzathokoza Mulungu m'malo mwathu, chifukwa cha zimene Iye adatichitira mwa kukoma mtima kwake.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera. Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Pemphererani mtendere wa Yerusalemu ponena kuti, “Anthu amene amakukonda iwe Yerusalemu, zinthu ziziŵayendera bwino.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu. Nthaŵi zonse pamene ndikukupemphererani nonsenu, ndimapemphera mokondwa. Ndiyeneradi kuthokoza chifukwa mwakhala mukugwirizana nane ndi kundithandiza kufalitsa Uthenga Wabwino, kuchokera tsiku limene mudayamba kukhulupirira mpaka tsopano.
Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.
Koma Ine ndakupempherera, kuti usaleke kundikhulupirira. Ndipo iweyo utatembenuka mtima, ukaŵalimbitse abale akoŵa.”
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife. Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi. Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo. Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake. Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake. Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.
Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu. Mundipempherere kuti Mulungu anditchinjirize, ndisagwe m'manja mwa anthu osakhulupirira am'Yudeya. Mupempherenso kuti anthu a Mulungu a ku Yerusalemu azilandire ndi manja aŵiri zoperekazi zimene ndatumidwa kuti ndikaŵapatse. Choncho, Mulungu akalola, ndidzafika kwanuko ndili wokondwa, ndipo ndidzasanguluka pocheza nanu.
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse.
Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”
Pulumutsani anthu anu, Inu Chauta, mudalitse amene mudaŵasankha. Mukhale mbusa wao, muŵasamale mpaka muyaya.
Motero Ine ndidzampatsa ulemu woyenerera akuluakulu. Adzagaŵana zofunkha ndi ankhondo amphamvu, popeza kuti adapereka moyo wake mpaka kufa, ndipo adamuyesa mnzao wa anthu ophwanya malamulo. Adasenza machimo a anthu ambiri, ndipo adaŵapempherera ochimwawo kuti akhululukidwe.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Nchifukwa chake sindilekeza kuthokoza Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani m'mapemphero anga, ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni.
Tsono palibe amene angaŵaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo.
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.
Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu.
Ifeyonso muzitipempherera kuti Mulungu atipatse mwai woti tilalike mau ake, makamaka kuti tilengeze chinsinsi chozama chokhudza Khristu. Chifukwa cha kulalika chinsinsichi ndine womangidwa m'ndende muno.
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake. Mtima wanga umayembekeza Chauta kupambana m'mene alonda amayembekezera mbandakucha, kupambanadi m'mene alonda amayembekezera mbandakucha.
Chauta adaona kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe adadabwa kuti palibe wochitapo kanthu. Tsono adapambana ndi mphamvu zakezake, ndipo adadzilimbitsa ndi kulungama kwake.
Pamene ndinkanyamuka kupita ku Masedoniya, paja ndidaakupempha kuti ukhalire ku Efeso. Kuli anthu ena kumeneko amene akuphunzitsa zina zachilendo, ndiye ndikufuna kuti iweyo uŵaletse.
Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.
Tcherani khutu, Inu Chauta, kuti mumve pemphero langa. Mverani kulira kwanga kopemba. Pa tsiku lamavuto ndimakuitanani, pakuti mumayankha mapemphero anga.
Inu Ambuye, Mulungu wathu, mutikomere mtima, ndi kudalitsa zonse zimene timachita, ndithu mudalitse ntchito zonse za manja athu.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa. Koma makamaka, monga mau a Mulungu akunenera, “Ngati mdani wako wamva njala, iwe umpatse chakudya. Ngati wamva ludzu, iwe umpatse madzi akumwa. Ukatero udzamchititsa manyazi kwambiri.” Musagonjere zoipazo, koma gonjetsani zoipa pakuchita zabwino.
Inu ana anga, monga mkazi amamva zoŵaŵa pochira, inenso ndikumva zoŵaŵa chifukwa cha inu mpaka moyo wa Khristu ukhazikike mwa inu.
Nchifukwa chake timakupemphererani nthaŵi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera moyo umene Iye adakuitanirani. Timapemphanso kuti ndi mphamvu zake akulimbikitseni kuchita zabwino zonse zimene mumalakalaka kuzichita, ndiponso ntchito zotsimikizira chikhulupiriro chanu.
Muzikumbukira am'ndende, ngati kuti mukuzunzikira nawo limodzi m'ndendemo. Muzikumbukira ovutitsidwa, pakuti inunso muli ndi thupi.
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.
Pemphero langa likwere kwa Inu ngati lubani, kukweza kwa manja anga kukhale ngati nsembe yamadzulo.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
Chimalizo cha zonse chayandikira. Nchifukwa chake khalani ochenjera ndi odziletsa, kuti muthe kupemphera.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Abale, chimene ndimakhumbitsa ndi mtima wanga wonse, ndipo chimene ndimapempha Mulungu, ndi chakuti Aisraele apulumuke.
Ine ndidzaŵafikitsa ku Ziyoni, phiri langa lopatulika. Ndidzaŵapatsa chimwemwe m'nyumba yanga yopemphereramo. Zopereka zao zootcha ndiponso nsembe zao zinanso ndidzazilandira pa guwa langa. Paja Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”
Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu,
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai.
Ansembe ao omwe adaphedwa ndi lupanga, ndipo akazi ao amasiye sadaŵalole kulira maliro.
Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Nchifukwa chake adaŵauza kuti akadaŵaononga, pakadapanda Mose wosankhidwa wake kuima pamaso pake, ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usaŵaononge.
Pamene adaona makamu a anthu, adaŵamvera chifundo, chifukwa iwo anali olema ndi ovutika ngati nkhosa zopanda mbusa. Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Mulungu ndi mboni yanga. Ndimamtumikira ndi mtima wanga wonse, pakulalika Uthenga Wabwino wonena za Mwana wake. Akudziŵa kuti ndimakukumbukirani kosalekeza m'mapemphero anga onse.
Tikamakupemphererani, nthaŵi zonse timathokoza Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Timathokoza chifukwa tamva kuti mumakhulupirira Khristu Yesu, ndiponso kuti mumakonda anthu onse a Mulungu.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
“Mukamapemphera ndidzakumverani, ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani. Mukaleka kuzunza anzanu, mukasiya kulozana chala, mukaleka kunena zoipa za anzanu,
Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
“Chenjerani kuti musanyoze ndi mmodzi yemwe mwa anaŵa. Ndithu ndikunenetsa kuti angelo ao Kumwamba amakhala pamaso pa Atate anga amene ali Kumwambako nthaŵi zonse.” [
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Wina akamanena kuti, “Ndimakonda Mulungu”, komabe nkumadana ndi mbale wake, ndi wonama ameneyo. Pakuti munthu wosakonda mbale wake amene wamuwona, sangathe kukonda Mulungu amene sadamuwone.
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Ndimakonda Chauta chifukwa amamva mau anga omupemba. Ndidakhulupirirabe ngakhale pamene ndinkati, “Ndazunzika koopsa.” Pamene ndinkachita mantha, ndidati, “Anthu ndi osakhulupirika.” Ndidzambwezera chiyani Chauta pa zabwino zonse zimene adandichitira? Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta, ndi yamtengowapatali pamaso pake. Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni, mwana wa mdzakazi wanu. Inu mwamasula maunyolo anga. Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Ndidzazipereka m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, mu mzinda wa Yerusalemu. Tamandani Chauta! Iye amatchera khutu kuti andimve, nchifukwa chake ndidzampempha nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Ndikukuitanani, Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Tcherani khutu kuti mumve liwu langa pamene ndikupemphera kwa Inu. Anthu oipa akodwe pamodzi mu ukonde wao womwe, koma ine ndipulumuke. Pemphero langa likwere kwa Inu ngati lubani, kukweza kwa manja anga kukhale ngati nsembe yamadzulo.
Koma mngeloyo adamuuza kuti, “Usaope, Zakariya, Mulungu wamva pemphero lako. Mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
Ndipo ngakhale mupemphe, simulandira, chifukwa mumapempha molakwa. Zimene mumapempha, mumafuna kungozimwazira pa zokukondweretsani basi.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Mundidziŵitse njira zanu, Inu Chauta, mundiphunzitse kuchita kufuna kwanu. Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao nchachiphamaso chabe, koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Koma ponena za Ziyoni adzati, “Onse adabadwira kumeneko,” chifukwa Wopambanazonse mwini wake ndiye amene adzaulimbitsa mzindawo.