Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


65 Mau a Mulungu Okhudza Zilankhulo

65 Mau a Mulungu Okhudza Zilankhulo

Ndipo chodabwitsa kwambiri n’chakuti chiyambi cha zilankhulo chili m’Mawu a Mulungu, ndipo uthenga wake wafikira anthu amitundu yosiyanasiyana. Mawu a Mulungu alipo m’Chichewa chomwe ndimalankhula, ndipo izi zimandipatsa mphamvu panthawi yovuta ngati palibe amene akundimvetsa.

Nthawi zina, zimandivuta kwambiri ndipo ndimamva ngati palibe amene akundimvetsa. Koma ndikamatsegula Baibulo, ndimamva Mulungu akulankhula nane m’chinenero changa. Ndimamva mtendere ndi chiyembekezo, ndipo ndimapeza mayankho a mavuto anga.

Baibulo ndi buku lofunika kwambiri pa moyo wanga. Limandiphunzitsa zoyenera kuchita ndi zosayenera kuchita. Ndili ndi mwayi waukulu chifukwa Mulungu, m’chifundo chake, anatipatsa mphatso yolankhulana wina ndi mnzake, kulikonse kumene tili.




Aroma 14:11

Pakuti kwalembedwa, Pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 11:1-9

Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi. Mibadwo ya Semu ndi iyi: Semu anali wa zaka zana limodzi ndipo anabala Aripakisadi, chitapita chigumula zaka ziwiri; ndipo Semu anakhala ndi moyo zaka mazana asanu, atabala Aripakisadi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zisanu nabala Sela; ndipo Aripakisadi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Sela, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Eberi; ndipo Sela anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza zitatu, atabala Eberi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza zinai, nabala Pelegi; ndipo Eberi anakhala ndi moyo zaka mazana anai kudza makumi awiri, atabala Pelegi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Reu; ndipo Pelegi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi zinai, atabala Reu, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo panali pamene anayendayenda ulendo kum'mawa, anapeza chigwa m'dziko la Sinara, ndipo anakhala kumeneko. Ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka makumi atatu kudza ziwiri, nabala Serugi: ndipo Reu anakhala ndi moyo zaka mazana awiri kudza zisanu ndi ziwiri, atabala Serugi, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka makumi atatu, nabala Nahori: ndipo Serugi anakhala ndi moyo zaka mazana awiri, atabala Nahori, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka makumi awiri kudza zisanu ndi zinai, nabala Tera: ndipo Nahori anakhala ndi moyo zaka zana limodzi kudza khumi ndi zisanu ndi zinai, atabala Tera, nabala ana aamuna ndi aakazi. Ndipo Tera anakhala ndi moyo zaka makumi asanu ndi awiri, nabala Abramu, ndi Nahori ndi Harani. Mibadwo ya Tera ndi iyi: Tera anabala Abramu, ndi Nahori, ndi Harani; ndipo Harani anabala Loti. Ndipo anafa Harani pamaso pa atate wake Tera m'dziko la kubadwa kwake, m'Uri wa kwa Akaldeya. Ndipo Abramu ndi Nahori, anadzitengera okha akazi; dzina lake la mkazi wa Abramu ndilo Sarai; ndi dzina lake la mkazi wa Nahori ndilo Milika, mwana wake wa Harani, atate wake wa Milika, ndi atate wake wa Isika. Ndipo ananenana wina ndi wina, Tiyeni tipange njerwa, tiziochetse. Ndipo anali ndi njerwa naziyesa miyala, ndi katondo anayesa matope. Koma Sarai anali wouma; analibe mwana. Ndipo Tera anatenga Abramu mwana wake wamwamuna, ndi Loti mwana wa Harani, mwana wake wamwamuna, ndi Sarai mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abramu; ndipo anatuluka pamodzi nao ku Uri wa kwa Akaldeya kuti amuke ku dziko la Kanani, ndipo anafika ku Harani, nakhala kumeneko. Masiku a Tera anali zaka mazana awiri kudza zisanu; ndipo anafa Tera m'Harani. Ndipo anati, Tiyeni, timange mudzi ndi nsanja, pamutu pake pafikire kumwamba; ndipo tidzipangire ife tokha dzina kuti tisabalalike pa dziko lonse lapansi. Ndipo Yehova anatsikira kudzaona mudzi ndi nsanja imene analinkumanga ana a anthu. Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chao chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kuchita. Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake. Ndipo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi, ndipo analeka kumanga mudzi. Chifukwa chake anatcha dzina lake Babele; pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:7

Mlomo wangwiro suyenera chitsiru; ngakhale mlomo wonama suyenera kalonga ndi pang'ono ponse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 11:6-7

Ndipo Yehova anati, Taonani, anthu ali amodzi, ndipo onse ali nacho chinenedwe chao chimodzi; ndipo ichi ayamba kuchita: ndipo tsopano palibe kanthu kakuletsedwa nao kamene akafuna kuchita. Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 81:5

Anachiika chikhale mboni kwa Yosefe, pakutuluka iye kudziko la Ejipito. Komwe ndinamva chinenedwe chosadziwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:3-4

Palibe chilankhulidwe, palibe mau; liu lao silimveka. Muyeso wao wapitirira pa dziko lonse lapansi, ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:49

Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:11

Iai, koma ndi anthu a milomo yachilendo, ndi a lilime lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 33:19

Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilime lachibwibwi, limene iwe sungalimve.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:39-40

Chifukwa chake, abale anga, funitsitsani kunenera, ndipo musaletse kulankhula malilime. Iye wakulankhula lilime, adzimangirira yekha, koma iye wakunenera amangirira Mpingo. Koma zonse zichitike koyenera ndi kolongosoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:6

Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 3:4-5

Ndipo wolalikira anafuulitsa, kuti, Akulamulirani inu anthu, mitundu ya anthu a manenedwe osiyana, kuti pakumva inu mau a lipenga, chitoliro, zeze, sansi, chisakasa, ngoli, ndi zoimbitsa zilizonse, mugwadire ndi kulambira fano lagolide adaliimika mfumu Nebukadinezara;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:1-12

Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa. Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero. Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa? Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sakhoza kutulutsa okoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 5:25-28

Ndipo lemba lolembedwa ndi ili: MENE MENE TEKEL UFARSIN. Kumasulira kwake kwa mau awa ndi uku: MENE, Mulungu anawerenga ufumu wanu, nautha. TEKEL, Mwayesedwa pamiyeso, nimupezeka mwaperewera. PERES, ufumu wanu wagawika, nuperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:17

Ndipo zizindikiro izi zidzawatsata iwo akukhulupirira: m'dzina langa adzatulutsa ziwanda; adzalankhula ndi malankhulidwe atsopano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:4-6

Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa. Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota. Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu. Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero. Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi. Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana. Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera. Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi m'Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona; nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe. Koma anali m'Yerusalemu okhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera kumtundu uliwonse pansi pa thambo. Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m'chilankhulidwe chake cha iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:28

Muno mulibe Myuda, kapena Mgriki, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:11

pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:46

Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malilime, ndi kumkuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:29

Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:6

Ndipo pamene Paulo anaika manja ake pa iwo, Mzimu Woyera anadza pa iwo; ndipo analankhula ndi malilime, nanenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:10

ndi kwa wina machitidwe a mphamvu; ndi kwa wina chinenero; ndi kwa wina chizindikiro cha mizimu; kwa wina malilime a mitundumitundu; ndi kwa wina mamasulidwe a malilime.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:17

Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:16

Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, ndipo ndidzafotokozera zonse anazichitira moyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:28

Ndipotu Mulungu anaika ena mu Mpingo, poyamba atumwi, achiwiri aneneri, achitatu aphunzitsi, pamenepo zozizwa, pomwepo mphatso za machiritso, mathandizo, maweruziro, malilime a mitundumitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:1

Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:21

Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:2

Pakuti iye wakulankhula lilime salankhula ndi anthu, koma ndi Mulungu; pakuti palibe munthu akumva; koma mumzimu alankhula zinsinsi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:11

ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:6

kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:5

Ndipo ndifuna inu nonse mulankhule malilime, koma makamaka kuti mukanenere; ndipo wakunenera aposa wakulankhula malilime, akapanda kumasulira, kuti Mpingo ukalandire chomangirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:10-11

Ilipo, kaya, mitundu yambiri yotere ya mau pa dziko lapansi, ndipo palibe kanthu kasowa mau. Chifukwa chake, ngati sindidziwa mphamvu ya mauwo ndidzakhala kwa iye wolankhulayo wakunja, ndipo wolankhulayo adzakhala wakunja kwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:11

akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:18-19

Ndiyamika Mulungu kuti ndilankhula malilime koposa inu nonse; koma mu Mpingo ndifuna kulankhula mau asanu ndi zidziwitso changa, kutinso ndikalangize ena, koposa kulankhula mau zikwi m'lilime.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:38-39

Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:34-37

Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima. Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chake chabwino, ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'chuma chake choipa. Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:21-22

Kwalembedwa m'chilamulo, Ndi anthu a malilime ena ndipo ndi milomo ina ndidzalankhula nao anthu awa; ndipo kungakhale kutero sadzamva Ine, anena Ambuye. Chotero malilime akhala ngati chizindikiro, si kwa iwo akukhulupirira, koma kwa iwo osakhulupirira; koma kunenera sikuli kwa iwo osakhulupirira, koma kwa iwo amene akhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:26-28

Nanga chiyani tsono, abale? Pamene musonkhana, yense ali nalo salimo, ali nacho chiphunzitso, ali nalo vumbulutso, ali nalo lilime, ali nacho chimasuliro. Muchite zonse kukumangirira. Ngati wina alankhula lilime, achite ndi awiri, koma oposa atatu iai, ndipo motsatana; ndipo mmodzi amasulire. Koma ngati palibe womasulira, akhale chete mu Mpingo, koma alankhule ndi iye yekha, ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 7:9

Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m'manja mwao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:30

Pakamwa pa wolungama palankhula zanzeru, ndi lilime lake linena chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 10:11

Ndipo ananena nane, Uyenera iwe kuneneranso pa anthu ndi mitundu, ndi manenedwe, ndi mafumu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:3

Anola lilime lao ngati njoka; pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:6

Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nao Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:10

Ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ndinazunzika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 109:2

pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira; anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:23

Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake asunga moyo wake kumavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 4:6

Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:26-35

Koma mngelo wa Ambuye analankhula ndi Filipo, nanena, Nyamuka, nupite mbali ya kumwera, kutsata njira yotsika kuchokera ku Yerusalemu kunka ku Gaza; ndiyo ya chipululu. Ndipo ananyamuka napita; ndipo taona munthu wa ku Etiopiya, mdindo wamphamvu wa Kandake, mfumu yaikazi ya Aetiopiya, ndiye wakusunga chuma chake chonse, amene anadza ku Yerusalemu kudzapemphera; ndipo analinkubwerera, nalikukhala pa galeta wake, nawerenga mneneri Yesaya. Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike kugaleta uyu. Ndipo Saulo anapasula Mpingo, nalowa nyumba ndi nyumba, nakokamo amuna ndi akazi, nawaika m'ndende. Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga? Koma anati, Ndingathe bwanji, popanda munthu wonditsogolera ine? Ndipo anapempha Filipo akwere nakhale naye. Koma palembo pamene analikuwerengapo ndipo: Ngati nkhosa anatengedwa kukaphedwa, ndi monga mwanawankhosa ali duu pamaso pa womsenga, kotero sanatsegula pakamwa pake. M'kuchepetsedwa kwake chiweruzo chake chinachotsedwa; mbadwo wake adzaubukitsa ndani? Chifukwa wachotsedwa kudziko moyo wake. Ndipo mdindoyo anayankha Filipo, nati, Ndikupempha, mneneri anena ichi za yani? Za yekha, kapena za wina? Ndipo Filipo anatsegula pakamwa pake, nayamba pa lembo ili, nalalikira kwa iye Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:44-48

Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalmo. Ndipo anawatsegulira mitima yao, kuti adziwitse malembo; ndipo anati kwa iwo, Kotero kwalembedwa, kuti Khristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu; ndi kuti kulalikidwe m'dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu. Inu ndinu mboni za izi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m'dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: Ndipo onani, panali chivomezi chachikulu; pakuti mngelo wa Ambuye anatsika Kumwamba, nafika kukunkhuniza mwalawo, nakhala pamwamba pake. ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 11:1

Ndipo dziko lapansi linali la chinenedwe chimodzi ndi chilankhulidwe chimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 11:7

Tiyeni, titsike, pomwepo tisokoneze chinenedwe chao, kuti wina asamvere chinenedwe cha mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 11:9

Chifukwa chake anatcha dzina lake Babele; pakuti kumeneko Yehova anasokoneza chinenedwe cha dziko lonse lapansi; kuyambira pamenepo Yehova anabalalitsa iwo pa dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:8

Ndipo nanga ife timva bwanji, yense m'chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 1:4

anyamata opanda chilema, a maonekedwe okoma, a luso la nzeru zonse, ochenjera m'kudziwa, a luntha lakuganizira, okhoza kuimirira m'chinyumba cha mfumu; ndi kuti awaphunzitse m'mabuku, ndi manenedwe a Ababiloni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 50:4

Ambuye Yehova wandipatsa Ine lilime la ophunzira, kuti ndidziwe kunena mau akuchirikiza iye amene ali wolema. Iye andigalamutsa m'mawa ndi m'mawa, nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 13:24

ndi ana ao analankhula mwina Chiasidodi, osadziwitsa kulankhula Chiyuda, koma monga umo amalankhula mtundu wao uliwonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 12:6

pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kutchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordani; ndipo anagwa a Efuremu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 10:31

Amenewa ndi ana a Semu, monga mwa mabanja ao, mwa zinenedwe zao, m'maiko ao, m'mitundu yao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 4:7

Ndipo masiku a Arita-kisereksesi Bisilamu, Mitiredati, Tabeele, ndi anzao otsala, analembera kwa Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya; ndi chilembedwe chake cha kalatayo anamlemba m'Chiaramu, namsanduliza m'Chiaramu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 18:26

Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, ndi Sebina, ndi Yowa, anati kwa kazembeyo, Mulankhule ndi anyamata anu m'Chiaramu; popeza tichimva ichi; musalankhule nafe m'Chiyuda, chomveka ndi anthu okhala palinga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Chauta Wamphamvuyonse, ulemerero ndi ulemu zikhale kwa Inu! Mulungu wanga Wamuyaya, mundiphunzitse tsiku ndi tsiku kulankhula mawu ogwirizana ndi mawu anu kuti ndikhale ndi chilankhulo cha chikhulupiriro, chifukwa kudzera mmenemo nditha kulankhulana nanu. Mundithandize kuyenda motsatira zimene ndimakhulupirira kuti chikhulupiriro changa chisakhale chosalankhula, koma kuti ndilankhule ndi phiri ndipo lisunthe, chifukwa ndithudi palibe vuto kapena cholepheretsa chilichonse chachikulu kuposa Inu. Ambuye, mundiphunzitse tsiku lililonse kukhala wonyamula ulemerero wanu kwa onse amene ali pafupi ndi ine ndipo kulikonse kulankhula chinenero chakumwamba kuti ndikwanitse kulankhula chinenero cha kusintha, chikhulupiriro ndi chipambano. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa