Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


104 Mauthenga a Mulungu Okhudza Golide

104 Mauthenga a Mulungu Okhudza Golide

Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, taganizirani za golide. Limayikidwa pamoto wamphamvu kuti lisungunuke, kuchotsa zoipa zonse. Koma motowo suyenera kukhala wamphamvu kwambiri moti ungawononge golidelo. Kenako, limakhomeredwa ndi nyundo, pang'onopang'ono, mpaka litakhala lokongola komanso lowala.

M'buku la Yobu 23:10, Baibulo limati: "Koma Iye adziwa njira yanga; Nditayesedwa ndidzatuluka ngati golide." Nthawi zina zimakhala zovuta kumvetsa, koma ifenso tili ngati golidelo. Pali zinthu m'miyoyo yathu zomwe ziyenera "kuwotchedwa" pamoto, kuti kuwala kwa Mulungu komwe kuli mkati mwathu kuwonekere. Sikuti tiyenera kudzitukumula, koma tiziwala chifukwa cha ubwino wa Mulungu.




Masalimo 119:127

Chifukwa chake ndikonda malamulo anu koposa golide, inde golide woyengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:32

Zitseko ziwiri zomwe zinali za mtengo wa azitona, anasemapo ngati akerubi ndi migwalangwa ndi maluwa oti gada, nawakuta ndi golide; inde anakutanso ndi golide akerubi ndi migwalangwayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:10

Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 13:12

Ndipo ndidzachepsa anthu koposa golide, ngakhale anthu koposa golide weniweni wa ku Ofiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:24

Ndipo ulikute ndi golide woona ndi kulipangira mkombero wagolide pozungulira pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 2:11-12

Dzina la wakuyamba Pisoni: umenewo ndiwo wozungulira dziko lonse la Havila, m'mene muli golide; golide wa dziko ali wabwino; ndimonso muli bedola ndi mwala wasohamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hagai 2:8

Siliva ndi wanga, ya golide ndi wanga, ati Yehova wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 2:32

Fano ili tsono, mutu wake unali wagolide wabwino, chifuwa chake ndi manja ake zasiliva, mimba yake ndi chuuno chake zamkuwa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 13:2

Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:3

Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golide ali ndi ng'anjo; koma Yehova ayesa mitima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 24:22

Ndipo panali zitatha kumwa ngamira, munthuyo anatenga mphete yagolide ya kulemera kwake sekeli latheka, ndi zingwinjiri ziwiri za m'manja ake, kulemera kwake masekeli khumi a golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:18

ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:21

Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; chitseko chilichonse pa chokha cha ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda nla golide woyengeka, ngati mandala openyekera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 4:1

Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika; miyala ya malo opatulika yakhuthulidwa pa malekezero a makwalala onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 24:53

Ndipo mnyamatayo anatulutsa zokometsera zasiliva ndi zagolide, ndi zovala, nampatsa Rebeka: ndipo anapatsa za mtengo wapatali kwa mlongo wake ndi amake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 3:22

koma mkazi yense adzafunse mnzake, ndi mlendo wokhala m'nyumba mwake, ampatse zokometsera zasiliva, ndi zokometsera zagolide, ndi zovala; ndipo mudzaveke nazo ana anu aamuna ndi aakazi; ndipo mudzafunkhe za Aejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 11:2

Lankhula tsopano m'makutu a anthu, kuti mwamuna yense apemphe kwa mnzake, ndi mkazi yense kwa mnzake, zokometsera zasiliva ndi zagolide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:35-36

Ndipo ana a Israele anachita monga mwa mau a Mose; napempha Aejipito zokometsera zasiliva, ndi zagolide, ndi zovala. Ndipo Yehova anapatsa anthu chisomo pamaso pa Aejipito, ndipo sanawakanize. Ndipo anawafunkhira Aejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:3

Ndipo choperekacho uchilandire kwa iwo ndi ichi: golide, ndi siliva, ndi mkuwa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:11

Ndipo ulikute ndi golide woona, ulikute m'kati ndi kubwalo, nulipangire mkombero wagolide pozungulira pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:17-18

Ndipo uzipanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu. Uzipanganso akerubi awiri agolide; uwasule mapangidwe ake, pa mathungo ake awiri a chotetezerapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 28:36

Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 32:2-4

Ndipo Aroni ananena nao, Thyolani mphete zagolide zili m'makutu a akazi anu, a ana anu aamuna ndi aakazi, ndi kubwera nazo kwa ine. Ndipo anatenga mwanawang'ombe anampangayo, namtentha ndi moto, nampera asalale, namwaza pamadzi, namwetsako ana a Israele. Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere? Ndipo Aroni anati, Asapse mtima mbuye wanga; udziwa anthuwa kuti akhumba choipa. Pakuti ananena nane, Tipangireni milungu yakutitsogolera; popeza Mose uyu, munthuyu anatikweza kuchokera m'dziko la Ejipito, sitidziwa chomwe chamgwera. Ndipo ndinanena nao, Aliyense ali naye golide amthyole; ndipo anandipatsa; ndipo ndinachiponya m'moto, ndimo anatulukamo mwanawang'ombe uyu. Ndipo pamene Mose anaona kuti anthu anamasuka, popeza Aroni adawamasula kuti awatonze adani ao, Mose anaima pa chipata cha chigono, nati, Onse akuvomereza Yehova, adze kwa ine. Pamenepo ana amuna onse a Levi anasonkhana kwa iye. Ndipo ananena nao, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Yense amange lupanga lake m'chuuno mwake, napite, nabwerere kuyambira chipata kufikira chipata, pakati pa chigono, naphe yense mbale wake, ndi yense bwenzi lake, ndi yense mnansi wake. Ndipo ana a Levi anachita monga mwa mau a Mose; ndipo adagwa tsiku lija anthu ngati zikwi zitatu. Popeza Mose adati, Mdzazireni Yehova manja anu lero, pakuti yense akhale mdani wa mwana wake wamwamuna, ndi mdani wa mbale wake; kuti akudalitseni lero lino. Ndipo anthu onse anathyola mphete zagolide zinali m'makutu mwao, nabwera nazo kwa Aroni Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti Mose anati kwa anthu, Mwachimwa kuchimwa kwakukulu; koma ndikwera kwa Yehova tsopano, kapena ndidzachita chotetezera uchimo wanu. Ndipo Mose anabwerera kunka kwa Yehova, nati, Ha! Pepani, anthu awa anachimwa kuchimwa kwakukulu, nadzipangira milungu yagolide. Koma tsopano, kapena mudzakhululukira kuchimwa kwao; koma ngati mukana, mundifafanizetu, kundichotsa m'buku lanu limene munalembera, Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m'buku langa. Ndipo tsopano, muka, tsogolera anthu kunka nao kumene ndinakuuza; taona, mthenga wanga akutsogolera; koma tsiku lakuwazonda Ine ndidzawalanga chifukwa cha kuchimwa kwao. Ndipo Yehova anakantha anthu, chifukwa anapanga mwanawang'ombe amene Aroni anapanga. Ndipo anazilandira ku manja ao, nachikonza ndi chozokotera, nachiyenga mwanawang'ombe; ndipo anati, Siyi milungu yako, Israele, imene inakukweza kuchokera m'dziko la Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:2

ndipo analikuta ndi golide woona m'kati ndi kunja, nalipangira mkombero wa golide pozungulira pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:6

Ndipo anapanga chotetezerapo cha golide woona; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:16

Anapanganso zipangizo za gomelo, mbale zake, ndi zipande zake, ndi mitsuko yake, ndi zikho zake zakuthira nazo, za golide woona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 37:23-24

Ndipo anapanga nyali zake zisanu ndi ziwiri ndi mbano zake, ndi zoolera zake, za golide woona. Anachipanga ichi ndi zipangizo zake zonse za talente wa golide woona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 8:9

Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 7:14

chipande chimodzi chagolide cha masekeli khumi, chodzala ndi chofukiza;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 31:50-51

Ndipo tabwera nacho chopereka cha Yehova, yense chimene anachipeza, zokometsera zagolide, unyolo, zikwinjiri, mphete zosindikizira, nsapule, ndi mkanda, kuchita chotetezera moyo wathu pamaso pa Yehova. Ndipo Mose ndi Eleazara wansembe analandira golideyo kwa iwowo, ndizo zokometsera zonse zokonzeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:25

Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:13

ndipo zitachuluka ng'ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitachulukanso siliva wanu ndi golide wanu, zitachulukanso zonse muli nazo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 17:17

Ndipo asadzichulukitsire akazi, kuti ungapatuke mtima wake; kapena asadzichulukitsire kwambiri siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 6:19

Koma siliva yense, ndi golide yense, ndi zotengera za mkuwa ndi chitsulo zikhala chopatulikira Yehova; zilowe m'mosungira chuma cha Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 7:21

pamene ndinaona pazofunkha malaya abwino a ku Babiloni, ndi masekeli mazana awiri a siliva, ndi chikute chagolide, kulemera kwake masekeli makumi asanu, ndinazikhumbira ndi kuzitenga; ndipo taonani, ndazibisa m'nthaka pakati pa hema wanga, ndi siliva pansi pakepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 8:24-26

Gideoni anatinso kwa iwo, Mundilole ndipemphe kanthu kamodzi kwa inu, mundipatse aliyense maperere mwa zofunkha zanu; pakuti anali nao maperere agolide, pokhala anali Aismaele. Ndipo anayankha, Kupereka tiwapereka; nayalapo chovala, naponyamo yense maperere a mwa zofunkha zao. Ndipo kulemera kwake kwa maperere agolide adawapempha ndiko masekeli chikwi chimodzi ndi mazana asanu ndi awiri; osawerenga mphande, ndi zitunga ndi zovala zachibakuwa za pa mafumu a ku Midiyani, osawerenganso maunyolo okhala pa makosi a ngamira zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 6:8

ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaletapo; nimuike zokometsera zagolide, zimene muzipereka kwa Iye ngati nsembe yopalamula, m'bokosi pambali pake; nimulitumize lichoke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 8:7

Ndipo Davide anatenga zikopa zagolide zinali ndi anyamata a Hadadezere, nabwera nazo ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:20-22

Ndipo m'kati mwa chipindacho, m'litali mwake munali mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri, kupingasa kwake mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake mikono makumi awiri; ndipo anamukuta ndi golide wayengetsa, nakutanso guwa la nsembe ndi matabwa amkungudza. Momwemo Solomoni anakuta m'kati mwa nyumba ndi golide woyengetsa, natambalika maunyolo agolide chakuno cha chipinda chamkati, namukuta ndi golide. Ndipo nyumba yonse anaikuta ndi golide mpaka adatha nyumba yonse, ndi guwa lonse la nsembe linali chakuno cha chipinda chamkati analikuta ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:30

Ndipo anakuta ndi golide pansi pake pa nyumba m'katimo ndi kunja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 7:48-50

Ndipo Solomoni anapanga zipangizo zonse za m'nyumba ya Yehova: guwa la nsembe lagolide, ndi gome lagolide loikapo mikate yoonekera; ndi zoikapo nyali za golide woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, chakuno cha chipinda chamkati, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolide; Ndipo makomo onse ndi mphuthu zonse zinali zaphwamphwa maonekedwe ake, ndipo zenera limodzi linapenyana ndi linzake mizere itatu. ndi zikho, ndi zozimira nyali, ndi mbale, ndi zipande, ndi zopalira moto za golide woyengetsa, ndi zomangira zitseko zagolide, za zitseko za chipinda cha m'katimo, malo opatulika kwambiri, ndiponso za zitseko za nyumba ya Kachisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 9:28

Ndipo iwo anafika ku Ofiri, natengako golide matalente mazana anai mphambu makumi awiri, nafika naye kwa mfumu Solomoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:2

Nafika ku Yerusalemu ndi ulendo wake waukulu, ndi ngamira zakunyamula zonunkhira, ndi golide wambiri, ndi timiyala ta mtengo wapatali; ndipo atafika kwa Solomoni anakamba naye zonse za m'mtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:10-11

Ndipo mkaziyo ananinkha mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zaunyinji ndi timiyala ta mtengo wapatali; sunafikanso unyinji wotero wa zonunkhira wolingana ndi uja mfumu yaikazi ya ku Sheba inapereka kwa mfumu Solomoni. Ndipo zombo za Hiramu zotengera golide ku Ofiri zinatenganso ku Ofiri mitengo yambiri yambawa, ndi timiyala ta mtengo wapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:14-18

Tsono kulemera kwake kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi kunali matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide. Osawerenganso winayo wa anthu a malonda oyendayenda, ndi wa amalonda ena, ndi wa mafumu onse a Arabiya, ndi wa akazembe onse a madera. Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri zagolide wonsansantha, chikopa chimodzi chinapangidwa ndi masekeli mazana asanu ndi limodzi. Ndi malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, lihawo limodzi linapangidwa ndi miyeso ya mina itatu ya golide; ndipo mfumu inazisungira zonse m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni. Ndipo mfumu inapanga mpando waukulu wachifumu waminyanga, naukuta ndi golide woyengetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:21-22

Ndipo zikho zomwera zonse za mfumu Solomoni zinali zagolide, ndi zotengera zonse za nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide yekhayekha, panalibe zasiliva, pakuti siliva anangoyesedwa opanda pake masiku onse a Solomoni. Popeza mfumu inali nazo panyanja zombo za ku Tarisisi, pamodzi ndi zombo za Hiramu; zombo za ku Tarisisi zinafika kamodzi zitapita zaka zitatu, zili nazo golide, ndi siliva, ndi minyanga, ndi apusi, ndi mbalame za zitsukwa zazitali za mawangamawanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 12:28

Potero mfumu inakhala upo, napanga anaang'ombe awiri agolide, nati kwa iwo, Kukulemetsani kukwera ku Yerusalemu; tapenyani Aisraele inu milungu yanu, imene inakutulutsani m'dziko la Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:2-7

Ndi mphamvu yanga yonse tsono ndakonzeratu nyumba ya Mulungu wanga, golide wa zija zagolide ndi siliva wa zija zasiliva, ndi mkuwa wa zija zamkuwa, chitsulo cha zija zachitsulo, ndi mtengo wa zija zamtengo, miyala yaberulo, ndi miyala yoikika, miyala yokometsera, ndi ya mawangamawanga, ndi miyala ya mtengo wake ya mitundumitundu ndi miyala yansangalabwe yochuluka. Ndipo Davide anati kwa khamu lonse, Mulemekeze tsono Yehova Mulungu wanu. Ndi khamu lonse linalemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao, nawerama, nalambira Yehova, ndi mfumu. Ndipo anamphera Yehova nsembe, napereka nsembe zopsereza kwa Yehova m'mawa mwake mwa tsiku lija, ndizo ng'ombe chikwi chimodzi, nkhosa zamphongo chikwi chimodzi, ndi anaankhosa chikwi chimodzi, pamodzi ndi nsembe zao zothira, ndi nsembe zochuluka za Aisraele onse: nadya namwa pamaso pa Mulungu tsiku lomwelo ndi chimwemwe chachikulu. Ndipo analonga ufumu Solomoni mwana wa Davide kachiwiri, namdzozera Yehova akhale kalonga, ndi Zadoki akhale wansembe. Momwemo Solomoni anakhala pa mpando wachifumu wa Yehova, ndiye mfumu m'malo mwa Davide atate wake, nalemerera, namvera iye Aisraele onse. Ndi akulu onse, ndi amuna amphamvu onse, ndi ana amuna onse omwe a mfumu Davide, anagonjeratu kwa Solomoni mfumu. Ndipo Yehova anakuza Solomoni kwakukulu pamaso pa Aisraele onse, nampatsa ulemerero wachifumu, wakuti, asanakhale iyeyu, panalibe mfumu ya Israele inali nao wotero. Momwemo Davide mwana wa Yese adakhala mfumu ya Aisraele onse. Ndipo nthawi yoti anakhala mfumu ya Israele ndiyo zaka makumi anai; zaka zisanu ndi ziwiri anakhala mfumu m'Hebroni, ndi zaka makumi atatu anakhala mfumu m'Yerusalemu. Nafa atakalamba bwino, wochuluka masiku, zolemera, ndi ulemerero; ndi Solomoni mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake. Zochita mfumu Davide tsono, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Samuele mlauli, ndi m'buku la mau a Natani mneneri, ndi m'buku la mau a Gadi mlauli; Ndiponso popeza ndikondwera nayo nyumba ya Mulungu wanga, chuma changachanga cha golide ndi siliva ndili nacho ndichipereka kunyumba ya Mulungu wanga, moonjezera ndi zonse ndazikonzeratu nyumba yopatulikayo; pamodzi ndi za ufumu wake wonse, ndi mphamvu yake, ndi za nthawizo zidampitira iye, ndi Israele, ndi maufumu onse a maiko. ndicho matalente zikwi zitatu za golide, golide wa Ofiri; ndi matalente zikwi zisanu ndi ziwiri a siliva woyengetsa, kumamatiza nazo makoma a nyumbazi; golide wa zija zagolide, ndi siliva wa zija zasiliva, ndi za ntchito zilizonse akuzipanga manja a amisiri. Ndani uyo afuna mwini kudzipatulira kwa Yehova lero lino? Pamenepo akulu a nyumba za makolo, ndi akulu a mafuko a Israele, ndi akulu a zikwi ndi a mazana pamodzi ndi iwo oyang'anira ntchito ya mfumu, anapereka mwaufulu, napereka ku utumiki wa nyumba ya Mulungu golide matalente zikwi zisanu, ndi madariki zikwi khumi; ndi siliva matalente zikwi khumi, ndi mkuwa matalente zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu, ndi chitsulo matalente zikwi zana limodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 1:15

Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golide zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza ichuluke ngati mikuyu yokhala kuchidikha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 3:4-6

Ndi chipinda cholowera chinali kukhomo kwa nyumba, m'litali mwake monga mwa kupingasa kwa nyumba munali mikono makumi awiri, ndi msinkhu wake zana limodzi mphambu makumi awiri; ndipo analikuta m'katimo ndi golide woona. M'nyumba yaikulu tsono anatchinga ndi mitengo yamlombwa, imene anaikuta ndi golide wabwino, nalembapo ngati migwalangwa ndi maunyolo. Ndipo anakuta nyumba ndi miyala ya mtengo wake; ndi golide wake ndiye golide wa Paravaimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 4:20-22

ndi zoikapo nyali ndi nyali zake za golide woona, zakuunikira monga mwa chilangizo chake chakuno cha chipinda chamkati; ndi maluwa, ndi nyali, ndi mbano zagolide, ndiwo golide wangwiro; ndi zozimira nyali, ndi mbale zowazira, ndi zipande, ndi mbale za zofukiza za golide woona; ndi kunena za polowera m'nyumba, zitseko zake za m'katimo za malo opatulika kwambiri, ndi zitseko za nyumbayi, ndiyo Kachisi, zinali zagolide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 9:9

Ndipo mkaziyo anapatsa mfumu matalente a golide zana limodzi mphambu makumi awiri, ndi zonunkhira zambiri ndithu, ndi timiyala ta mtengo wake; panalibe zonunkhira zina zonga zija mfumu yaikazi ya ku Sheba anapatsa mfumu Solomoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 9:13-17

Kulemera kwake tsono kwa golide anafika kwa Solomoni chaka chimodzi ndiko matalente mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza asanu ndi limodzi a golide; osawerenga uja anabwera naye amalonda oyendayenda, ndi amalonda ena; ndipo mafumu onse a Arabiya, ndi akazembe a dziko, anadza naye golide ndi siliva kwa Solomoni. Ndipo mfumu Solomoni anapanga zikopa mazana awiri za golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera golide wonsansantha masekeli mazana awiri. Napanganso malihawo mazana atatu a golide wonsansantha, chikopa chimodzi chinathera masekeli mazana atatu a golide; ndipo mfumu inazilonga m'nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni. Mfumu inapanganso mpando wachifumu waukulu wa minyanga, naukuta ndi golide woona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 24:14

Ndipo ataitsiriza, anabwera nazo ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, napanga nazo zipangizo za nyumba ya Yehova, zipangizo za kutumikira nazo, ndi kupereka nsembe nazo, ndi zipande, ndi zipangizo za golide ndi siliva. Ndipo anapereka kosalekeza nsembe zopsereza m'nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 1:4

Ndipo aliyense wotsala pamalo paliponse agonerapo iye, anthu a kumalo kwake amthandize ndi siliva, ndi golide, ndi zoweta, ndi chuma, pamodzi ndi nsembe yaufulu ya kwa nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 8:25-27

ndi kuwayesera siliva, ndi golide, ndi zipangizo, ndizo chopereka cha kwa nyumba ya Mulungu wathu, chimene mfumu, ndi aphungu ake, ndi akalonga ake, ndi Aisraele onse anali apawa, adapereka. Ndipo ndinawayesera m'dzanja mwao matalente a siliva mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu, ndi zipangizo zasiliva matalente zana limodzi, ndi zikho zagolide makumi awiri za madariki chikwi chimodzi, ndi zipangizo ziwiri za mkuwa wabwino wonyezimira wokhumbika ngati golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 7:70-71

Ndipo ena a akulu a nyumba za makolo anapereka kuntchito. Kazembeyo anapereka kuchuma madariki agolide chikwi chimodzi, mbale zowazira makumi asanu, malaya a ansembe makumi atatu. Enanso a akulu a nyumba za makolo anapereka kuchuma cha ntchitoyi, madariki agolide zikwi makumi awiri, ndi miyeso ya mina ya siliva zikwi ziwiri mphambu mazana awiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Estere 1:6

panali nsalu zolenjeka zoyera, zabiriwiri, ndi zamadzi, zomangika ndi zingwe za thonje labafuta, ndi lofiirira, pa zigwinjiri zasiliva, ndi nsanamira zansangalabwi; makama anali a golide ndi siliva pa mayalidwe a miyala yofiira, ndi yoyera, ndi yoyezuka, ndi yakuda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 22:24-25

Ndipo utaye chuma chako kufumbi, ndi golide wa ku Ofiri ku miyala ya kumitsinje. Ndipo Wamphamvuyonse adzakhala chuma chako, ndi ndalama zako zofunika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 28:15-19

Silipezeka ndi golide, sayesapo siliva mtengo wake. Sailinganiza ndi golide wa Ofiri, ndi sohamu wa mtengo wake wapatali kapena safiro. Golide ndi krustalo sizilingana nayo; ndi kusinthana kwake, siisinthanika ndi zisambiro za golide woyengetsa. Korali kapena ngale sizikumbukikapo. Mtengo wake wa nzeru uposa wa korali wofiira. Topazi wa Kusi sufanana nayo, sailinganiza ndi golide wolongosoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 45:9

Mwa omveka anu muli ana akazi a mafumu; ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu wovala golide wa ku Ofiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:13

Pogona inu m'makola a zoweta, mukhala ngati mapiko a njiwa okulira ndi siliva, ndi nthenga zake zokulira ndi golide woyenga wonyezimira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:14-15

pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golide woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:10

Landirani mwambo wanga, si siliva ai; ndi nzeru kopambana ndi golide wosankhika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:19

Chipatso changa chiposa golide, ngakhale golide woyengeka; phindu langa liposa siliva wosankhika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:16

Kodi kulandira nzeru sikupambana ndi golide, kulandira luntha ndi kusankhika koposa siliva?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:12

Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 2:8

ndinakundikanso siliva ndi golide ndi chuma cha mafumu ndi madera a dziko; ndinaitanitsa amuna ndi akazi akuimba ndi zokondweretsazo za ana a anthu, ndizo zoimbira za mitundumitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nyimbo ya Solomoni 1:11

Tidzakupangira nkhata zagolide ndi njumu zasiliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:7

Dziko lao ladzala siliva ndi golide, ngakhale chuma chao nchosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magaleta ao ngosawerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:20

Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 60:9

Zoonadi, zisumbu zidzandilindira Ine; zidzayamba ndi ngalawa za Tarisisi kutenga ana ako amuna kutali, golide wao ndi siliva wao pamodzi nao, chifukwa cha dzina la Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israele, popeza Iye wakukometsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 60:17

M'malo mwa mkuwa ndidzatenga golide, ndi m'malo mwa chitsulo ndidzatenga siliva, ndi m'malo mwa mtengo ndidzatenga mkuwa, ndi m'malo mwa miyala ndidzatenga chitsulo; ndidzakuikira akapitao a mtendere, ndi oyang'anira ntchito a chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:9

Abwera ndi siliva wa ku Tarisisi, wosulasula wopyapyala ndi golide wa ku Ufazi, ntchito ya mmisiri ndi manja a woyenga; zovala zao ndi nsalu ya madzi ndi yofiirira; zonsezi ndi ntchito za muomba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:7

Babiloni wakhala chikho chagolide m'dzanja la Yehova, amene analedzeretsa dziko lonse lapansi; amitundu amwa vinyo wake; chifukwa chake amitundu ali ndi misala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 4:1-2

Ha! Golide wagugadi; golide woona woposa wasandulika; miyala ya malo opatulika yakhuthulidwa pa malekezero a makwalala onse. Manja a akazi achisoni anaphika ana aoao; anali chakudya chao poonongeka mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga. Yehova wakwaniritsa kuzaza kwake, watsanulira ukali wake; anayatsa moto m'Ziyoni, unanyambita maziko ake. Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirire, ngakhale onse okhala kunja kuno, kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu. Ndicho chifukwa cha machimo a aneneri ndi mphulupulu za ansembe ake, amene anakhetsa mwazi wa olungama pakati pake. Asochera m'makwalala ngati akhungu, aipsidwa ndi mwazi; anthu sangakhudze zovala zao. Amafuula kwa iwo, Chokani, osakonzeka inu, chokani, chokani, musakhudze kanthu. Pothawa iwo ndi kusochera, anthu anati mwa amitundu, sadzagoneranso kuno. Mkwiyo wa Yehova unawalekanitsa, sadzawasamaliranso; iwo sanalemekeze ansembe, sanakomere mtima akulu. Maso athu athedwa, tikali ndi moyo, poyembekeza thandizo chabe; kudikira tinadikira mtundu wosatha kupulumutsa. Amalondola mapazi athu, sitingayende m'makwalala athu; chitsiriziro chathu chayandikira, masiku athu akwaniridwa; pakuti chitsiriziro chathu chafikadi. Otilondola anaposa ziombankhanga za m'mlengalenga m'liwiro lao, anatithamangitsa pamapiri natilalira m'chipululu. Ana a Ziyoni a mtengo wapatali, olingana ndi golide woyengetsa, angoyesedwa ngati mbiya zadothi zozipanga manja a woumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 7:19

Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golide wao chinthu chodetsedwa; siliva wao ndi golide wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi chokhumudwitsa cha mphulupulu zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:13

Ndipo unadzikometsera ndi golide, ndi siliva, ndi chovala chako ndi bafuta ndi silika ndi yopikapika; unadya ufa wosalala, ndi uchi, ndi mafuta; ndipo unali wokongola woposa ndithu, ndipo unapindulapindula kufikira unasanduka ufumu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:17

Unatenganso zokometsera zako zokoma za golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndinakupatsa, ndi kudzipangira mafano a amuna, ndi kuchita nao chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 3:1

Mfumu Nebukadinezara anapanga fano lagolide, msinkhu wake mikono makumi asanu ndi limodzi, ndi thunthu lake mikono isanu ndi umodzi; analiimika pa chidikha cha Dura, m'dera la ku Babiloni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 2:8

Pakuti sanadziwa kuti ndine ndinampatsa tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi kumchulukitsira siliva ndi golide, zimene anapanga nazo Baala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 3:5

Popeza inu munatenga siliva wanga ndi golide wanga, ndi kulonga zofunika zanga zokoma m'akachisi anu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 8:6

kuti tigule osauka ndi ndalama, ndi aumphawi ndi nsapato, ndi kugulitsa nsadwa za tirigu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nahumu 2:9

Funkhani siliva, funkhani golide; pakuti palibe kutha kwake kwa zosungikazo, kwa chuma cha zipangizo zofunika zilizonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 13:9

Ndi gawo lachitatulo ndidzalitengera kumoto, ndi kuwayenga ngati ayenga siliva, ndi kuwayesa monga ayesa golide; adzaitana dzina langa, ndipo ndidzawamvera; ndidzati, Awa ndi anthu anga; ndi iwo adzati, Yehova ndi Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:3

ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsa siliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golide ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m'chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 2:11

Ndipo pofika kunyumba anaona kamwanako ndi Maria amake, ndipo anagwa pansi namgwadira Iye; namasula chuma chao, nampatsa Iye mitulo, ndiyo golide ndi lubani ndi mure.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-21

Musadzikundikire nokha chuma pa dziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma m'Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:16-17

Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa Kachisi, wadzimangirira. Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:19

Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:6

Koma Petro anati, Siliva ndi golide ndilibe; koma chimene ndili nacho, ichi ndikupatsa, M'dzina la Yesu Khristu Mnazarayo, yenda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:29

Popeza tsono tili mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofanafana ndi golide, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:12

Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golide, siliva, miyala ya mtengo wake, mtengo, udzu, dziputu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:9

Momwemonso, akazi adziveke okha ndi chovala choyenera, ndi manyazi, ndi chidziletso; osati ndi tsitsi lake loluka, ndi golide kapena ngale, kapena malaya a mtengo wake wapatali;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:20

Koma m'nyumba yaikulu simuli zotengera za golide ndi siliva zokha, komatunso za mtengo ndi dothi; ndipo zina zaulemu, koma zina zopanda ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:4

okhala nayo mbale ya zofukiza yagolide ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golide, momwemo munali mbiya yagolide yosungamo mana, ndi ndodo ya Aroni idaphukayo, ndi magome a chipangano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:11-12

Koma atafika Khristu, Mkulu wa ansembe wa zokoma zilinkudza mwa, chihema chachikulu ndi changwiro choposa, chosamangika ndi manja, ndiko kunena kuti, chosati cha chilengedwe ichi, kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi anaang'ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi kumalo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:7

kuti mayesedwe a chikhulupiriro chanu, ndiwo a mtengo wake woposa wa golide amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ochitira chiyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa vumbulutso la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:18-19

podziwa kuti simunaomboledwa ndi zovunda, golide ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu achabe ochokera kwa makolo anu: koma ndi mwazi wa mtengo wake wapatali monga wa mwanawankhosa wopanda chilema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Khristu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:3-4

Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golide, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:12-13

Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolide; ndipo pakati pa zoikapo nyalizo wina wonga Mwana wa Munthu atavala chofikira kumapazi ake, atamangira lamba lagolide pachifuwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 17:4

Ndipo mkazi anavala chibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golide, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale; nakhala nacho m'dzanja lake chikho chagolide chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chigololo chake,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:18-21

Ndipo mirimo ya linga lake ndi yaspi; ndipo mzindawo ngwa golide woyengeka, wofanana ndi mandala oyera. Maziko a linga la mzinda anakometsedwa ndi miyala ya mtengo, ya mitundumitundu; maziko oyamba, ndi yaspi; achiwiri, ndi safiro; achitatu, ndi kalikedo; achinai, ndi smaragido; Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake. achisanu, ndi sardonu; achisanu ndi chimodzi, ndi sardiyo; achisanu ndi chiwiri, ndi krusolito; achisanu ndi chitatu, ndi berulo; achisanu ndi chinai, ndi topaziyo; akhumi, ndi krusoprazo; akhumi ndi achimodzi, ndi huakinto; akhumi ndi chiwiri, ndi ametusto. Ndipo zitseko khumi ndi ziwiri ndizo ngale khumi ndi ziwiri; chitseko chilichonse pa chokha cha ngale imodzi. Ndipo khwalala la mzinda nla golide woyengeka, ngati mandala openyekera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga wamuyaya, Wapamwamba, m'dzina la Yesu ndikubwera kwa Inu, Inu nokha ndinu woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa kwakukulu. Atate Woyera, ndikuyandikira kwa Inu podziwa kuti palibe wina ngati Inu, pakali pano ndikupereka moyo wanga wonse kwa Inu, ndikupempha kuti mundipatse mphamvu ndipo tsiku ndi tsiku ndizifuna Inu kwambiri kuposa golide ndi siliva. Mzimu Woyera, ndithandizeni kugwira mawu anu, osadandaula ndi zina, koma ndisunge malonjezano anu chifukwa siliva ndi yanu, golide ndi yanu, ndipo mudzapitiriza kupereka zonse zomwe ndikusowa. Ambuye, ndipatseni nzeru ndi kulimba mtima kuti mtima wanga ukhale woyera kuti ndidziwe momwe ndingakhalire pakati pa mbadwo woipa, kuti ngakhale zinthu zili bwanji, ndikhale ndi chikhulupiriro cholimba chomwe chidzayesedwe ngati golide ndipo chidzapezeka choyenera ulemerero mtsogolo muubwenzi wanu. Ndipatseni kumvetsetsa kuti chimwemwe ndi masautso ndizofunikira pakukula kwanga, chifukwa chitsimikizo changa chachikulu ndichakuti simundisiya ndekha, koma mundipatse chisomo kuti ndipambane. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa