Mzimu Woyera, yemwenso amatchedwa Mtonthozi, ndi munthu wokongola kwambiri amene ungakomane naye. Sakungotonthozetsa, koma amandiphunzitsanso ndi kundilanga.
Ndikofunika kudziwa kuti Mtonthozi sangotitonthoza nthawi zovuta zokha, koma amandiwongoleranso, amandipatsa mphamvu, ndi kundiphunzitsa choonadi. Ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, mphamvu yake imakhala mwa ine chifukwa ndakhulupirira.
Ntchito yake ndi yambiri: amatonthoza chisoni changa, amandipatsa mtendere pakati pa mavuto, amapempherera ine, ndi kundithandiza kumvetsa ziphunzitso za Yesu.
Kuganizira mozama za Mzimu Woyera kumandithandiza kuzindikira kufunika kwa kukhala kwake m'moyo wanga. Kumandikumbutsa kuti sindili ndekha paulendo wanga wauzimu ndipo sindiyenera kunyamula mavuto anga ndekha.
Mzimu Woyera alipo kuti andilimbitse ndikafooka, kuti andipatse chiyembekezo ndikakumana ndi mavuto, ndi kundikumbutsa zabwino ndi kukhulupirika kwa Mulungu.
Pakati pa masautso ndi mavuto a moyo, Mzimu Woyera amandipatsa mphamvu zopitirira. Amanditonthoza ndi chikondi chake ndi kundidzazitsa ndi chidaliro kuti, ngakhale pazovuta, Mulungu akugwira ntchito m'zinthu zonse kuti zindiyamikire.
Komanso, Mzimu Woyera amandivumbulutsira choonadi cha Mawu a Mulungu. Amandithandiza kumvetsa malemba, kuzindikira chifuniro cha Mulungu, ndi kukula mwauzimu. Ndi chitsogozo chake, ndimasinthika ndikukhoza kukhala moyo wotsogozedwa ndi mfundo ndi makhalidwe a Ufumu wa Mulungu.
Komabe ndikukuuzani zoona, kuti nkwabwino koposa kwa inu kuti ndichoke. Pakuti ngati sindichoka, Nkhoswe ija siidzabwera kwa inu. Koma ngati ndipita, ndidzaitumiza kwa inu.
Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.
Pamenepo Mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unali pa mtendere. Udakhazikika, ndipo anthu ochuluka adaloŵamo chifukwa anthu ake ankayenda moopa Ambuye, ndipo Mzimu Woyera ankaŵalimbikitsa.
Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse.
Pakuti monga tikumva zoŵaŵa kwambiri pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatilimbitsa mtima kwambiri.
“Koma pali Nkhoswe imene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate. Nkhosweyo ndi Mzimu wa choona wofumira mwa Atate. Iyeyo akadzabwera, adzandichitira umboni.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo.
Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza.
Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu.
“Ndidaona m'mene ankachitira, komabe ndidzaŵachiritsa. Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza. Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse ine mtumiki wanu, monga momwe mudalonjezera.
Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu. Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini.
Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza. Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu.
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?
Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu?
Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni.
Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.
Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye, mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa, mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu, mzimu wopatsa kudziŵa zinthu ndi kuwopa Chauta.
Paja Malembo akuti, ‘Munthu wokhulupirira Ine, mtima wake udzakhala ngati gwelo la mitsinje ya madzi opatsa moyo.’ ” (Pakutero Yesu ankanena za Mzimu Woyera amene anthu okhulupirira Iye analikudzalandira. Nthaŵi imeneyo nkuti Mzimu Woyera asanafike, chifukwa Yesu anali asanalandire ulemerero wake.)
Tsono tikamati, “Ambuye,” tikunena Mzimu Woyera. Ndipo kumene kuli Mzimu wa Ambuye, kuli ufulu.
Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
Anthu akakuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, chifukwa ndiye kuti Mzimu wa ulemerero, Mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira.
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu.
Inu mwakhala mukutsata chitsanzo chathu ndi cha Ambuye. Ngakhale mudapeza masautso ambiri, mudalandira mau athu mwa chimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera.
Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”
Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera Iye.”
Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene Mzimu wa Mulungu amaŵatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye. Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno. Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa.
Tsono iye adandiwuza kuti ndidziŵitse Zerubabele uthenga wa Chauta wakuti, “Inde udzapambana, koma osati ndi nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi mzimu wanga.
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu. Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu. Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa. Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Mulungu ndiye amene adatikonzeratu kuti tilandire zimenezi, ndipo adatipatsa Mzimu Woyera ngati chikole chake.
Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.
Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Madalitso a Ambuye Yesu Khristu ndi chikondi cha Mulungu ndiponso chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.
Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere.
Koma inu okondedwa, muzithandizana kuti uzikulirakulira moyo wanu, umene udakhazikika pa maziko a chikhulupiriro chanu changwiro. Muzipemphera ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mudzisunge m'chikondi cha Mulungu podikira moyo wosatha, umene Ambuye athu Yesu Khristu adzakupatseni mwa chifundo chake.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m'madzi ndi mwa Mzimu Woyera, sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. Chobadwa mwa munthu ndi thupi chabe, koma chobadwa mwa Mzimu Woyera ndi mzimu.
Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona.
Mzimu Woyera nayenso amatitsimikizira zimenezi. Poyamba Iye akuti, “Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo, akutero Ambuye: ndidzaika Malamulo anga m'mitima mwao, ndidzachita kuŵalemba m'maganizo ao.” Pambuyo pake akutinso, “Sindidzaŵakumbukiranso konse machimo ao ndi zolakwa zao.”
Khristu adachita zimenezi, kuti dalitso limene Mulungu adaalonjeza Abrahamu, lipatsidwe kwa anthu a mitundu yonse kudzera mwa Khristu Yesu, ndipo kuti pakukhulupirira tilandire Mzimu Woyera amene Mulungu adaatilonjeza.
Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.
Anthu omvera khalidwe loipalo, amaika mtima pa zilakolako zathupi. Koma anthu omvera Mzimu Woyera, amaika mtima pa zimene Mzimu Woyerayo afuna. Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Pajatu odzalankhula si ndinu ai, koma Mzimu wa Atate anu ndiye amene adzalankhula kudzera mwa inu.
Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu.
ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni. Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene aŵapempha.”
Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.”
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu,
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Motero munthu wokana mau ameneŵa, sakukana munthu chabe ai, koma akukana Mulungu amene amakupatsani Mzimu wake Woyera.
Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Ndipo pamene ndinkalankhula kapena kulalika, sindinkalankhula moonetsa nzeru, kuyesa kukopa anthu, koma mau anga anali otsimikizika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.
Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera. Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika.
Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”
Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”
Paja mau a aneneri sadadze konse ndi kufuna kwa munthu yekha, koma Mzimu Woyera adaŵalankhulitsa mau ochokera kwa Mulungu.
Koma Mulungu adzatitumizira mzimu wake, kuchokera kumwamba, ndipo dziko lachipululu lidzasanduka lachonde, minda yonse idzabereka dzinthu dzambiri. Pamenepo m'dziko lonse mudzakhala chilungamo, kuyambira ku chipululu mpaka ku minda yachonde. Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.
Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo.
Mulungu ndi amene amatikhazikitsa pamodzi nanu mwa Khristu. Ndiye amene adatidzoza, natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole.
Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.
Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali. Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa. Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani? Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga. Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya. Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse.