Mtima wanga uli phee. Ndikudziwa kuti mtendere weniweni, mtendere wosatha, suchokera m'dziko lino. Mtendere umene dziko limapereka ndi waufupi, ngati mphepo yozizira m'chilimwe. Umabwera ndipo umapita mwachangu.
Koma mtendere umene ndimalankhula uwu, mtendere umene ndimamva mu mtima mwanga, ndi wosiyana. Uwu ndi mtendere wa Mzimu Woyera, mphatso yochokera kwa Mulungu. Ndi mtendere umene umatilimbitsa ngakhale pakati pa mavuto.
Inde, mavuto alipo. Timakumana nawo tsiku ndi tsiku. Koma dziwani ichi, mavuto amenewa ndi amene amatipanga, amatikonzekeretsa kuti tilandire mtendere weniweni wa Mulungu. Ndi monga mbiya ya dothi yomwe imawotchedwa pamoto kuti ikhale yolimba.
Sitingathe kudzipangira tokha mtendere weniweni. Mtendere wathu ungakhale waufupi, wopanda maziko olimba. Koma mtendere wa Mzimu Woyera ndi wozama, ndi wosatha. Umakhala nafe nthawi zonse, ngakhale m'mavuto.
Tikuyembekezera tsiku limene Mulungu adzabweranso. Mpaka tsiku limenelo lifike, tiyeni tilimbikitsane ndi mtendere wa Mzimu Woyera. Mtendere umene sudzatha, umene umaposa kumvetsa kwathu konse. Mtendere weniweni.
Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.
Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Phunzitseni, kuti ndizichita zofuna Inu, pakuti ndinu Mulungu wanga. Mzimu wanu wabwino unditsogolere pa njira yanu yosalala.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka. Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita. Koma ngati Mzimu Woyera akutsogolerani, ndiye kuti sindinunso akapolo a Malamulo a Mose.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”
Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.
Ambuye, eniake mtendere amene, akupatseni mtenderewo nthaŵi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.
Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.
Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri.
Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe, ndipo adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tiziyenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka. Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere.
Akadzakutengerani ku milandu, musadzade nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Kodi tikakambe bwanji?’ Kapena kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Mudzapatsidwa pa nthaŵi imeneyo mau oti munene. Atumwi khumi ndi aŵiriwo maina ao ndi aŵa: Woyamba ndi Simoni, wotchedwa Petro, ndipo mbale wake Andrea; Yakobe, mwana wa Zebedeo, ndi mbale wake Yohane; Pajatu odzalankhula si ndinu ai, koma Mzimu wa Atate anu ndiye amene adzalankhula kudzera mwa inu.
“Akadzakutengerani ku milandu ku nyumba zamapemphero, kapena kwa mafumu ndiponso kwa akulu a Boma, musati mudzavutike nkumati, ‘Kaya ndikayankha bwanji? Ndikanena chiyani?’ Popeza kuti Mzimu Woyera adzakudziŵitsani pa nthaŵi yomweyo zimene mudzayenera kunena.”
Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.
“Koma pali Nkhoswe imene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate. Nkhosweyo ndi Mzimu wa choona wofumira mwa Atate. Iyeyo akadzabwera, adzandichitira umboni.
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo.
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Pamene Petro ankalingalirabe za zimene adaaziwona m'masomphenya zija, Mzimu Woyera adamuuza kuti, “Iwe, anthu atatu akukufuna. Anali munthu wotsata zachipembedzo, ndipo iye pamodzi ndi banja lake lonse ankaopa Mulungu. Ankathandiza kwambiri Ayuda osauka, ndipo ankapemphera Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi. Nyamuka, tsika, upite nawo osakayika, pakuti ndaŵatuma ndine.”
Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” “Pambuyo pake adaŵapatsa oweruza kufikira nthaŵi ya mneneri Samuele. Kenaka anthu adapempha kuti aŵapatse mfumu, ndipo Mulungu adaŵapatsa Saulo, mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, iye nkuŵalamulira pa zaka makumi anai. Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ Mwa zidzukulu za Davideyo Mulungu adasankha Yesu kuti akhale Mpulumutsi wa Aisraele, monga momwe adaalonjezera kale. Iyeyo asanayambe ntchito, Yohane ankalalikira Aisraele onse kuti atembenuke mtima ndi kubatizidwa. Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’ “Ine abale, zidzukulu za Abrahamu, ndi ena nonse oopa Mulungu, uthenga wa chipulumutsowu Mulungu watumizira ife. Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu. Ngakhale sadapeze konse chifukwa chomuphera, komabe adapempha Pilato kuti Yesuyo aphedwe. Ndipo atachita zonse zimene zidalembedwa za Iye, adamtsitsapo pa mtanda paja namuika m'manda. Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma. Koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa, ndipo pa masiku ambiri adakhala akuwonekera kwa anthu aja amene adaamperekeza ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya. Amenewo ndiwo amene akumchitira umboni kwa anthu tsopano. Ndipo ife tikukulalikirani Uthenga Wabwino wakuti zilipo zimene Mulungu adaaŵalonjeza makolo athu. Tsono zimene adaalonjezazo Iye watichitire ifeyo, zidzukulu zao, pakuukitsa Yesu kwa akufa. Monganso mudalembedwera m'Salimo lachiŵiri kuti, “ ‘Iwe ndiwe Mwana wanga, Ine lero ndakubala.’ Ndipo zakuti adamuukitsa kwa akufa kuti asaole konse, Mulungu adati, ‘Ndidzakupatsani madalitso opatulika ndi okhulupirika amene ndidalonjeza Davide.’ Nchifukwa chake m'Salimo lina akutinso, “ ‘Simudzalekerera Woyera wanu kuti aole.’ Paja Davide adati atakwaniritsa zimene Mulungu adaakonzeratu pa masiku a mbadwo wake, adamwalira naikidwa m'manda pamodzi ndi makolo ake, ndipo thupi lake lidaola. Koma uja Mulungu adamuukitsa kwa akufayu sadaole ai. Tsono abale, dziŵani kuti chifukwa cha Yesuyo tikukulalikirani zakuti machimo amakhululukidwa. Ndipo kudzera mwa Iye yemweyo aliyense wokhulupirira amapeza chipulumutso chathunthu chimene simukadatha kuchipata potsata malamulo a Mose. Barnabasi ndi Saulo, otumidwa ndi Mzimu Woyera aja, adapita ku Seleukiya. Kuchokera kumeneko adayenda m'chombo nakafika ku chilumba cha Kipro.
Paulo ndi anzake aja adapitirira dera la Frijiya ndi la Galatiya, pakuti Mzimu Woyera adaaŵaletsa kulalika mau a Mulungu ku Asiya. Pamene adafika ku malire a Misiya, adayesa kuloŵa m'dera la Bitiniya, koma Mzimu wa Yesu sadaŵalole.
Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Mulungu adachita zimenezi, kuti chilungamo chimene Malamulo a Mose amatipempha, chiwoneke kwathunthu mwa ife amene sitimveranso khalidwe lathu lopendekera ku zoipa, koma timamvera Mzimu Woyera.
Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Pajatu odzalankhula si ndinu ai, koma Mzimu wa Atate anu ndiye amene adzalankhula kudzera mwa inu.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.
Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu. Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini. Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso.
natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole.
Tsono tikamati, “Ambuye,” tikunena Mzimu Woyera. Ndipo kumene kuli Mzimu wa Ambuye, kuli ufulu. Tonsefe, opanda chophimba nkhope yathu, timaonetsa ulemerero wa Ambuye, monga momwe galasi limaonetsera nkhope ya munthu. Monsemo Ambuye, amene ali Mzimu, amatisandutsa kuti tifanefane naye, ndi kukhala nawo ulemerero wake mochulukirachulukira.
Chimene ndikufuna kunena ndi ichi: Mulole Mzimu Woyera kuti azikutsogolerani. Mukatero, pamenepo simudzachita zimene khalidwe lanu lokonda zoipa limalakalaka.
Koma ngati Mzimu Woyera akutsogolerani, ndiye kuti sindinunso akapolo a Malamulo a Mose.
Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu. Khristu akakhala mwa inu, ngakhale thupi lanu lidzafadi chifukwa cha uchimo, komabe mzimu wanu udzakhala ndi moyo, popeza kuti Mulungu wakuwonani kuti ndinu olungama pamaso pake. Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa. Motero abale, tili ndi ngongole, komatu ngongole yake si yakuti tizigonjera khalidwe lathu lokonda zoipa, ndi kumachita chifuniro chake. Pakuti ngati m'moyo mwanu mutsata khalidwelo, mudzafa. Koma ngati ndi chithandizo cha Mzimu Woyera mupha zilakolako zanu zathupi, mudzakhala ndi moyo. Onse amene Mzimu wa Mulungu amaŵatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye. Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno. Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza. Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.
Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu.
Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.
Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.
Nchifukwa chake tsono, monga Mzimu Woyera akunenera, “Lero lino mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira pomuukira Mulungu, tsiku la kumuyesa m'chipululu muja.
Mzimu Woyera nayenso amatitsimikizira zimenezi. Poyamba Iye akuti, “Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo, akutero Ambuye: ndidzaika Malamulo anga m'mitima mwao, ndidzachita kuŵalemba m'maganizo ao.”
Koma inu, Khristu adakudzozani ndi Mzimu Woyera amene amakhala mwa inu, ndipo sipafunikanso wina woti akuphunzitseni. Mzimu Woyerayo, amene mudadzozedwa naye, amakuphunzitsani zonse. Zimene amakuphunzitsani nzoona, si zonama ai. Nchifukwa chake, monga momwe adakuphunzitsirani, khalani mwa Khristu.
Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.
Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera.
Koma inu okondedwa, muzithandizana kuti uzikulirakulira moyo wanu, umene udakhazikika pa maziko a chikhulupiriro chanu changwiro. Muzipemphera ndi mphamvu za Mzimu Woyera.