Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


146 Mau a Mulungu: Chikumbutso Chakuti Iye Ndi Thanthwe Lathu

146 Mau a Mulungu: Chikumbutso Chakuti Iye Ndi Thanthwe Lathu


Masalimo 18:2

Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye; chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:2-3

Ndipo anati, Yehova ndiye thanthwe langa, ndi ngaka yanga, ndi Mpulumutsi wanga, wangadi. Iye ananditulutsanso ku malo akulu; Iye anandipulumutsa, chifukwa akondwera ndi ine. Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa; monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho. Pakuti ndinasunga njira za Yehova, osapatukira ku zoipa kusiya Mulungu wanga. Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga; ndipo za malemba ake, sindinawapatukira. Ndinakhalanso wangwiro kwa Iye, ndipo ndinadzisunga kusachita kuipa kwanga. Chifukwa chake Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa; monga mwa kuyera kwanga pamaso pake. Ndi chifundo Inu mudzadzionetsa wachifundo, ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro. Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima; ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza. Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa; koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse. Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova; ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga. Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:2

Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:6-7

Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, msanje wanga, sindidzagwedezeka. Pa Mulungu pali chipulumutso changa ndi ulemerero wanga. Thanthwe la mphamvu yanga ndi pothawirapo panga mpa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:4

Khulupirirani Yehova nthawi yamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:22

Koma Yehova wakhala msanje wanga; ndi Mulungu wanga thanthwe lothawirapo ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:3

Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:1

Wolemekezeka Yehova thanthwe langa, wakuphunzitsa manja anga achite nkhondo, zala zanga zigwirane nao:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:4

namwa onse chakumwa chauzimu chimodzimodzi; pakuti anamwa mwa thanthwe lauzimu lakuwatsata; koma thanthwelo ndiye Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:4

Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:31

Pakuti Mulungu ndani wosati Yehova? Ndipo thanthwe ndani wosati Mulungu wathu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:1

Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:47

Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la chipulumutso changa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:26

Iye adzanditchula, ndi kuti, Inu ndinu Atate wanga, Mulungu wanga, ndi thanthwe la chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:3

Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka; mwalamulira kundipulumutsa; popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 61:2

Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:8

Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa lililonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:15

kulalikira kuti Yehova ngwolunjika; Iye ndiye thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe chosalungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1-2

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso. Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi. Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu. Chifukwa chake sitidzachita mantha, lingakhale lisandulika dziko lapansi, angakhale mapiri asunthika, nakhala m'kati mwa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:18

Mwaleka Thanthwe limene linakubalani, mwaiwala Mulungu amene anakulengani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 17:10

Chifukwa iwe waiwala Mulungu wa chipulumutso chako, sunakumbukira thanthwe la mphamvu zako; chifukwa chake iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zachilendo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:1-2

Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye. Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu. Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri, kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu. Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:9

Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:2-3

Munditcherere khutu lanu; ndipulumutseni msanga. Mundikhalire ine thanthwe lolimba, nyumba yamalinga yakundisunga. Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime. Wolemekezeka Yehova, pakuti anandichitira chifundo chake chodabwitsa m'mudzi walinga. Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu. Kondani Yehova, Inu nonse okondedwa ake, Yehova asunga okhulupirika, ndipo abwezera zochuluka iye wakuchita zodzitama. Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova. Pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa; ndipo chifukwa cha dzina lanu ndiyendetseni bwino, ndipo nditsogolereni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 33:21-22

Ndipo Yehova anati, Taona pali Inepo pali malo, ndipo uime pathanthwe; ndipo kudzakhala, pakupitira ulemerero wanga, ndidzakuika mu mpata wa thanthwe, ndi kukuphimba ndi dzanja langa, mpaka nditapitirira;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:26

Likatha thupi langa ndi mtima wanga, Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga, ndi cholandira changa chosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:29

Inu mudzakhala ndi nyimbo, monga usiku, podya phwando lopatulika; ndi mtima wokondwa, monga pomuka wina ndi chitoliro, kufikira kuphiri la Yehova, kuthanthwe la Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:5

Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa m'tsenjezi mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:1-2

Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse. palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako. Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, akusunge m'njira zako zonse. Adzakunyamula pa manja ao, ungagunde phazi lako pamwala. Udzaponda mkango ndi mphiri; udzapondereza msona wa mkango ndi chinjoka. Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa. Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:2

Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:24-25

Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe; ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; koma siinagwa; chifukwa inakhazikika pathanthwepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:31

Popeza thanthwe lao nlosanga Thanthwe lathu, oweruza a pamenepo ndiwo adani athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:32

Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova? Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:24

Limbikani ndipo Iye adzalimbitsa mtima wanu, inu nonse akuyembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:1

Mverani Ine, inu amene mutsata chilungamo, inu amene mufuna Yehova; yang'anani kuthanthwe, kumene inu munasemedwamo, ndi kuuna kwa dzenje, kumene inu munakumbidwamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:8

Khulupirirani pa Iye nyengo zonse, anthu inu, tsanulirani mitima yanu pamaso pake. Mulungu ndiye pothawirapo ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:18

Pamene ndinati, Litereka phazi langa, chifundo chanu, Yehova, chinandichirikiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:3

Mulungu wa thanthwe langa, Iye ndidzamkhulupirira; chikopa changa, ndi nyanga ya chipulumutso changa, nsanja yanga yaitali, ndi populumukirapo panga; Mpulumutsi wanga, mundipulumutsa kuchiwawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:22

Mwala umene omangawo anaukana wakhala mutu wa pangodya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:46

Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa; nakwezeke Mulungu wa chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:4-5

amene pakudza kwa Iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu, inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:1-2

Ndikhulupirira Inu, Yehova. Ndisachite manyazi nthawi zonse. Pakuti adani anga alankhula za ine; ndipo iwo akulalira moyo wanga apangana upo, ndi kuti, Wamsiya Mulungu. Mlondoleni, mgwireni; popeza palibe wompulumutsa. Musandikhalire kutali, Mulungu; fulumirani kundithandiza, Mulungu. Adani a moyo wanga achite manyazi, nathawe; chotonza ndi chimpepulo zikute ondifunira choipa. Koma ine ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzaonjeza kukulemekezani. Pakamwa panga padzafotokozera chilungamo chanu, ndi chipulumutso chanu tsiku lonse; pakuti sindidziwa mawerengedwe ake. Ndidzamuka mu mphamvu ya Ambuye Yehova; ndidzatchula chilungamo chanu, inde chanu chokha. Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwitsa zanu. Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo. Chilungamo chanunso, Mulungu, chifikira kuthambo; Inu amene munachita zachikulu, akunga Inu ndani, Mulungu? Ndikwatuleni m'chilungamo chanu, ndi kundilanditsa, nditcherereni khutu lanu ndi kundipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:10

Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:8

Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:14

Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:9

Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:9

Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga! Udaika Wam'mwambamwamba chokhalamo chako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:37

Pamenepo adzati, Ili kuti milungu yao, thanthwe limene anathawirako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 28:16

chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m'Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 17:7

Onetsani chifundo chanu chodabwitsa, Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:39-40

Koma chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, Iye ndiye mphamvu yao m'nyengo ya nsautso. Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako. Ndipo Yehova awathandiza, nawalanditsa; awalanditsa kwa oipa nawapulumutsa, chifukwa kuti anamkhulupirira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:7

Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 2:2

Palibe wina woyera ngati Yehova; palibe wina koma Inu nokha; palibenso thanthwe longa Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:13

Cheza cha pamaso pake makala a moto anayaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:2

Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:1

Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:18-19

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:2

Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 33:6

Ndipo kudzakhala chilimbiko m'nthawi zako, chipulumutso chambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko chuma chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:4

Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:22

Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:14

Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 32:27

Taona, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse; kodi kuli kanthu kondilaka Ine?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:3

Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nahumu 1:7

Yehova ali wabwino, ndiye polimbikirapo tsiku la msauko; ndipo adziwa iwo omkhulupirira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29

Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye ameme alibe mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 14:14

Yehova adzakugwirirani nkhondo, ndipo inu mudzakhala chete.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 12:2

Taonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupirira, sindidzaopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, Iye ndiye chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:6

Kotero kuti tinena molimbika mtima, Mthandizi wanga ndiye Ambuye; sindidzaopa; adzandichitira chiyani munthu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:27

Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 3:3

Ndipo Inu Yehova, ndinu chikopa changa; ulemerero wanga, ndi wondiweramutsa mutu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 1:9

Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:10

Khalani chete, ndipo dziwani kuti Ine ndine Mulungu, Ndidzabuka mwa amitundu, ndidzabuka pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:10

Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:3

Lingakhale gulu la ankhondo limanga misasa kuti andithyole, mtima wanga sungachite mantha; ingakhale nkhondo ikandiukira, inde pomweponso ndidzakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 25:4

Chifukwa Inu mwakhala linga la aumphawi, linga la osowa m'kuvutidwa kwake, pobisalira chimphepo, mthunzi wa pa dzuwa, pamene kuomba kwa akuopsa kufanana ndi chimphepo chakuomba tchemba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:19

Anandifikira ine tsiku la tsoka langa; koma Yehova anali mchirikizo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:11-12

Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri, kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu. Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:2

Imbirani ulemerero wa dzina lake; pomlemekeza mumchitire ulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:5

Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:1

Ndipo Davide analankhula kwa Yehova mau a nyimbo iyi tsikuli Yehova anampulumutsa m'dzanja la adani ake onse, ndi m'dzanja la Saulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:11

Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yake; funani nkhope yake nthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:14-16

Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m'mwamba, popeza adziwa dzina langa. Adzandifuulira Ine ndipo ndidzamyankha; kunsautso ndidzakhala naye pamodzi; ndidzamlanditsa, ndi kumchitira ulemu. Ndidzamkhutitsa ndi masiku ambiri, ndi kumuonetsera chipulumutso changa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:16

Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 61:3-4

Pakuti munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine. Ndidzagoneragonerabe m'chihema mwanu; ndidzathawira mobisalamo m'mapiko anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:4-5

Pakuti chilichonse chabadwa mwa Mulungu chiligonjetsa dziko lapansi; ndipo ichi ndi chigonjetso tichigonjetsa nacho dziko lapansi, ndicho chikhulupiriro chathu. Koma ndani iye wogonjetsa dziko lapansi, koma iye amene akhulupirira kuti Yesu ndiye Mwana wa Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:33

Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalingonjetsa dziko lapansi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:4

Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera, nandilanditsa m'mantha anga onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:18

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:7-8

Pakuti munakhala mthandizi wanga; ndipo ndidzafuula mokondwera mu mthunzi wa mapiko anu. Moyo wanga uumirira Inu. Dzanja lamanja lanu lindigwiriziza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:1-2

Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse, pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu ku mibadwomibadwo. Mudathyola Rahabu, monga munthu wophedwa; munabalalitsa adani anu ndi mkono wa mphamvu yanu. Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake. Munalenga kumpoto ndi kumwera; Tabori ndi Heremoni afuula mokondwera m'dzina lanu. Muli nao mkono wanu wolimba; m'dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka. Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wachifumu wanu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu. Odala anthu odziwa liu la lipenga; ayenda m'kuunika kwa nkhope yanu, Yehova. Akondwera m'dzina lanu tsiku lonse; ndipo akwezeka m'chilungamo chanu. Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao; ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka. Pakuti chikopa chathu chifuma kwa Yehova; ndi mfumu yathu kwa Woyera wa Israele. Pamenepo munalankhula m'masomphenya ndi okondedwa anu, ndipo mudati, Ndasenza thandizo pa chiphona; ndakweza wina wosankhika mwa anthu. Pakuti ndinati, Chifundo adzachimanga kosaleka; mudzakhazika chikhulupiriko chanu m'Mwamba mwenimweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:8-9

Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu. Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:6

Chifukwa kwalembedwa m'lembo, Taona, ndiika m'Ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:19-20

Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu; zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera; omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:3-4

Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu. Khulupirirani Yehova nthawi yamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:2

Ndiye chifundo changa, ndi linga langa, msanje wanga, ndi Mpulumutsi wanga; chikopa changa, ndi Iye amene ndimtama; amene andigonjetsera anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:5-6

Wodala munthu amene akhala naye Mulungu wa Yakobo kuti amthandize, chiyembekezo chake chili pa Yehova, Mulungu wake. Amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 104:18

Mapiri atali ndiwo ayenera zinkhoma; pamatanthwe mpothawirapo mbira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 8:14

Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala m'Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:5

Mau onse a Mulungu ali oyengeka; ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:10

ndipo iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:1

Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 50:7

Pakuti Ambuye Yehova adzandithangata Ine; chifukwa chake sindinasokonezedwa; chifukwa chake ndakhazika nkhope yanga ngati mwala, ndipo ndidziwa kuti sindidzakhala ndi manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:6

Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwao, ndipo anawalanditsa m'kupsinjika kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:19

Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu, kumene munachitira iwo akukhulupirira Inu, pamaso pa ana a anthu!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 30:6

Ndipo Davide anadololoka kwambiri, pakuti anthu ananena za kumponya iye miyala, pakuti mtima wao wa anthu onse unali ndi chisoni, yense chifukwa cha ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anadzilimbikitsa mwa Yehova Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 52:12

Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:3-4

Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 33:20-22

Moyo wathu walindira Yehova; Iye ndiye thandizo lathu ndi chikopa chathu. Pakuti mtima wathu udzakondwera mwa Iye, chifukwa takhulupirira dzina lake loyera. Yehova, chifundo chanu chikhale pa ife, monga takuyembekezani Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:3-4

Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:114

Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:1-2

Aleluya; Ulemekeze Yehova, moyo wanga. Yehova adzachita ufumu kosatha, Mulungu wako, Ziyoni, ku mibadwomibadwo. Aleluya. Ndidzalemekeza Yehova m'moyo mwanga; ndidzaimbira zomlemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:8-9

ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:8

Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:18

Ndiponso Ine ndinena kwa iwe, kuti iwe ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazika Mpingo wanga; ndipo makomo a dziko la akufa sadzagonjetsa uwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:11

Pakuti lembo litere, Amene aliyense akhulupirira Iye, sadzachita manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:1-2

Ndikweza maso anga kumapiri: Thandizo langa lidzera kuti? Thandizo langa lidzera kwa Yehova, wakulenga zakumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:15

Koma Yesuruni anasanduka wonenepa, natazira; wasanduka wonenepa, wakula, wakuta ndi mafuta; pamenepo anasiya Mulungu amene anamlenga, napeputsa thanthwe la chipulumutso chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 17:6

Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebu; ndipo upande thanthwe, nadzatulukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anachita chomwecho pamaso pa akulu a Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:13

Anamuyendetsa pa misanje ya dziko lapansi, ndipo anadya zipatso za m'minda; namyamwitsa uchi wa m'thanthwe, ndi mafuta m'mwala wansangalabwe;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:21

Ndipo iwo sanamve ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawatulutsira madzi kutuluka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:28-30

Pamenepo afuulira kwa Yehova m'kusauka kwao, ndipo awatulutsa m'kupsinjika kwao. Asanduliza namondwe akhale bata, kotero kuti mafunde ake atonthole. nawasokolotsa kumaiko, kuchokera kum'mawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kunyanja. Pamenepo akondwera, popeza pagwa bata; ndipo Iye awatsogolera kudooko afunako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 19:25

Koma ndidziwa kuti Mombolo wanga ali ndi moyo, nadzauka potsiriza pafumbi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:50

Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu; nachitira chifundo wodzozedwa wake, Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:8

Ndipo, Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa. Kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 45:22

Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 95:1

Tiyeni tiimbire Yehova mokondwera; tifuule kwa thanthwe la chipulumutso chathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:1

Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 61:1-2

Imvani mfuu wanga, Mulungu; mverani pemphero langa. Ku malekezero a dziko lapansi ndidzafuulira kwa Inu, pomizika mtima wanga. Nditsogolereni kuthanthwe londiposa ine m'kutalika kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5-6

Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita. Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:7

Ena atama magaleta, ndi ena akavalo; koma ife tidzatchula dzina la Yehova Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:23

tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa