Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


107 Mau a Mulungu Okhudza Ana

107 Mau a Mulungu Okhudza Ana

Ana inu, tiyeni tiganizire ana athu, ndi amene akufuna chisamalo, chikondi, ndi kumvetsetsa kwambiri m'nyumba mwathu. Tiyenera kuwasamalira nthawi zonse, ndipo nthawi yathu yabwino kwambiri tiyenera kuigwiritsa ntchito ndi iwo.

Masiku ano, ana athu akukumana ndi mavuto ambiri; mdani akufuna kuwavulaza kuti awaletse kukula m'chikhulupiriro. Anthu ambiri sakusamala ndipo zoipa zikuchulukirachulukira. Anthu oipa akufuna kuwavulaza ana amene Yesu anati, "Lolani ana aang'ono abwere kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Kumwamba ndi wa otere."

Mwana aliyense ali ndi cholinga chabwino; Atate wakumwamba amawakonda kwambiri ndipo amatiuza kuti tikhale ngati iwo. Ndikukulimbikitsani kuti muzisamalira ana aang'ono m'nyumba mwanu, muziwateteza, ndipo ngati muli ndi mphamvu, muziwachitira zabwino. Mulungu adzakudalitsani chifukwa cha zimenezi.

Tsiku lililonse, ana ambiri amatayidwa, amazunzidwa, ndipo sakulandira chilungamo. Thandizani kukula kwawo ndipo muwachitire zinthu zabwino zomwe zingawathandize kuiwala zopweteka ndi chisoni chawo. Pali ana ambiri omwe ali m'misewu omwe akufuna chakudya, chitonthozo, ndi pokhala, ndipo alibe zovala zokwanira. Ndibwino kuwalimbikitsa ndi mawu abwino, koma ngati mungathe kuchita zambiri, musazengereze.

Yang'anani m'maso mwawo, ndipo monga momwe Yesu anakukomerani mtima, mukhale nacho chifundo ndipo musanyalanyaze. Dziko lino likufuna kuti ana a Mulungu adzaze ndi chikondi, ndipo inu mwamuitanidwa kuchita ntchito yofunika kwambiriyi.




Masalimo 127:3

Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:14

Koma Yesu anati, Tilekeni tiana, musatikanize kudza kwa Ine: chifukwa Ufumu wa Kumwamba uli wa totere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:1-3

Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:14

Koma pamene Yesu anaona anakwiya, ndipo anati kwa iwo, Lolani tiana tidze kwa Ine; musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:4

Sitidzazibisira ana ao, koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, ndi mphamvu yake, ndi zodabwitsa zake zimene anazichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:13

Ndipo ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:16

Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:6-7

Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 1:27-28

Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa chopempha changa ndinachipempha kwa Iye; chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:8

Mwananga, tamva mwambo wa atate wako, ndi kusasiya chilangizo cha amai ako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:9

Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13-14

Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:21

Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 33:5

Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:11

Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:12

Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:17

Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:10

Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenya chipenyere nkhope ya Atate wanga wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:17

Ndipo adzamtsogolera Iye, ndi mzimu ndi mphamvu ya Eliya, kutembenuzira mitima ya atate kwa ana ao, ndi osamvera kuti atsate nzeru ya olungama mtima; kukonzeratu Ambuye anthu okonzeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:1

Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 127:4-5

Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:12

Uzilemekeza atate wako ndi amai ako; kuti achuluke masiku ako m'dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:6

Zidzukulu ndizo korona wa okalamba; ndipo ulemerero wa ana ndiwo atate ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:11

Iye adzadyetsa zoweta chake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa pachepa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:36-37

Ndipo anatenga kamwana, nakaika pakati pao, nakayangata, nanena nao, Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:52

Ndipo Yesu anakulabe m'nzeru ndi mumsinkhu, ndi m'chisomo cha pa Mulungu ndi cha pa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:2

Mbeu yake idzakhala yamphamvu pa dziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 14:1

Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadzicheka, kapena kumeta tsitsi pakati pa maso chifukwa cha akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:15

Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:9

Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:9

Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:26-27

Ndipo kudzakhala, pamene ana anu adzanena ndi inu, Kutumikiraku muli nako nkutani? Mudzati, Ndiko nsembe ya Paska wa Yehova, amene anapitirira nyumba za ana a Israele m'Ejipito, pamene anakantha Aejipito, napulumutsa nyumba zathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:15

Nyengo zanga zili m'manja mwanu, mundilanditse m'manja a adani anga, ndi kwa iwo akundilondola ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14

Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:10

M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:13

Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu: Anadalitsa ana anu m'kati mwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 18:19

Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:13-14

Usamane mwana chilango; pakuti ukammenya ndi nthyole safa ai. Udzammenya ndi nthyole, nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 28:9

Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:37-38

Ndipo anapereka ana ao aamuna ndi aakazi nsembe ya kwa ziwanda, nakhetsa mwazi wosachimwa, ndiwo mwazi wa ana ao aamuna ndi aakazi, amene anawaperekera nsembe mafano a Kanani; m'mwemo analidetsa dziko ndi mwaziwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:42

Ndipo amene aliyense adzamwetsa mmodzi wa ang'ono awa chikho chokha cha madzi ozizira, pa dzina la wophunzira, indetu ndinena kwa inu, iye sadzataya mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:46-47

nati nao, Ikani mitima yanu pa mau onse ndikuchitirani nao mboni lero; kuti muuze ana anu asamalire kuwachita mau onse a chilamulo ichi. Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m'dziko limene muolokera Yordani, kulilandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:7

Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Wokonda mwambo akonda kudziwa; koma wakuda chidzudzulo apulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:15

Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:17

Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 11:6

Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwanawankhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwanawambuzi; ndipo mwanawang'ombe ndi mwana wa mkango ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:1

Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 2:40

Ndipo mwanayo anakula nalimbika, nalikudzala ndi nzeru; ndi chisomo cha Mulungu chinali pa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:7-8

Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo; mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru. Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima; malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:10

kuti mukayenda koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu ntchito yonse yabwino, ndi kukula m'chizindikiritso cha Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:7

Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:20

Mwana wanzeru akondweretsa atate wake; koma munthu wopusa apeputsa amake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:14

Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:2

lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 148:12-13

Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:1

Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere tchimo ndi tchimo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:15

Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:165

Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri; ndipo alibe chokhumudwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:25

Mwana wopusa achititsa atate wake chisoni, namvetsa zowawa amake wombala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:13

Ndikulemberani, atate, popeza mwamzindikira Iye amene ali kuyambira pachiyambi. Ndikulemberani, anyamata, popeza mwamlaka woipayo. Ndakulemberani, ana, popeza mwazindikira Atate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 33:1-2

Ndipo Yakobo anatukula maso ake, taonani, anadza Esau, ndi pamodzi naye anthu mazana anai. Ndipo anagawira ana kwa Leya, ndi kwa Rakele, ndi kwa adzakazi awiri aja. Ndipo Yakobo anati, Iaitu, ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, mulandire mphatso yanga pa dzanja langa; pakuti popeza ndinaona nkhope yanu, monga anthu aona nkhope ya Mulungu, ndipo inu mwandivomereza ine. Landiranitu mdalitso wanga umene wafika kwa inu, pakuti Mulungu wandichitira ine zaufulu, ndipo zanganso zindifikira. Ndipo anamkakamiza, nalandira. Ndipo Esau anati, Tiyeni timuke; nditsogolera ndine. Ndipo anati kwa iye, Mbuyanga adziwa kuti ana ali ambowa, ndipo nkhosa ndi zoweta ndili nazo zilinkuyamwitsa: ndipo akathamangitsa tsiku limodzi zoweta zonse zidzafa. Mbuyanga atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzazitsogolera pang'onopang'ono monga mwa mayendedwe a zoweta zili pamaso panga, ndi monga mwa mayendedwe a ana, mpaka ndifike kwa mbuyanga ku Seiri. Ndipo Esau anati, Ndikusiyire anthu ena amene ali ndi ine. Ndipo iye anati, Chifukwa chanji? Ndipeze ine ufulu pamaso pa mbuyanga. Ndipo Esau anabwera tsiku lomwelo kunka ku Seiri. Ndipo Yakobo anankabe ulendo wake ku Sukoti, namanga nyumba yake pamenepo, namanga makola a zoweta zake: chifukwa chake dzina lake la kumeneko ndi Sukoti. Ndipo Yakobo anafika ndi mtendere kumudzi wa Sekemu umene uli m'dziko la Kanani, pamene anachokera ku Padanaramu; namanga tsasa pandunji pa mudzipo. Ndipo anagula ndi ndalama zana limodzi dera la munda kumeneko anamanga hema wake, pa dzanja la ana ake a Hamori atate wake wa Sekemu. Ndipo anaika adzakazi ndi ana ao patsogolo, ndi Leya ndi ana ake pambuyo pao, ndi Rakele ndi Yosefe pambuyo pa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:11

Idzani ananu ndimvereni ine, ndidzakulangizani zakumuopa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:9

Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:1

Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:164

Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi, chifukwa cha maweruzo anu alungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 13:14

Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa m'Ejipito, m'nyumba ya akapolo, ndi dzanja lamphamvu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:74

Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera; popeza ndayembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:15-17

Ndipo anadza nao kwa Iye ana amakanda kuti awakhudze; koma pamene ophunzira anaona anawadzudzula. Koma Yesu anawaitana, nanena, Lolani ana adze kwa Ine, ndipo musawaletse; pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa otere. Indetu ndinena kwa inu, Aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:27

Ukangofuna, mwananga, kusochera kusiya mau akudziwitsa, leka kumva mwambo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 71:5

Pakuti Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:30

Iye wosakhala pamodzi ndi Ine akana Ine, ndi iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwazamwaza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:4

Ndipo iwo adzamanga mabwinja akale, nadzamanga pa miunda yakale, nadzakonzanso midzi yopasuka, mabwinja a mibadwo yambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 49:10

Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 1:39

Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa chabwino kapena choipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:28

Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:16

nanena kwa Iye, Mulinkumva kodi chimene alikunena awa? Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Inde: simunawerenga kodi, M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munafotokozera zolemekeza?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:24

Wolekerera mwanake osammenya amuda; koma womkonda amyambize kumlanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11

musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 148:1-5

Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje. Nyama za kuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka. Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu; zinduna ndi oweruza onse a padziko. Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo. Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya. Mlemekezeni, angelo ake onse; mlemekezeni, makamu ake onse. Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:1

Imba, iwe wouma, amene sunabala; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabala mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:26

Atsegula pakamwa pake ndi nzeru, ndipo chilangizo cha chifundo chili pa lilime lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:5

Akubzala ndi misozi adzatuta ndi kufuula mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:20

Ana inu, mverani akubala inu m'zonse, pakuti ichi Ambuye akondwera nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:147

Ndinafuula kusanake: ndinayembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:4

Pokhala iwe wa mtengo wapatali pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:15

Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana; koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:6

Ndipo popeza muli ana, Mulungu anatumiza Mzimu wa Mwana wake alowe m'mitima yathu, wofuula Abba! Atate!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 92:12-14

Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa; adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni. Iwo ookedwa m'nyumba ya Yehova, adzaphuka m'mabwalo a Mulungu wathu. Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:9

Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:20

Ndipo Iye anakweza maso ake kwa ophunzira ake, nanena, Odala osauka inu; chifukwa uli wanu ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:5

Mau onse a Mulungu ali oyengeka; ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1-3

Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa. Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha. Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:13

ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:76

Eya, ndipo iwetu kamwanawe, udzanenedwa mneneri wa Wamkulukulu; pakuti udzatsogolera Ambuye, kukonza njira zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:15

ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:2

Ndiye chifundo changa, ndi linga langa, msanje wanga, ndi Mpulumutsi wanga; chikopa changa, ndi Iye amene ndimtama; amene andigonjetsera anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:25

Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:4

ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:6

Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:3

nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 1:4-7

Ndipo anadza kwa ine mau a Yehova, kuti, Ndisanakulenge iwe m'mimba ndinakudziwa, ndipo usanabadwe ndinakupatula iwe; ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu. Ndipo ndinati, Ha, Ambuye Mulungu! Taonani, sindithai kunena pakuti ndili mwana. Koma Yehova anati kwa ine, Usati, ndine mwana pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 8:2

M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 6:24-26

Yehova akudalitse iwe, nakusunge; Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo; Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, wamuyaya, wamphamvu ndi wamkulu, Inu nokha ndinu woyenera ulemerero ndi ulemu wonse! M'dzina la Yesu ndimabwera pamaso panu kudandaulira ana, dalitsani mitima yawo ndipo wachiritseni ku matenda onse a thupi ndi auzimu, awamasulireni ku zovuta zonse Ambuye. Awadzazitseni ndi chisomo chanu, nzeru ndipo awapatse chikhulupiriro champhamvu kuti athe kugonjetsa mavuto omwe angakumane nawo akamakula. Awapatseni mphamvu ndi kuwaphunzitsa kuti azichita chifuniro chanu mosabwerera m'mbuyo, kapena kusokonezeka. Mulungu wokondedwa, Inu amene ndinu chishango ndi chitetezo cha ana anu, ndikupemphani kuti muwateteze ku zoyipa, chidani ndi kuipitsidwa, komanso ku zinthu zoipa za dziko lino, pakuti Mawu anu amati: «Aliyense amene angakhumudwitse mmodzi wa ana aang'ono amenewa amene amakhulupirira Ine, zingakhale bwino kwa iye ngati atapachikidwa mwala waukulu m'khosi mwake, n'kumizidwa m'nyanja yaikulu». Thirani Mzimu Woyera pa iwo ndi mphamvu kuti anenere za mkamwa mwanu ndipo akhale atumiki a uthenga wanu wabwino, awapatse makolo anzeru ndi achikondi kuti awaphunzitse zabwino ndi kumvera. Ndikulengeza machiritso, kubwezeretsedwa ndi moyo wosatha pa iwo. Atate dalitsani zonse zomwe achita, maphunziro awo, ntchito zawo, zosangalatsa zawo. Pangani mapazi awo ngati a nswala, Mulungu wanga, awatsogolereni panjira yolungama ndipo awamasulireni ku choipa ndi mayesero, chotsani ubwenzi uliwonse ndi chikoka chilichonse chomwe chingawapatutse kwa Inu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa