Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a m’Baibulo Okhudza Chigololo

110 Mau a m’Baibulo Okhudza Chigololo

Ndikufuna tikambirane nkhani yofunika kwambiri, nkhani ya chigololo. Mwina ukudziwa kuti chigololo ndi kugonana kwa anthu osakwatirana. Baibulo limatiuza momveka bwino mu 1 Akorinto 6:18 kuti, "Thawani dama. Machimo ena onse amene munthu angachite ali kunja kwa thupi lake, koma wochita dama amachimwira thupi lake lomwe."

Chigololo ndi tchimo, ndipo sichikondweretsa Mulungu. Iye akufuna kuti uzitsatira malamulo ake kuti ukhale ndi moyo wabwino, mwakuthupi komanso mwauzimu. Ugonde wosaloleka ukhoza kubweretsa mavuto aakulu, kuphatikizapo imfa.

Ngati wakhala ukuchita tchimoli, dziwa kuti sudachedwa. Ukhoza kusiya lero lomwe ndi kupempha Yesu kuti akukhululukire. Mulungu ndi wachifundo ndipo amakhululukira onse olapa machimo awo.

Monga Akhristu, tiyenera kudziwa kuti Mulungu analenga kugonana kuti anthu abereke ana komanso kuti mwamuna ndi mkazi wake azisangalalana. Sikuti kugonana ndi kwakuthupi kokha, komanso ndi kwauzimu ndi kwamalingaliro pakati pa awiri okwatirana.




Aroma 1:29

anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21

Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:19

Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:1

Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati pa inu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:5

Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa m'ufumu wa Khristu ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5-6

Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano; chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:21-22

Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:24

Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:3

Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:9

Ndipo Ine ndinena kwa inu, Amene aliyense akachotsa mkazi wake, kosakhala chifukwa cha chigololo, nadzakwatira wina, achita chigololo: ndipo iye amene akwatira wochotsedwayo, achita chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:32

koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:8

Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:4

Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:7

Pakuti Mulungu sanaitana ife titsate chidetso, koma chiyeretso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:9

Kapena simudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:3-5

Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu, kosati m'chiliro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19

Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:18

Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:13

Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamtu pao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:22

Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:21

kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:20

Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:22

Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:6-7

Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wake kumvula; Ine ndine Yehova. Usamavula atate wako, ndi mai wako; ndiye mai wako, usamamvula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:28

koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:13

Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi silili la chigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:14

Usachite chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:15

Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:10

Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:9

Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:2-5

Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha. Yense akhale m'maitanidwe m'mene anaitanidwamo. Kodi unaitanidwa uli kapolo? Usasamalako; koma ngati ukhozanso kukhala mfulu, chita nako ndiko. Pakuti iye amene anaitanidwa mwa Ambuye, pokhala ali kapolo, ali mfulu ya Ambuye: momwemonso woitanidwayo, pokhala ali mfulu, ali kapolo wa Khristu. Munagulidwa ndi mtengo wake; musakhale akapolo a anthu. Yense, m'mene anaitanidwamo, abale, akhale momwemo ndi Mulungu. Koma kunena za anamwali, ndilibe lamulo la Ambuye; koma ndikuuzani choyesa iye, monga wolandira chifundo kwa Ambuye kukhala wokhulupirika. Chifukwa chake ndiyesa kuti ichi ndi chokoma chifukwa cha chivuto cha nyengo yino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali. Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi. Koma ungakhale ukwatira, sunachimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanachimwa. Koma otere adzakhala nacho chisautso m'thupi, ndipo ndikulekani. Koma ichi nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe; Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna. ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu; ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita. Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye; koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake. Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m'thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo. Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa. Koma wina akayesa kuti achitira mwana wake wamkazi chosamuyenera, ngati palikupitirira pa unamwali wake, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; akwatitsidwe. Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nao ulamuliro wa pa chifuniro cha iye yekha, natsimikiza ichi mumtima mwa iye yekha, kusunga mwana wake wamkazi, adzachita bwino. Chotero iye amene akwatitsa mwana wake wamkazi achita bwino, ndipo iye wosamkwatitsa achita koposa. Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye. Mkazi alibe ulamuliro wa pa thupi lake la iye yekha, koma mwamuna ndiye; koma momwemonso mwamuna alibe ulamuliro wa pa thupi la iye yekha, koma mkazi ndiye. Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali, monga mwa kuyesa kwanga; ndipo ndinagiza kuti inenso ndili naye Mzimu wa Mulungu. Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:12-14

Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika. Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:20-21

Koma chikakhala choona ichi, kuti zizindikiro zakuti ndiye namwali zidamsowa namwaliyo; pamenepo azimtulutsa namwaliyo ku khomo la nyumba ya atate wake, ndipo amuna a mudzi wake azimponya miyala kuti afe; popeza anachita chopusa m'Israele, kuchita chigololo m'nyumba ya atate wake; chotero uzichotsa choipacho pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 22:22

Akampeza munthu alikugona ndi mkazi wokwatibwa ndi mwamuna; afe onse awiri, mwamuna wakugona ndi mkazi, ndi mkazi yemwe; chotero muzichotsa choipacho mwa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:16-17

Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake; wosiya bwenzi la ubwana wake, naiwala chipangano cha Mulungu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:3-5

Pakuti milomo ya mkazi wachiwerewere ikukha uchi; m'kamwa mwake muti see koposa mafuta. Chimaliziro chake nchowawa ngati chivumulo, ndi chakuthwa ngati lupanga lakuthawa konsekonse. Mayendedwe ake atsikira kuimfa; mapazi ake aumirira kumanda;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:20-23

Pakuti ukondwerenji, mwananga, ndi mkazi wachiwerewere, ndi kufungatira chifuwa cha mkazi wachilendo? Pakuti njira za munthu zili pamaso pa Yehova, asinkhasinkha za mayendedwe ake onse. Zoipa zakezake zidzagwira woipa; adzamangidwa ndi zingwe za uchimo wake. Adzafa posowa mwambo; adzasochera popusa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:24-29

Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa, ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere. Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake. Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengo wapatali. Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake, osatentha zovala zake? Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka, osapsa mapazi ake? Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:32

Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru; wofuna kuononga moyo wakewake ndiye amatero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 7:5-7

Kuti zikutchinjirizire kwa mkazi wachiwerewere, kwa mlendo wamkazi wosyasyalika ndi mau ake. Pakuti pa zenera la nyumba yanga ndinapenyera pamwamba pake; ndinaona pakati pa achibwana, ndinazindikira pakati pa ang'ono mnyamata wopanda nzeru,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 7:21-23

Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake, ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake. Mnyamatayo amtsata posachedwa, monga ng'ombe ipita kukaphedwa; ndi monga unyolo umadza kulanga chitsiru; mpaka muvi ukapyoza mphafa yake; amtsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziwa kuti adzaononga moyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:17-18

madzi akuba atsekemera, ndi chakudya chobisika chikoma. Ndipo mwamunayo sadziwa kuti akufa ali konko; omwe achezetsa utsiru ali m'manda akuya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:27-28

Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya; ndipo mkazi wachiwerewere ndiye mbuna yopapatiza. Pakuti abisalira ngati wachifwamba, nachulukitsa anthu a chiwembu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:26

ndipo ndinapeza kanthu kowawa koposa imfa, ndiko mkazi amene ndiye msampha, mtima wake ukunga maukonde, manja ake ndiwo matangadza; yemwe Mulungu amuyesa wabwino adzapulumuka kwa iye; koma wochimwa adzagwidwa naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:27-28

Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:18

Iye ananena kwa Iye, Otani? Ndipo Yesu anati, Usaphe, Usachite chigololo, Usabe, Usachite umboni wonama,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:21-23

Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: zoipa izi zonse zituluka m'kati, nizidetsa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:11-12

Ndipo Iye ananena nao, Munthu aliyense akachotsa mkazi wake, nakakwatira wina, achita chigololo kulakwira mkaziyo; ndipo ngati mkazi akachotsa mwamuna wake, nakwatiwa ndi wina, achita chigololo iyeyu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:18

Yense wakusudzula mkazi wake, nakwatira wina, achita chigololo; ndipo iye amene akwatira wosudzulidwayo, achita chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:3-5

Koma alembi ndi Afarisi anabwera naye kwa Iye mkazi wogwidwa m'chigololo, ndipo pamene anamuimika iye pakati, Pakulankhula Iye zimenezi ambiri anakhulupirira Iye. Chifukwa chake Yesu ananena kwa Ayuda aja adakhulupirira Iye, Ngati mukhala inu m'mau anga, muli ophunzira anga ndithu; ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani. Anamyankha iye, Tili mbeu ya Abrahamu, ndipo sitinakhala akapolo a munthu nthawi iliyonse; munena bwanji, Mudzayesedwa afulu? Yesu anayankha iwo, nati, Indetu, indetu, ndinena kwa inu kuti yense wakuchita tchimo ali kapolo wa chimolo. Koma kapolo sakhala m'nyumba nthawi yonse; mwana ndiye akhala nthawi yonse. Chifukwa chake ngati Mwana adzakuyesani inu aufulu, mudzakhala mfulu ndithu. Ndidziwa kuti muli mbeu ya Abrahamu; koma mufuna kundipha Ine, chifukwa mau anga alibe malo mwa inu. Zimene ndinaona Ine kwa Atate, ndilankhula; ndipo inunso muchita chimene mudamva kwa atate wanu. Anayankha nati kwa iye, Atate wathu ndiye Abrahamu. Yesu ananena nao, Ngati muli ana a Abrahamu, mukadachita ntchito za Abrahamu. ananena kwa Iye, Mphunzitsi, mkazi uyu wagwidwa alimkuchita chigololo. Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite. Inu muchita ntchito za atate wanu. Anati kwa Iye, Sitinabadwa ife m'chigololo; tili naye Atate mmodzi ndiye Mulungu. Yesu anati kwa iwo, Mulungu akadakhala Atate wanu, mukadakonda Ine; pakuti Ine ndinatuluka, ndi kuchokera kwa Mulungu; pakuti sindinadza kwa Ine ndekha, koma Iyeyu anandituma Ine. Simuzindikira malankhulidwe anga chifukwa ninji? Chifukwa simungathe kumva mau anga. Inu muli ochokera mwa atate wanu mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaime m'choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza. Koma Ine, chifukwa ndinena choonadi, simukhulupirira Ine. Ndani mwa inu anditsutsa Ine za tchimo? Ngati ndinena choonadi, simundikhulupirira Ine chifukwa ninji? Iye wochokera kwa Mulungu amva zonena za Mulungu; inu simumva chifukwa chakuti simuli a kwa Mulungu. Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda? Yesu anayankha, Ndilibe chiwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa. Koma m'chilamulo Mose anatilamula, tiwaponye miyala otere. Chifukwa chake Inu munena chiyani za iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 15:20

koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 15:29

kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 21:25

Koma kunena za amitundu adakhulupirirawo, tinalembera ndi kulamulira kuti asale zoperekedwa kwa mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:26-27

Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 7:2-3

Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo. Ndipo chotero ndipeza lamulo ili, kuti, pamene ndifuna chabwino, choipa chiliko. Pakuti monga mwa munthu wa m'kati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m'ziwalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la uchimo m'ziwalo zanga. Munthu wosauka ine; adzandilanditsa ndani m'thupi la imfa iyi? Ndiyamika Mulungu, mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Ndipo chotero ine ndekha ndi mtimatu nditumikira chilamulo cha Mulungu; koma ndi thupi nditumikira lamulo la uchimo. Ndipo chifukwa chake, ngati iye akwatiwa ndi mwamuna wina, pokhala mwamuna wake wamoyo, adzanenedwa mkazi wachigololo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamuloli; chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:13-14

Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai. Koma valani inu Ambuye Yesu Khristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:18-20

Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha. Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:2

Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:9

Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 7:39

Mkazi amangika pokhala mwamuna wake ali ndi moyo; koma atamwalira mwamuna ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:14-15

Musakhale omangidwa m'goli ndi osakhulupirira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Khristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupirira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupirira?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:2

Ndipo kuyenera woyang'anira akhale wopanda chilema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wodzisunga, wodziletsa, wolongosoka, wokonda kuchereza alendo, wokhoza kuphunzitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:2

akazi akulu ngati amai; akazi aang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:14-15

Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye ang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira; pakuti adayamba ena kupatuka ndi kutsata Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:1-5

Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro, mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira m'Antiokeya, m'Ikonio, m'Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa. Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo. Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa. Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:12

ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:14-15

koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:11

Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:3

Pakuti nthawi yapitayi idatifikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:2

Ndipo ambiri adzatsata zonyansa zao; chifukwa cha iwo njira ya choonadi idzanenedwa zamwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:10

koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:18-19

Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, iwo amene adayamba kupulumukira a mayendedwe olakwawo; ndi kuwalonjezera iwo ufulu, pokhala iwo okha ali akapolo a chivundi; pakuti iye amene munthu agonjedwa naye, ameneyonso adzakhala kapolo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:16

Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:4

Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:7

Monga Sodomu ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kutsata zilakolako zachilendo, iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chilango cha moto wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:14

Komatu ndili nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira chiphunzitso cha Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye chokhumudwitsa pamaso pa ana a Israele, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nachite chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:20-22

Komatu ndili nako kotsutsana ndi iwe, kuti ulola mkazi Yezebele, wodzitcha yekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasocheretsa akapolo anga, kuti achite chigololo ndi kudya zoperekedwa nsembe kwa mafano. Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake. Taona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akuchita chigololo naye kuwalonga m'chisautso chachikulu, ngati salapa iwo ndi kuleka ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:21

ndipo sanalapa mbanda zao, kapena nyanga zao, kapena chigololo chao, kapena umbala wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:4

Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoundukula kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 17:1-2

Ndipo anadza mmodzi mwa angelo asanu ndi awiri akukhala nazo mbale zisanu ndi ziwiri, nalankhula ndi ine, nanena, Idza kuno, ndidzakuonetsa chitsutso cha mkazi wachigololo wamkulu, wakukhala pa madzi ambiri, ndipo ali mafumu asanu ndi awiri asanu adagwa, imodzi iliko, yinayo siinadze; ndipo pamene ifika iyenera iyo kukhala kanthawi. Ndipo chilombo chinalicho, ndi kulibe, icho chomwe ndicho chachisanu ndi chitatu, ndipo chili mwa zisanu ndi ziwirizo, nichimuka kuchitayiko. Ndipo nyanga khumi udaziona ndiwo mafumu khumi, amene sanalandire ufumu; koma alandira ulamuliro ngati mafumu, ora limodzi, pamodzi ndi chilombo. Iwo ali nao mtima umodzi, ndipo apereka mphamvu ndi ulamuliro wao kwa chilombo. Iwo adzachita nkhondo pa Mwanawankhosa, ndipo Mwanawankhosa adzawalaka, chifukwa ali Mbuye wa ambuye, ndi Mfumu ya mafumu; ndipo adzawalakanso iwo akukhala naye, oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika. Ndipo anena ndi ine, Madziwo udawaona uko akhalako mkazi wachigololoyo ndiwo anthu, ndi makamu, ndi mitundu, ndi manenedwe. Ndipo nyanga khumi udaziona, ndi chilombo, izi zidzadana ndi mkazi wachigololoyo, nizidzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nizidzadya nyama yake, nizidzampsereza ndi moto. Pakuti Mulungu anapatsa kumtima kwao kuchita za m'mtima mwake, ndi kuchita cha mtima umodzi ndi kupatsa ufumu wao kwa chilombo, kufikira akwaniridwa mau a Mulungu. Ndipo mkaziyo unamuona, ndiye mudzi waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko. amene mafumu a dziko anachita chigololo naye, ndipo iwo akukhala padziko analedzera ndi vinyo wa chigololo chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 17:5

ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:3

Chifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anachita naye chigololo; ndipo ochita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyerera kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:9

Ndipo mafumu a dziko ochita chigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwake, poima patali,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:15-19

Imwa madzi a m'chitsime mwako, ndi madzi oyenda a m'kasupe mwako. Kodi magwero ako ayenera kumwazika kunja, ndi mitsinje ya madzi m'makwalala? Ikhale ya iwe wekha, si ya alendo okhala nawe ai. Adalitsike kasupe wako; ukondwere ndi mkazi wokula nayo. Ngati mbawala yokonda ndi chinkhoma chachisomo, maere ake akukwanire nthawi zonse; ukodwe ndi chikondi chake osaleka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:22

Monga chipini chagolide m'mphuno ya nkhumba, momwemo mkazi wokongola wosasinkhasinkha bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 3:9

Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lake inaipitsa dziko, ndipo anachita chigololo ndi miyala ndi mitengo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 13:27

Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:3

Koma sendererani kuno chifupi, inu ana amuna a watsenga, mbeu yachigololo ndi yadama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 4:10-11

Ndipo adzadya, koma osakhuta; adzachita chigololo, koma osachuluka; pakuti waleka kusamalira Yehova. Chigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 4:13-14

Pamwamba pa mapiri aphera nsembe, nafukiza pazitunda, patsinde pa thundu, ndi minjali, ndi mkundi; popeza mthunzi wake ndi wabwino, chifukwa chake ana anu akazi achita uhule, ndi apongozi anu achita chigololo. Sindidzalanga ana anu akazi pochita iwo uhule, kapena apongozi anu pochita chigololo iwo; pakuti iwo okha apatukira padera ndi akazi achiwerewere, naphera nsembe pamodzi ndi akazi operekedwa ku uhule; ndi anthu osazindikirawo adzagwetsedwa chamutu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 16:26

Wachitanso chigololo ndi Ejipito oyandikizana nawe, akulu thupi, ndi kuchulukitsa chigololo chako kuutsa mkwiyo wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 23:19-21

Koma anachulukitsa zigololo zake, nakumbukira masiku a ubwana wake, muja anachita chigololo m'dziko la Ejipito. Wobadwa ndi munthu iwe, panali akazi awiri, mai wao ndi mmodzi; Ndipo anaumirira amuna ao amene nyama yao ikunga ya abulu, ndi kutentha kwao ngati kutentha kwa akavalo. Momwemo wautsanso choipa cha ubwana wako, pakukhudza Aejipito nsonga za mawere ako, chifukwa cha mawere a ubwana wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 23:27

Motero ndidzakuleketsera choipa chako, ndi chigololo chako chochokera m'dziko la Ejipito; ndipo sudzazikwezeranso maso ako, kapena kukumbukiranso Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:17

Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:13

Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:8

Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:12-13

Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:22-24

kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:4

yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8-9

Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: ameneyo mumkanize okhazikika m'chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:23

Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:9

Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:5-6

Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:7

Potero mverani Mulungu; koma kanizani mdierekezi, ndipo adzakuthawani inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:8

Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Chauta wanga wachifundo ndi wamuyaya, Ambuye Wamkulukulu! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Woyera, ndi woyenera kutamandidwa ndi kupembedzedwa konse. Atate Woyera, ndikubwera kwa inu podziwa kuti ndinu nokha amene mungandilanditse ku ukapolo uliwonse umene ukundimanga ku dama. Ndikukupemphani kuti Mzimu wanu Woyera utsogolere moyo wanga kotero kuti maganizo anga, malingaliro anga, ndi zilakolako zanga zilamulidwe ndi kukhalapo kwanu ndipo mphamvu yanu ikhale ikukwaniritsa zofooka zanga. Ndilangizeni kukhala ndi mtima wofunitsitsa kumvera mawu anu ndi kusiya chilichonse chimene chimandilimbikitsa kuchita dama, kuti kuyambira tsano chilichonse chimene ndichita chikhale mogwirizana ndi chifuniro chanu. Simunandiyitane ku zodetsa, koma ku chiyeretso, ndikupemphani kuti munditeteze ku mayesero, ku mawu okopa ndi onyenga. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa