Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo

- Zotsatsa -


102 Mau a m'Baibulo Okhudza Nsembe

102 Mau a m'Baibulo Okhudza Nsembe

Nsembe ndi mphatso yopatulika kwa Mulungu, yodziwika ndi kumvera, khama, ndi kudzipereka, ndi chiyembekezo cholandira madalitso. Ndi kupereka kwa Ambuye chilichonse chimene akufuna popanda kumukana chilichonse, kumvera malamulo ake mosazengereza ndipo popanda kufuna mafotokozedwe.

Mwa Yesu tikuona chitsanzo chabwino cha izi: Mulungu anafuna kubwezeretsa mtendere pakati pa dziko lapansi ndi Iye, chifukwa tchimo linkatilepheretsa kukhala mu ulemerero wake, koma nsembe ya Yesu imatipatsa mwayi wopembedza Atate wathu wakumwamba mwaufulu. Nsembe zimene umapereka m'moyo wako nthawi zonse zimakupatsa cholinga, ndipo n’chifukwa chake umazichita mwachangu, ukuyembekezera kuona zotsatira zake.

Ambuye wathu sanasamale za ululu umene ankamva; cholinga chake chokha chinali kuchita chifuniro cha Atate wake padziko lapansi. Mulungu anapereka Mwana wake kuti tisatayike, ndiye, kodi iwe uli wokonzeka kupereka chiyani kwa Mulungu?

Akakupempha chinachake, uyenera kukhala wokonzeka kuvomereza popanda kukaikira mavuto amene amabwera chifukwa chomvera malamulo ake, potero kusonyeza chikondi chenicheni chomwe chingakupangitse kusiya dyera, kudzikuza, ndi kufuna kutchuka kwa anthu. Nsembe zimene umapereka si zongofuna kusonyeza anthu ena, koma ndi zochita zachikondi kwa Mlengi wako. Usakane kupereka nthawi yako, ndalama zako, kapena banja lako, chifukwa ngakhale kachitidwe kakang'ono kangayambitse zinthu zazikulu.

Mulungu anapereka moyo wa Mwana wake kuti atipulumutse, ndipo ndi nsembe zathu, masiku ano anthu ambiri akupulumutsidwa ku gehena. Ngakhale nthawi zina nsembe ingakhale yowawa, khala ndi chikhulupiriro kuti Mzimu Woyera adzakuthandiza nthawi zonse ndipo sadzakusiya.




Eksodo 20:24

Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 1:3-4

Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova. Ndipo aike dzanja lake pamutu pa nsembe yopsereza; ndipo idzalandiridwa m'malo mwake, imtetezere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:17

Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:22

Ndipo monga mwa chilamulo zitsala zinthu pang'ono zosayeretsedwa ndi mwazi, ndipo wopanda kukhetsa mwazi palibe kukhululukidwa kwa machimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:5

Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:17

Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa chikhulupiriro chanu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:5

inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:24

Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:22

Ndipo apereke nsembe zachiyamiko, nafotokozere ntchito zake ndi kufuula mokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 29:18

Pamenepo upsereze nkhosa yamphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza ya Yehova, ya fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:20

mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:32

Iye amene sanatimana Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:3

likumbukire zopereka zako zonse, lilandire nsembe yako yopsereza;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 4:27-31

Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula; akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake mbuzi yaikazi, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita. Aike dzanja lake pamutu pa nsembe yauchimo, naiphe nsembe yauchimo pamalo pa nsembe yopsereza. akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo. Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe. Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:15

Potero mwa Iye tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:2

ndipo Iye ndiye chiombolo cha machimo athu; koma wosati athu okha, komanso a dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:28

pakuti ichi ndi mwazi wanga wa pangano wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri ku kuchotsa machimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:21

Ameneyo sanadziwa uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:3

Kuchita chilungamo ndi chiweruzo kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:25

amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:6-8

Nsembe ndi chopereka simukondwera nazo; mwanditsegula makutu. Nsembe yopsereza ndi yamachimo simunapempha. Pamenepo ndinati, Taonani, ndadza; m'buku mwalembedwa za Ine, kuchita chikondwero chanu kundikonda, Mulungu wanga; ndipo malamulo anu ali m'kati mwamtima mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:11

Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:27

Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira; mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:14

Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:57

koma ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife chigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:2

ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:23-24

Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:8

Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:17

Ndidzapereka kwa Inu nsembe yachiyamiko, ndipo ndidzaitanira dzina la Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:14

Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:10

Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:18

Pakuti Khristunso adamva zowawa kamodzi, chifukwa cha machimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma wopatsidwa moyo mumzimu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:8

Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:22

Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:29-30

Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m'Gehena. Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:5

ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:14

Pereka kwa Mulungu nsembe yachiyamiko; numchitire Wam'mwambamwamba chowinda chako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:4

Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:3

Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:18

Koma ndili nazo zonse, ndipo ndisefukira; ndadzazidwa, popeza ndalandira kwa Epafrodito zija zidachokera kwanu, mnunkho wa fundo labwino, nsembe yolandirika, yokondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:26

chikadatero, kukadamuyenera kumva zowawa kawirikawiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi pa chitsirizo cha nthawizo waonekera kuchotsa uchimo mwa nsembe ya Iye yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 6:25-30

Lankhula ndi Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yauchimo ndi ichi: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yauchimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulika kwambiri. Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka chifukwa cha zoipa; aidyere m'malo opatulika, pa bwalo la chihema chokomanako. Aliyense akakhudza nyama yake adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wake wina pa chovala chilichonse, utsuke chimene adauwazacho m'malo opatulika. Ndipo mphika wadothi umene anaphikamo nyamayi auswe, koma ngati anaiphika mu mphika wamkuwa, atsuke uwu, nautsukuluze ndi madzi. Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulika kwambiri. kapena anapeza chinthu chotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa chimodzi cha izi zonse amachita munthu, ndi kuchimwapo; Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:7

koma ngati tiyenda m'kuunika, monga Iye ali m'kuunika, tiyanjana wina ndi mnzake, ndipo mwazi wa Yesu Mwana wake utisambitsa kutichotsera uchimo wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:19

Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo, ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu; pamenepo adzapereka ng'ombe pa guwa lanu la nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 22:13

Ndipo Abrahamu anatukula maso ake nayang'ana taonani, pambuyo pake nkhosa yamphongo yogwiridwa ndi nyanga zake m'chiyangoyangomo; ndipo ananka Abrahamu nakatenga nkhosa yamphongoyo, naipereka nsembe yopsereza m'malo mwa mwana wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:6

amene anadzipereka yekha chiombolo m'malo mwa onse; umboni m'nyengo zake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:6-7

Ndidzasamba manja anga mosalakwa; kuti ndizungulire guwa la nsembe lanu, Yehova; kuti ndimveketse mau a chiyamiko, ndi kulalikira ntchito zanu zonse zozizwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:39

Ndipo anamuka patsogolo pang'ono, nagwa nkhope yake pansi, napemphera, nati, Atate ngati nkutheka, chikho ichi chindipitirire Ine; koma si monga ndifuna Ine, koma Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:3

Ndipo anapatsa nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, chilemekezo cha kwa Mulungu wanga; ambiri adzachiona, nadzaopa, ndipo adzakhulupirira Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:16

Koma musaiwale kuchitira chokoma ndi kugawira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:7-9

Pakuti palibe mmodzi wa ife adzikhalira ndi moyo yekha, ndipo palibe mmodzi adzifera yekha. Pakuti tingakhale tili ndi moyo, tikhalira Ambuye moyo; kapena tikafa, tifera Ambuye; chifukwa chake tingakhale tili ndi moyo, kapena tikafa, tikhala ake a Ambuye. Pakuti, chifukwa cha ichi Khristu adafera, nakhalanso ndi moyo, kuti Iye akakhale Ambuye wa akufa ndi wa amoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:12

Chifukwa chake ndidzamgawira gawo ndi akulu; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wake kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula machimo a ambiri, napembedzera olakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:7

Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:4

Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 96:8

Mpatseni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani kumabwalo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:4

amene anadzipereka yekha chifukwa cha machimo athu, kuti akatilanditse ife m'nyengo ya pansi pano yino yoipa, monga mwa chifuniro cha Mulungu ndi Atate wathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:25

Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 22:29-30

Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike. Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova. Idyedwe tsiku lomwelo; musamasiyako kufikira m'mawa; Ine ndine Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1-2

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa. Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu lili lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu uli wamoyo chifukwa cha chilungamo. Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu. Chifukwa chake, abale, ife tili amangawa si ake a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi; pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo. Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu. Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate! Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye. Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife. Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu. Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 141:2

Pemphero langa liikike ngati chofukiza pamaso panu; kukweza manja anga kuikike ngati nsembe ya madzulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:17

Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:7

Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:108

Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga, ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 29:42

Ikhale nsembe yopsereza yosalekeza ya mwa mibadwo yanu, pa khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kumene ndidzakomana nanu, kulankhula nawe komweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:51

Ndipo onani, chinsalu chotchinga cha m'Kachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi; ndipo dziko linagwedezeka, ndi miyala inang'ambika;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:13

ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:17

Ndi chikhulupiriro Abrahamu, poyesedwa, anapereka nsembe Isaki, ndipo iye mene adalandira malonjezano anapereka mwana wake wayekha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:6

Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 4:5

Iphani nsembe za chilungamo, ndipo mumkhulupirire Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 69:30-31

Ndidzalemekeza dzina la Mulungu ndi kuliimbira, ndipo ndidzambukitsa ndi kumyamika. Ndipo chidzakomera Yehova koposa ng'ombe, inde mphongo za nyanga ndi ziboda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:24

amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:9

Musandichotsere mzimu wanga pamodzi ndi olakwa, kapena moyo wanga pamodzi ndi anthu okhetsa mwazi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:18

Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawirikawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:35

Ndipo pamene anampachika Iye, anagawana zovala zake ndi kulota maere:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 54:6

Ine mwini ndidzapereka nsembe yaufulu kwa Inu, ndidzayamika dzina lanu, Yehova, pakuti nlokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:8

Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:12

Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 29:31

Pamenepo Hezekiya anayankha, nati, Tsopano mwadzipatulira kwa Yehova, senderani, bwerani nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika kunyumba ya Yehova. Ndi msonkhano unabwera nazo nsembe zophera ndi nsembe zoyamika, ndi onse a mtima wofuna mwini anabwera nazo nsembe zopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:26

kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:14

koposa kotani nanga mwazi wa Khristu amene anadzipereka yekha wopanda chilema kwa Mulungu mwa Mzimu wosatha, udzayeretsa chikumbu mtima chanu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:5

Mundisonkhanitsire okondedwa anga; amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 31:54

Ndipo Yakobo anapereka nsembe paphiripo, naitana abale ake kuti adye chakudya; ndipo anadya chakudya, nagona paphiripo usiku wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:16

kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 130:7

Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:24

podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:13-15

Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzakuchitirani zowinda zanga, zimene inazitchula milomo yanga, ndinazinena pakamwa panga posautsika ine. Ndidzakufukizirani nsembe zopsereza zonona, pamodzi ndi chofukiza cha mphongo za nkhosa; ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:7

Koma mukadadziwa nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; simukadaweruza olakwa iwo osachimwa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 22:2

Ndipo anati, Tengatu mwana wako, wamwamuna wayekhayo, Isaki, amene ukondana naye, numuke ku dziko la Moriya; numpereke iye kumeneko nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri lomwe ndidzakuuza iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 8:20

Ndipo Nowa anamanga guwa la nsembe la Yehova; natengapo nyama zodyedwa zonse ndi mbalame zodyedwa zonse napereka nsembe zopsereza paguwapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:12

koma Iye, m'mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu chikhalire;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 17:11

Pakuti moyo wa nyama ukhala m'mwazi; ndipo ndakupatsani uwu pa guwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 4:35

nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa pa guwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 5:10

Ndipo aikonze inzake ikhale nsembe yopsereza, monga mwa lemba lake; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa adachimwira, ndipo adzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 3:21

Yehova Mulungu ndipo anapangira Adamu ndi mkazi wake malaya azikopa, nawaveka iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 4:4

Ndiponso Abele anatenga iyenso mwana woyamba wa nkhosa zake ndi mafuta omwe. Yehova ndipo anayang'anira Abele ndi nsembe yake:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 16:30

popeza tsikuli adzachitira inu chotetezera, kukuyeretsani; adzakuyeretsani, kukuchotserani zoipa zanu zonse pamaso pa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 16:15

Pamenepo aiphe mbuzi ya nsembe yauchimo, ndiyo yophera anthu, nalowe nao mwazi wake m'tseri mwa nsalu yotchinga, nachite nao mwazi wake monga umo anachitira ndi mwazi wa ng'ombe, nauwaze pachotetezerapo ndi chakuno cha chotetezerapo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:13

Ndipo mwaziwo udzakhala chizindikiro kwa inu pa nyumba zimene mukhalamo; pamene ndiona mwaziwo ndidzapitirira inu, ndipo sipadzakhala mliri wakukuonongani, pakukantha Ine dziko la Ejipito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, ndimakukondani ndipo ndikuthokozani chifukwa cha chikondi chanu chopanda malire ndi chifundo chanu. Zikomo chifukwa cha kukoma mtima kwanu kwa ine, nthawi zonse mumandionetsera chifundo chanu. Ambuye Yesu, zikomo chifukwa chobwera kudziko lino kudzandipulumutsa ku uchimo ndi kundipatsa moyo wosatha. Ambuye, zikomo chifukwa cha nsembe iliyonse yomwe mudapereka kuti ine ndikhale womasuka ku imfa. Mzimu Woyera, mundiphunzitse kupereka nsembe yoyamika tsiku lililonse, mosasamala kanthu za mavuto omwe ndikukumana nawo. Monga Paulo ndi Sila, ndikhale ndi nyimbo mkamwa mwanga kuti zitseko zitseguke. Ndifuna kupereka nsembe yachikondi kwa inu monga Abrahamu. Ndisungeni ndikukulemekezani Mulungu, monga momwe Davide anachitira. Atate, m'dzina la Yesu, ndikupemphani kuti munditsogolere ndi kuyika chikondi ndi chidziwitso mumtima mwanga kuti ndipereke nsembe zoyenera kwa inu monga momwe Abele anachitira. Munditsuke ndi kundiyera ndi magazi anu Yesu kuti ndikhale woyenera pamaso pa Mulungu wanga ndi kukusondweretsani nthawi zonse. Inu wokondedwa wanga ndinu chitsanzo chachikulu cha nsembe, pakuti lemba limati: "koma Khristu atapereka nsembe imodzi yokha ya machimo nthawi zonse, anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu." Zikomo Ambuye chifukwa cha chikhulupiriro chomwe mwandipatsa, zikomo chifukwa choti ndinu chitsanzo changa cha chikondi, cha chikhululukiro, ndi cha nsembe. Zikomo Ambuye chifukwa cha moyo wanga, banja langa, nyumba yanga, anzanga, chifukwa chondiletsa kugawana zonse zomwe mumandipatsa nawo. Zikomo Ambuye chifukwa cha kukoma mtima kwanu kopanda malire ndi chikhululukiro, m'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa