Ndikayang'ana chilengedwe cha Mulungu, kukongola kwake konse, ndimadabwa kwambiri ndi ukulu wake ndi dongosolo lake labwino. Kuyambira kale, anthufe timayesetsa kumvetsa dziko ndi cholinga chake m'njira zosiyanasiyana. Koma Baibulo limatipatsa njira yoona zinthu yotithandiza kumvetsa bwino dzikoli.
M'mavesi oyamba a buku la Genesis, timapeza kuti Mulungu ndiye analenga thambo ndi dziko lapansi, ndi zonse zili mmenemo. "Pachiyambi Mulungu analenga thambo ndi dziko lapansi." (Genesis 1:1). Mawu awa, ochepa koma ofunika kwambiri, amatiuza kuti chilengedwe chonse chinachokera kwa Mulungu. Dziko linapangidwa ndi Mlengi Wamkulu.
Baibulo limatilimbikitsa kuona kupitirira zomwe maso athu akuona, ndikuganizira cholinga chenicheni cha chilengedwechi. Mu Salmo 19:1, limati: "Zakumwamba zimalengeza ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo limasonyeza ntchito ya manja ake." Apa tikuona kuti dziko sili mboni chete ya ukulu wa Mulungu, koma limalankhulanso za kukhalapo ndi mphamvu zake kwa ife.
Dziko limatilimbikitsa kuona ukulu wa Mulungu m'chilengedwe chake. Limatithandiza kumvetsa kuti dziko limene tikukhala ndilo umboni wa chikondi, mphamvu, ndi nzeru za Mlengi wathu.
Ndi chikhulupiriro tizindikira kuti maiko ndi a m'mwamba omwe anakonzedwa ndi mau a Mulungu, kotero kuti zinthu zopenyeka sizinapangidwa zochokera mwa zoonekazo.
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.
Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.
Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mwini kumwamba ndi dziko lapansi;
Napemphera Hezekiya pamaso pa Yehova, nati, Yehova Mulungu wa Israele wakukhala pakati pa akerubi, Inu ndinu Mulungu mwini wake, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi; munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, amene mukhala pa akerubi, Inu ndinu Mulungu, Inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Atero Yehova, Mombolo wako, ndi Iye amene anakuumba iwe m'mimba, Ine ndine Yehova, amene ndipanga zinthu zonse, ndi kufunyulula ndekha zakumwamba, ndi kuyala dziko lapansi; ndani ali ndi Ine?
pakuti mwa Iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yachifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa Iye ndi kwa Iye.
Yehova atero: Likaleka kukhala pangano langa la usana ndi usiku, ngati sindinalemba malemba a kumwamba ndi dziko lapansi;
Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwake khamu lao lonse.
Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndivomerezana ndi Inu, Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:
Zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa.
Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;
Inu ndinu Yehova, nokhanu; mwalenga thambo, kumwambamwamba, ndi khamu lao lonse, dziko lapansi, ndi zonse zili pomwepo, nyanja ndi zonse zili m'mwemo, ndi Inu muzisunga zamoyo zonsezi, ndi khamu lakumwamba lilambira Inu.
Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine.
Pakuti taona, Iye amene aumba mapiri, nalenga mphepo, nafotokozera munthu maganizo ake, nasanduliza m'mawa ukhale mdima, naponda pa misanje ya dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova Mulungu wa makamu.
Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake;
Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira. pamene ibwatama m'ngaka mwao, nikhala mobisala kulaliramo? Amkonzeratu khungubwi chakudya chake ndani, pamenepo ana ake afuulira kwa Mulungu, naulukauluka osowa chakudya? Analemba malire ake ndani, popeza udziwa? Anayesapo chingwe chake ndani? Maziko ake anakumbidwa pa chiyani? Kapena anaika ndani mwala wake wa pangodya, muja nyenyezi za m'mawa zinaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe?
Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?
Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;
Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina ao, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.
Ndipo Mulungu anati, Pakhale zounikira pa thambo la kumwamba, zakulekanitsa usana ndi usiku; zikhale zizindikiro ndi nyengo, ndi masiku, ndi zaka; Zikhale zounikira m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi: ndipo kunatero. Ndipo Mulungu anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching'ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe. Mulungu ndipo adaika zimenezo m'thambo la kumwamba, kuti ziunikire pa dziko lapansi. Nizilamulire usana ndi usiku, nizilekanitse kuyera ndi mdima: ndipo anaona Mulungu kuti kunali kwabwino.
Amene analenga zakumwamba mwanzeru; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene analenga miuni yaikulu; pakuti chifundo chake nchosatha. Dzuwa liweruze usana; pakuti chifundo chake nchosatha. Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku; pakuti chifundo chake nchosatha.
Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu.
Ndipo kumwamba kudzalemekeza zodabwitsa zanu, Yehova; chikhulupiriko chanunso mu msonkhano wa oyera mtima.
Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova;
muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga.
Yehova anakhazika dziko ndi nzeru; naika zamwamba ndi luntha. pakuti adzakuonjezera masiku ambiri, ndi zaka za moyo ndi mtendere. Zakuya zinang'ambika ndi kudziwa kwake; thambo ligwetsa mame.
Inde dzanja langa linakhazika maziko a dziko lapansi, ndi dzanja langa lamanja linafunyulula m'mwamba; pakuziitana Ine ziimirira pamodzi.
Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.
Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.
ameneyo, pokhala ali chinyezimiro cha ulemerero wake, ndi chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe chake, nanyamula zonse ndi mau a mphamvu yake, m'mene adachita chiyeretso cha zoipa, anakhala pa dzanja lamanja la Ukulu m'Mwamba,
Munakhazika dziko lapansi kalelo; ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu. Zidzatha izi, koma Inu mukhala: Inde, zidzatha zonse ngati chovala; mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika: Koma Inu ndinu yemweyo, ndi zaka zanu sizifikira kutha.
Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekezero a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati chinsalu, naliyala monga hema wakukhalamo;
Pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula;
Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.
Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo. Mfumu imene ya ulemerero ndani? Yehova wa makamumakamu, ndiye Mfumu ya ulemerero. Pakuti Iye analimanga pazinyanja, nalikhazika pamadzi.
Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.
Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.
Taonani, awa ndi malekezero a njira zake; ndi chimene tikumva za Iye ndi chinong'onezo chaching'ono; koma kugunda kwa mphamvu yake akudzindikiritsa ndani?
Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu; wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno; dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.
Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.
Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu. Nyanja siyo, yaikulu ndi yachitando, m'mwemo muli zokwawa zosawerengeka; zamoyo zazing'ono ndi zazikulu.
Ndani wayesa madzi m'dzanja lake, nayesa thambo ndi chikhato, ndi kudzaza fumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo?
Kodi Mulungu sakhala m'mwamba m'tali? Ndipo penyani kutalika kwake kwa nyenyezi, zili m'talitali.
Aleluya. Lemekezani Yehova kochokera kumwamba; mlemekezeni m'misanje. Nyama za kuthengo ndi zoweta zonse; zokwawa, ndi mbalame zakuuluka. Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu; zinduna ndi oweruza onse a padziko. Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana. Alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo. Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya. Mlemekezeni, angelo ake onse; mlemekezeni, makamu ake onse. Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi; mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira. Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo. Alemekeze dzina la Yehova; popeza analamulira, ndipo zinalengedwa. Anazikhazikanso kunthawi za nthawi; anazipatsa chilamulo chosatumphika.
Pakuti milungu yonse ya mitundu ya anthu ndiyo mafano, koma Yehova analenga zakumwamba.
koma kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye, ndi ife kufikira kwa Iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Khristu, amene zinthu zonse zili mwa Iye, ndi ife mwa Iye.
Iye analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake, nakhazikitsa dziko lapansi ndi nzeru yake, nayala thambo ndi kuzindikira kwake; polankhula Iye, pali unyinji wa madzi m'mwamba, ndipo akweretsa nkhungu ku malekezero a dziko lapansi, alenga mphezi idzetse mvula, natulutsa mphepo m'zosungira zake.
ndi okhala pa dziko lapansi onse ayesedwa achabe; ndipo Iye achita mwa chifuniro chake m'khamu la kumwamba ndi mwa okhala pa dziko lapansi; ndipo palibe woletsa dzanja lake, kapena wakunena naye, Muchitanji?
Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.
Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu, munakonza kuunika ndi dzuwa. Munaika malekezero onse a dziko lapansi; munalenga dzinja ndi malimwe.
chifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamaliza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse zili m'menemo, napumula tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika.
Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenge mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu; Ine ndine Yehova; ndipo palibenso wina.
waiwala Yehova Mlengi wako, amene anayala m'mwamba, nakhazika maziko a dziko lapansi, ndi kuopabe tsiku lonse chifukwa cha ukali wa wotsendereza, pamene iye akonzeratu kupasula? Uli kuti ukali wa wotsendereza?
Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m'mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.
Tamverani ichi, Yobu. Taimani, mulingirire zodabwitsa za Mulungu. Kodi mudziwa umo Mulungu azilangizira zimenezi, nawalitsa mphezi ya m'mtambo mwake? Kodi mudziwa madendekeredwe ake a mitambo, zodabwitsa za Iye wakudziwa mwangwiro?
Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti? Sangalalani inu pamodzi ndi Yerusalemu, ndipo kondwani chifukwa cha iye, inu nonse amene mumkonda; sangalalani kokondwa pamodzi ndi iye, inu nonse akumlira maliro; kuti mukayamwe ndi kukhuta ndi mawere a zitonthozo zake; kuti mukafinye mkaka ndi kukondwerera ndi unyinji wa ulemerero wake. Pakuti atero Yehova, Taonani ndidzamfikitsira mtendere ngati mtsinje, ndi ulemerero wa amitundu ngati mtsinje wosefukira. Inu mudzayamwa, ndi kunyamulidwa pambali, ndi kululuzidwa pa maondo. Monga munthu amene amake amtonthoza mtima, momwemo ndidzatonthoza mtima wanu; ndipo mudzatonthozedwa mtima m'Yerusalemu. Ndipo mudzachiona, ndipo mtima wanu udzasangalala, ndipo mafupa anu adzakula ngati msipu; ndipo dzanja la Yehova lidzadziwika ndi atumiki ake, ndipo adzakwiyira adani ake. Pakuti taonani, Yehova adzafika m'moto, ndi magaleta ake adzafanana ndi kamvulumvulu; kubwezera mkwiyo wake ndi ukali, ndi kudzudzula ndi malawi amoto. Pakuti Yehova adzatsutsana ndi moto, ndi lupanga lake, ndi anthu onse; ndi ophedwa a Yehova adzakhala ambiri. Iwo amene adzipatulitsa nadziyeretsa, kuti amuke kuminda tsatanetsatane, ndi kudya nyama ya nkhumba, ndi chonyansa, ndi mbewa, adzathedwa pamodzi, ati Yehova. Pakuti Ine ndidziwa ntchito zao ndi maganizo ao; nthawi ikudza yakudzasonkhanitsa Ine a mitundu yonse ndi zinenedwe zonse, ndipo adzafika nadzaona ulemerero wanga. Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu. Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.
Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.
Kumwamba kulalikira chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake.
Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati fumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono.
Lemekeza Yehova, moyo wanga; Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkulukulu; Atumiza akasupe alowe m'makwawa; ayenda pakati pa mapiri: Zimamwamo nyama zonse za kuthengo; mbidzi zipherako ludzu lao. Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo, zimaimba pakati pa mitawi. Iye amwetsa mapiri mochokera m'zipinda zake: Dziko lakhuta zipatso za ntchito zanu. Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka; ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu, ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake, ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu. Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka; m'mwemo mbalame zimanga zisa zao; pokhala chumba mpa mitengo ya mikungudza. Mapiri atali ndiwo ayenera zinkhoma; pamatanthwe mpothawirapo mbira. Anaika mwezi nyengo zake; dzuwa lidziwa polowera pake. muvala ulemu ndi chifumu. Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala; ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga.
Atate, amene mwandipatsa Ine, ndifuna kuti, kumene ndili Ine, iwonso akhale pamodzi ndi Ine; kuti ayang'anire ulemerero wanga, umene mwandipatsa Ine; pakuti munandikonda Ine lisanakhazikike dziko lapansi.
Pamene anakhazika mlengalenga ndinali pompo; pamene analemba pazozama kwetekwete; polimbitsa Iye thambo la kumwamba, pokula akasupe a zozama. Poikira nyanja malire ake, kuti madzi asapitirire pa lamulo lake; polemba maziko a dziko.
Pakuti ichi aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;
ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake pa dziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova.
Iye amwetsa mapiri mochokera m'zipinda zake: Dziko lakhuta zipatso za ntchito zanu. Ameretsa msipu ziudye ng'ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m'nthaka;
Igwani pansi, inu m'mwamba, kuchokera kumwamba, thambo litsanulire pansi chilungamo; dziko lapansi litseguke, kuti libalitse chipulumutso, nilimeretse chilungamo chimere pamodzi; Ine Yehova ndinachilenga chimenecho.
Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.
nalumbira kutchula Iye amene ali ndi moyo kunthawi za nthawi, amene analenga m'mwamba ndi zinthu zili momwemo, ndi dziko lapansi ndi zinthu zili momwemo, ndi nyanja ndi zinthu zili momwemo kuti sipadzakhalanso nthawi:
Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.
Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.
yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.
Ndi pamwamba pa thambolo linali pamitu pao panali chifaniziro cha mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati mwala wa safiro; ndipo pa chifaniziro cha mpando wachifumu panali chifaniziro ngati maonekedwe ake a munthu wokhala pamwamba pake. Ndipo ndinapenya ngati chitsulo chakupsa, ngati maonekedwe ake a moto m'kati mwake pozungulira pake, kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake; ndipo kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake ndinaona ngati maonekedwe ake a moto; ndi kunyezimira kudamzinga. Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwake pozungulira pake. Ndiwo maonekedwe a chifaniziro cha ulemerero wa Yehova. Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.
Amene analenga miuni yaikulu; pakuti chifundo chake nchosatha. Dzuwa liweruze usana; pakuti chifundo chake nchosatha. Mwezi ndi nyenyezi ziweruze usiku; pakuti chifundo chake nchosatha.
ndi kunena ndi mau akulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m'mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.
Ndipo aphunzitsi adzawala ngati kunyezimira kwa thambo; ndi iwo otembenuza ambiri atsate chilungamo ngati nyenyezi kunthawi za nthawi.
Afanana ndi Inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi Inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?
Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha; Yehova akondwere mu ntchito zake; amene apenyerera pa dziko lapansi, ndipo linjenjemera; akhudza mapiri, ndipo afuka.
Chikhulupiriko chanu chifikira mibadwomibadwo; munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa. Kunena za maweruzo anu alimbikira kufikira lero; pakuti onsewa ndiwo atumiki anu.
Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi.
Ntchito za Yehova nzazikulu, zofunika ndi onse akukondwera nazo. Chochita Iye ncha ulemu, ndi ukulu: Ndi chilungamo chake chikhalitsa kosatha.
Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.