Chifundo cha Mulungu n’chachulukitsitsa, mpaka chingati chiposa moyo weniweniwo. Tangoganizani, moyo wanga ukanakhala wopanda phindu ndikanapanda kuona chikondi cha Mulungu m’mawa uliwonse. Amandikonda kwambiri moti sanandisiye ngakhale ndili ndi zolakwa zambiri.
Ndani angapeze mtendere ngati chifundo cha Mulungu sichingawonekere pa moyo wake? Ine sindingathe kuganiza wina aliyense. Munthu wopanda Mulungu ali ngati chotengera chopanda kanthu, wodzala ndi uchimo ndipo ali mu dziko lachitayiko.
Koma Mulungu atandiwonetsa kukoma mtima kwake, ndimazindikira zonse zomwe amandithandiza kuyambira ndikadzuka mpaka ndikagona. Ndikamaganizira zoyipa zomwe ndimachita ndi kuipa kwanga, mtima wanga umakhudzidwa kwambiri moti ndimayamba kuthokoza Mulungu nthawi zonse.
Kungoti ndikupumirabe ndi chizindikiro cha chifundo cha Mulungu pa ine. Wandikhululukira, wanditsuka uchimo wanga, ndipo wanatenga chilango chomwe ndinayenera kulandira. Chifukwa cha ichi, ndiyenera kuthokoza. Tsegulani pakamwa panu, muthokoze Mulungu. Wakhalandi wabwino, wakuganizirani, wakuonani ndi maso achikondi, ndipo sanakanepo chifundo chake chachikulu, chifundo chomwe sichingathe kutha.
Yamikirani lero ndi nthawi zonse chikondi chachikulu cha Yesu kwa inu, yamikirani magazi ake amtengo wapatali, ndipo mulowe mu chikondi Chake.
Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni. Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.
Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu. Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.
Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Amitundu onse adandizinga, zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Adandizinga, inde, adandizinga: Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Kundikankha anandikankha ndikadagwa; koma Yehova anandithandiza. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa. M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso: Dzanja lamanja la Yehova likwezeka, Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu. Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova. Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai. Nditsegulireni zipata za chilungamo; ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova. Anene tsono Israele, kuti chifundo chake nchosatha.
Kumbukirani, Yehova, nsoni zanu ndi chifundo chanu; pakuti izi nza kale lonse. Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.
Pakuti mapiri adzachoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakuchokera iwe, kapena kusunthika chipangano changa cha mtendere, ati Yehova amene wakuchitira iwe chifundo.
Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu;
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.
Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.
Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.
Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, wotitonthoza ife m'nsautso yathu yonse, kuti tidzathe ife kutonthoza iwo okhala m'nsautso iliyonse, mwa chitonthozo chimene titonthozedwa nacho tokha ndi Mulungu.
Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa.
Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana; kwa iwo akusunga chipangano chake, ndi kwa iwo akukumbukira malangizo ake kuwachita.
Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa. Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.
Israele, uyembekezere Yehova; chifukwa kwa Yehova kuli chifundo, kwaonso kuchulukira chiombolo. Ndipo adzaombola Israele ku mphulupulu zake zonse.
Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.
Ndinali mwana ndipo ndakalamba; ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zilinkupempha chakudya.
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima;
Mundiyankhe Yehova; pakuti chifundo chanu nchokoma; munditembenukire monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu.
kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni?
Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga. Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga. Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere Mzimu wanu Woyera. Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu; ndipo mzimu wakulola undigwirizize. Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu; ndipo olakwa adzabwera kwa Inu. Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu, ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu. Ambuye, tsegulani pa milomo yanga; ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu. Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka; nsembe yopsereza simuikonda. Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa. Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu; mumange malinga a miyala a Yerusalemu. Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo, ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu; pamenepo adzapereka ng'ombe pa guwa lanu la nsembe. Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga, ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.
Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.
Koma pamene kukoma mtima, ndi chikondi cha pa anthu, cha Mpulumutsi wathu Mulungu zidanoneka, zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo atali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake. Zisoni zambiri zigwera woipa; koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova. Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima. Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake; ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.
Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.
Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu.
Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,
Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; chifukwa chake bwererani, nimukhale ndi moyo.
Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse.
Mundichitire chifundo, Yehova; pakuti ndalefuka ine. Mundichize, Yehova; pakuti anthunthumira mafupa anga.
Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zokoma zanu mufafanize machimo anga.
Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.
amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe;
Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo.
Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Iye amene anapandira Aejipito ana ao oyamba; pakuti chifundo chake nchosatha. Natulutsa Israele pakati pao; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anagawa magawo Nyanja Yofiira; pakuti chifundo chake nchosatha. Napititsa Israele pakati pake; pakuti chifundo chake nchosatha. Nakhuthula Farao ndi khamu lake m'Nyanja Yofiira: pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anatsogolera anthu ake m'chipululu; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anapanda mafumu akulu; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndipo anawapha mafumu omveka; pakuti chifundo chake nchosatha. Sihoni mfumu ya Aamori; pakuti chifundo chake nchosatha. Yamikani Mulungu wa milungu; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndi Ogi mfumu ya Basani; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndipo anapereka dziko lao likhale chosiyira; pakuti chifundo chake nchosatha. Chosiyira cha kwa Israele mtumiki wake; pakuti chifundo chake nchosatha. Amene anatikumbukira popepuka ife; pakuti chifundo chake nchosatha. Natikwatula kwa otisautsa; pakuti chifundo chake nchosatha. Ndiye wakupatsa nyama zonse chakudya; pakuti chifundo chake nchosatha. Yamikani Mulungu wa kumwamba; pakuti chifundo chake nchosatha. Yamikani Mbuye wa ambuye; pakuti chifundo chake nchosatha.
Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi? Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.
woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.
Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.
komatu mwa ichi anandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Khristu akaonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha.
Chilungamo ndi chiweruzo ndiwo maziko a mpando wachifumu wanu; chifundo ndi choonadi zitsogolera pankhope panu.
ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi.
Yehova adzanditsirizira za kwa ine: Chifundo chanu, Yehova, chifikira kunthawi zonse: Musasiye ntchito za manja anu.
ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa, Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu pakati pa anthu amitundu, ndidzaimbira dzina lanu.
Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu, chifukwa cha dzina lanu.
Pemphani, ndipo chidzapatsidwa kwa inu; funani, ndipo mudzapeza; gogodani, ndipo chidzatsegulidwa kwa inu;
Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani, monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.
tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbu mtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.
Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawachitira chifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.
Mundimvetse chifundo chanu mamawa; popeza ndikhulupirira Inu: Mundidziwitse njira ndiyendemo; popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.
Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.
Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.
Pakuti monga m'mwamba mutalikira ndi dziko lapansi, motero chifundo chake chikulira iwo akumuopa Iye. Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.
Pakuti chifundo chanu nchachikulu kufikira m'mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo.
Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake.
Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,
Ndipo Mulungu wa chisomo chonse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wake wosatha mwa Khristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda chilema mwini wake, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.
Pakuti mphulupulu zanga zapitirira pamutu panga; ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera.
Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.
Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.
koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho, tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),
popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wachifundo; sadzakusiyani, kapena kukuonongani, kapena kuiwala chipangano cha makolo anu chimene analumbirira iwo.
Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.
ndipo ng'ambani mitima yanu, si zovala zanu ai; ndi kutembenukira kwa Yehova Mulungu wanu; pakuti Iye ndiye wachisomo, ndi wodzala chifundo, wosapsa mtima msanga, ndi wochuluka kukoma mtima, ndi woleka choipacho.
Koma Yehova anali ndi Yosefe namchitira iye zokoma, nampatsa ufulu pamaso pa woyang'anira kaidi.
zosati zochokera m'ntchito za m'chilungamo, zimene tidazichita ife, komatu monga mwa chifundo chake anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa.
Chifukwa chakusathedwa ife ndicho chifundo cha Yehova, pakuti chisoni chake sichileka, chioneka chatsopano m'mawa ndi m'mawa; mukhulupirika ndithu.
Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.
M'mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi chiweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza.
Inde ukoma ndi chifundo zidzanditsata masiku onse a moyo wanga, ndipo ndidzakhala m'nyumba ya Yehova masiku onse.
Ndi chifundo Inu mudzadzionetsa wachifundo, ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro.