Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


106 Mauvesi Ovuta Kufotokoza a M'Baibulo

106 Mauvesi Ovuta Kufotokoza a M'Baibulo

Ndikukuuzani inu, palibe chofanana ndi kudzionera wekha. Mukakhala ndi Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku, mumapeza njira yabwino yolankhulira uthenu kwa ena. Uthenu umenewu ukhoza kusintha miyoyo ya anthu ambiri.

Palibe chomwe chimakhudza mtima wa munthu kuposa uthenu womwe wabwera chifukwa choona zinthu ndi maso ako. Komabe, Mzimu Woyera ndiye chinsinsi chachikulu. Iye ndiye amadziwa zonse ndipo amatipatsa nzeru zomwe timafunikira kuti timvetse bwino Mawu a Mulungu.

Tisamadalire kwambiri maganizo athu okha kapena nkhani za anthu ena. Zinthu zimenezi sizingatithandize kulankhula bwino uthenu ngati sitinazione tokha. Tikamadalira maganizo athu okha, nthawi zina tingasowe choti tinene.

Mzimu Woyera akufunitsitsa kutiphunzitsa lero. Mulole kuti akuthandizeni kumvetsa ndi kufotokoza uthenu wanu m'njira yoti ena amvetse.




1 Petro 3:18-19

Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo. Ndipo ali ngati mzimu choncho, adapita kukalalika kwa mizimu imene inali m'ndende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 2:1

Tsiku lina pamene angelo a Mulungu ankabwera kudzadziwonetsa pamaso pa Chauta, nayenso Satana adafika nawo limodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:18

Pano pafunika nzeru. Yemwe ali ndi nzeru atanthauze nambala ya chilomboyo, pakuti nambalayo ikutanthauza munthu. Nambala yake ndi 666.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 6:1-4

Nthaŵi imeneyo anthu anali atayamba kuchuluka pa dziko lonse lapansi, ndipo adabereka ana aakazi. Anali ndi ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti. Koma anthu ena onse anali oipa pamaso pa Mulungu, ndipo kuipa kwao kudawanda ponseponse. Mulungu atayang'ana dziko lapansi, adaona kuti ndi lonyansa, chifukwa anthu onse anali oipa kwambiri. Choncho Mulungu adauza Nowa kuti, “Ndatsimikiza mu mtima kuti ndiwononge anthu onse. Ndidzaŵaononga kotheratu chifukwa dziko lonse lapansi ladzaza ndi ntchito zao zoipa. Udzipangire chombo ndipo uchipange ndi matabwa a mtengo wa mnjale. Upange zipinda m'menemo, ndipo uchimate phula kunja kwake ndi m'kati momwe. M'litali mwake mwa chombocho mukhale mamita 140. M'mimba mwake mukhale mamita 23, ndipo msinkhu wake ukhale wa mamita 13 ndi theka. Upange denga la chombocho, ndipo usiye mpata wa masentimita 50 pakati pa dengalo ndi mbali zake. Uchimange mosanjikiza, chikhale cha nyumba zitatu, ndipo m'mbali mwake mukhale chitseko. Ndidzagwetsa mvula yachigumula pa dziko lapansi, kuti iwononge zamoyo zonse. Zonse zapadziko zidzafa, koma iweyo ndidzachita nawe chipangano. Udzaloŵe m'chombomo iwe pamodzi ndi mkazi wako, ndi ana ako pamodzi ndi akazi ao. Ndipo udzatengenso nyama za mtundu uliwonse, yaimuna ndi yaikazi, kuti zisungidwe ndi moyo. Ana aamuna a Mulungu adaona kuti ana aakazi a anthu anali okongola, nayamba kukwatira amene ankaŵakonda. Mbalame za mtundu uliwonse ndi nyama zazikulu ndi zokwaŵa zomwe, zidzaloŵe m'chombo kuti zisungidwe ndi moyo. Udzatengenso zakudya za mtundu uliwonse kuti inu ndi nyamazo muzidzadya.” Motero Nowa adachitadi zonse zimene Mulungu adamlamula. Tsono Chauta adati, “Sindidzalola anthu kukhala ndi moyo mpaka muyaya, popeza kuti munthu ndi thupi limene limafa. Kuyambira tsopano adzangokhala zaka 120.” Pa masiku amenewo, ngakhale pambuyo pakenso, panali anthu amphamvu ataliatali pa dziko lapansi. Anthu ameneŵa ndi amene ankabadwa mwa akazi omwe adaakwatiwa ndi ana a Mulungu aja. Iwoŵa anali ngwazi zomveka ndiponso anthu otchuka pa masiku akalewo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 33:20

Chauta adaonjeza kuti, “Koma sungathe kuwona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu angathe kundiwona Ine, nakhala moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 11:7

Nkhumba: imeneyi njonyansa kwa inu, chifukwa ngakhale ziboda zake nzogaŵikana ndipo mapazi ake ngogaŵikananso, koma siibzikula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 20:16-17

Koma mukadzalanda mizinda imene ili m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsaniyo, muphe aliyense. Muŵaononge kotheratu onse anthu aŵa: Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi, monga momwe Chauta Mulungu wanu adakulamulirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 11:30-31

Yefita adalumbira kwa Chauta kuti, “Mukandithandiza kugonjetsa Aamoniŵa, aliyense amene atuluke pakhomo pa nyumba yanga kudzandichingamira pobwerera, nditagonjetsa Aamoniwo, adzakhala wake wa Chauta ndipo ndidzampereka kuti akhale nsembe yopsereza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 24:1

Nthaŵi ina Chauta adaŵakwiyiranso Aisraele, choncho adautsa mtima wa Davide kuti aŵavutitse. Adamuuza kuti, “Pita ukaŵerenge Aisraele ndi Ayuda.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 13:18

Nkhalambayo idamuuza kuti, “Inenso ndine mneneri monga inu nomwe, ndipo mngelo adalankhula nane nandiwuza kuti, ‘Ubwerere naye limodzi kunyumba kwako, kuti akadye chakudya ndiponso akamweko madzi.’ ” Nkhalambayo inkamuuza zabodza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 38:1-4

Apo Chauta adayankha Yobe m'kamvulumvulu kuti, Ndidailembera malire, ndidaiikira mipiringidzo ndi zitseko zake. Tsono ndidati, ‘Ufike mpaka apo osabzolapo, mafunde ako amphamvuwo aime pomwepo.’ “Kodi chibadwire chako udalamulapo dzuŵa kuti lituluke m'maŵa, ndi kuti mbandakucha ukhalepo pa nthaŵi yake? Kodi iweyo udalamulapo kuti kuŵala kwa mbandakuchawo kuunikire dziko lonse lapansi, kuti kuthaŵitse anthu oipa obisala pamenepo? Chifukwa cha kuŵala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala ngati zilembo za chidindo pa mtapo. Kuŵala kwa dzuŵa sikuŵafika anthu oipa, choncho sangathe kugwira ntchito zao. “Kodi udakayendapo pansi penipeni pa nyanja ndi kukafika pa magwero ake? Kodi adakuwonetsa iwe zipata za imfa? Kodi udaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wokhawokha? Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziŵa? Undiwuze tsono ngati umazidziŵa zonsezi. “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuŵala ili kuti? Nanga mdima, kwao nkuti? “Kodi ndiwe amene ukusokoneza uphungu wanga polankhula mau opanda nzeru? Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwaoko zimenezi, kodi ukuidziŵa njira yopita kwaoko? Makamaka ukudziŵadi ati, poti paja nthaŵi imeneyo nkuti iweyo utabadwa, ndipo zaka zako kuchuluka ati! “Kodi udaloŵamo m'nyumba zosungiramo chisanu, kapena m'mene amasungira matalala? Zimenezi ndazisungira nthaŵi ya mavuto, ndidzazitumiza nthaŵi yomenyana nkhondo. Kodi udapitako kumene kumatulukira dzuŵa, kapena kumene kumachokera mphepo yakuvuma? “Kodi ndani amene adakonza ngalande za mvula? Ndani adakonza njira zodzeramo mphezi? Ndani amagwetsa mvula pa chipululu popanda anthu, ku dziko kumene sikukhala anthu. Ndani amathirira dziko louma lagwaa, kotero kuti udzu umamerapo? “Kodi mvula ili ndi bambo wake? Nanga madzi a mame adaŵabeleka ndani? Kodi chisanu choundana adachibala ndani? Nanga adabereka chipale chochokera kumwamba ndani? Onetsa chamuna, ndidzakufunsa, ndipo undiyankhe. Ndani amasandutsa madzi kuti alimbe ngati mwala, pamene madzi apanyanja amazizira, nalimba kuti gwaa? “Kodi Nsangwe iwe ungazimange maunyolo? Kodi zingwe za Akamwiniatsatana iwe ungathe kuzimasula? Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake? Kodi ungathe kutsogolera nyenyezi yaikulu ya Chimbalangondo pamodzi ndi tiana take? Kodi malamulo a mlengalenga umaŵadziŵa? Nanga ulamuliro wake, kodi ungaukhazikitse pa dziko lapansi? “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo kuti igwetse mvula ya chigumula? Kodi ungathe kutumiza zing'aning'ani kuti zing'anipe, ndi kugwera pa malo amene iwe ukufuna? Ndani amene adayala mitambo bwino mu mlengalenga? Nanga ndani adalangiza mvula kuti igwere pakutipakuti? Wanzeru ndani amene angathe kuŵerenga mitambo, nanga ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo amene amasandutsa fumbi matope, ndi kuumba zibumi? “Kodi iwe ungathe kuufunira chakudya mkango? Kodi ungathe kuipatsa chakudya misona yake ija, “Kodi udaali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi? Undiwuze ngati ndiwe womvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 6:2

Ana aamuna a Mulungu adaona kuti ana aakazi a anthu anali okongola, nayamba kukwatira amene ankaŵakonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:17

ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 137:9

Adzakhala wodala munthu amene adzatenga makanda ako ndi kuŵakankhanthitsa ku thanthwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:28

Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:4-5

Chitsiru usamachiyankha potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti ungafanefane nacho. Koma mwina uzichiyankha chitsiru potsata uchitsiru wake, kuwopa kuti chingamadziyese chanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 3:19-21

Zimene zimachitikira anthu, zomwezonso zimachitikira nyama. Monga chinacho chimafa, chinacho chimafanso. Zonsezo zimapuma mpweya umodzimodzi, munthu saposa nyama. Zonsezi nzopandapake. pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo. Zonse zimapita kumodzimodzi. Zonsezo nzochokera ku dothi, ndipo zimabwerera kudothi komweko. Kodi ndani angatsimikize kuti mzimu wa munthu ndiwo umakwera kumwamba, koma mpweya wa nyama umatsikira kunsi kwa nthaka?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 45:7

“Ndimalenga kuŵala ndi mdima, ndimadzetsa madalitso ndi tsoka. Ndine, Chauta, amene ndimachita zonsezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:18

Ana akutolera nkhuni, atate akusonkha moto, akazi akukanda ufa kuti aphike makeke, kuchitira ulemu amene amati ndi mfumukazi yakumwamba. Iwowo amathira nsembe yazakumwa kwa milungu ina, kuti andipsetse mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 20:25-26

Kuwonjezera pamenepo ndidaŵapatsa malamulo amene sankaŵakomera, ndiponso malangizo amene sakadatha kupeza nawo moyo wabwino. Ndidaŵalekerera kuti adziipitse ndi zopereka zao, makamaka pakupereka ana ao achisamba ngati nsembe zootcha. Ndidatero kuti ndiŵadetse nkhaŵa, ndipo kuti adziŵe kuti Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:29-30

Ngati diso lako la ku dzanja lamanja likuchimwitsa, likolowole nkulitaya. Ndi bwino koposa kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kusiyana nkuti thupi lako lonse aliponye ku Gehena. “Ngodala anthu amene ali osauka mumtima mwao, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, lidule nkulitaya. Ndi bwino kuti utayepo chiwalo chako chimodzi, kupambana kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:34

“Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Sindidadzapereke mtendere ai, koma nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:31-32

Nchifukwa chake ndikunenetsa kuti Mulungu adzakhululukira anthu tchimo lililonse, ngakhale mau achipongwe omunyoza Iyeyo. Koma munthu wochita chipongwe Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira. Chimodzimodzinso aliyense wonenera zoipa Mwana wa Munthu, Mulungu adzamkhululukira. Koma aliyense wonenera zoipa Mzimu Woyera, Mulungu sadzamkhululukira konse nthaŵi ino, ngakhalenso nthaŵi ilikudza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:46

Tsono nthaŵi ili ngati 3 koloko, Yesu adafuula kwakukulu kuti, “Eli, Eli, lama sabakatani?” Ndiye kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:16

Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:26

“Aliyense wofuna kukhala wophunzira wanga, azikonda Ine koposa atate ake ndi amai ake, mkazi wake ndi ana ake, abale ake ndi alongo ake, ndiponso koposa ngakhale moyo wake womwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:53

Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:30

Ine ndi Atate ndife amodzi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:26

Tsono adaŵachitira maere anthu aŵiriwo. Maerewo adagwera Matiasi, ndipo iyeyo adawonjezedwa pa gulu lija la atumwi khumi ndi mmodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 9:13

Paja Malembo akuti, “Yakobe ndidaamukonda, koma Esau ndidaadana naye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:7-8

Bwanji tsono? Aisraele sadapeze zimene ankafunafuna. Koma anthu pang'ono chabe amene Mulungu adaŵasankha ndiwo adazipeza. Otsalawo adagontha m'khutu, monga Malembo anenera kuti, “Mulungu adaŵapatsa mtima wosatha kumvetsa zinthu, ndipo mpaka lero lino waŵasandutsa osatha kupenya ndi osatha kumva.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 11:27-30

Nchifukwa chake tsono, munthu akadya mkate umenewu, kapena kumwa chikho cha Ambuyechi mosayenera, apalamula mlandu wonyoza thupi la Ambuye ndiponso magazi ao. Koma munthu aziyamba wadziwona bwino asanadyeko mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi. Pakuti amene adya mkate umenewu ndi kumwa chikho chimenechi, koma osalizindikira thupi la Ambuye, akudziitanira chilango pamene akudya ndi kumwa. Koma ndifuna kuti mudziŵe kuti Khristu ndiye mutu wa mwamuna aliyense, mwamuna ndiye mutu wa mkazi, ndipo Mulungu ndiye mutu wa Khristu. Nchifukwa chake ambiri mwa inu akudwala, akufooka, ndipo ena amwalirapo kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:29

Ngati Yesu sadauke kwa akufa, nanga amafunanji anthu amene amabatizidwa m'malo mwa amene adafa? Ngati akufa sauka konse, nanga chifukwa chiyani anthu amabatizidwa m'malo mwao?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:7-9

Koma kuwopa kuti ndingamadzitukumule chifukwa cha zazikulu kwambiri zimene Ambuye adandiwululira, Mulungu adandipatsa cholasa ngati minga m'thupi. Adalola wamthenga wa Satana kuti azindimenya, kuti ndingamanyade kwambiri. Pamenepo ndidapempha Ambuye katatu kuti andichotsere chimenechi, koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:12

Ndikadakonda kuti amene akukuvutaniwo angodzithena basi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:4

Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:29

Paja Iye adakupatsani mwai, osati wakungokhulupirira Khristu ai, komanso wakumva zoŵaŵa chifukwa cha Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:16-17

Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:21

koma zonse muziziyesa bwino, kuti muwonetsetse ngati nzoona. Musunge zimene zili zabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:4-6

Anthu amene adataya chikhulupiriro chao, nkosatheka kuŵatsitsimutsa kuti atembenuke mtima. Iwowo kale Mulungu adaaŵaunikira, adaalaŵako mphatso yochokera Kumwamba, nkulandira nao Mzimu Woyera. Ndipo adazindikira kukoma kwa mau a Mulungu, ndi mphamvu za nthaŵi imene inalikudzafika. Tsono akamkana Mulungu tsopano, akuchita ngati kumpachika iwo omwe Mwana wa Mulungu, ndi kumnyozetsa poyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:26-27

Pakuti tikamachimwirachimwira mwadala, kwina tikudziŵa choona, palibenso nsembe ina iliyonse ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo. Pamenepo chotitsalira si china ai, koma kumangodikira ndi mantha chiweruzo, ndiponso moto woopsa umene udzaononga otsutsana ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:24

Mukuwonatu kuti zochita zake za munthu ndizo zimamsandutsa wolungama pamaso pa Mulungu, osati chikhulupiriro chokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:16

Wina akaona mbale wake akuchita tchimo losadzetsa imfa, apemphere, ndipo Mulungu adzampatsa moyo mbale wakeyo. Ndikunenatu za ochita tchimo losadzetsa imfa. Koma lilipo tchimo lina lodzetsa imfa, za tchimo limenelo sindikunena kuti apemphere ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:5

Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:11-15

Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse. Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo. Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake. Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri. Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 21:24-25

diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi, kutentha ndi moto kulipa kutentha ndi moto, bala kulipa bala, ndipo mkwingwirima kulipa mkwingwirima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 25:11-12

Anthu aŵiri akamamenyana ndipo mkazi wa mmodzi pofuna kupulumutsa mwamuna wake, agwira mdani wakeyo ku moyo, musamchitire chifundo mkazi ameneyo, mumdule dzanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 16:20

Kenaka Delila adafuula kuti, “Inu amuna anga, Afilisti aja akubwera.” Samisoni adadzuka akuganiza kuti, “Ndituluka monga momwe ndimachitira nthaŵi zonse, ndipo ndidzimasula.” Koma sadadziŵe kuti Chauta wamsiya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 15:3

Pitani tsono, mukaŵathire nkhondo Aamalekewo, mukaononge kwathunthu zinthu zao zonse. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe, mukaphe amuna, akazi, ana ndi makanda omwe. Mukaphenso ng'ombe, nkhosa, ngamira ndi abulu onse.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 2:11-12

Tsono iwowo akuyendabe ndi kumakamba, adangoona galeta lamoto ndi akavalo ake amoto zikuŵasiyanitsa aŵiriwo. Ndipo Eliya adakwera kumwamba m'kamvulumvulu. Elisa adaona zimenezi nafuula kuti, “Bambo wanga, Bambo wanga! Magaleta a Aisraele ndi anthu ake okwera pa akavalo.” Ndipo sadamuwonenso Eliyayo. Tsono Elisa adagwira zovala zake nazing'amba paŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 1:21

Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:13-16

Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:4-5

“Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuŵamva ifeyo, ndipo adalandira zoŵaŵa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa. Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:11

Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 37:1-14

Mphamvu ya Chauta idandigwira, Mzimu wa Chauta udandinyamula nkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa. Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo. Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa ameneŵa ndi Aisraele onse. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu ndi ouma, chiyembekezo chathu chidataika, taonongekeratu.’ Nchifukwa chake uŵalalikire ndi kuŵauza kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo. Ndidzakubwezerani ku dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzafukula manda anu ndi kukutulutsanimo, inu anthu anga. Tsono ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo, pambuyo pake ndidzakukhazikani m'dziko lanu. Choncho mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:13-14

“Loŵerani pa chipata chophaphatiza. Pajatu chipata choloŵera ku chiwonongeko nchachikulu, ndipo njira yake ndi yofumbula, nkuwona anthu amene amadzerapo ndi ambiri. Koma chipata choloŵera ku moyo nchophaphatiza, ndipo njira yake ndi yosautsa, nkuwona anthu amene amaipeza ndi oŵerengeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:31-46

“Pamene Mwana wa Munthu adzabwera ndi ulemerero wake, pamodzi ndi angelo onse, adzachita kukhalira pa mpando wake wachifumu. Adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse pamaso pake, ndipo adzaŵalekanitsa monga momwe mbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. Nkhosa adzazikhazika ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi ku dzanja lake lamanzere. Tsono Iyeyo ngati Mfumu adzauza a ku dzanja lamanjawo kuti, ‘Bwerani kuno inu odalitsidwa a Atate anga. Loŵani mu ufumu umene adakukonzerani chilengedwere dziko lapansi. Paja Ine ndidaali ndi njala, inu nkundipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu nkundipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu nkundilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu nkundiveka. Ndinkadwala, inu nkumadzandizonda. Ndidaali m'ndende, inu nkumadzandichezetsa.’ Apo olungama aja adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, ife nkukupatsani chakudya, kapena muli ndi ludzu, ife nkukupatsani chakumwa? Ndi liti tidaakuwonani muli mlendo, ife nkukulandirani kunyumba kwathu, kapena muli wamaliseche, ife nkukuvekani? Ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife nkudzakuchezetsani?’ Koma asanu ochenjera aja adaatenga mafuta ena apadera m'nsupa zao. Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti nthaŵi iliyonse pamene munkamuchitira zimenezi wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkachitira Ine amene.’ “Pambuyo pake Mfumuyo idzauzanso a ku dzanja lake lamanzere aja kuti, ‘Chokani apa, inu otembereredwa. Pitani ku moto wosatha, umene Mulungu adakonzera Satana ndi angelo ake. Ine ndidaali ndi njala, inu osandipatsa chakudya. Ndidaali ndi ludzu, inu osandipatsa chakumwa. Ndidaali mlendo, inu osandilandira kunyumba kwanu. Ndidaali wamaliseche, inu osandiveka. Ndinkadwala, ndidaalinso m'ndende, inu osadzandichetsa.’ Apo nawonso adzati, ‘Ambuye, ndi liti tidaakuwonani muli ndi njala, kapena muli ndi ludzu, kapena wamaliseche, ndi liti tidaamvapo kuti mukudwala kapena kuti muli m'ndende, ife osachitapo kanthu?’ Mfumuyo idzaŵayankha kuti, ‘Ndithu ndikunenetsa kuti, nthaŵi iliyonse pamene munkakana kuthandiza wina aliyense mwa abale anga ngakhale otsika kwambiriŵa, munkakana kuthandiza Ine amene.’ Pamenepo iwowo adzachoka kumapita ku chilango chosatha, olungama aja nkumapita ku moyo wosatha.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:19-31

“Panali munthu wina wachuma, amene ankavala zovala zamtengowapatali, ndipo ankasangalala ndi kudyerera masiku onse. Tsono mbuye wakeyo adamuitana, namufunsa kuti, ‘Nchiyani chimene ndikumva za iwe? Undifotokozere za ukapitao wako, pakuti sungakhalenso kapitao ai.’ Panalinso munthu wina, dzina lake Lazaro, amene ankadzagona pa khomo la munthu wachuma uja. Iyeyu anali ndi zilonda m'thupi lonse. Ankalakalaka kudya nyenyeswa zimene zinkagwa pansi kuchokera pa tebulo la wachuma uja. Koma si pokhapo, ngakhale agalu ankabwera kumadzanyambita zilonda zake. “Munthu wosauka uja adamwalira, angelo nkumunyamula, nakamtula m'manja mwa Abrahamu. Munthu wachuma uja nayenso adamwalira, naikidwa m'manda. Pamene ankazunzika ku Malo a anthu akufa, wachuma uja adayang'ana kumwamba naona Abrahamu ali patali, ndi Lazaro ali pambali pakepa. Pamenepo adanena mokweza mau kuti, ‘Atate Abrahamu, mundichitire chifundo. Tumani Lazaro aviike nsonga ya chala chake m'madzi kuti adzaziziritseko lilime langa, pakuti ndikuzunzika koopsa m'moto muno.’ Koma Abrahamu adati, ‘Mwana wanga, kumbukira kuti udalaandiriratu zokondweretsa ukadali ndi moyo, pamene Lazaro adaalandira zoŵaŵa. Koma tsopano iye akusangalala kuno, pamene iwe ukuzunzika kwambiri. Ndiponso pakati pa ife ndi inu pali chiphompho, kotero kuti ofuna kuchoka kuno kuwolokera kwanuko, sangathe ai. Chimodzimodzinso kuchoka kwanuko kuwolokera kuno.’ “Apo wachuma uja adati, ‘Ndipotu ndikukupemphani atate, kuti mumtume Lazaroyo apite ku nyumba ya bambo wanga. Kumeneko ndili ndi abale anga asanu. Akaŵachenjeze, kuwopa kuti iwonso angabwere ku malo ano amazunzo.’ Koma Abrahamu adati, ‘Iwo ali ndi mabuku a Mose ndi a aneneri. Amvere zam'menemo.’ Apo kapitaoyo adayamba kuganiza mumtima mwake kuti, ‘Ndichite chiyani, popeza kuti mbuye wanga akundilanda ukapitao? Kulima, ai, ndilibe mphamvu. Kupemphapempha, ainso, kukundichititsa manyazi. Iye adati, ‘Iyai, atate Abrahamu, koma wina atauka kwa akufa nkupita kwa iwo, apo adzatembenuka mtima.’ Koma Abrahamu adamuuza kuti, ‘Ngatitu iwo samvera Mose ndi aneneri, sangathekenso ngakhale wina auke kwa akufa.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:2-3

M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.” Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. “Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. “Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:1-4

Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m'nyumba imodzi. ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma, ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuŵamva anthuŵa akulankhula m'zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.” Onse adazizwa ndi kuthedwa nzeru, ndipo adayamba kufunsana kuti, “Kodi chimenechi nchiyani?” Koma ena ankangoseka nkumati, “Aledzera vinyo watsopano.” Koma Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Ayuda, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu kuno, tamverani ndipo mumvetsetse bwino mau anga. Anthuŵa sadaledzere ai, monga mukuganizira inu, pakuti nthaŵi idakali 9 koloko m'maŵa. Koma zimenezi ndi zomwe mneneri Yowele adalosa kuti, “ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto. Ndithu, pa masiku amenewo ndidzaika Mzimu wanga ngakhale mwa akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndipo azidzalalika za Mulungu. Ndidzachita zozizwitsa ku thambo lakumwamba, ndipo pansi pano zizindikiro izi: magazi, moto ndi utsi watolotolo. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Dzuŵa lidzangoti bii ngati mdima ndipo mwezi udzangoti psuu ngati magazi, lisanafike tsiku la Ambuye Mulungu lalikulu ndi laulemerero. Pamenepo aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba, adzapulumuka.’ “Inu Aisraele mverani mau aŵa. Yesu wa ku Nazarete anali munthu amene Mulungu adamtuma kwa inu. Mulungu adakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zozizwitsa ndi zizindikiro zimene ankachita kudzera mwa Iyeyo pakati panu, monga mukudziŵa. Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m'mene Iye amadziŵiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda. Koma Mulungu adammasula ku zoŵaŵa za imfa, namuukitsa kwa akufa, chifukwa kunali kosatheka kuti agonjetsedwe ndi imfa. “Paja Davide ponena za Iye adati, ‘Ndinkaona Ambuye Mulungu pamaso panga nthaŵi zonse, pakuti amakhala ku dzanja langa lamanja kuti ndingagwedezeke. Nchifukwa chake mtima wanga udakondwa, ndipo ndinkalankhula mosangalala. Ndithu, ngakhale thupi langa lomwe lidzapumula m'manda, ndikhulupirira kuti simudzandisiya ku Malo a anthu akufa, kapena kulekerera Woyera wanu kuti aole. Mudandidziŵitsa njira zopita ku moyo, ndipo mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’ “Abale anga, ndingathe kulankhula nanu monenetsa za kholo lathu Davide. Iye adamwalira, naikidwa m'manda, ndipo manda ake alipo mpaka pano. Ndipo adaona ngati timalaŵi ta moto tooneka ngati malilime tikugaŵikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. Paja iye anali mneneri, ndipo ankadziŵa zimene Mulungu adamlonjeza molumbira zakuti mmodzi mwa zidzukulu zake ndiye adzaloŵe ufumu wake. Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti, “ ‘Iye sadasiyidwe ku Malo a anthu akufa, ndipo thupi lake silidaole.’ Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi. Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira. Pajatu Davide sadakwere kupita Kumwamba, koma iye yemwe adati, “ ‘Ambuye adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’ “Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.” Pamene anthu aja anamva zimenezi, zidaŵalasa mtima, ndipo adafunsa Petro ndi atumwi ena aja kuti, “Abale, tsono ifeyo tichite chiyani?” Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.” Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:15

Koma zikadzanyeka ndi moto, sadzalandira mphotho. Inde mwiniwakeyo adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wangopulumuka m'moto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:10

Pakuti tonsefe tiyenera kukaimirira poyera pamaso pa Khristu kuti atiweruze. Kumeneko aliyense adzalandira zomuyenerera, molingana ndi zimene adachita pansi pano, zabwino kapena zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:8-9

Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:18-19

Ndakhala ndikukuuzani kaŵirikaŵiri, ndipo tsopano ndikubwerezanso molira misozi, kuti pali ambiri amene mayendedwe ao akutsimikiza kuti amadana ndi mtanda wa Khristu. Mathero ao nkuwonongeka. Zosangalatsa thupi chabe ndizo zili ngati mulungu wao. Amanyadira zimene akadayenera kuchita nazo manyazi, ndipo amangoika mtima pa zapansipano zokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:15

Koma mkazi adzapulumukabe kudzera m'kubala ana, malinga akalimbikira modzichepetsa m'chikhulupiriro, m'chikondi ndi m'kuyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:6

Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:13-14

Pamene munthu akuyesedwa ndi zinyengo, asanene kuti, “Mulungu akundiika m'chinyengo.” Paja Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zinyengo, ndipo Iyeiyeyo saika munthu aliyense m'chinyengo. Koma munthu aliyense amayesedwa ndi zinyengo pamene chilakolako cha mwiniwakeyo chimkopa ndi kumkola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:2

Mulungu Atate adakusankhani, monga Iye adaziganiziratu kuyambira pa chiyambi, kuti Mzimu Woyera akuyeretseni ndipo kuti mumvere Yesu Khristu, ndi kutsukidwa ndi magazi ake. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wonka nuchulukirachulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:3-4

Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziŵa. Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:27

Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 4:7

Ukadachita zabwino, ndikadakondwera nawe. Koma chifukwa choti wachita zoipa, tchimo lakukhalirira pa khomo ngati chilombo cholusa. Likulakalaka kuti likugwire, koma iweyo uligonjetse tchimolo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:14

Musadzapembedze mulungu wina aliyense, chifukwa Chauta amene dzina lake ndi Kansanje, ndi Mulungu wansanjedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 20:13

Munthu akagona ndi munthu wamwamuna mnzake ngati mkazi, onsewo achita chinthu chonyansa, ndipo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 14:21

Nyama iliyonse yofa yokha, musadye. Alendo okha amene mumakhala nawo, alekeni adye, kapena mungogulitsa nyamayo kwa alendo ena. Pajatu inu ndinu opatulika a Chauta, Mulungu wanu. Musaphike mwanawankhosa kapena mwanawambuzi mu mkaka wa make.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 12:11-14

Tsono Ine Chauta ndikuti, ndithu ndidzakugwetsera tsoka pabanja pako pomwepo. Ndidzakuchotsera akazi ako, iweyo ukupenya, ndi kuŵapereka kwa mnzako wina, ndipo adzagona nawo akazi ako dzuŵa likuwomba mtengo. Iwe unkachita zimenezo m'seri, koma Ine ndidzazichita pamaso pa Aisraele onse, masana ndithu.’ ” Apo Davide adauza Natani kuti, “Ndidachimwira Chauta.” Natani adati, “Chauta wakukhululukirani machimo anu, simufa. Komabe, popeza kuti pochita zimenezi mwanyoza Chauta kotheratu, mwana amene akubalireniyo adzafa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:8

Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko, ndikagona m'dziko la anthu akufa, Inu muli momwemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 1:18

Paja nzeru zambiri zimadzetsa chisoni chambiri, munthu akamaonjezera nzeru, ndiye kuti akuwonjezeranso chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:8-9

Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 4:6

Anthu anga akuwonongeka chifukwa Ine sandidziŵa. Ndidzakukanani kuti musanditumikire ngati ansembe, chifukwa choti mwakana kuphunzitsa za Ine. Mwaiŵala malamulo a Mulungu wanu, tsono Inenso Mulungu wanu ndidzaiŵala ana anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 1:3

Komabe ndakonda Yakobe, koma Esau ndadana naye. Dziko lake lamapiri ndalisandutsa chipululu, dziko limene ndidampatsa ndalisandutsa la nkhandwe zam'chipululu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:24-30

Yesu adaŵaphera fanizo linanso. Adati, “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Munthu wina adaafesa mbeu zabwino m'munda mwake. Koma anthu onse ali m'tulo, mdani wake adabwera, nkufesa namsongole pakati pa tirigu, nachokapo. Tsono pamene mmera udakula nkuyamba kuchita njere, namsongole uja nayenso adayamba kuwoneka. Antchito a mwinimunda uja adadzamufunsa kuti, ‘Bwana, kodi suja mudaafesa mbeu zabwino m'munda mwanu? Nanga bwanji mukuwonekanso namsongole?’ Iye adaŵayankha kuti, ‘Ndi mdani amene wachita zimenezi.’ Antchito aja adamufunsa kuti, ‘Bwanji tikamzule?’ Koma iye adati, ‘Iyai, mungakazulire kumodzi ndi tirigu pozula namsongoleyo. Yesu adalankhula nawo zambiri m'mafanizo. Adati, “Munthu wina adaapita kukafesa mbeu. Zilekeni zikulire pamodzi zonse mpaka nyengo yodula. Pa nthaŵi imeneyo ndidzauza odula kuti, Yambani mwazula namsongole, mummange m'mitolo kuti mukamtenthe. Kenaka musonkhanitse tirigu ndi kukamthira m'nkhokwe yanga.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:24

Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:27

Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu nkosathekadi, koma ndi Mulungu ai, nkotheka. Paja ndi Mulungu zonse nzotheka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:38

Muzipereka moolowa manja, ndipo Mulungu adzakuchitirani momwemo: adzakupatsirani m'thumba mwanu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwatu muyeso womwe mumagwiritsa ntchito poweruza ena, Mulungu adzagwiritsa ntchito womwewo pokuweruzani inu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:30

“Ine sindingathe kuchita kanthu pandekha. Ndimaweruza monga momwe Atate amandiwuzira. Ndipo ndimaweruza molungama, popeza kuti sinditsata zimene ndifuna Ineyo, koma zimene afuna Atate amene adandituma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 9:16

Motero chachikulu si zimene munthu azifuna, kapena zimene munthu amayesetsa kuchita, koma chachikulu ndi chifundo cha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:14

Munthu wodalira nzeru zake zokha sangalandire zimene zimachokera kwa Mzimu wa Mulungu. Amaziyesa zopusa, ndipo sangathe kuzimvetsa, popeza kuti zimalira kukhala ndi Mzimu Woyera kuti munthu azimvetse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:3-4

Koma ngakhale Uthenga Wabwino umene timalalika uli wophimbika, ngwophimbika kwa okhawo amene akutayika. Iwoŵa sakhulupirira, popeza kuti Satana, amene ali mulungu wa dziko lino lapansi, adachititsa khungu maganizo ao, kuwopa kuti angaone kuŵala kwa Uthenga Wabwino. Kuŵalako kumaonetsa ulemerero wa Khristu, ndipo mwa Iyeyu Mulungu mwini amaoneka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:17

Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:11

Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:12-14

Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:3-5

Chimene Mulungu akufuna ndi ichi: mukhale oyera mtima, ndiye kuti muzipewa dama. Aliyense mwa inu adziŵe kulamula thupi lake, pakulilemekeza ndi kulisunga bwino, osalidetsa. Musamangotsata zilakolako zonyansa, monga amachitira akunja, amene sadziŵa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:16-17

Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:14

Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:1-2

Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Zikomo Ambuye, lero ndikupuma chifukwa cha chikondi chanu ndipo ndikulankhula za chifundo chanu chachikulu pa moyo wanga, zikomo chifukwa cha chakudya ndi chisamaliro chanu. Ndikupemphani lero Ambuye, kuti mundipatse mphamvu pa mphatso ya kuphunzitsa ndi kuti tsiku lililonse ndizilemera ndi nzeru kuti ndizigawire kwa ena. Ambuye Yesu, zikomo chifukwa ndinu mphunzitsi wabwino koposa ndipo kuchokera kwa inu kumachokera nzeru zonse ndi chidziwitso, chifukwa chake ndikupemphani kuti mundipatse chisomo ndi chiyanjo nthawi yomwe ndiyenera kufotokoza vesi lomwe limandikhumudwitsa. Ndikudziwa kuti Mzimu Woyera anditsogolera ndi kundipatsa mawu oyenera kufikira mitima ya omwe amandimvera. Ndikupemphani kuti mundidzaze ndi nzeru zolalikira vesi lililonse ndipo kudzera mwa Mzimu Woyera wanu ndiziphunzitsa ena ndi chipiriro ndi luso. Ndithandizeni tsiku lililonse kukhala ndi mtima woyenera kugawa mawu anu modzichepetsa. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa