Zikomo kwambiri kwa Mulungu chifukwa cha bambo anga, munthu wapadera amene Ambuye anandipatsa kuti anditsogolere m'njira Yake. Ndikupempherera kuti alandila mphamvu ndi chitsogozo cha Mzimu Woyera nthawi zonse.
Abambo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu ndipo m'malemba oyera muli lemba loti tiyenera kuwalemekeza, chifukwa ndi lamulo limodzi mwa malamulo khumi, ndipo ndi loyamba lomwe lili ndi lonjezo. Monga momwe lemba la Aefeso 6:2-3 limati, "Lemekeza atate wako ndi amayi wako (ndilo lamulo loyamba lomwe lili ndi lonjezo), kuti zinthu zikuyendere bwino, ndi kuti ukhalitse padziko lapansi."
Tiyeni tithokoze Mulungu chifukwa cha bambo amene ndili nawo ndi kuwadalitsa ndi mavesi awa. Ndi dalitso lalikulu kukhala ndi bambo m'moyo wanga!
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Akupatse zimene mtima wako ukukhumba, akuthandize kuti zonse zimene wakonza zichitikedi.
Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
Mbuye wakeyo adamuuza kuti, ‘Udachita bwino kwabasi, ndiwe mtumiki wabwino ndi wokhulupirika. Tsono popeza kuti udakhulupirika pa zinthu zochepa, ndidzakuika kuti uziyang'anira zinthu zambiri. Bwera udzakondwere pamodzi ndi ine, mbuye wako.’
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta, zidzukulu ndi mphotho yake. Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja mwa munthu wankhondo. Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere. Sadzamchititsa manyazi akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.
Munthu abwino amakhala mwachilungamo, ndipo Mulungu amadalitsa ana amene amatsata njira yake.
Khalidwe la kudzipereka ndi kukhulupirika zisakuthaŵe, makhalidwe ameneŵa uziyenda nawo ngati mkanda wam'khosi, uŵalembe mumtima mwako. Usamakangane ndi munthu popanda chifukwa pamene iyeyo sadakuchite choipa chilichonse. Usachite naye nsanje munthu wachiwawa, usatsanzireko khalidwe lake lililonse. Paja Chauta amanyansidwa ndi munthu woipa, koma olungama okha amayanjana nawo. Chauta amatemberera nyumba ya anthu oipa, koma malo okhalamo anthu abwino amaŵadalitsa. Anthu onyoza, Iye amaŵanyoza, koma odzichepetsa Iye amaŵakomera mtima. Anthu anzeru adzalandira ulemu, koma zitsiru adzazichititsa manyazi. Choncho udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino pamaso pa Mulungu ndi pa anthunso.
Ana inu, mverani malangizo a atate anu, tcherani khutu, kuti mupate nzeru zodziŵira zinthu. Mwana wanga, umvere ndi kuvomera zimene ndikunena. Ukatero, zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa njira yake ya nzeru. Ndakutsogolera pa njira za moyo wolungama. Ukamayenda, mapazi ako sazidzaombana. Ukamathamanga, sudzakhumudwa ai. Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo. Usayende m'njira za anthu oipa, usatsate m'mapazi mwa anthu ochimwa. Njira zao uzipewe, usapitemo konse. Uzilambalale, ndi kungozipitirira. Iwo ajatu sangagone, mpaka atachita ndithu choipa. Tulo sangatiwone, mpaka atakhumudwitsapo munthu. Paja kuchita zoipa ndiye chakudya chao, kuchita ndeu ndiye chakumwa chao. Koma njira ya anthu okondweretsa Mulungu, ili ngati kuŵala kwa mbandakucha, kumene kumanka kukukulirakulira mpaka dzuŵa litafika pamutu. Njira ya anthu oipa ili ngati mdima wandiweyani. Satha kuzindikira kuti aphunthwa pa chiyani. Ine ndikukupatsani malamulo abwino, musasiye zimene ndikukuphunzitsani.
Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.
Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.
Iyeyo adzayanjanitsa atate ndi ana ao, ana ndi atate ao, kuwopa kuti ndingadzabwere kudzatemberera dziko lanu kuti liwonongeke.”
ndi m'chipululu muja. Inu mudaona njira yonse m'mene adakufikitsirani kuno, kuti adakunyamulani monga momwe bambo amanyamulira mwana wake.”
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu.
Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe, chimene chili chabwino. Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi: uzichita zolungama, uzikhala wachifundo, ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.
Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.
Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.
Ngati simufuna kutumikira Chauta, sankhani lero lomwe lino amene muti mudzamtumikire, kapena ndi milungu ya Aamori amene mukukhala nawo m'dziko mwao. Koma ine pamodzi ndi banja langa lonse, tidzatumikira Chauta.”
Paja mukudziŵa kuti, tinkasamala aliyense mwa inu monga momwe amachitira bambo ndi ana ake. Tinkakulimbitsani mtima, kukuthuzitsani mtima ndi kukupemphani kuti mayendedwe anu akhale okomera Mulungu, amene amakuitanani kuti mukaloŵe mu Ufumu wake waulemerero.
Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.
Muzipirira masautso kuti muphunzirepo makhalidwe oyenera. Mulungu amakutengani ngati ana ake m'zochita zake zonse. Kodi nkale lonse analipo mwana amene bambo wake sadamlange?
Ndamsankha iyeyu kuti alamule ana ake ndi mabanja ake akutsogolo kuti azidzamvera mau anga, pochita zabwino ndi zolungama. Choncho ndidzachita zonse zimene ndidamlonjeza.”
Ngati wina aliyense saŵapatsa zofunika achibale ake, makamaka a m'banja mwake momwe, ameneyo wataya chikhulupiriro chake, ndipo kuipa kwake nkoposa kwa munthu wosakhulupirira.
“Choncho adanyamukadi napita kwa bambo wake. Koma akubwera patali, bambo wake adamuwona, namumvera chisoni. Adamthamangira, namkumbatira, nkumamumpsompsona. Mwanayo adati, ‘Atate, ndidachimwira Mulungu wakumwamba, ndi inu nomwe. Sindili woyenera kuchedwanso mwana wanu.’ Koma bambo wake adauza antchito ake kuti, ‘Thamangani mukatenge mkanjo wabwino kwambiri, mumuveke. Mumuvekenso mphete ku chala, ndi nsapato ku mapazi. Ndipo katengeni mwanawang'ombe wonenepa uja, muphe kuti tidye, tikondwere. Chifukwa mwana wangayu adaafa, koma tsopano wakhalanso moyo; adaatayika, koma tsopano wapezeka.’ Ndiye pompo chikondwerero chidayamba.
Khalani maso, khalani okhazikika m'chikhulupiriro chanu, chitani chamuna, khalani amphamvu. Zonse zimene muchita, muzichite mwachikondi.
Adapereka mau odzichitira umboni kwa Yakobe, adakhazikitsa malamulo ake mu Israele. Adalamula makolo athu kuti aziŵaphunzitsa ana ao malamulowo. Adalola kukwiya, osadziletsa, sadaŵapulumutse ku imfa, koma adapereka moyo wao ku miliri. Adapha ana achisamba onse a Aejipito, ana oyamba a mphamvu zao, m'zithando za zidzukulu za Hamu. Tsono Mulungu adaŵatulutsa anthu ake ngati nkhosa, naŵatsogolera m'chipululu ngati zoŵeta. Adaŵatsogolera bwino lomwe kotero kuti sanalikuwopa, koma nyanja idamiza adani ao. Adaŵafikitsa ku dziko lake loyera, ku dziko lamapiri limene adaŵagonjetsera ndi dzanja lake lamphamvu. Adapirikitsa mitundu ina ya anthu, kuŵachotsa m'njira. Adagaŵagaŵa dziko la anthuwo kuti likhale la anthu ake, adakhazikitsa mafuko a Israele m'midzi ya anthuwo. Komabe Aisraele adamuputa ndi kumuukira Mulungu Wopambanazonse, sadasunge malamulo ake, koma iwo adakhala okanika ndi osakhulupirika monga makolo ao. Adapotoka ngati uta wosakhulupirika. Iwo adakwiyitsa Mulungu ndi akachisi ao opembedzerako mafano ku mapiri. Adamupsetsa mtima chifukwa cha mafano ao osemawo. Pamene Mulungu adamva zimenezi, adakwiya kwambiri, ndipo adakana Aisraele kotheratu. Motero mbadwo wakutsogolo wa ana amene sanabadwebe, udzaŵadziŵa, ndipo nawonso udzafotokozera ana ake.
“Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa.
Mwaiŵala kodi mau olimbitsa mtima aja, amene Mulungu amakulankhulani ngati ana ake? Mauwo ndi aŵa: “Mwana wanga, usanyozere malango a Ambuye, kapena kutaya mtima pamene Iwo akudzudzula. Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.”
Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza, usakane zimene mai wako akukuphunzitsa. Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako, zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.
Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo.
Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera. Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana. Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga. Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu. Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima. Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo. Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira. Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye. Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima. Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro. Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse. Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”
Inunso amuna, muzikhala moŵamvetsa bwino akazi anu. Muziŵachitira ulemu popeza kuti iwowo ndi mtundu wofookerapo, ndiponso ngolandira nanu pamodzi mphatso ya Mulungu, imene ili moyo wosatha. Muzitero, kuti pasakhale kanthu koletsa mapemphero anu.
Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka, m'kati mwa nyuma yako. Ana ako adzakhala ngati tiziphukira taolivi, kuzungulira tebulo lako. Zoonadi, ndimo m'mene adzakhalire wodala munthu woopa Chauta.
Nchifukwa chake tsono ndikugwadira Atate, amene banja lililonse Kumwamba ndi pansi pano limatchulidwa ndi dzina lao.
Tamandani Chauta! Ngwodala munthu woopa Chauta, wokonda kusunga malamulo ake. Munthu woipa amaona zimenezi, ndipo amapsa nazo mtima. Amakukuta mano nazimirira. Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse. Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi. Ana a munthuyo adzakhala odala.
Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo.
Mukhale tcheru, ndipo musadzaiŵale zonse zimene mudaziwona. Zimenezo zisachoke m'mitima mwanu pa moyo wanu wonse. Muzizifotokoza kwa ana anu ndi kwa zidzukulu zanu zomwe.
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru amakondweretsa atate ake, koma mwana wopusa amanyoza amai ake.
Ndani mwa atatenu, mwana wake atampempha nsomba, iye nkumupatsa njoka? Kapena atampempha dzira, iye nkumupatsa chinkhanira? Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene aŵapempha.”
Uzichita zimene Chauta Mulungu wako akulamula. Uziyenda m'njira za Chauta, uzimvera mau, malangizo ndi malamulo a Mulungu, monga momwe adalembedwera m'malamulo a Mose, kuti zonse zizikuyendera bwino kulikonse kumene ungapite.
Kumbukirani zakale, lingalirani zamakedzana ndithu, funsani atate anu, akuuzani zimene zidachitika. Funsani akuluakulu, akufotokozerani zakalezo.
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.
Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga. Akamadzandichimwira, ndizidzamulanga monga m'mene bambo amalangira ana ake. Koma sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, monga m'mene ndidaachitira ndi Saulo, amene ndidamkana, kuti uloŵe ufumu ndiwe.
Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.
Amoyo, amoyo okha, ndiwo amakutamandani, monga m'mene ndikuchitira ine tsopanomu. Atate amauza ana ao za kukhulupirika kwanu.
Mwana wanga Solomoni mumpatse mtima wangwiro, kuti azisunga malamulo ndi malangizo anu ndi kuŵatsata bwino ndithu, ndiponso kuti amange nyumba imene ine ndaipezera zofunika zonsezi.”
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”