Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


59 Mau a m’Baibulo a Sabata Lopatulika

59 Mau a m’Baibulo a Sabata Lopatulika

Palibe chomwe ine ndingachite kuti ndichotse kuipa kwanga ndekha ndikupeza chipulumutso. Kuipa komwe kuli mumtima mwanga sikundiyeneretsa nsembe ya Khristu. Koma chikondi chake chachikulu chinapambana machimo anga ndipo chinathira chisomo chake mumtima mwako kuti udzapulumuke.

Nthawi ya Pasika iyenera kukhala nthawi yoti tiganizire mozama ndikuthokoza Mulungu. Ndi nthawi yomwe ife Akhristu timakumbukira imfa ndi kuuka kwa Yesu, Ambuye ndi Mpulumutsi wathu. Koma sikuti ndikutanthauza kuti umukumbukire pa nthawiyi yokha. Palibe phindu kukhala ndi Pasika ngati moyo wako wonse uli wodzala ndi machimo.

Chofunika ndi chakuti uzikondwerera zowawa za Yesu ndikukhala moyo wolungama pamaso pake, kuchita zomwe zimamukondweretsa, osati tsiku limodzi lokha, koma nthawi zonse zomwe ukupuma.

Chifukwa cha nsembe ya Yesu pa mtanda, machimo athu akhululukidwa ndipo miyoyo yathu yapulumutsidwa, ndipo zonsezi adazichita chifukwa cha chikondi. Yohane 5:24 imati, “Zoonadi, zoonadi, ndikuti kwa inu, wakumva mau anga, nakhulupirira iye amene anandituma ine, ali nawo moyo wosatha, ndipo sadzalowa mlandu, koma wadutsa chochokera ku imfa kulowa m’moyo.”




1 Akorinto 15:20

Koma ai, Khristu adauka ndithu kwa akufa. Pakati pa onse amene adafa, ndiye woyamba kuuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:7

Muchotse chofufumitsira chakalechi cha uchimo, kuti mukhale oyera mtima ndithu, ngati buledi watsopano wosafufumitsa, monga momwe muliri ndithu, pakuti Khristu, Mwanawankhosa wathu wa Paska, adaphedwa kale ngati nsembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 23:46

Tsono Yesu adanena mokweza mau kuti, “Atate ndikupereka mzimu wanga m'manja mwanu.” Atanena zimenezi, adatsirizika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:9

Anthu ochuluka amene anali patsogolo, ndi amene anali m'mbuyo, adayamba kufuula kuti, “Ulemu kwa Mwana wa Davide. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye. Ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:28-29

Adamuvula zovala zake, namuveka chovala chofiira. Adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa ndodo m'dzanja lake lamanja. Kenaka adayamba kumgwadira, namaseŵera naye mwachipongwe nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:33

Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankaŵakomera mtima kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 19:30

Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse ndakwaniritsa.” Kenaka adaŵeramitsa mutu, napereka mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:6

Koma mnyamatayo adaŵauza kuti, “Musade nkhaŵa. Mukufuna Yesu wa ku Nazarete, uja adaampachika pa mtandayu. Wauka, sali muno. Taonani, si apa pamene adaamuika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:24

“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:5-6

Akazi aja adachita mantha naŵeramitsa nkhope zao pansi. Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Mukudzafuniranji munthu wamoyo pakati pa anthu akufa? Atatero Yesu adaŵatsogolera kuchokera mumzindamo mpaka ku mudzi wa Betaniya. Kumeneko adakweza manja ake naŵadalitsa. Akuŵadalitsa choncho, adalekana nawo, natengedwa kupita Kumwamba. Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. Tsono ankasonkhana m'Nyumba ya Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi akutamanda Mulungu. Sali muno ai, wauka. Kumbukirani zimene adaakuuzani akadali ku Galileya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:4

Adaikidwa m'manda, mkucha wake adauka, monga Malembo anenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:14

Mulungu adaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo mwa mphamvu yake adzatiwukitsa ifenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 11:25-26

Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 14:36

Adanenanso kuti, “Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:25-26

Tipulumutseni, tikukupemphani Inu Chauta. Chauta, tikukupemphani kuti zinthu zitiyendere bwino. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Chauta. Tikufunirani madalitso ochokera m'nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:3

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:17-19

Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, ophunzira aja adadza nafunsa Yesu kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?” Iye adaŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu kwa munthu wina wake. Mukanene kuti, ‘Aphunzitsi akuti nthaŵi yao ili pafupi, akudzadyera kwanu kuno phwando la Paska pamodzi ndi ophunzira ao.’ ” Ophunzira aja adapita nakachita zomwe Yesu adaaŵauza, nakakonzadi za phwando la Paska.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 9:9

Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni. Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu. Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu. Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu, bulu wake kamwana tsono.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 20:8-9

Pamenepo wophunzira wina uja, amene adaayambira kufika ku manda, nayenso adaloŵa; ndipo ataona zimenezi, adakhulupirira. Mpaka nthaŵi imeneyo iwo aja anali asanamvetse Malembo akuti Yesu adzayenera kuuka kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:37

Pamwamba pa mutu wake adaalembapo mau osonyeza mlandu womuphera, akuti, “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 20:18-19

“Tilitu pa ulendo wopita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo. Iwo akamuweruza ndi kugamula kuti aphedwe, ndipo akampereka kwa anthu akunja. Amenewo akamchita chipongwe, akamkwapula, nkumupachika pa mtanda; koma mkucha wake Iye adzauka kwa akufa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:26-28

Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, idyani, ili ndi thupi langa.” Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu. Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:4

Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:9

Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:11-12

Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake. Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:50-51

Koma Yesu adafuulanso kwakukulu, napereka mzimu wake. Pompo chinsalu chochinga chija cha m'Nyumba ya Mulungu chidang'ambika pakatimpakati, kuyambira pamwamba mpaka pansi. Kudachita chivomezi, ndipo matanthwe adang'ambika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:36-46

Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti, “Inu bakhalani pano, Ine ndikupita uko kukapemphera.” Adatengako Petro ndi ana aŵiri aja a Zebedeo. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima. Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, komatu mukhale maso pamodzi nane.” Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.” Ankakambirana za njira yoti agwirire Yesu mochenjera, nkumupha. Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Mongadi nonsenu mwalephera kukhala maso pamodzi nane ngakhale pa kanthaŵi kochepa? Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.” Adachokanso kachiŵiri nakapemphera kuti, “Atate, ngati chikho chamasautsochi sichingandichoke, mpaka nditamwa ndithu, chabwino, zimene mukufuna zichitike.” Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera. Yesu adaŵasiyanso, napita kukapemphera kachitatu, akunena mau amodzimodzi omwe aja. Pambuyo pake adabwera kwa ophunzira ake nati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Ndipotu nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akukaperekedwa kwa anthu ochimwa. Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:19-20

Kenaka Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagawira ophunzira aja, ndipo adati, “Ili ndi thupi langa limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi kuti muzindikumbukira.” Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti aphere Yesu. Paja iwo ankaopa anthu. Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:1-2

M'maŵa kutacha, akulu onse a ansembe ndi akulu a Ayuda adapanga upo kuti aphe Yesu. nagulira munda wa mmisiri wa mbiya, monga momwe Ambuye adaandilamulira.” Tsono Yesu adaimirira pamaso pa bwanamkubwa. Iyeyo adamufunsa kuti, “Kodi iwe, ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu adati, “Mwanena nokha.” Koma pamene akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda aja ankamuneneza, Yesu sadayankhepo kanthu. Apo Pilato adamufunsa kuti, “Kodi sukumva zonse akukunenezazi?” Koma Yesu sadamuyankhe kanthu, kotero kuti bwanamkubwa uja adadabwa kwambiri. Pa nthaŵi ya chikondwerero cha Paska, bwanamkubwa ankaŵamasulira anthu mkaidi mmodzi, yemwe iwo ankafuna. Pa nthaŵi imeneyo panali mkaidi wina wodziŵika, dzina lake Barabasi. Tsono anthu atasonkhana, Pilato adaŵafunsa kuti, “Mukufuna kuti ndikumasulireni uti, Barabasi kapena Yesu, wotchedwa Khristu?” Adaatero chifukwa adaadziŵa kuti Yesuyo anthuwo angodzampereka chifukwa cha kaduka chabe. Pilato ali pa mpando woweruzira milandu, mkazi wake adamtumizira mau. Adati, “Musaloŵerepo pa nkhani ya munthu wolungamayo. Inetu maloto andivuta kwambiri usiku chifukwa cha Iyeyo.” Adammanga, napita naye kwa Pilato, bwanamkubwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:27-31

Pamenepo asilikali a bwanamkubwa adatenga Yesu nakaloŵa naye kunyumba kwa bwanamkubwa. Adasonkhanitsa gulu lonse la asilikali anzao nazinga Yesu. Adamuvula zovala zake, namuveka chovala chofiira. Adaluka nsangamutu yaminga naiika pamutu pake, ndipo adamgwiritsa ndodo m'dzanja lake lamanja. Kenaka adayamba kumgwadira, namaseŵera naye mwachipongwe nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda.” Pamene Yudasi, wopereka Yesu kwa adani ake uja, adaona kuti Yesu mlandu wamuipira, nthumanzi idamugwira. Tsono adakaŵabwezera akulu a ansembe ndi akulu a Ayudawo ndalama makumi atatu zasiliva zija. Adamthira malovu, natenga ndodo ija nkumamumenya nayo m'mutu. Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 12:12-13

M'maŵa mwake anthu ambirimbiri amene anali atabwera ku chikondwerero cha Paska chija, adamva kuti Yesu akubwera ku Yerusalemu. Motero adatenga nthambi za kanjedza natuluka kukamchingamira. Ankafuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu! Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye! Idalitsidwe Mfumu ya Israele!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:32-33

Pamene ankatuluka mumzindamo, adakumana ndi munthu wina, dzina lake Simoni, wa ku Kirene. Tsono asilikali aja adamkakamiza kuti asenze mtanda wa Yesu. Ndipo adafika ku malo otchedwa Gologota, (ndiye kuti “Malo a Chibade cha Mutu.”)

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:8

Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 23:33-34

Pamene adafika ku malo otchedwa Chibade cha Mutu, adapachika Yesu komweko pa mtanda. Komwekonso adapachika zigaŵenga zija, china ku dzanja lamanja, china ku dzanja lamanzere. Yesu adati, “Atate, muŵakhululukire anthuŵa, chifukwa sakudziŵa zimene akuchita.” Iwo aja adagaŵana zovala zake pakuchita maere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 19:28-30

Yesu adaadziŵa kuti tsopano zonse wakwaniritsa. Tsono kuti zipherezere zimene Malembo adaanena, Iye adati, “Ndili ndi ludzu.” Pomwepo panali mbiya yodzaza ndi vinyo wosasa. Asilikali aja adaviika chinkhupule m'vinyo wosasayo, nkuchitsomeka ku kamtengo ka hisope, nachifikitsa pakamwa pake. nadza kwa Iye nkumanena kuti, “Tikuwoneni, mfumu ya Ayuda!” Ndipo adayamba kumuwomba makofi. Yesu atalandira vinyo wosasayo adati, “Zonse ndakwaniritsa.” Kenaka adaŵeramitsa mutu, napereka mzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:5

Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:24

Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:1-10

Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala ndi Maria wina uja adabwera mbandakucha pa tsiku lotsatira Sabatalo, kudzaona manda aja. Apo Yesu adaŵauza kuti, “Musaope. Pitani, kauzeni abale anga kuti apite ku Galileya. Akandiwonera kumeneko.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:1-2

Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji? Chifukwa chiyani simukundithandiza mpang'ono pomwe, chifukwa chiyani simukumva mau a kubuula kwanga? Ndakhala ndikudalira Inu chibadwire changa, Inu mwakhala Mulungu wanga kuyambira pamene mai wanga adandibala. Musandikhalire kutali, pakuti mavuto ali pafupi kundigwera, ndipo palibe wina wondithandiza. Nkhunzi zambiri zandizungulira. Adani amphamvu ngati nkhunzi za ku Basani andizinga. Andiyasamira kukamwa, ngati mkango wobangula wofuna kundikadzula. Moyo wanga watayika ngati madzi, mafupa anga aweyeseka. Mtima wanga uli ngati sera, wasungunuka m'kati mwanga. Kukhosi kwanga kwauma ngati phale, lilime langa lakangamira ku nsagwada. Inu mwandisiya pa fumbi kuti ndifere pomwepo. Anthu ankhanza andizinga ngati mimbulu. Aboola manja anga ndi mapazi anga. Mafupa anga akuwonekera, koma anthu aja akungondiyang'anitsitsa akukondwera poona kuti ndikuvutika. Agaŵana zovala zanga, ndipo achitira malaya anga maere. Koma Inu Chauta musakhale kutali. Inu, mphamvu zanga, fulumirani kudzandithandiza. Mulungu wanga, ine ndimalira usana, koma Inu simundiyankha, ndimalira usiku, koma sindipeza mpumulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:1-8

Tsiku la Sabata ya Ayuda litapita, Maria wa ku Magadala, ndi Maria, mai wa Yakobe, ndiponso Salome adakagula zonunkhira kuti akadzoze mtembo wa Yesu. Mariayo adapita kukauza amene ankakhala ndi Yesu aja. Iwowo nkuti ali ndi chisoni ndipo akungolira. Ngakhale atamva kuti Yesu ali moyo, ndipo kuti Maria wamuwona, iwo sadakhulupirire. Pambuyo pake Yesu, ali ndi maonekedwe osiyana, adaonekera ophunzira ake ena aŵiri, pamene iwowo anali pa ulendo kunja kwa mzinda wa Yerusalemu. Ophunzirawo adabwerera kudzauza anzao aja, koma iwonso sadaŵakhulupirire. Potsiriza Yesu adaonekera ophunzira khumi ndi mmodzi aja alikudya. Adaŵadzudzula chifukwa cha kusakhulupirira kwao ndi kupulupudza kwao, chifukwa sadakhulupirire anzao aja amene adaamuwona Iye atauka kwa akufa. Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino. Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa. Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo, ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuŵapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.” Ambuye Yesu atalankhula nawo, adatengedwa kupita Kumwamba, nakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu. M'mamaŵa ndithu pa tsiku lotsatira Sabatayo, adapita kumanda kuja, dzuŵa litatuluka. Tsono ophunzira aja adanka nalalika ponseponse. Ambuye ankagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo ankatsimikiza mau ao ndi zozizwitsa zimene ankachita.] Ankafunsana kuti, “Kodi ndani akatichotsere chimwala cha pakhomo pa manda chija?” Koma poyang'anitsitsa adaona kuti chimwalacho achigubuduza kale; tsonotu chinali chachikuludi. Ataloŵa m'mandamo adaona mnyamata wakhala pansi mbali ya ku dzanja lamanja, atavala mkanjo woyera. Azimaiwo adadzidzimuka. Koma mnyamatayo adaŵauza kuti, “Musade nkhaŵa. Mukufuna Yesu wa ku Nazarete, uja adaampachika pa mtandayu. Wauka, sali muno. Taonani, si apa pamene adaamuika. Koma inu pitani mukauze ophunzira ake, makamaka Petro, kuti, ‘Iye watsogola kunka ku Galileya. Mukamuwonera kumeneko, monga muja adakuuziranimu.’ ” Pamenepo azimaiwo adatuluka nkuthaŵako kumandako, popeza kuti adaagwidwa ndi mantha, mpaka kumangonjenjemera. Ndipo chifukwa cha manthawo sadauze munthu aliyense kanthu. [

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:5-6

Koma mngeloyo adalankhula ndi azimai aja naŵauza kuti, “Inu musaope ai. Ndikudziŵa kuti mukufuna Yesu, uja adaampachika pa mtandayu. Sali muno ai, wauka monga muja adaaneneramu. Bwerani, dzaoneni pamene adaagona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:1-7

M'mamaŵa pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, azimai aja adapita ku manda, atatenga zonunkhira zimene adaakakonza. Azimaiwo anali Maria wa ku Magadala, Yohana, ndi Maria, amake a Yakobe. Iwo pamodzi ndi anzao ena adasimbira atumwi aja zonsezi. Koma zimenezo atumwiwo adangoziyesa zam'kutu, mwakuti sadaŵakhulupirire azimaiwo. [ Komabe Petro adanyamuka nathamangira ku manda. Adaŵeramiramo naona nsalu zamaliro zokha, kenaka nkubwerera kunyumba akudabwa ndi zimene zidaachitikazo.] Tsiku lomwelo ophunzira aŵiri ankapita ku mudzi wotchedwa Emausi. Kuchokera ku Emausi kufika ku Yerusalemu ndi mtunda wokwanira ngati makilomita khumi ndi limodzi. Ankakambirana za zonse zimene zidaachitika. Akukambirana choncho nkumafunsana, Yesu mwiniwake adayandikira nkumatsagana nawo. Koma maso ao adaachita chidima, mwakuti sadamzindikire. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi mukunka mukukambirana zotani panjira pano?” Apo iwo adaima, nkhope zao zili zakugwa ndi chisoni, kenaka mmodzi, dzina lake Kleopa, adamufunsa kuti, “Kodi mlendo ndinu nokha m'Yerusalemu muno, wosadziŵa zimene zachitika m'menemo masiku apitaŵa?” Yesu adaŵafunsa kuti, “Zotani?” Iwo adati, “Za Yesu wa ku Nazarete. Iye anali mneneri amene mau ake ndi zochita zake zinali zamphamvu pamaso pa Mulungu ndi pa anthu omwe. Adapeza chimwala chija chili chogubuduza kale kuchoka pakhomo pa manda aja. Akulu a ansembe ndi akulu athu ena adampereka kuti azengedwe mlandu ndi kuphedwa, ndipo adampachika pa mtanda. Ife tinkayembekeza kuti Iyeyo ndiye adzaombole Aisraele, koma ha! Ndi dzana pamene zidachitika zonsezi. Komanso azimai ena a m'gulu lathu anatidabwitsa. Iwowo anapita ku manda m'mamaŵa, ndiye amati sadaupeze mtembo wake. Tsono atabwerako amadzasimba kuti anaona angelo amene anaŵauza kuti Yesu ali moyo. Ena mwa ife anapita kumandako, ndipo anakapezadi monga momwe azimai aja amasimbira, koma Iyeyo sadamuwone ai.” Apo Yesu adati, “Ha! Koma ndiye ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zija zimene aneneri adanena. Kodi inu simukudziŵa kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa zonsezi kuti aloŵe mu ulemerero wake?” Kenaka Yesu adayamba kuŵatanthauzira zimene zidalembedwa za Iye m'Malembo onse, kuyambira pa mabuku a Mose mpaka mabuku a aneneri onse. Atayandikira kumudzi kumene ankapita, Yesu adachita ngati akupitirira. Koma iwo adamuumiriza kuti, “Mukhale nafe konkuno, poti kwayamba kuda; onani dzuŵa likuloŵa.” Apo Iye adakaloŵa m'nyumba nakakhala nawo. Adaloŵa m'mandamo koma sadaupeze mtembo wa Ambuye Yesu. Pamene adakhala nawo podyera, Yesu adatenga buledi, ndipo atathokoza Mulungu, adamnyema naŵagaŵira. Nthaŵi yomweyo maso ao adatsekuka, namuzindikira, Iye nkuzimirira. Tsono iwo adayamba kukambirana kuti, “Zoonadi ndithu, mitima yathu inachita kuti phwii, muja amalankhula nafe panjira paja, nkumatitanthauzira Malembo.” Nthaŵi yomweyo adanyamuka kubwerera ku Yerusalemu. Adakapeza ophunzira khumi ndi mmodzi aja atasonkhana pamodzi ndi anzao ena, akunena kuti, “Ambuye adaukadi, ndipo Simoni waŵaona.” Tsono nawonso aŵiri aja adafotokoza zimene zidaachitika panjira paja, ndiponso m'mene iwo adaamzindikirira pamene Iye ankanyema buledi. Iwo akulankhula choncho, Yesu mwiniwake adadzaimirira pakati pao nati, “Mtendere ukhale nanu.” Koma iwo adadzidzimuka, nkuchita mantha poyesa kuti akuwona mzukwa. Tsono Yesu adati, “Mukuvutikiranji, mukudzipheranji ndi mafunso m'mitima mwanu? Onani manja anga ndi mapazi anga, kuti ndine ndithu. Khudzeni muwone, paja mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuwona kuti Ine ndili nazo.” Akadali othedwa nzeru choncho pa zimenezo, adangoona anthu aŵiri ovala zovala zonyezimira ataimirira pafupi ndi iwo. Atanena zimenezi adaŵaonetsa manja ake ndi mapazi ake. Iwo sankakhulupirirabe chifukwa cha chimwemwe, ndipo adaathedwa nzeru. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi pano muli nako kanthu kakudya?” Adampatsa chidutsu cha nsomba yootcha. Iye atalandira nsombayo, adaidya iwo akuwona. Kenaka adaŵauza kuti, “Nzimenezitu zimene ndinkakuuzani pamene ndinali nanu. Paja ndinkanena kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m'Malamulo a Mose, m'mabuku a aneneri, ndi m'buku la Masalimo.” Tsono adaŵathandiza kuti amvetse bwino Malembo. Adaŵauza kuti, “Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zoŵaŵa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao. Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi. Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera Kumwamba.” Akazi aja adachita mantha naŵeramitsa nkhope zao pansi. Anthuwo adaŵafunsa kuti, “Mukudzafuniranji munthu wamoyo pakati pa anthu akufa? Atatero Yesu adaŵatsogolera kuchokera mumzindamo mpaka ku mudzi wa Betaniya. Kumeneko adakweza manja ake naŵadalitsa. Akuŵadalitsa choncho, adalekana nawo, natengedwa kupita Kumwamba. Iwo adampembedza, pambuyo pake nkubwerera ku Yerusalemu ndi chimwemwe chachikulu. Tsono ankasonkhana m'Nyumba ya Mulungu nthaŵi ndi nthaŵi akutamanda Mulungu. Sali muno ai, wauka. Kumbukirani zimene adaakuuzani akadali ku Galileya. Paja adaakuuzani kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa m'manja mwa anthu ochimwa, kupachikidwa pa mtanda, ndi kuuka kwa akufa patapita masiku atatu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 20:1-18

Pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, m'mamaŵa ndithu kudakali kamdima, Maria wa ku Magadala adadza ku manda a Yesu. Adaona kuti chimwala chija chachotsedwa kale pa khomo la mandawo. Pambuyo pake ophunzirawo adabwerera kwao. Maria adakhalabe chilili panja pafupi ndi manda, akulira. Akulira choncho, adaŵerama kusuzumira m'mandamo, naona angelo aŵiri ovala zovala zoyera. Angelowo adaakhala pansi, wina kumutu, wina kumapazi pamalo pamene padaagona mtembo wa Yesu paja. Iwo adamufunsa kuti, “Inu mai, mukuliranji?” Iye adati, “Chifukwa aŵachotsa Ambuye anga ndipo sindikudziŵa kumene akaŵaika.” Atanena zimenezi adacheuka, naona Yesu ataimirira pomwepo, koma sadamzindikire kuti ndi Yesu. Tsono Yesu adamufunsa kuti, “Mai iwe, ukuliranji? Ukufuna yani?” Maria ankayesa kuti ndi wakumundako, motero adamuuza kuti, “Bambo, ngati mwaŵachotsa ndinu, mundiwuze kumene mwakaŵaika, kuti ndikaŵatenge.” Yesu adati, “Maria!” Iye adacheuka, nanena kuti, “Raboni!” (Ndiye kuti “Aphunzitsi” pa chihebri) Yesu adamuuza kuti, “Usandigwire, pakuti sindinakwerebe kupita kwa Atate. Koma pita kwa abale anga, ukaŵauze kuti, ‘Ndikukwera kupita kwa Atate anga, omwe ali Atate anunso, Mulungu wanga, yemwe ali Mulungu wanunso.’ ” Maria wa ku Magadalayo adapita, nakauza ophunzira aja kuti, “Ndaŵaona Ambuye,” ndipo adaŵakambira zimene Ambuyewo adaamtuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:1-3

M'mamaŵa pa tsiku lotsatira Sabata ya Ayuda, azimai aja adapita ku manda, atatenga zonunkhira zimene adaakakonza. Azimaiwo anali Maria wa ku Magadala, Yohana, ndi Maria, amake a Yakobe. Iwo pamodzi ndi anzao ena adasimbira atumwi aja zonsezi. Koma zimenezo atumwiwo adangoziyesa zam'kutu, mwakuti sadaŵakhulupirire azimaiwo. [ Komabe Petro adanyamuka nathamangira ku manda. Adaŵeramiramo naona nsalu zamaliro zokha, kenaka nkubwerera kunyumba akudabwa ndi zimene zidaachitikazo.] Tsiku lomwelo ophunzira aŵiri ankapita ku mudzi wotchedwa Emausi. Kuchokera ku Emausi kufika ku Yerusalemu ndi mtunda wokwanira ngati makilomita khumi ndi limodzi. Ankakambirana za zonse zimene zidaachitika. Akukambirana choncho nkumafunsana, Yesu mwiniwake adayandikira nkumatsagana nawo. Koma maso ao adaachita chidima, mwakuti sadamzindikire. Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi mukunka mukukambirana zotani panjira pano?” Apo iwo adaima, nkhope zao zili zakugwa ndi chisoni, kenaka mmodzi, dzina lake Kleopa, adamufunsa kuti, “Kodi mlendo ndinu nokha m'Yerusalemu muno, wosadziŵa zimene zachitika m'menemo masiku apitaŵa?” Yesu adaŵafunsa kuti, “Zotani?” Iwo adati, “Za Yesu wa ku Nazarete. Iye anali mneneri amene mau ake ndi zochita zake zinali zamphamvu pamaso pa Mulungu ndi pa anthu omwe. Adapeza chimwala chija chili chogubuduza kale kuchoka pakhomo pa manda aja. Akulu a ansembe ndi akulu athu ena adampereka kuti azengedwe mlandu ndi kuphedwa, ndipo adampachika pa mtanda. Ife tinkayembekeza kuti Iyeyo ndiye adzaombole Aisraele, koma ha! Ndi dzana pamene zidachitika zonsezi. Komanso azimai ena a m'gulu lathu anatidabwitsa. Iwowo anapita ku manda m'mamaŵa, ndiye amati sadaupeze mtembo wake. Tsono atabwerako amadzasimba kuti anaona angelo amene anaŵauza kuti Yesu ali moyo. Ena mwa ife anapita kumandako, ndipo anakapezadi monga momwe azimai aja amasimbira, koma Iyeyo sadamuwone ai.” Apo Yesu adati, “Ha! Koma ndiye ndinu anthu opusa, osafuna kukhulupirira msanga zonse zija zimene aneneri adanena. Kodi inu simukudziŵa kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa zonsezi kuti aloŵe mu ulemerero wake?” Kenaka Yesu adayamba kuŵatanthauzira zimene zidalembedwa za Iye m'Malembo onse, kuyambira pa mabuku a Mose mpaka mabuku a aneneri onse. Atayandikira kumudzi kumene ankapita, Yesu adachita ngati akupitirira. Koma iwo adamuumiriza kuti, “Mukhale nafe konkuno, poti kwayamba kuda; onani dzuŵa likuloŵa.” Apo Iye adakaloŵa m'nyumba nakakhala nawo. Adaloŵa m'mandamo koma sadaupeze mtembo wa Ambuye Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:4

Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:28

Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:16

Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:6

Tonse tidaasokera ngati nkhosa. Aliyense mwa ife ankangodziyendera. Ndipo Chauta adamsenzetsa iyeyo machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:57-60

Chisisira chitagwa, kudafika munthu wina wolemera, wochokera ku Arimatea, dzina lake Yosefe. Nayenso anali wophunzira wa Yesu. Iyeyu adakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Pilato adalamula kuti ampatse mtembowo. Tsono Yosefe adautenga, naukulunga m'nsalu yoyera yabafuta. Akulu a ansembe aja adatola ndalamazo nati, “Malamulo athu satilola kuika ndalamazi m'bokosi la chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, popeza kuti ndi za magazi.” Adakauika m'manda ake atsopano ochita chosema m'thanthwe. Tsono adagubuduzira chimwala pa khomo kuti atseke pamandapo, nachoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:23-24

Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m'mene Iye amadziŵiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda. Koma Mulungu adammasula ku zoŵaŵa za imfa, namuukitsa kwa akufa, chifukwa kunali kosatheka kuti agonjetsedwe ndi imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:14

Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:19-22

Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake. Ndiponso tili ndi Wansembe wamkulu woyang'anira nyumba ya Mulungu. Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18-20

Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano. Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:55-57

“Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?” Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo. Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:15

Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:2

Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:21

Kuyambira nthaŵi imeneyo Yesu adayamba kudziŵitsa ophunzira ake kuti, “Ndiyenera kupita ku Yerusalemu, kumeneko akulu a Ayuda ndi akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo adzandizunza kwambiri. Ndidzaphedwa koma mkucha wake ndidzauka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ulemerero ndi kukwezedwa kukhale kwanu! Zikomo chifukwa cha nsembe yanu, chochitika chofunika chomwe chinasintha mbiri ya anthu onse. M'sabata lino loyera pamene tikukumbukira nsembe ndi kuuka kwanu, ndikupempha kuti mudziwike mumtima mwa anthu, osati ngati tsiku lokondwerera chabe, koma chaka chonse chomwe tiyenera kukhala moyo wodzipereka kwa inu. Sikuti ndi za tsiku, kapena chipembedzo ndi miyambo, koma za ubale ndi kukumana nanu, kuti tikhale ndi chikhulupiriro chokhazikika pa amene anagonjetsa imfa, anauka ndipo tsopano ali moyo. Mawu anu amati: "Ndipo popeza anaopa, ndipo anaweramitsa nkhope zawo pansi, iwo anati kwa iwo: Muwafuniranji iye amene ali moyo pakati pa akufa?". Ambuye, ndikupemphani kuti mutsegule nzeru za omwe akukufunani pakati pa akufa, kudzera muzithunzi kapena mutapachikidwa pamtengo chifukwa munatsika mtanda ndipo tsopano mumakhala mwa ife kudzera mwa Mzimu Woyera wanu, komanso mukufuna kukhala mumtima mwa aliyense amene akuitana kukhalapo kwanu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa