Ndikufuna ndikuuzeni kuti kuwonetsa Mulungu ndiye chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanga wa utate. Mulungu ndiye chitsanzo chabwino kwambiri cha utate ndi chikondi chomwe ndingathe kuchitsatira.
Monga kholo, ndili ndi udindo wotsogolera banja langa mwauzimu ndi kuyang'anira moyo wauzimu wa aliyense amene ndimakhala naye. Ukwati si dzina lokha ayi, koma ndi kuwonetsa chikondi ndi kukhala moyo wotsatira mawu a Mulungu.
Ambiri angafune kuti akapeza buku lotsogolera pa nkhaniyi, koma lerolino tili ndi chitsogozo chabwino kwambiri. Mukamasakasaka Mulungu, mudzapeza kuunika kwakukulu kuti mudziwe chochita. Yesetsani kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Mulungu tsiku lililonse kuti mukhale ndi ubwenzi wabwino ndi ana anu.
Kulera mwana kumaphatikizapo kuphunzitsa mwanayo malinga ndi msinkhu wake, ndipo izi zimayamba kuyambira ali wakhanda. Yesu akutiphunzitsa kulangiza ana njira yake, yomwe ndiyo njira, choonadi, ndi moyo.
Malinga ndi lemba la Miyambo 22:6, kuti ndikhale kholo labwino ndiyenera kusunga malamulo a Mulungu ndi kumvera mawu ake.
Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.
monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha,
Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ichi nchabwino. Chotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yake. Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba. Mwa ichi mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima chitsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutachita zonse, mudzachilimika. Chifukwa chake chilimikani, mutadzimangira m'chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu; mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha Uthenga Wabwino, Lemekeza atate wako ndi amai ako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano), chifukwa cha umene ndili mtumiki wa m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula. Koma kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndichita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tikiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye; amene ndamtuma kwa inu chifukwa cha ichicho, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu. Mtendere ukhale kwa abale, ndi chikondi, pamodzi ndi chikhulupiriro, zochokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Khristu. Akhale nacho chisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Khristu m'chosaonongeka. kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.
Nthyole ndi chidzudzulo zipatsa nzeru; koma mwana womlekerera achititsa amake manyazi.
Usamane mwana chilango; pakuti ukammenya ndi nthyole safa ai. Udzammenya ndi nthyole, nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda. Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru, mtima wanga wa inedi udzakondwa. Imso zanga zidzasangalala, polankhula milomo yako zoongoka. Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse. Pakutitu padzakhala mphotho; ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.
Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba?
Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga?
Komanso, tinali nao atate a thupi lathu akutilanga, ndipo tinawalemekeza; kodi sitidzagonjera Atate wa mizimu koposa nanga, ndi kukhala ndi moyo?
Miyambo ya Solomoni: Mwana wanzeru akondweretsa atate; koma mwana wopusa amvetsa amake chisoni.
kuti akalangize akazi aang'ono akonde amuna ao, akonde ana ao, akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.
Taonani, nthawi yachitatu iyi ndapukwa ine kudza kwa inu, ndipo sindidzakusaukitsani; pakuti sindifuna zanu, koma inu; pakuti ana sayenera kuunjikira atate ndi amai, koma atate ndi amai kuunjikira ana.
Taonani, ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m'mimba ndicho mphotho yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m'dzanja lake la chiphona. Wodala munthu amene anadzaza nayo phodo lake: sadzachita manyazi iwo, pakulankhula nao adani kuchipata.
Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu; ndipo muziwaphunzitsa mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.
Mwananga, usapeputse mwambo wa Yehova, ngakhale kutopa ndi kudzudzula kwake; pakuti Yehova adzudzula omwe awakonda; monga atate mwana amene akondwera naye.
Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba? Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira? Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?
ndi kuchipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wake wamwamuna, m'njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m'malo muno.
Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.
Chifukwa ndamdziwa iye kuti alamulire ana ake ndi banja lake la pambuyo pake, kuti asunge njira ya Yehova, kuchita chilungamo ndi chiweruziro, kuti Yehova akamtengere Abrahamu chomwe anamnenera iye.
Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wake. Koma pakudza iye kutali atate wake anamuona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa. Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu. Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake; ndipo idzani naye mwanawang'ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere; chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.
Ndipo ngati kutumikira Yehova kukuipirani mudzisankhire lero amene mudzamtumikira, kapena milungu imene anaitumikira makolo anu okhala tsidya lija la mtsinje, kapena milungu ya Aamori amene mukhala m'dziko lao; koma ine, ndi a m'nyumba yanga, tidzatumikira Yehova.
Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake, ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.
M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu;
monga mudziwa kuti tinachitira yense wa inu pa yekha, monga atate achitira ana ake a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni, kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wake wa Iye yekha, ndi ulemerero.
Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.
Mukapirira kufikira kulangidwa Mulungu achitira inu monga ngati ana; pakuti mwana wanji amene atate wake wosamlanga? Koma ngati mukhala opanda chilango, chimene onse adalawako, pamenepo muli am'thengo, si ana ai.
Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha; Tamvera mwananga, nulandire mau anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka. Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru, ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama. Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda; ukathamanga, sudzaphunthwa. Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako. Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa. Pewapo, osapitamo; patukapo, nupitirire. Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera. Pakuti amadya chakudya cha uchimo, namwa vinyo wa chifwamba. Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee. Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa. pakuti ndikuphunzitsani zabwino; musasiye chilangizo changa.
Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m'njira zake. Pakuti udzadya za ntchito ya manja ako; wodala iwe, ndipo kudzakukomera. Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m'mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako. Taonani, m'mwemo adzadalitsika munthu wakuopa Yehova.
Anakhazika mboni mwa Yakobo, naika chilamulo mwa Israele, ndizo analamulira atate athu, akazidziwitse ana ao; Analambulira mkwiyo wake njira; sanalekerere moyo wao usafe, koma anapereka moyo wao kumliri. Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito, ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu. Koma anatulutsa anthu ake ngati nkhosa, nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'chipululu. Ndipo anawatsogolera mokhulupirika, kotero kuti sanaope; koma nyanja inamiza adani ao. Ndipo anawafikitsa kumalire a malo ake oyera, kuphiri ili, dzanja lamanja lake lidaligula. Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao. Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba, osasunga mboni zake; koma anabwerera m'mbuyo, nachita zosakhulupirika monga makolo ao, anapatuka ngati uta wolenda. Ndipo anautsa mtima wake ndi malo amsanje ao, namchititsa nsanje ndi mafano osema. Pakumva ichi Mulungu, anakwiya, nanyozatu Israele; kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao.
Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.
nimupatse Solomoni mwana wanga mtima wangwiro kusunga malamulo anu, mboni zanu, ndi malemba anu, ndi kuchita izi zonse, ndi kumanga chinyumbachi chimene ndakonzeratu mirimo yake.
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro. Taonani, malembedwe akuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini. Onse amene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu. Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu. Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi. Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano. Ndipo onse amene atsatsa chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu. Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen. Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.
Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe; akapanda kusunga mudzi Yehova, mlonda adikira chabe.
Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang'ana iwe.
Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake m'ulemerero mwa Khristu Yesu.